Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mwamuna
“Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha.”—AEFESO 5:33.
1, 2. (a) Ndi ku ukulu wotani kumene kusudzulana kuliri vuto m’dziko lerolino? (b) Mosiyanako, ndi mkhalidwe wina uti womwe ulipo?
PAKATI pa ma 1980, Psychology Today inasimba kuti: “Okwatirana oposa miliyoni imodzi pa chaka [mu U.S.A.] tsopano amathetsa ziyembekezo zawo za chimwemwe m’kusudzulana; avereji ya utali wa ukwati mu United States iri zaka 9.4. . . . Ndithudi, chimawoneka pa nthaŵi zina kuti palibe wina aliyense kunja kumeneko yemwe ali wokwatira mwachimwemwe.” (June 1985) Kulingalira achikulire limodzinso ndi ana, chimenecho chimafikira ku chifupifupi anthu 3,000,000 pa chaka oyambukiridwa ndi ukwati wosweka mu kokha dziko limodzi. Koma kusudzulana kuli vuto la dziko lonse, chomwe chimasonyeza kuti chikondi ndi ulemu zikusoweka mu maukwati mamiliyoni angapo.
2 Ku mbali ina, pali “gulu lina [limene] limawonekera kunyalanyazidwa: okwatirana aja amene mwanjira inayake amakhoza kukhala pamodzi, omwe samalola china chirichonse kuposa imfa yeniyeniyo kuwapasula iwo.” (Psychology Today) Chotero, palinso mamiliyoni a okwatirana omwe amagwira ntchito zolimba kusunga ukwati wawo pamodzi.
3. Kodi ndi mafunso otani omwe tingadzifunse ife eni?
3 Kodi ukwati wanu uli bwanji? Kodi pali kudzimva kotentha kwa chikondi ndi ulemu pakati pa mwamuna ndi mkazi? Kodi chikondi choterocho chiripo pakati pa makolo ndi ana m’banja lanu? Kapena kodi nthaŵi zina mumadzipeza inu eni mukuyenda m’njira yosalekeka ya kukwiyitsana ndi kusakhulupirirana? Popeza kuti palibe aliyense wa ife amene ali wangwiro, mikhalidwe yovuta ingabuke m’nyumba iriyonse, ngakhale kumene onse akuyesera kukhala Achikristu, popeza kuti “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.
4. Ndimotani mmene Paulo ndi Petro akusonyezera yemwe ali ndi thayo lalikulu m’banja lachimwemwe?
4 M’chiyang’aniro cha chenicheni chakuti mavuto angabuke m’nyumba iriyonse, ndani yemwe ali ndi thayo lokulira m’kusunga banja m’njira ya mtendere ndi yogwirizana? Atumwi Paulo ndi Petro akupereka yankho mu uphungu wachindunji wopezeka m’makalata awo. Paulo analemba kuti: “Ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa [mwamuna aliyense, NW] ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Iye ananenanso kuti: “Ndi kumverana wina ndi mnzake m’kuwopa Kristu. Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW].” (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:21-23) Mu mkhalidwe umodzimodziwo, Petro analemba kuti: “Momwemonso [kutsatira chitsanzo cha Kristu], akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha.”—1 Petro 2:21-3:1.
Kristu—Chitsanzo Chodzetsa Mpumulo
5, 6. Ndimotani mmene Yesu Kristu aliri chitsanzo m’kusonyeza umutu?
5 M’chigwirizano ndi uphungu womwe wangotchulidwa kumenewo, mwamuna ndiye mutu wa m’Malemba wa banja. Koma kodi ndi m’lingaliro lotani mmene iye aliri mutu? Ndimotani mmene umutu uyenera kuchitidwira? Amuna ena angachipeze icho kukhala chopepuka kufuna ulemu mwa kuwumirira kuti iwo ali ‘mutu wa nyumba, ndipo Baibulo limanena tero.’ Koma kodi ndimotani mmene chimenecho chimalinganirana ndi chitsanzo cha Kristu? Kodi Kristu monyada anafuna ulemu kuchokera kwa atsatiri ake? Kodi tingapeze nthaŵi iriyonse pamene iye ananena modzitukumula kuti: “Ndani yemwe ali Mwana wa Mulungu pano? Mufunikira kundilemekeza ine!” Mosiyanako, Yesu anapeza ulemu. Motani? Mwa chitsanzo chake chabwino mu mkhalidwe, kalankhulidwe, ndi kachitidwe kachifundo kwa ena.—Marko 6:30-34.
