Mutu 3
“Tsopano Uwauze” Mawu Awa
1. (a) Kodi Yesu ndi Yeremiya anali ofanana m’njira ziti? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yeremiya mu utumiki wathu?
YESU KHRISTU ndiye chitsanzo chathu chabwino kwambiri pa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino. Koma n’zochititsa chidwi kuti kale nthawi zina anthu akaona Yesu ankaganiza za mneneri Yeremiya. (Mat. 16:13, 14) Mofanana ndi Yesu, Yeremiya analamulidwa ndi Mulungu kuti agwire ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, nthawi ina Mulungu anamuuza kuti: “Tsopano uwauze kuti, ‘Yehova . . . wanena kuti . . . . ’” (Yer. 13:12, 13; Yoh. 12:49) Komanso pamene Yeremiya ankachita utumiki wake, anasonyeza makhalidwe ofanana ndi a Yesu.
2. Kodi zimene anthu akufunikira kuchita masiku ano zikufanana bwanji ndi zimene Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya ankafunikira kuchita?
2 Koma anthu ena a Mboni anganene kuti: ‘Ntchito yathu yolalikira ndi yosiyana ndi ya Yeremiya. Iye anali mneneri wa Mulungu ku mtundu wa anthu amene anali odzipereka kale kwa Mulungu, pamene anthu ambiri amene ife timawalalikira sadziwa Yehova.’ Zimenezi n’zoona. Koma pofika m’nthawi ya Yeremiya, Ayuda ambiri anali “opanda nzeru” ndipo anali atasiya kulambira Mulungu woona. (Werengani Yeremiya 5:20-22.) Iwo anafunikira kusintha kuti azilambira Yehova m’njira yovomerezeka. N’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu akufunika kuphunzira kuopa Yehova ndi kuyamba kumulambira m’njira yoyenera, kaya amanena kuti ndi Akhristu kapena ayi. Choncho, tiyeni tione mmene tingatumikirire Mulungu woona ndi kuthandiza anthu, potengera chitsanzo cha Yeremiya.
‘YEHOVA ANAKHUDZA PAKAMWA PANGA’
3. Kodi Mulungu anachita chiyani kwa Yeremiya kumayambiriro kwa utumiki wake, ndipo mneneriyu anamva bwanji mumtima?
3 Mungakumbukire kuti pamene Yeremiya ankayamba utumiki wake monga mneneri, anauzidwa kuti: “Upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene. Usachite mantha chifukwa cha nkhope zawo, pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’” (Yer. 1:7, 8) Kenako Mulungu anachita chinthu chimene Yeremiya sankayembekezera. Yeremiya akutiuza kuti: “Yehova anatambasula dzanja lake ndi kukhudza pakamwa panga. Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: ‘Ndaika mawu anga m’kamwa mwako. Taona, lero ndakupatsa mphamvu.’” (Yer. 1:9, 10) Kuyambira nthawi imeneyo, Yeremiya anadziwa kuti adzayamba kulankhula moimira Mulungu Wamphamvuyonse.a Yeremiya anayamba kuchita utumiki wopatulika mwakhama kwambiri chifukwa chakuti Mulungu ankamuthandiza nthawi zonse.—Yes. 6:5-8.
4. Kodi mungafotokoze zitsanzo ziti za anthu amene amagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri?
4 Masiku ano, Yehova sakhudza ndi dzanja mtumiki wake aliyense ngati mmene anachitira ndi Yeremiya. Komabe, pogwiritsa ntchito mzimu wake, amapatsa atumiki akewo mtima wofunitsitsa kulalikira uthenga wabwino, ndipo ambiri a iwo amagwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. Mwachitsanzo, ganizirani za mlongo wina wa ku Spain, dzina lake Maruja, amene mikono ndi miyendo yake zinafa zaka zoposa 40 zapitazo. Mlongoyu amavutika kulalikira khomo ndi khomo, choncho amapeza njira zina zimene zimamuthandiza kuti azilalikira mwakhama. Imodzi mwa njira zimenezi ndi kulemba makalata. Maruja ali ndi mwana wamkazi amene amalemba zonse zimene iye akumuuza. Nthawi ina Maruja ndi mwana wakeyo anagwirizana kuti alembe makalata kwa mwezi wonse. Pa ntchitoyi, iwo anatumizira anthu makalata oposa 150, ndipo m’kalata iliyonse ankaikamonso kapepala kamodzi kofotokoza za m’Baibulo. Chifukwa cha khama lawoli, anthu ambiri a m’mudzi wapafupi ndi kwawoko anamva uthenga wabwino. Nthawi ina Maruja anauza mwana wakeyo kuti, “Ngati pa gulu la anthu amene analandira makalata athu aja pali munthu wowongoka mtima, Yehova atithandiza kuti tipeze munthu woti tiziphunzira naye Baibulo.” Mkulu wina wa mumpingo wa komweko analemba kuti: “Ndikuthokoza Yehova potipatsa alongo ngati Maruja, amene amaphunzitsa anthu ena kuti aziona zinthu zauzimu kuti n’zofunika kwambiri.”
5. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Yeremiya kukhalabe wakhama ngakhale kuti anthu sankafuna kumvetsera uthenga wake? (b) N’chiyani chingakuthandizeni inuyo kukhalabe wakhama pa ntchito yolalikira uthenga wabwino?
5 M’nthawi ya Yeremiya, anthu ambiri a ku Yerusalemu ‘sankakondwera’ ndi choonadi cha Mulungu. Ndiye kodi mneneriyu anasiya kulalikira chifukwa chakuti anthu ambiri sankafuna kumvetsera uthenga wake? Ayi sanasiye. Yeremiya ananena kuti: “Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova. Ndatopa ndi kukhala chete.” (Yer. 6:10, 11) Kodi inuyo mungatani kuti mukhalebe ndi khama ngati Yeremiya? Njira imodzi ndiyo kuganizira mozama mwayi wapadera umene muli nawo woimira Mulungu woona. Inu mukudziwa kuti anthu otchuka m’dzikoli amanyoza dzina la Mulungu woona. Ganiziraninso mmene atsogoleri azipembedzo asocheretsera anthu a m’gawo lanu. Atsogoleri amenewo achita zofanana ndi zimene ansembe a m’nthawi ya Yeremiya anachita. (Werengani Yeremiya 2:8, 26, 27.) Mosiyana ndi zimenezo, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene inu mukulengeza, ndi umboni wakuti Mulungu akusonyeza anthu onse kukoma mtima kwake. (Maliro 3:31, 32) Choncho kuganizira mfundo zimenezi kungakuthandizeni kukhalabe akhama polalikira uthenga wabwino ndi kuthandiza anthu okhala ngati nkhosa.
6. Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto akuluakulu ati?
6 Mwina mungavomereze kuti nthawi zina zimavuta kukhalabe akhama pochita utumiki wachikhristu. Nayenso Yeremiya anakumana ndi mavuto akuluakulu pamene ankatumikira Yehova, ndipo ena mwa mavutowo anali aneneri onyenga. Chitsanzo chimodzi mungachipeze pa Yeremiya chaputala 28. Anthu ambiri sankamvera uthenga wake, ndipo nthawi zina Yeremiya ankaona ngati ali yekhayekha. (Yer. 6:16, 17; 15:17) Komanso nthawi zina ankakumana ndi adani amene ankafuna kumupha.—Yer. 26:11.
N’chifukwa chiyani mungakhulupirire kuti Yehova adzakuthandizani kuthana ndi mavuto amene mukukumana nawo polalikira uthenga wabwino?
“MWANDIDABWITSA INU YEHOVA”
7, 8. Kodi Mulungu ‘anadabwitsa’ bwanji Yeremiya?
7 Nthawi inayake, pamene anthu ankanyoza Yeremiya ndi kumunenera mawu achipongwe tsiku ndi tsiku, iye anauza Yehova mmene zimenezi zinam’khudzira mumtima. Mwachitsanzo, pa Yeremiya 20:7, 8, (Werengani.) mneneriyu ananena kuti Mulungu ‘anamudabwitsa.’ Kodi mukuganiza kuti Mulungu anadabwitsa bwanji mneneri wake wokhulupirikayu?
