“Tiyeninso Tichotse Cholemera Chirichonse”
“Ndiri wachisoni kwambiri ndi wolefulidwa maganizo,” anadandaula motero Mary. Akumaloza kumtolo wamathayo Achikristu, mkazi Wachikristu ameneyu anawonjezera kuti: “Ndimawona mabwenzi akuvutika ndi kutopako. Nanenso ndimamva kutopa ndi kupsinjika. Chonde ndithandizeni kumvetsetsa chifukwa chake.”
KODI nanunso mumalingalira kuti muli pansi pa kupsinjika, otopa kwambiri osakhoza kusenza mokwanira mathayo anu ateokratiki? Kodi nthaŵi zina kumawonekera kuti uminisitala Wachikristu uli katundu wolemera, mtolo wosanyamulika? Akristu ambiri okhulupirika amakhala ndi nyengo yokhwethemula maganizo, popeza kuti tiri nthaŵi zonse ozingidwa ndi zipsinjo zoipa zimene zingachepetse chimwemwe chathu. Kukhala Mkristu weniweni lerolino kulidi chitokoso. Chotero, panthaŵi zina ena angauwone uminisitala Wachikristu kukhala mtolo wolemera.
Kufunafuna Nakatande
Malemba amakumveketsa bwino lomwe kuti Yehova sanatiyikire zofunidwa zosayenera. Mtumwi Yohane ananena kuti ‘malamulo a Mulungu saali olemetsa.’ (1 Yohane 5:3) Mofananamo Yesu anauza otsatira ake kuti: “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:29, 30) Mowonekera bwino sichiri chifuniro cha Yehova kuti timve tiri othodwetsedwa kapena kutopetsedwa muutumiki wathu kwa iye.
Pamenepa, kodi Mkristu wokhulupirika angawone motani mathayo ake Achikristu monga katundu wolemera? Mwachiwonekere, mbali zingapo zikuphatikizidwa. Tamverani mawu aŵa a mtumwi Paulo akuti: “Tiyeninso tichotse cholemera chirichonse . . . , ndipo tiyeni tithamange mwachipiriro mpikisano umene waikidwa pamaso pathu.” (Ahebri 12:1, NW) Mawu a Paulo amasonyeza kuti Mkristu nthaŵi zina angaike zothodwetsa zosafunikira pa iyemwini. Zimenezi kwakukulukulu sizimalowetsamo machimo okulira. Koma Mkristu angapange zolakwa m’zosankha zimene zingacholoŵanitse koposa moyo wake, kukupangitsa kovutirapo kwa iye kuthamanga mpikisano umene waikidwa pamaso pathu.
Lingaliro Lachikatikati la Zinthu Zakuthupi
Mwachitsanzo, talingalirani nkhani ya ntchito yakudziko. M’maiko ambiri, mikhalidwe yazachuma ingasiye Mkristu ali wopanda chosankha kusiyapo kugwira ntchito kwa maora ochulukira. Komabe, anthu kaŵirikaŵiri amaloŵa ntchito kokha kuti apeze chipambano kapena kukundika zinthu zosangulutsa. Mwakupendanso zofunika zawo zenizeni, Akristu ena akupeza kukhala kwanzeru kupanga masinthidwe mumkhalidwe wawo wa ntchito. Zimenezi zinali motero ndi Debbie ndi mwamuna wake, amene onse aŵiri ndi Mboni za Yehova. Debbie akuti: “Mkhalidwe wathu wandalama unali utasintha, ndipo panalibenso kufunika kwenikweni kwa ine kupitirizabe kugwira ntchito ya nthaŵi yonse. Koma kunali kovuta kuileka.” Posapita nthaŵi anayamba kumva chitsenderezo chakukhala ndi zambiri zochita. Iye akufotokoza kuti: “Loweruka linali tsiku langa lokha lomasuka lakuchita ntchito ya panyumba. Kaŵirikaŵiri sindinangolingalira zakupita muutumiki wakumunda. Ndinamva kuipa za icho, ndipo chikumbumtima changa chinkandivuta, komabe ndinakonda ntchito yanga! Pomalizira pake, ndinafunikira kuyang’anizana ndi zenizeni. Panali kokha yankho limodzi. Ndinasiya ntchito.” Zowonadi, masinthidwe aakulu motero angakhale osatheka kwa ena. Komabe, kupendedwa kosamalitsa kwa ndandanda ya ntchito yanu kungavumbule kufunika kwa masinthidwe ena.