6 Chotero mfungulo ku kusonyeza umuto moyenera monga mwamuna ndi tate iri kutsatira chitsanzo cha Yesu Kristu. Ngakhale kuti Yesu sanakwatirepo, njira imene anachitira ndi ophunzira ake iri chitsanzo kaamba ka amuna. Chimenecho motsimikizirika chimapereka chitokoso kwa mwamuna aliyense, popeza kuti Yesu ali chitsanzo changwiro. (Ahebri 4:15; 12:1-3) Mosasamala kanthu za chimenecho, kuyandikira kumene mwamuna amadza ku chitsanzo cha Kristu, kudzakhalanso kuzama kwa chikondi ndi ulemu zimene iye adzasonyezedwa. Chotero, tiyeni tiyang’ane moyandikira kwenikweni mtundu wa munthu amene Yesu anali.—Aefeso 5:25-29; 1 Petro 2:21, 22.
7. Nchiyani chimene Yesu anapereka kwa atsatiri ake, ndipo kuchokera ku magwero otani?
7 Pa chochitika china, Yesu ananena kwa khamu kuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” Tsopano, nchiyani chimene Yesu anapatsa amvetseri ake? Mpumulo wauzimu! Koma kodi mpumulowo ukachokera ku magwero otani? Iye anali atangonena kuti: “Palibe wina adziŵa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.” Ichi chinasonyeza kuti Yesu akakhoza kupereka mpumulo wauzimu mwa kuvumbula Atate wake kwa atsatiri ake owona. Koma ndemanga za Yesu zinasonyezanso kuti mpumulo ukadza kuchokera m’kuyanjana ndi iye, popeza kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.”—Mateyu 11:25-30.
Mmene Mungakhalire Amuna ndi Atate Odzetsa Mpumulo
8. Ndi m’njira zotani mmene mwamuna ndi atate angakhalire wodzetsa mpumulo?
8 Mawu a Yesu amatithandiza ife kuwona kuti mwamuna Wachikristu ayenera kukhala wodzetsa mpumulo ku banja lake ponse paŵiri m’njira zauzimu ndi zaumwini. Ndi chitsanzo cha kufatsa kwake ndi kuphunzitsa, iye ayenera kuthandiza banja lake kudziŵa Atate wakumwamba bwino lomwe. Mkhalidwe wake uyenera kuwunikira malingaliro ndi kachitidwe ka Mwana wa Mulungu. (Yohane 15:8-10; 1 Akorinto 2:16) Chiri chodzetsa mpumulo kwa onse m’banja kuyanjana ndi mwamuna woteroyo chifukwa chakuti ali mwamuna wokonda, atate, ndi bwenzi. Iye ayenera kukhala wofikirika ndi kusakhala wotanganitsidwa kwenikweni kaamba ka kufunsidwa. Ndithudi, iye ayenera kudziŵa mmene angamvetserere, osati kokha kumva.—Yakobo 1:19.
9. Ndi vuto lotani limene nthaŵi zina limayambukira akulu mu mpingo?
9 Ichi chimabweretsa kumaganizo vuto limene nthaŵi zina limayambukira akulu mu mpingo ndi m’mabanja awo. Mkulu kaŵirikaŵiri amakhala wotanganitsidwa kusamalira zosoŵa zauzimu za mpingo. Iye ayenera kukhazikitsa chitsanzo chabwino m’chigwirizano ndi misonkhano Yachikristu, utumiki, ndi ntchito yoŵeta. (Ahebri 13:7, 17) Ngakhale kuli tero, akulu ena, m’chenicheni, adzitopetsa iwo eni kaamba ka mpingo. M’kupita kwa nthaŵi iwo anyalanyaza mabanja awo, nthaŵi zina ndi zotulukapo zowawitsa. Mu nkhani imodzi mkulu anali wotanganitsidwa kwambiri kuti aphunzire ndi mwana wake wamwamuna. Iye anakonzekera winawake kuchita iko!
10. Ndimotani mmene akulu angakhalire olinganizika m’kusamalira umutu wawo mu mpingo ndi kunyumba?
10 Kodi nchiyani chimene chokumana nacho chimenechi chikugogomezera? Kufunika kwa mwamuna kusungirira kulinganiza pakati pa mathayo a mpingo ndi aja a mkazi wake ndi banja. Mwachitsanzo, pambuyo pa misonkhano akulu kaŵirikaŵiri amakhala otanganitsidwa ndi mavuto ndi kukambitsirana. Ngati chiri chotheka ndi chogwira ntchito, kodi sichikakhala chodzetsa mpumulo kwa mkulu woteroyo kupanga makonzedwe kaamba ka winawake kuti atenge mkazi wake ndi ana ku nyumba, m’malo mwa kuwalola iwo kuyembekeza kwa maora angapo m’Nyumba ya Ufumu? M’chigwirizano ndi zofunika za Baibulo, chinganenedwe kuti ‘kuŵeta kumayambira panyumba.’ Ngati mkulu anyalanyaza banja lake, iye angaike pangozi kuikidwa kwake. Chotero, akulu, khalani olingalira ndipo ganizirani zosoŵa za m’malingaliro, uzimu, ndi zina za banja lanu.—1 Timoteo 3:4, 5; Tito 1:5, 6.