8 Yehova ‘anadabwitsa’ mneneri wakeyu pomuchitira zinthu zabwino zimene iye sankayembekezera. Yeremiya ankaona kuti anthu akumutsutsa kwambiri moti payekha sangakwanitse kuchita utumiki umene Mulungu anam’patsa. Koma mothandizidwa ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Yeremiya anakwanitsa kuchita utumikiwo. Choncho tinganene kuti Yehova anamusowetsa chonena Yeremiya, chifukwa anasonyeza kuti iye ndi wamphamvu kwambiri kuposa Yeremiyayo komanso kuposa maganizo onse a mneneriyu. Munthu wa Mulunguyu atayamba kuona kuti sangachitire mwina koma kusiya utumiki wake, Yehova anamupatsa mtima wofuna kupitirizabe utumikiwo. Izi n’zomwe zinadabwitsa kwambiri Yeremiya. Mulungu anasonyeza kuti ndi wamphamvu kwambiri kuposa zofooka za mneneriyu. Choncho Yeremiya anapitiriza kulalikira, ngakhale kuti anthu sankamvetsera uthenga wake, sankafuna kucheza naye komanso ankamuchitira nkhanza.
9. N’chifukwa chiyani lemba la Yeremiya 20:11 lili lolimbikitsa kwa inu?
9 Kwa Yeremiya, Yehova anali ngati “msilikali wamphamvu ndi woopsa” amene ankamuthandiza. (Yer. 20:11) Inunso Mulungu angakulimbikitseni kuti mupitirize kumulambira m’njira yoyenera, komanso kuti mupitirize kuchita utumiki wanu mwakhama ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto odetsa nkhawa.
10. Kodi mwatsimikiza ndi mtima wonse kuchita chiyani anthu akamakutsutsani?
10 Mtumwi Paulo anatsimikizira mfundo imeneyi pamene ankalimbikitsa Akhristu omwe ankatsutsidwa. Iye analemba kuti: “Makhalidwe anu akhale oyenera uthenga wabwino wa Khristu. Kuti . . . ndizimva . . . kuti mukulimbikira mu mzimu umodzi. Ndipo ndi mtima umodzi, mukulimbika pamodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha uthenga wabwino. Komanso simukuchita mantha m’njira iliyonse ndi okutsutsani.” (Afil. 1:27, 28) Mofanana ndi Yeremiya komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi, mungathe kudalira kwambiri Mulungu Wamphamvuyonse pamene mukuchita utumiki wanu, ndipo muyenera kuchita zimenezo kumene. Anthu ena akamakunyozani kapena kukuzunzani, muzikumbukira kuti Yehova ali pambali panu ndipo angakupatseni mphamvu. Iye anachita zimenezi kwa Yeremiya ndipo wachitanso zimenezi kwa abale athu ambirimbiri. Choncho angachitenso chimodzimodzi kwa inu. M’pempheni kuti akuthandizeni, ndipo mukhale ndi chikhulupiriro kuti ayankha pemphero lanu. Ndipotu inunso Mulungu ‘angakudabwitseni’ atakupatsani mphamvu kuti musachite mantha koma mulimbe mtima n’kuthana ndi mavuto amene mukukumana nawo. Zoonadi, mungathe kuchita zinthu zambiri zimene munkaona kuti simungazikwanitse.—Werengani Machitidwe 4:29-31.
11, 12. (a) Kodi mungasinthe bwanji zinthu kuti muzitha kulankhula ndi anthu ambiri mu utumiki wanu? (b) Kodi chithunzi chimene chili patsamba 39 chikusonyeza kuti mungachite chiyani malinga ndi mmene zinthu zilili kwanuko?
11 Zimene tikuwerenga zokhudza utumiki wa Yeremiya zingatithandize m’njira zosiyanasiyana kuti tizilengeza uthenga wabwino mogwira mtima kwambiri. Yeremiya atatumikira monga mneneri wa Yehova kwa zaka zoposa 20, ananena kuti: “Ine ndakhala ndikukuuzani mawuwo, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kukuuzani mawu akewo koma simunandimvere.” (Yer. 25:3) Zoonadi, Yeremiya ankayamba utumiki wake m’mawa kwambiri, osati mochedwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chimenechi? M’mipingo yambiri muli ofalitsa amene amadzuka m’mawa kwambiri n’kumakalalikira anthu m’malo okwerera basi kapena sitima. M’madera akumidzi, anthu ambiri a Mboni amalawirira m’mawa n’kumakalalikira alimi m’minda yawo kapena anthu ena m’malo awo ogwirira ntchito. Kodi pali njira zina zimene inuyo mungagwiritse ntchito potengera chitsanzo cha Yeremiya amene anachita utumiki wake mokhulupirika? Kodi mungathe kudzuka m’mawa kwambiri kuti mukafike mofulumira pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda?
