Kulankhulana Muuminisitala Wachikristu
‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.’—MATEYU 28:19.
1. Kodi ndintchito yotani yopatsidwa ndi Kristu imene imasonyeza kufunika kwa kulankhulana?
NTCHITO ya Yesu yotchulidwa pamwambapa, imatipatsa chitokoso chakulankhulana ndi anthu muuminisitala wathu pamene timapita kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, ndikukhala ndi phande m’mbali zonse za kulalikira Ufumu. Ntchito imeneyo imaphatikizapo thayo lakudziŵikitsa chowonadi chonena za Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi Ufumu Waumesiya umene Yesu akulamulira tsopano.—Mateyu 25:31-33.
2. Kuti tilankhulane mogwira mtima, kodi tifunikira chiyani?
2 Kodi ndimotani mmene tingalankhulire mogwira mtima? Choyamba, tiyenera kukhulupirira mawu ameme tikulankhula. Kunena m’mawu ŵena, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu kuti Yehova ndiye Mulungu wowona yekha, kuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu, ndikuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu. Mwanjira imeneyo, zimene timaphunzitsa zidzachokera mumtima, ndipo tidzakhala tikulabadira uphungu wa Paulo kwa Timoteo wakuti: ‘Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a chowonadi.’—2 Timoteo 2:15.
Kulankhulana Kopanda Mawu
3-5. (a) Kodi ndimotani mmene tingalankhulire ngakhale osanena liwu? (b) Kodi ndizokumana nazo zotani zimene zimatsimikizira zimenezi?
3 Kaŵirikaŵiri kulankhulana kumaphatikizapo mawu. Koma, kwenikwenidi, timalankhulana ndi anthu ngakhale tisanakambe nawo. Motani? Mwa kachitidwe kathu ndi njira imene timavalira ndi kupesera. Zaka zingapo zapitazo mishonale womaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anali kuyenda pasitima ya pamadzi kupita ku gawo lake lachilendo. Atayenda masiku angapo panyanja, mlendo wina anamfunsa chifukwa chimene analiri wosiyana kotheratu ndi onse omwe anakwera sitimayo. Mishonaleyo anali kulankhula chinachake chopindulitsa—kuti iye anali ndi miyezo yosiyana ndipo anali wofikirika—mwakawonekedwe kake kokha ndi khalidwe. Izi zinapereka kwa mishonaleyo mwaŵi wabwino wakupereka umboni.
4 Kachiŵirinso, mlongo wina yemwe anaima m’khwalala akumagaŵira mabuku Abaibulo kwa anthu odutsa anamwetulira mwaubwenzi kwa mkazi wina yemwe anadutsa pafupi naye. Mkaziyu anayamba kutsika makwerero onka kusiteshoni yasitima yoyenda pansi panthaka. Ndiyeno anasintha maganizo ake, nabwerera kwa mlongoyo, napempha phunziro Labaibulo lapanyumba. Kodi nchiyani chimene chinamkondweretsa? Ngakhale kuti sanagaŵiridwe bukhu Labaibulo, anamwetuliridwa mwaubwenzi ndi Mboni yomwe inali kuchita ntchito yam’khwalalayo.
5 Chitsanzo chachitatu: Gulu la Mboni zachichepere linali kudya m’lesitilanti ndipo anadabwa pamene mlendo anafika pagome lawo ndikuwalipirira zakudya zawozo. Kodi nchifukwa ninji anachita zimenezo? Iye anakondweretsedwa ndi khalidwe lawo. Popanda kunena liwu kwa mlendoyo, Akristu achichepere ameneŵa analankhula kuti anali anthu owopa Mulungu. Mwachiwonekere, mwa khalidwe lathu, kawonekedwe, ndi ubwenzi, timalankhula ngakhale tisananene liwu.—Yerekezerani ndi 1 Petro 3:1, 2.