11, 12. Ndimotani mmene mwamuna Wachikristu angapezere chirikizo la banja lake, ndipo ndi mafunso otani amene mwamuna aliyense angadzifunse iyemwini?
11 Mwamuna Wachikristu wodzetsa mpumulo sadzakhalanso wogwiritsira ntchito mphamvu molakwa kapena wankhalwe, kupanga zigamulo popanda kufunsa banja lake. Mwinamwake chigamulo chiyenera kupangidwa m’chigwirizano ndi kusintha kwa ntchito kapena malo a nyumba kapena ngakhale nkhani yopepuka yonga zosangulutsa za banja. Popeza kuti ziŵalo zonse za banja zidzayambukiridwa, kodi sichikakhala chanzeru ndi chachifundo kufunsa onsewo? Malingaliro awo angamuthandize iye kufika pa chigamulo, chanzeru, cholingalira kwenikweni. Kenaka chidzakhala chopepuka kwa onse m’banja kumuchirikiza iye.—Yerekezani ndi Miyambo 15:22.
12 Kuchokera ku zomwe zatchulidwazo, chiri chowonekera kuti mwamuna Wachikristu ndi atate sali kokha munthu wopereka chilango m’nyumba. Iye ayenera kukhalanso wodzetsa mpumulo. Amuna ndi atate, kodi muli onga Kristu? Kodi muli odzetsa mpumulo ku banja lanu?—Aefeso 6:4; Akolose 3:21.
Kukhala Monga mwa Chidziŵitso
13. Petro akupereka uphungu wabwino wotani kwa amuna?
13 Monga momwe zawonedwera kale, ponse paŵiri Petro ndi Paulo amapereka uphungu wabwino kwa okwatirana. Pokhala mwamuna wokwatira, Petro anali ndi mwaŵi woŵirikiza kaŵiri mu uphungu wake—chokumana nacho ndi chitsogozo cha mzimu woyera. (Mateyu 8:14) Iye analunjikitsa uphungu wachindunji kwa amuna onse, akumanena kuti: “Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu [chachikazi, NW].” Kutembenuza kopeputsidwa kochitidwa ndi J. W. C. Wand kumaŵerenga kuti: “Amuna mwa njira yofananayo ayenera kugwiritsira ntchito maprinsipulo Achikristu ndi luntha ku unansi wawo ndi akazi awo.”—1 Petro 3:7.
14. Ndi mafunso otani omwe tsopano akubuka?
14 Tsopano, nchiyani chomwe chimatanthauza kukhala ndi mkazi “monga mwa chidziŵitso” kapena “kugwiritsira ntchito maprinsipulo Achikristu ndi luntha”? Ndimotani mmene mwamuna angaperekere ulemu kwa mkazi wake? Ndithudi, ndimotani mmene mwamuna Wachikristu ayenera kumvetsera uphungu wa Petro?
15. (a) Nchifukwa ninji maukwati ena amalephera? (b) Nchiyani chomwe chiri chitokoso chenicheni mu ukwati?
15 Maukwati ambiri azikidwa kokha pa maziko a kuthupi ndi kukoka kwa kugonana. Komabe, ukwati wosatha sungatsimikiziridwe pa maziko a kuwoneka bwino kokha, popeza kuti izi ziri zosakhalitsa. Imvi ndi makwinya potsirizira pake zimabwera kwa awo amene akhala okwatirana kwa zaka zambiri. Koma kumbukirani kuti ukwati uli kugwirizanitsa kwa maganizo aŵiri, maumunthu aŵiri, zizoloŵezi za kumbuyo ziŵiri ndi unyinji wa mapindu auzimu, ndi malirime aŵiri. Ichi chimapereka chitokoso ndithu! Komabe, kumvetsetsa chimenechi kuli kofunika ku ukwati wachimwemwe.—Miyambo 17:1; 21:9.
16. ‘Kukhala naye monga mwa chidziŵitso’ kumaphatikizapo chiyani?