12 Kuwonjezera pamenepo, m’madera ambiri kawirikawiri zimayenda bwino zedi kulalikira khomo ndi khomo masana ndi madzulo. Ofalitsa ena amalalikira ngakhale usiku. Iwo amakalalikira kwa anthu ogwira ntchito m’malo ogulitsira mafuta, m’malo odyera ndi m’malo ena ochitira malonda, amene amakhala otsegula masana ndi usiku wonse. Kodi inuyo mungasinthe nthawi imene mumalowera mu utumiki kuti muzilalikira pa nthawi imene mungapeze anthu panyumba kapena kumalo ena?
N’chifukwa chiyani mukukhulupirira kuti Yehova akukuthandizani pa ntchito yanu yolengeza uthenga wake?
13, 14. (a) Kodi chitsanzo cha Yeremiya chikugwirizana bwanji ndi kupanga maulendo obwereza? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kupitanso kwa anthu amene munawalalikira?
13 Nthawi zina Yehova ankauza Yeremiya kuti akalengeze uthenga wa ulosi ataimirira pachipata cha kachisi kapena cha mzinda wa Yerusalemu. (Yer. 7:2; 17:19, 20) Pamene Yeremiya ankalengeza uthengawo pachipata, anthu ambiri ankamva mawu a Yehova. Komanso popeza kuti anthu ambiri, monga anthu otchuka a mumzindawo komanso amalonda, ankadutsa pa zipata zomwezomwezo nthawi zonse, Yeremiya ayenera kuti analankhula ndi anthu ena mobwerezabwereza kuti awathandize kumvetsa uthenga womwe anali atawauza kale. Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani pa nkhani yopanga maulendo obwereza kwa anthu amene asonyeza chidwi?
14 Yeremiya ankadziwa kuti ntchito imene ankagwira monga mneneri wa Mulungu idzathandiza anthu kuti adzapulumuke. Nthawi ina, atalephera kulankhula ndi anthu monga mmene Mulungu anamuuzira, anatumiza mnzake Baruki kuti akalankhule nawo m’malo mwa iyeyo. (Werengani Yeremiya 36:5-8.) Kodi tingamutsanzire bwanji Yeremiya pa zimene anachitazi? Tikalonjeza mwininyumba kuti tidzabweranso, kodi timakwaniritsa lonjezo lathu? Zikativuta kupita ku ulendo wobwereza kapena kukachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba, kodi timapempha munthu wina kuti apiteko? Yesu ananena kuti: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde.” (Mat. 5:37) M’pofunika kuti tizikwaniritsa malonjezo athu, chifukwa tikuimira Mulungu wa choonadi komanso wadongosolo.—1 Akor. 14:33, 40.
15, 16. (a) Kodi anthu ambiri awonjezera bwanji utumiki wawo potengera chitsanzo cha Yeremiya? (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo wina wa m’dziko la Chile, mogwirizana ndi chithunzi chomwe chili patsamba 40?
15 Yeremiya analimbikitsa Ayuda amene anali ku Babulo powalembera kalata yonena za “lonjezo” la Yehova lakuti adzawabwezeretsa kudziko lawo. (Yer. 29:1-4, 10) Masiku ano, tingathenso kuuza anthu ambiri “lonjezo” la zinthu zabwino zimene Yehova adzachite posachedwapa. Tingachite zimenezi powalembera anthuwo makalata kapena kuwaimbira foni. Kodi mungagwiritse ntchito njira zimenezi pothandiza achibale anu kapena anthu ena amene ali kutali kapenanso anthu omwe n’zovuta kuwapeza?