Pangakhale njira zina zakudzichepetsera ife eni zothodwetsa zosafunikira. Kodi bwanji ponena za kuchepetsa chiŵerengero cha maulendo athu okasanguluka, zochitika za maseŵera, kapena chosangulutsa china—kuphatikizapo nthaŵi yotheredwa m’kuwonerera wailesi yakanema? Ndipo ngakhale pambuyo pakupeza kukhazikika kofunika m’mbali zimenezi, masinthidwe anthaŵi zonse angafunikire kusunga kukhazikika koteroko.
Kukhala Olingalira Kuli Kofunika
Kukhala olingalira m’nkhani zotero kudzatithandiza kusinthira ku mikhalidwe yatsopano pamene ibuka. Chotero, tingasunge lingaliro lotsimikizirika muuminisitala wathu.—Aefeso 5:15-17; Afilipi 4:5.
Kodi mumadzipeza inu mwini otsenderezedwa ku kuyendera limodzi ndi zimene ena amachita muutumiki wa Mulungu? Zimenezinso zingawonjezere nkhaŵa ndi kugwiritsidwa mwala ku moyo wanu. Pamene kuli kwakuti chitsanzo chabwino cha ena chingakulimbikitsenidi kuchita zowonjezereka, kukhala olingalira kudzakuthandizani kukhazikitsa zonulirapo zofikirika zogwirizana ndi mikhalidwe yanu ndi maluso. Malemba amatiuza kuti: “Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, sichifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iyemwini.”—Agalatiya 6:4, 5.
Zizoloŵezi za m’malowo ndi miyambo zingawonjezerenso zothodwetsa zathu. M’tsiku la Yesu anthu anali otopetsedwa ndi kuyesayesa kugwirizana ndi malamulo ochuluka achipembedzo ndi miyambo yokhazikitsidwa ndi anthu. Lerolino, anthu a Yehova amasulidwa ku miyambo yachipembedzo chonyenga. (Yerekezerani ndi Yohane 8:32.) Chikhalirechobe, Mkristu akakhoza kukhala wotanganitsidwa mosayenerera ndi zizoloŵezi za kumaloko. Mwachitsanzo, nthaŵi zina zochitika zonga ngati maukwati zimaphatikizapo zizoloŵezi zopambanitsa kwambiri. Zizoloŵezi zimenezi zingakhale zosalakwika, ndipo zingakhaledi zokopa ndi zokondweretsa. Komabe, Akristu sangakhale ndi nthaŵi kapena ndalama zoti achitire zinthu zonse zoterozo, ndipo kuyesayesa kutero kukhoza kuwonjezera zothodwetsa zina zosafunikira.
Talingalirani zimene zinachitika pamene Yesu anachezera mkazi wotchedwa Marita. Mmalo mwakupindula mokwanira ndi nzeru yake yaumulungu, “Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri.” Iye anali wothodwetsedwa ndi zinthu zambiri. (Luka 10:40) Koma Yesu mokoma mtima anapereka lingaliro lakuti iye angapeputse makonzedwe ake achakudya kotero kuti apindule ndi kuphunzitsa kwake. (Luka 10:41, 42) Zimenezi zimafotokoza bwino lomwe mwafanizo kuti kulama maganizo ndi kukhala olingalira zidzakuthandizani kupeza uchikatikati woyenera muuminisitala Wachikristu.—Yakobo 3:17.
Kulama maganizo kulinso kofunika pamene mukusankha mabwenzi anu. Miyambo 27:3 amachenjeza kuti: “Mwala wolemera, nchenga ndiwo katundu; mkwiyo wachitsiru upambana kulemera kwake.” Nthaŵi zonse, mabwenzi anu apamtima adzakhala ndi chisonkhezero cholimba pa njira yanu yakulingalira. Kuyanjanabe ndi awo amene amafulumira kupeza zifukwa ndi kusuliza ena mumpingo kungafese mbewu za kulefulidwa ndi kulingalira koipa mwa inu. (1 Akorinto 15:33) Ngati muzindikira kuti chimenechi ndicho vuto, masinthidwe anzeru mwa amene muyanjana nawo akhoza kupeputsa mtolo wanu.