16 Pakati pa zinthu zina, kuti mwamuna Wachikristu akhale ndi mkazi wake “monga mwa chidziŵitso” chimatanthauza kuti iye ndithudi afunikira kumvetsetsa zosoŵa za mkaziyo. Izi siziri kokha zosoŵa zakuthupi koma, chofunika koposa, zosoŵa zake zamalingaliro, maganizo, ndi uzimu. Ngati iye ‘akhala ndi mkaziyo monga mwa chidziŵitso,’ iye adzamvetsetsa thayo lake lopatsidwa ndi Mulungu. Chidzatanthauzanso kuti iye amalemekeza ulemu wachikazi wa mkaziyo. Ichi chiri kokha chosiyana ndi kawonedwe kosungidwa ndi Osadziŵa ena m’tsiku la Petro, pakati pa amene “akazi ananyalanyazidwa monga zolengedwa zapansi, zaunyama, ndi zopanda udongo.” (The Anchor Bible) Kutembenuza kwamakono kwa Chispanish kumaika mawu a Petro motere: “Ponena za amuna: khalani ndi kuchenjera m’moyo wanu wogawana, mukumasonyeza kulingalira kaamba ka mkaziyo, chifukwa cha kukhala kwake wa kapangidwe kosalimba kwenikweni.” (Nueva Biblia Española) Ichi chimapanga nsonga yabwino imene amuna nthaŵi zina amaiŵala.
17. (a) Pakati pa zochititsa zina, nchiyani chomwe chikuphatikizidwa mu “kapangidwe kosalimba” ka ‘chotengera chachikazi chochepa mphamvu? (b) Ndi njira imodzi iti imene mwamuna angasonyezere ulemu kaamba ka ulemu wa mkazi wake?
17 Nchifukwa ninji mkazi ali “wa kapangidwe kosalimba kwenikweni”? Pakati pa zinthu zina, chiri chifukwa cha mphatso yake ya kubala ana. Moyo wake wobala ana uli wogonjetseredwa ku kusamba komwe kumaphatikiza nyengo ya masiku angapo pamene angakhale akudzimva mwa njira inayake wokhala ndi polekezera kapena wokhala pansi pa kutsenderezedwa. Ngati mwamuna alephera kuika ichi m’malingaliro ndi kupanga zokhumba zofananazo pa mkazi wake tsiku lirilonse la mwezi, iye adzalephera kulemekeza ulemu wa mkaziyo. Mwanjira imeneyo iye adzakhala akusonyeza kuti amakhala ndi iye monga mwa umbuli wadyera, mmalo mwa chidzŵitso.—Levitiko 18:19; 1 Akorinto 7:5.
Kupereka Ulemu ku Chotengera Chachikazi
18. (a) Ndi m’chizoloŵezi choipa chiti mmene okwatirana ena amagwera? (b) Ndimotani mmene mwamuna Wachikristu afunikira kuchitira?
18 Njira ina mu imene mwamuna angasonyezere chikondi ndi ulemu kaamba ka mkazi wake iri mwa kusonyeza ndi kulongosola kuyamikira kaamba ka iye ndi mikhalidwe yake. Mwamuna angagwere m’chizoloŵezi chopanga ndemanga zosakomera ponena za mkazi wake kapena kumupanga iye kukhala chandamali cha maseŵera ake oseka. Mwinamwake mwamuna woteroyo amaganiza kuti ichi chimathandizira kumuika iye m’kuwunika kwabwino koposa. M’chenicheni, ngakhale kuli tero, chiyambukiro chimakhala chosiyanako, popeza ngati iye mokhazikika amapanga mkazi wake kuwoneka chitsiru, funso lodziwikiratu liri lakuti: Nchifukwa ninji anakwatira mkazi wopusa chotero? Ndithudi, chikawoneka kuti kokha mwamuna wopanda chisungiko ndi yemwe akatembenukira ku machenjera oterowo. Mwamuna wokonda amalemekeza mkazi wake.—Miyambo 12:18; 1 Akorinto 13:4-8.
19. Nchifukwa ninji sichikakhala cholondola kwa mwamuna kupeputsa mkazi wake?
19 M’maiko ena, amuna ali ndi mwambo wa kupeputsa akazi awo monga mkhalidwe wa kuwoneka kukhala wodekha. Mwachitsanzo, mwamuna wa Chijapan adzadziŵitsa mkazi wake ndi liwu lakuti “Gusai,” lomwe limatanthauza ‘mkazi wopusa kapena chitsiru.’ Cholinga cha ichi chiri chakuti munthu winayo ayenera kulinganiza mkhalidwewo ndi ndemanga yolinganako ponena za mkaziyo. Ngati mwamuna Wachikristu apanga mtundu umenewu wa kuwunikira, kodi iye ndi ndithudi ‘akupereka ulemu’ kwa mkazi wake monga mmene Petro anaperekera uphungu? Kuyang’ana nkhanizo kuchokera ku mbali ina, kodi iye akulankhuladi chowonadi kwa mnansi wake? Kodi iye mowonadi amakhulupirira kuti mkazi wake ali chitsiru?—Aefeso 4:15, 25; 5:28, 29.