Kukambitsirana Nkofunika m’Kulankhulana
6. Fotokozani mwafanizo mmene kukambitsirana kuliri kofunika koposa polankhulana.
6 Kuti tilankhulane mwamawu ndi anthu ponena za mbiri yabwino, tifunikira kukonzekera, osati kulankhula molamula, koma kukambitsirana nawo. Timaŵerenga mobwerezabwereza kuti Paulo anakambitsirana ndi awo amene anayesa kuwapatsa mbiri yabwino. (Machitidwe 17:2, 17; 18:19) Kodi ndimotani mmene tingatsanzirire chitsanzo chake? Eya, mikhalidwe yomaipirabe yadziko ingapangitse ena kukaikira kukhalako kwa Mulungu wamphamvuyonse wachikondi amene amasamalira anthu. Komabe, tingakambitsirane nawo kuti Mulungu ali ndi nthaŵi ya kanthu kalikonse. (Mlaliki 3:1-8) Chifukwa chake, Agalatiya 4:4 amanena kuti pamene nthaŵi yoikika ya Mulungu inafika, anatumiza Mwana wake padziko lapansi. Izi zinachitika patapita zaka zikwi zambiri kuyambira pamene analonjeza kwa nthaŵi yoyamba kuchita zimenezo. Mofananamo, nthaŵi yake yoikika ikadzafika, adzathetsa kuvutika ndi kuipa. Ndiponso, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Mulungu ali ndi zifukwa zabwino zakulolera kuipa kupitiriza kwa nthaŵi yaitali. (Yerekezerani ndi Eksodo 9:16.) Kukambitsirana zimenezi, ndi kuchilikiza kukambitsirana kumeneko ndi mafanizo ndi umboni wamphamvu Wamalemba, kudzathandiza owona mtima kuzindikira kuti kuchuluka kwa kuipa sikungagwiritsiridwe ntchito monga maziko a chitsutso chakuti Yehova kulibeko kapena samasamala.—Aroma 9:14-18.
7, 8. Kodi ndimotani mmene kukambitsirana kungatithandizire kulankhula ndi Myuda Wamwambo?
7 Bwanji ngati pamene mukupita kunyumba ndi nyumba, mwininyumba anena kwa inu kuti: “Ndine Myuda. Sindiri wokondweretsedwa.” Kodi mungapitirize motani? Mbale wina akusimba za chipambano mwakugwiritsira ntchito mafikiridwe aŵa: ‘Nditsimikiza kuti mudzagwirizana nane kuti Mose anali mmodzi wa aneneri aakulu koposa amene Mulungu anagwiritsirapo ntchito. Ndipo kodi mumadziŵa kuti iye ananena motere pa Deuteronomo 31:29: ‘Pakuti ndidziŵa kuti nditamwalira ine . . . mudzapatuka m’njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa’? Mose anali mneneri wowona, chotero mawu ake anayenera kukwaniritsidwa. Kodi tinganene kuti mawuwo anakwaniritsidwa pamene Mulungu anatumiza Mesiya kwa Ayuda ndipo chimenecho ndicho chifukwa chake Ayuda sanamlandire? Zimenezi zingakhale zimene zinachitika. Tsopano ngati ndizo zinachitika ndipo anali olakwa, kodi chimenecho chingakhale chifukwa chimene inuyo ndi ine tiyenera kupangira cholakwa chofananacho?’
8 Kumbukiraninso kuti Ayuda avutitsidwa kwambiri ndi Chikristu Chadziko, makamaka m’zaka za zana lino. Chotero mungakonde kuuza mwininyumbayo kuti sitinatengeko mbali. Mwachitsanzo, mungafune kunena kuti: ‘Kodi mumadziŵa kuti pamene Hitler anali kulamulira, Mboni za Yehova zinatsutsa kukana kwake Ayuda? Nazonso zinakana kunena kuti “Heil Hitler” ndi kutumikira m’gulu lake lankhondo.’a
9, 10. Kodi ndimotani mmene kukambitsirana kungagwiritsiridwe ntchito kuthandiza munthu yemwe amakhulupirira moto wahelo?