Khalani Wodzichepetsa Poyenda ndi Mulungu
Pa Mika 6:8, timapeza funso losonkhezera maganizo ili: “Ndipo Yehova afunanji nawe koma . . . kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Kudzichepetsa kumalongosoledwa monga kuzindikiridwa kwa zoperewera mwa munthuwe. Awo amene samazindikira zoperewera zawo angadzitopetse iwo eni ndi mathayo ochulukira koposa. Zimenezi zachitika kwa Akristu okula msinkhu, ngakhale oyang’anira, zikumachititsa kulefulidwa, kugwiritsidwa mwala, ndi kutaikiridwa kwa chimwemwe. Kenneth, mkulu Wachikristu, anavomera kuti: “Ndinadziwona ndekha ndikulowa m’kuchita tondovi, ndipo ndinati, ‘Sindizalola zimenezi kuchitika kwa ine.’ Chotero ndinachepetsa ena amathayo anga ndi kusumika maganizo pa chimene ndikakhoza kuchita.”
Ngakhale mneneri wodzichepetsa Mose anali ndi vuto m’kuzindikira zoperewera zake. Chotero Yetero, mpongozi wake, anazindikiritsa Mose kulingalira bwino za kuchuluka kopambana kwa ntchito imene akayesayesa kuisamalira mwa iye yekha. “Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi?” anafunsa Yetero. “Chinthu uchichitachi sichiri chabwino ayi. Udzalema konse . . . pakuti chikulaka chinthu ichi; sungathe kuchichita pawekha. . . . Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, . . . ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe, koma milandu yaing’ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.” Mose mwamsanga anayamba kugawira ntchito yake kwa ena, mwakutero kupeza mpumulo kuchokera kuchimene chinali kukhala mtolo wosasenzeka.—Eksodo 18:13-26.
Pachochitika china Mose anati kwa Yehova: “Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.” Panonso, yankho linali kusankha ena. Zimenezi zingakhalenso yankho la vuto lanu ngati muwona kuti mukugonjetsedwa ndi mathayo ochuluka kopambana.—Numeri 11:14-17.
Yehova Amatithandiza Kusenza Thayo
Yesu ananena kuti goli lake linali lofewa ndi katundu wake wopepuka koma osati wopanda kulemera. Goli limene Yesu anatiitanira kulisenza ife eni siliri goli laulesi. Liri goli lakudzipatulira kotheratu kwa Mulungu monga wophunzira wa Yesu Kristu. Chotero, mlingo wakutiwakuti wakulemera kapena chitsenderezo umaphatikizidwa ndi kukhala Mkristu weniweni. (Mateyu 16:24-26; 19:16-29; Luka 13:24) Pamene mikhalidwe yadziko ikuipaipabe, zitsenderezo zidzawonjezereka. Komabe, tiri ndi chifukwa chabwino chakukhalira otsimikizira m’kapenyedwe kathu chifukwa chakuti chiitano cha Yesu chimasonyeza kuti ena akhoza kuloŵa pansi pa goli lake limodzi naye ndi kuti iye adzawathandiza.a Chotero, malinga ngati titsatira chitsogozo cha Kristu, thayo lathu lidzakhalabe lokhoza kusenzeka chifukwa chakuti iye adzatithandiza.
Mulungu amasamalira amene amamkonda, ndipo amatetezera mitima ndi mphamvu za kulingalira za onse amene mwapemphero amamsenzetsa nkhaŵa zawo. (Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7; 1 Petro 5:6, 7) “Wolemekezeka Yehova, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wachipulumutso chathu,” anatero wamasalmo. (Salmo 68:19) Inde, khalani otsimikizira kuti Mulungu adzakusenzeraninso katundu tsiku ndi tsiku ngati muchotsa cholemera chirichonse ndi kuthamanga ndi chipiriro makaniwo oikidwa pamaso panu.
[Mawu a M’munsi]
a Kumasulira kwa mawu amtsinde ndiko kwakuti: “Lowani pansi pa goli langa limodzi nane,” NW.
[Chithunzi patsamba 24]
Akulu anzeru ali ofunitsitsa kugaŵira ena ntchito zawo ndi kugawana mathayo awo