16 Masiku ano, ofalitsa a Ufumu akamatengera chitsanzo cha Yeremiya amene anakwaniritsa utumiki wake, kawirikawiri zinthu zimawayendera bwino kwambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina m’dziko la Chile anakumana ndi mayi wina amene ankatuluka m’malo ena okwerera sitima. Mayiyu anasangalala kwambiri atamva uthenga wa m’Baibulo ndipo anavomera kuti mlongoyo azipita kunyumba kwake kuti azikakambirana nkhani za m’Baibulo. Koma pamene ankasiyana, mlongoyo sanalembe adiresi ya mayiyo. Kenako mlongoyo anazindikira kuti m’pofunika kuti akathandize mayi uja kuti chidwi chake pa choonadi chikule, choncho anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Tsiku lotsatira, anapitanso kumalo okwerera sitima aja pa nthawi yofanana ndi ya tsiku loyamba lija, ndipo anakumananso ndi mayiyo. Pa nthawiyo analemba bwinobwino adiresi ya mayiyu ndipo tsiku lina anapita kunyumba kwake kukamuthandiza kuti amvetse Malemba. Ifenso tisamaiwale kuti posachedwapa Mulungu aweruza dziko la Satanali, koma amene angalape ndi kukhulupirira uthenga wabwino, adzapulumuka. (Werengani Maliro 3:31-33.) Choncho tiyeni tithandize anthu kumvetsa mfundo imeneyi polalikira m’gawo lathu mwakhama.
“MWINA ADZAMVERA NDIPO ALIYENSE WA IWO ADZABWERERA”
17. Kodi mungatsanzire bwanji Yeremiya m’gawo lanu?
17 Yehova sankafuna kuti anthu awonongedwe. Kutatsala zaka pafupifupi 10 kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwe, Mulungu anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti anene kuti anthu amene adzapite ku ukapolo ku Babulo adzabwerera kwawo. Timawerenga kuti: “Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino, ndipo ndidzawabwezeretsa kudziko lino. Pamenepo ndidzawalimbitsa, osati kuwapasula. Ndidzawabzala, osati kuwazula.” Kenako Yeremiya anauza anthuwo kuti: ‘Muli ndi tsogolo labwino.’ (Yer. 24:6; 26:3; 31:17) Yeremiya ankaona anthu mmene Mulungu amawaonera. Pochita utumiki wake, iye ankaderadi anthu nkhawa ndipo ankawauza mawu a Yehova ochonderera akuti: “Bwererani chonde, aliyense asiye njira zake zoipa ndipo sinthani zochita zanu kuti zikhale zabwino.” (Yer. 35:15) Kodi mungaganizire njira zina zimene inuyo mungasonyezere chidwi kwa anthu a m’gawo lanu?
18, 19. (a) Kodi tiyenera kupewa maganizo ati tikamalalikira uthenga wabwino? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo ati amenenso Yeremiya anali nawo?
18 Yeremiya sanasiye kukonda kwambiri anthu. Mwachitsanzo, pamene Yerusalemu ankawonongedwa, iye anapitiriza kuwamvera chisoni. (Werengani Maliro 2:11.) Ayuda anakumana ndi mavutowo chifukwa cha kusamvera kwawo. Komabe, Yeremiya sananene kuti, ‘Pajatu ndinkakuuzani ine.’ M’malomwake, anawamvera chisoni kwambiri chifukwa cha zimene zinawachitikirazo. Chimodzimodzinso ifeyo. Tisamachite utumiki wathu mwamwambo chabe kapena n’cholinga choti anthu azitiona. Koma khama lathu pochitira umboni lizisonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu wathu wodabwitsa, komanso timakonda kwambiri anthu amene anawalenga m’chifaniziro chake.
19 Palibe ntchito kapena udindo uliwonse m’dzikoli umene ungapose ntchito yochitira umboni za Mulungu woona. Yeremiya nayenso ankaona choncho, ndipo analemba kuti: “Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya. Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova.” (Yer. 15:16) Tikamalalikira uthenga wabwino, anthu ambiri adzadziwa Mulungu amene anawapatsa moyo komanso adzayamba kumukonda. Ndipo zimenezi zidzatheka tikamachita utumiki wathu mwakhama komanso mwachikondi, ngati mmene Yeremiya anachitira.
Mukaganizira chitsanzo cha Yeremiya, kodi ndi njira zina ziti zofalitsira ‘malonjezo’ a Yehova zimene mungayese kuzigwiritsa ntchito?
a Apa Yehova ankalankhula kudzera mwa mngelo. Kalero, nthawi zambiri Yehova akamapereka uthenga kwa anthu kudzera mwa mngelo, zinkakhala ngati Yehovayo akulankhula yekha.—Ower. 13:15, 22; Agal. 3:19.