20. (a) Ndi mkhalidwe wotsutsana wotani womwe ungayambike pakati pa mwamuna ndi mkazi? (b) Ndimotani mmene ungapewedwere?
20 Nthaŵi zina mwamuna adzasonyeza kusoŵeka kwa chikondi ndi ulemu kokha mwa kuiwala kuti mkazi wake alinso mlongo wake Wachikristu, osati kokha m’Nyumba ya Ufumu komanso kunyumba ndi pa chochitika chirichonse. Ndi chopepuka chotani nanga kukhala wachifundo ndi wodekha pa holo ndi kukhala wosalamulirika ndi wankhalwe kunyumba! Chotero ndi woyenerera chotani nanga uphungu wa Paulo! Iye analemba kuti: “Tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.” “Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.” (Aroma 14:19; 15:2) Kulibe mnansi wapafupi kwenikweni kuposa mwamuna kapena mkazi.
21. Nchiyani chimene amuna angachite kulimbikitsa akazi awo?
21 Chotero, mwamuna wokonda Wachikristu adzasonyeza kuyamikira kaamba ka mkazi wake mwa mawu ndi zochita. Monga mmene wolemba ndakatulo wosadzitchula dzina anachilongosolera icho kuti:
“Pakati pa kusamalira kwa ndewu za mu ukwati
Mosasamala kanthu za kutopa ndi moyo wa zamalondazi
Ngati mumamuŵerengera mkazi wanu wokondekadi—
Muwuzeni iye tero! . . .
Inu muli wake ndipo wake yekha;
Inu mumadziŵa bwino lomwe kuti iye ali wanokha;
Musadikire kuzokota icho pa mwala—
Muwuzeni iye tero!”
Nsonga zimenezi zikuchilikizidwa mowonekera bwino ndi amayi a Mfumu yakale Lemueli. M’mbali, iye analongosola mkazi wabwino koposa m’mawu awa: “Ana ake amuna ndi cholinga chimodzi amamutcha mkaziyo chimwemwe; mwamuna wakenso, ndipo amaimba zitamando zake: ‘Akazi ambiri amasonyeza mmene iwo aliri othekera; koma iwe umapambana onsewo.’” (Miyambo 31:1, 28, 29, The New English Bible) Amuna, kodi mumatamanda akazi anu mokhazikika, kapena kodi chimenecho chinali kokha cha popalana ubwenzi?
22, 23. Ndi pachiyani pamene ukwati wachipambano wazikidwa?
22 Kuchokera pa kulingalira kwachidule kumeneku, chiri chowonekera kuti kwa mwamuna kuti asonyeze chikondi ndi ulemu mu ukwati wake, sichiri chokwanira kokha kubweretsa malipiro kunyumba. Ukwati wachipambano umazikidwa pa unansi wokondeka, wokhulupirika, ndi wolingalira. (1 Petro 3:8, 9) Pamene zaka zipita, unansi umenewu uyenera kuzama pamene mwamuna ndi mkazi ayamikira maubwino a wina ndi mnzake ndi nyonga ndi kuphunzira kunyalanyalaza ndi kukhululukira zifooko za wina ndi m’nzake.—Aefeso 4:32; Akolose 3:12-14.
23 Ngati mwamuna atenga chitsogozo m’kusonyeza chikondi ndi ulemu, banja lonse lidzadalitsidwa. Koma kodi ndi thayo lotani limene mkazi Wachikristu ayenera kuchita mu banja lachimwemwe? Nkhani yotsatira idzakambitsirana chimenecho ndi mafunso olinganako.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Ndani yemwe ali ndi thayo lalikulu mu ukwati wachimwemwe, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Ndimotani mmene amuna angatsatirire chitsanzo chodzetsa mpumulo cha Kristu?
◻ Ndi kulinganiza kotani kumene kukufunika pakati pa mathayo a mpingo ndi banja?
◻ Ndimotani mmene mwamuna ‘angakhalire ndi mkazi wake monga mwa chidziŵitso’?
◻ Nchiyani chomwe chimatanthauza ‘kupereka ulemu kwa mkazi monga chotengera chochepa mphamvu’?
[Chithunzi patsamba 11]
Mkulu wolinganizika amadziŵa kuti kuŵeta kumayambira panyumba