Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kupindula Kuchokera ku Mafanizo a Yesu
PAMENE ophunzira abwera kwa Yesu pambuyo pa mawu ake kwa khamu pa gombe, iwo ali ofunitsitsa kudziwa ponena za njira yake yatsopano ya kuphunzitsira. Ah, iwo akhala ali kumumva akugwiritsira ntchito mafanizo pambuyopo, osati mokulira chotero. Chotero iwo afuna kudziwa: “Kodi nchifukwa ninji mulankhula ndi iwo m’mafanizo?”
Chifukwa chimodzi akuchitira tero ndi kukwaniritsa mawu amneneri: “Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira, ndidzatchuia zinsinsi zoyambira kale.” Koma kuli zowonjezereka ku izo kuposa ichi. Kugwiritsira ntchito kwake kwa mafanizo kukutumikira cholinga chakuthandiza kuvumbulutsa mkhalidwe wamtima wa anthu.
Mchenicheni, anthu ambiri ali osangalatsidwa mwa Yesu kokha monga wopereka nkhani waluso ndi wochita zozizwitsa, osati amene ayenera kutumikiridwa monga Ambuye ndi kutsatiridwa mopanda dyera. Iwo sakufuna kusokonezedwa mu kawonedwe kawo kazinthu kapena njira yawo ya moyo. Iwo sakufuna kuti uthengawo ulowerere kumlingo umenewo. Chotero Yesu akuti:
“Chifukwa chache ndiphiphiritsira iwo m’mafanizo, chifukwa kuti akuwona samawona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. Ndipo adzachitidwa kwa iwo mawu adanenera Yesaya amene anati, . . . Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa.”’
“Komabe,” Yesu akupitiriza, “maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya. zimene muziwona, koma sanaziwona; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.”
inde, atumwi 12 amenewo ndi awo amene anali nawo anali ndi mitima yosalema. Chotero Yesu anati: “Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za ufumu wa Mulungu; koma kwa otsala ndinena nawo mwamafanizo.” Chifukwa chachikhumbo chawo kaamba ka kumvetsetsa, Yesu akupereka kwa ophunzira ake kulongosola kwa fanizo la wofesa.
“Mbewuzo ndizo mawu a Mulungu” Yesu akutero, ndipo nthakayo ndi mtima. Ponena za mbewu zofesedwa pa thanthwe mphepete mwa njira, iye akulongosola: “Akudza Mdyerekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.”
Kumbali ina, mbewu zodzalidwa pa thanthwe zikutanthauza mitima ya anthu omwe analandira mawu ndi chikondwerero. Komabe, chifukwa chakuti mawuwo analibe mizu m’mitima ya otero, anthu amenewa amangopatuka pamene nthawi ya mayesero kapena chizunzo ifika.
Ponena za mbewu imene inagwa pakati pa minga, Yesu akupitiriza, kuti imanena za anthu amene anamva mawu. Awa, ngakhale kuli tero, amatengedwa ndi nkhawa ndi chuma ndi zokondweretsa zamoyo, chotero amatsamwitsidwa kotheratu ndipo sakhwimitsa zipatso zaumphumphu.
Pomalizira, ponena za mbewu zodzalidwa panthaka yabwino, Yesu akuti, awa ali amene, pambuyo pakumva mawu ndi mitima yabwino, amasunga iwo ndikubala zipatso zakupirira.
Ndi wodalitsidwa chotani nanga ophunzira amenewa omwe amufuna Yesu ndi kupeza matanthauzo akuphunzitsa kwake! Yesu akufuna kuti zifaniziro zake zimvedwe, kuti agawire chowonadi kwa ena. “Nyali simatengedwa ndi kuvundikiridwa ndi chotengera kapena kuikidwa pansi pa kama, kodi imatero?’ iye akufunsa. Ayi, “iyo imatengedwa ndi kuikidwa pachoikapo nyali.” Chotero Yesu akuwonjezera: “Chifukwa chake yang’anirani mamvedwe anu.” Mateyu 13:10-23, 34-36; Marko 4:10-25, 33, 34; Luka 8:9-18; Masalmo 78:2; Yesaya 6:9, 10.
◆ Ndi chifukwa ninji Yesu analankhula mu mafaniziro?
◆ Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu akudzisonyezera iwo eni kukhala osiyana ndi khamu?
◆ Kodi ndi malongosoledwe otani amene Yesu akupereka ponena za fanizo la wofesa?