9 Pokalamira kulankhula ndi munthu amene amakhulupirira moto wahelo, mungakambitsirane kuti ngati munthu ayenera kuvutika kwamuyaya m’helo, iye ayenera kukhala ndi moyo wosakhoza kufa. Munthu wokhulupirira moto waheloyo adzavomereza msanga. Ndiyeno mungatchule cholembedwa cha kulengedwa kwa Adamu ndi Hava ndikumfunsa mokoma mtima ngati wawona kuti cholembedwacho chikutchula za moyo wosakhoza kufa woterowo. Popitiriza kukambitsirana kwanu, mungapereke chidwi chake ku Genesis 2:7, pamene Baibulo limatiuza kuti Adamu anakhala wamoyo. Ndipo tawonani chimene Mulungu ananena kuti chikakhala chotulukapo cha tchimo la Adamu: ‘M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.’ (Genesis 3:19) Chotero, Adamu moyowo anabwerera kufumbi.
10 Mungasumikenso chidwi ku chenicheni chakuti palibe pena paliponse m’cholembedwa cha Genesis pamene Mulungu amatchula za kuvutika kosatha m’moto wahelo. Pamene Mulungu anachenjeza Adamu kusadya chipatso choletsedwacho, iye anati: “Tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Sanatchule moto wahelo! Ngati chotulukapo chenicheni cha kuchimwa kwa Adamu sichikanakhala imfa, ‘kubwerera kufumbi,’ koma kuvutika kwamuyaya, kodi Mulungu m’chiweruzo chake cholungama sakanafotokoza zimenezi momvekera bwino? Chifukwa chake, kukambitsirana kosamalitsa ndi kokoma mtima kungathandize munthu wowona mtima kuwona kulakwika kwa chikhulupiriro chake. Tisanyalanyaze konse kufunika kwa kukambitsirana pamene tikugaŵana chowonadi cha Mawu a Mulungu ndi ena.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:24-26; 1 Yohane 4:8, 16.
Mikhalidwe Yofunika pa Kulankhulana Kogwira Mtima
11-13. Kodi ndimikhalidwe Yachikristu yotani imene ingatithandize kulankhulana mogwira mtima?
11 Tsopano, kodi ndimikhalidwe yotani imene tiyenera kukulitsa kuti tilankhule chowonadi Chaufumu mogwira mtima koposa? Eya, kodi chitsanzo cha Yesu chimatiuzanji? Pa Mateyu 11:28-30, timaŵerenga mawu ake motere: ‘Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.’ Mmenemo tikuwona imodzi ya mfungulo za chipambano cha Yesu m’kulankhula. Anali wofatsa ndi wodzichepetsa mtima. Anthu owongoka mtima anapeza kuti iye anali wodzetsa mpumulo. Mtumwi Paulo anakhazikitsanso chitsanzo chabwino, popeza kuti, monga momwe anauzira akulu ochokera ku Efeso, kuyambira tsiku loyamba limene anafika kwa iwo, iye anali kutumikira Ambuye ‘ndi kudzichepetsa konse.’—Machitidwe 20:19.
12 Mwakusonyeza kwathu kudekha ndi kudzichepetsa nthaŵi zonse, ena adzapeza kuti nafenso tiri odzetsa mpumulo, ndipo kudzakhala kosavuta kwa ife kulankhula nawo. Mkhalidwe wina uliwonse mwachidziŵikire ukaika chochinga pakati pa ife ndi awo amene tikuyesayesa kulankhula nawo. Zowonadi, ‘nzeru iri ndi odzichepetsa.’—Miyambo 11:2.
13 Kuti tipereke chidziŵitso mogwira mtima, tiyeneranso kukhala oleza mtima ndi ochenjera. Mtumwi Paulo analidi wochenjera pamene anachitira umboni kwa anthanthi osonkhana pamaso pake pa Phiri la Mars. Iye anapereka mbiri yabwino m’njira imene iwo anamvetsetsa. (Machitidwe 17:18, 22-31) Ngati tikufuna kulankhula mwachipambano ndi amvetseri athu, tiyenera kulabadira uphungu umene mtumwi Paulo anapereka kwa Akolose pamene ananena kuti: “Lolani kuti kukambitsirana kwanu nthaŵi zonse kukhale kwachisomo, ndipo osati kosukuluka konse; phunzirani mmene mungalankhulire bwino koposa ndi munthu aliyense amene mukumana naye.” (Akolose 4:6, The New English Bible) Nthaŵi zonse kalankhulidwe kathu kayenera kukhala kabwino. Kalankhulidwe koteroko kadzatsegula maganizo a amvetseri athu, pamene kuli kwakuti ndemanga zosalingalira zikaŵapangitsa kutseka maganizo awo.
14. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe womasuka, wakukambitsirana ungatithandizire kulankhula ndi ena?
14 Timafuna kuwonekera omasuka nthaŵi zonse. Ichi chimathandiza kumasula amvetseri athu. Kukhala womasuka kumatanthauza osati kukhala wofuna kulankhula tokha basi. M’malomwake, ndi mkhalidwe wosafulumira ndi mafunso aubwenzi, timapatsa amvetseri athu mwaŵi wakufotokoza zakukhosi kwawo. Makamaka pamene tikuchitira umboni mwamwaŵi kuli kwanzeru kulimbikitsa munthu winayo kulankhula. Mwachitsanzo, Mboni ina inakhala pampando umodzi ndi wansembe wa Roma Katolika mu ndege. Kwanyengo yoposa ola limodzi, Mboniyo inapitiriza kufunsa wansembeyo mafunso ochenjera, ndipo wansembeyo, poyankha, ndiye analankhula kwa nthaŵi yaitali. Koma pamene nthaŵi yoti alekane inafika, wansembeyo anali atatenga mabuku angapo Abaibulo. Kafikidwe koleza mtima koteroko kadzatithandiza kusonyeza mkhalidwe wina wofunikira, ndiwo chisomo.
15, 16. Kodi ndimotani mmene chisomo chingatithandizire polankhulana?
15 Chisomo chimatanthauza kudziika m’malo mwa ena. Mtumwi Paulo anazindikira mokwanira kufunika kwa chisomo, monga momwe zingawonedwere ku zimene analembera Akorinto: ‘Pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadziloŵetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindikhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo; kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo. Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.’—1 Akorinto 9:19-22.
16 Kuti titsanzire mtumwi Paulo m’mbali zimenezi, tifunikira kukhala ochenjera, ozindikira, ndi akuthwa maso. Chisomo chidzatithandiza kulankhula chowonadi kwa amvetseri athu mogwirizana ndi njira yawo yakuganiza ndi kukambitsirana. Bukhu lakuti Kukambitsirana za m’Malemba limapereka chithandizo chochuluka m’nkhaniyi. Khalani nalo nthaŵi zonse muuminisitala wanu.
Chikondi—Thandizo m’Kulankhulana
17. Pa mikhalidwe yonse Yachikristu, kodi ndiuti umene uli wofunika koposa m’kulankhula chowonadi mogwira mtima, ndipo kodi umasonyezedwa motani?
17 Kudekha, kudzichepetsa, kuleza mtima, ndi chisomo nzofunika m’kulankhulana mogwira mtima popereka chidziŵitso. Komabe, choposa zonse chimene chidzatithandiza kukhala achipambano m’kufikira mitima ya ena ndicho chikondi chopanda dyera. Yesu anachita chifundo ndi anthu chifukwa chakuti anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” Chinali chikondi chimene chinamsonkhezera Yesu kunena kuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 9:36; 11:28) Nafenso timafuna kupumulitsa anthu ndi kuwathandiza kuloŵa pamsewu wopita kumoyo chifukwa chakuti timaŵakonda. Uthenga wathu ngwachikondi, chotero tiyeni tipitirize kuupereka m’njira yachikondi. Chikondi chimenechi chimawonekera mwakumwetulira kwaubwenzi, kukoma mtima ndi kudekha, chimwemwe ndi kutentha.
18. Kodi tingamutsanzire motani Paulo, monga momwe anatsanzirira Mbuyeyo?
18 M’mbali imeneyi mtumwi Paulo anali wotsanzira wabwino wa Mbuye wake, Yesu Kristu. Kodi nchifukwa ninji anali wachipambano koposa nkuyambitsa mpingo umodzi pambuyo pa unzake? Chifukwa cha changu chake? Inde. Komanso nchifukwa cha chikondi chimene anasonyeza. Onani mafotokozedwe ake achikondi ponena za mpingo watsopano wa Tesalonika: ‘Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m’mene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu siuthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.’ Kutsanzira Paulo kudzatithandiza m’zoyesayesa zathu za kulankhulana.—1 Atesalonika 2:7, 8.
19. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulola gawo losabala zipatso kutikhwethemula?
19 Ngati tachita zimene tingathe m’kulankhula ndipo talephera kututa zotulukapo zokhumbidwa, kodi tiyenera kukhwethemulidwa? Kutalitali. Ophunzira Baibulo (monga momwe Mboni za Yehova zinali kudziŵikira kalelo) ankanena kuti, kuti avomereze chowonadi, anthu ayenera kukhala ndi mikhalidwe itatu. Iwo ayenera kukhala owona mtima, odzichepetsa, ndi anjala yauzimu. Sitingayembekezere anthu osawona mtima kuvomereza chowonadi mwachiyanjo; ndiponso sitingayembekezere anthu odzitukumula kapena onyada kumvetsera ku mbiri yabwino. Ndiponso, ngakhale ngati munthu angakhale wowona mtima ndi wodzichepetsa, iye sadzavomereza chowonadi ngati alibe njala yauzimu.
20. Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zonse kunganenedwe kuti zoyesayesa zathu sizinapite pachabe?
20 Mosakaikira anthu ambiri amene munakumana nawo m’gawo lanu adzakhala opanda mkhalidwe umodzi kapena yochulukirapo ya mikhalidwe itatu imeneyi. Mneneri Yeremiya anali ndi chokumana nacho chofananacho. (Yeremiya 1:17-19; yerekezerani ndi Mateyu 5:3.) Chikhalirechobe, zoyesayesa zathu sizidzapita pachabe. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikulengeza dzina la Yehova ndi Ufumu wake. Mwakulalikira kwathu ndikufika kwathu pamakomo, timaŵachenjeza oipa. (Ezekieli 33:33) Ndipo musaiwale konse kuti mwa kuyesayesa kwathu kulankhula chowonadi ndi ena, timapindula nafenso. (1 Timoteo 4:16) Timalimbitsa chikhulupiriro chathu ndikusunga chiyembekezo chathu cha Ufumu kukhala chowala. Ndiponso, timasunga umphumphu wathu ndipo chotero timakhala ndi phande m’kuyeretsa dzina la Yehova Mulungu, kukondweretsa mtima wake.—Miyambo 27:11.
21. Kodi tinganene chiyani mwachidule?
21 Mwachidule: Kulankhulana ndiko kupereka chidziŵitso kogwira mtima. Luso lakulankhulana liri lofunika koposa, ndipo pamene kulankhulana kulekeka, pangakhale chivulazo chachikulu. Tawona kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ali olankhula aakulu koposa ndikuti Yesu Kristu anapereka ngalande yolankhulira m’tsiku lathu. Tawonanso kuti mwa kapesedwe kathu ndi khalidwe, timalankhula, kutumiza mauthenga kwa ena. Taphunzira kuti kukambitsirana kumachita mbali yofunika koposa m’kuyesayesa kwathu kulankhula ndi anthu ndipo kuti tilankhulane mogwira mtima, tifunikira kukhala odekha ndi odzichepetsa, kusonyeza chisomo, kukhala oleza mtima, ndipo kuposa zonse, kusonkhezeredwa ndi mtima wodzaza ndi chikondi. Ngati tikulitsa mikhalidwe imeneyi ndikutsatira zitsanzo za m’Baibulo, tidzakhala olankhula Achikristu achipambano.—Aroma 12:8-11.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze malingaliro owonjezereka a mmene mungalankhulire ndi Ayuda okhulupirira ndi ena, onani Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 21-4.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene kulankhulana kumayambira mawu asanalankhulidwe?
◻ Kodi nziti zomwe ziri zitsanzo zina za kulankhulana mwakukambitsirana kogwira mtima?
◻ Kodi ndimikhalidwe yotani imene inatheketsa Yesu Kristu ndi Paulo kulankhula mogwira mtima?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhwethemulidwa ngati zotulukapo zikuchedwa?