MUTU 13
Zimene Yesu Anachita Atayesedwa
MATEYU 4:1-11 MALIKO 1:12, 13 LUKA 4:1-13
YESU ANAYESEDWA NDI SATANA
Yesu atangobatizidwa, mzimu wa Mulungu unamutsogolera kupita kuchipululu cha Yudeya. Pa nthawiyi, Yesu anali ndi zinthu zambiri zoti aziganizire. Mwina mukukumbukira kuti pa nthawi imene ankabatizidwa, “kumwamba kunatseguka.” (Mateyu 3:16) Zimenezi zinachititsa kuti akumbukire zimene anaphunzira komanso zimene ankachita ali kumwamba. Mpake kuti analidi ndi zambiri zoti aziganizire.
Yesu anakhala m’chipululu masiku 40, usana ndi usiku. Pa nthawi yonseyi sankadya chilichonse. Kenako Yesu atamva njala kwambiri, Satana Mdyerekezi anabwera kudzamuyesa ndipo ananena kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.” (Mateyu 4:3) Yesu anakana kuchita zimene anamuuzazo chifukwa ankadziwa kuti kunali kulakwa kugwiritsa ntchito mphamvu zake zotha kuchita zozizwitsa n’cholinga choti angokwaniritsa zofuna zake.
Koma Mdyerekezi sanalekere pomwepo. Anayesanso njira ina. Anamuuza Yesu kuti adziponye kuchokera pakhoma la mpanda wa kachisi. Koma Yesu anakana kuchita zinthu modzionetsera. Pogwiritsira ntchito Malemba, Yesu anasonyeza kuti n’kulakwa kuyesa Mulungu mwa njira imeneyi.
Kenako Mdyerekezi anayesanso Yesu kachitatu pomuonetsa “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Kenako anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.” Nthawi yomweyo Yesu anakana ndipo ananena kuti: “Choka Satana!” (Mateyu 4:8-10) Yesu sanalole kuchita zinthu zoipa chifukwa ankadziwa kuti ndi Yehova yekha amene ayenera kutumikiridwa. Iye anasankha kukhala wokhulupirika kwa Mulungu.
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikazi? Zimene zinachitikazi zikusonyeza kuti Satana ndi weniweni osati khalidwe linalake loipa ngati mmene anthu ena amaganizira. Iye alipodi kungoti sitingamuone. Komanso zikusonyeza kuti maulamuliro onse apadziko lapansi ali m’manja mwa Mdyerekezi. Ndiye n’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Satana anachita pofuna kum’patsa Yesu maulamulirowa kunali kumuyesa?
Tikutero chifukwa chakuti Mdyerekezi ananena kuti akhoza kupatsa Yesu maulamuliro onse apadziko lapansi ngati atangomugwadira n’kumuweramira kamodzi kokha. Masiku anonso Mdyerekezi angagwiritse ntchito njira imeneyi pofuna kutiyesa. Akhoza kutiyesa potipatsa mwayi wokhala ndi chuma, udindo wapamwamba kapena kukhala munthu wotchuka m’dzikoli. Choncho ndi nzeru kutsatira chitsanzo cha Yesu pokhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale titayesedwa bwanji. Koma kumbukirani kuti Mdyerekezi anamusiya Yesu “kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Ndi zimenenso angachite kwa ifeyo, choncho ndi bwino kukhala tcheru nthawi zonse.