-
Simudziwa Zimene ZidzalolaNsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
Khoka
15, 16. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la khoka. (b) Kodi khokali likuimira chiyani, ndipo kodi fanizo limeneli likusonyeza mbali iti ya kukula kwa Ufumu?
15 Chofunika kwambiri kuposa chiwerengero cha anthu omwe amati ndi ophunzira a Yesu Khristu ndicho mtundu wa ophunzirawo. Yesu anasonyeza mbali imeneyi ya kukula kwa Ufumu pamene ananenanso fanizo la khoka. Iye anati: “Ndiponso ufumu wa kumwamba uli ngati khoka loponyedwa m’nyanja limene limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.”—Mat. 13:47.
16 Khokali, lomwe likuimira ntchito yolalikira Ufumu, limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu. Yesu anapitiriza kuti: “[Khokalo] likadzala amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi, kenako amasankha zabwino ndi kuziika m’zotengera, koma zosafunika amazitaya. Ndi mmenenso zidzakhalira pamapeto a dongosolo lino la zinthu: angelo adzapita ndi kukachotsa oipa pakati pa olungama ndipo adzawaponya mu ng’anjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”—Mat. 13:48-50.
17. Kodi kusankha, kapena kuti kulekanitsa, kotchulidwa m’fanizo la khoka kukuchitika nthawi iti?
17 Kodi kusankha kumeneku, kapena kuti kulekanitsa, kukunena za chiweruzo chomaliza cha nkhosa ndi mbuzi chimene Yesu anati chidzachitika iye akadzafika mu ulemerero wake? (Mat. 25:31-33) Ayi. Chiweruzo chomaliza chimenecho chidzachitika Yesu akadzabwera pa chisautso chachikulu. Koma kulekanitsa kumene kukunenedwa m’fanizo la khoka kukuchitika “pamapeto,” kapena kuti nthawi ya mathedwe “a dongosolo lino la zinthu.”b Nthawi imeneyi ndi imene tikukhalamoyi, imene ikutifikitsa ku chisautso chachikulu. Ndiyeno kodi ntchito yolekanitsa imeneyi ikuchitika motani masiku ano?
18, 19. (a) Kodi ntchito yolekanitsa ikuchitika motani masiku ano? (b) Kodi anthu amitima yabwino akufunika kuchita chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi patsamba 21.)
18 Nsomba zophiphiritsa mamiliyoni ambiri zochokera m’nyanja ya anthu zimabwera mu mpingo wa Yehova masiku ano. Zina zimapezeka pa Chikumbutso, zina zimabwera ku misonkhano yathu, ndipo zinanso zimasangalala kuphunzira Baibulo. Koma kodi nsomba zonsezi zimakhala Akhristu enieni? Nsombazo ‘zingakokeredwe kumtunda’ inde, koma Yesu akunena kuti “zabwino” zokha ndi zimene akuzisonkhanitsa m’zotengera, ndipo zotengerazi zikuimira mipingo yachikhristu. Zosafunika zikutayidwa, ndipo pamapeto pake zidzaponyedwa m’ng’anjo ya moto yophiphiritsa, imene ikuimira chiwonongeko cha m’tsogolo.
19 Mofanana ndi nsomba zosafunika, anthu ambiri amene ankaphunzira Baibulo ndi anthu a Yehova asiya kuphunzira. Ena omwe anabadwira m’mabanja achikhristu sanafunepo kukhala otsatira mapazi a Yesu. Mpaka pano iwo akhala asakufuna kutumikira Yehova, kapena atamutumikira kwa nthawi ndithu, asiya kumutumikira.c (Ezek. 33:32, 33) Komabe, m’pofunika kwambiri kuti anthu onse amitima yabwino alole kusonkhanitsidwa m’mipingo yonga zotengera ndi kukhalabe m’malo achitetezo amenewa lisanafike tsiku lomaliza la chiweruzo.
-
-
Simudziwa Zimene ZidzalolaNsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
20, 21. (a) Kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mafanizo a Yesu okhudza kukula? (b) Kodi inu mukufunitsitsa kuchita chiyani?
20 Ndiyeno, kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mwachidule mafanizo a Yesu okhudza kukula? Choyamba, mofanana ndi kukula kwa kambewu ka mpiru, zinthu za Ufumu zakula modabwitsa kwambiri padziko lapansi. Palibe chimene chingaletse ntchito ya Yehova kufalikira. (Yes. 54:17) Ndiponso, chitetezo chauzimu chaperekedwa kwa anthu amene ‘apeza malo okhala mu mthunzi [wa mtengowo].’ Chachiwiri, Mulungu ndi amene amakulitsa. Mofanana ndi mmene chofufumitsa chobisika chimafufumitsira ufa wonse, kukula kumeneku kwakhala kovuta kukuzindikira kapena kukumvetsa, koma kukulako kukuchitika ndithu. Chachitatu, sikuti anthu onse amene analabadira asonyeza kuti ndi nsomba zofunika. Ena akhala ngati nsomba zosafunika za m’fanizo la Yesu.
-
-
Simudziwa Zimene ZidzalolaNsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
b Ngakhale kuti lemba la Mateyo 13:39-43 likunena mbali ina ya ntchito yolalikira Ufumu, nthawi ya kukwaniritsidwa kwake ndi nthawi yomwenso fanizo la khoka likukwaniritsidwa, yomwe ndi “pamapeto,” kapena kuti nthawi ino ya mathedwe “a dongosolo lino la zinthu.” Ntchito yolekanitsa nsomba zophiphiritsa ndi yochitika mopitiriza, monga mmene ntchito yofesa ndi kukolola ikupitirizira panthawi yonseyi.—Nsanja ya Olonda, October 15, 2000, masamba 25-26; Lambirani Mulungu Woona Yekha, masamba 178-181, ndime 8-11.
-