Kodi Mawu a Mulungu Amaphunzitsa za Kubadwanso kwa Moyo?
ALIYENSE amene afufuza Baibulo ndi chiyembekezo chopeza chichirikizo cha chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo adzagwiritsidwadi mwala. Palibe pamene mudzapeza kuti anthu anakhalako ndi miyoyo yapapitapo. Ndiponso, simudzapeza mawu onga “kubadwanso kwa moyo” kapena “kusamuka kwa moyo” kapena “moyo wosafa” m’Baibulo.
Komabe, ena amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo amayesa kufotokoza kusoŵa kumeneku kwa chichirikizo Chabaibulo mwa kunena kuti lingaliro la kubadwanso kwa moyo linali lofala kwambiri m’nthaŵi zakale kwakuti mafotokozedwe alionse akanakhala osafunikira. Zoona, chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo nchakale kwambiri, koma mosasamala kanthu ndi utali wa nthaŵi imene chakhalako kapena ndi mmene chinalili chofala kapena chosafala, funso likupitirizabe lakuti, Kodi Baibulo limachiphunzitsa?
Pa 2 Timoteo 3:16, 17, mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Inde, Baibulo ndilo Mawu ouziridwa a Mulungu, njira yake yolankhulira ku banja laumunthu. Ndipo monga momwe Paulo analembera, limakhozetsa wofuna kudziŵa woona mtima kukhala “woyenera, wokonzeka” kuyankha mafunso onse ofunika onena za moyo, kuphatikizapo mafunso onena za nthaŵi yakale, yamakono, ndi yamtsogolo.
Paulo analembanso kuti: “Pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Popeza kuti Baibulo lili ndi malingaliro a Mulungu, osati a anthu opanda ungwiro, sikuyenera kutidabwitsa kuti Baibulo limasiyana nthaŵi zambiri ndi malingaliro a munthu ngakhale ngati ameneŵa akhala otchuka kwa zaka. Koma mwina munganene kuti, ‘Kodi Baibulo, m’malo ena, silimatchulako za kubadwanso kwa moyo?’
Malemba Amene Amamvedwa Molakwa
Awo amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo amanena kuti Baibulo limatchula za nkhaniyo pa Mateyu 17:11-13, pamene Yesu akugwirizanitsa Yohane Mbatizi ndi Eliya mneneri wakale. Lembali limati: “Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, . . . Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nawo za Yohane Mbatizi.”
Ponena zimenezi, kodi Yesu anatanthauza kuti Yohane Mbatizi anali moyo wobadwanso wa mneneri Eliya? Yohane mwiniyo anadziŵa kuti sanali. Panthaŵi ina pamene anafunsidwa kuti, “Ndiwe Eliya kodi?” Yohane anayankha momvekera bwino kuti: “Sindine iye.” (Yohane 1:21) Komabe, kudanenedweratu kuti Yohane akatsogolera Mesiya “ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya.” (Luka 1:17; Malaki 4:5, 6) M’mawu ena, Yohane Mbatizi anali “Eliya” m’lingaliro lakuti anachita ntchito yofanana ndi ija ya Eliya.
Pa Yohane 9:1, 2, timaŵerenga kuti: “Ndipo popita, [Yesu] anaona munthu ali wosaona chibadwire. Ndipo akuphunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?” Ena amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo amanena kuti popeza kuti munthuyu anabadwa wosaona, tchimo lake liyenera kukhala litachitika m’moyo wapapitapo.
Koma mosasamala kanthu za chilichonse chimene chinachititsa funso la ophunzirawo, yankho la Yesu liyenera kukhala maziko ogamulirapo. Iye anati: “Sanachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake.” (Yohane 9:3) Zimenezi zimatsutsa kubadwanso kwa moyo, kumene kumapereka lingaliro lakuti kupunduka kumachititsidwa ndi machimo a m’moyo wapapitapo. Nsonga yakuti palibe aliyense amene angachimwe asanabadwe inatchulidwanso ndi Paulo pamene analemba za Esau ndi Yakobo kuti “asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa.”—Aroma 9:11.
Chiukiriro, Osati Kubadwanso kwa Moyo
Ngakhale kuti Baibulo silimachirikiza chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo, palibe aliyense amene afunikira kugwiritsidwa mwala. Uthenga wa Baibulo umapereka kanthu kena kotonthoza kwambiri kuposa lingaliro la kubadwanso m’dziko lodzala matenda, chisoni, zopweteka, ndi imfa. Chimene Baibulo limapereka sichili chotonthoza chabe komanso ndi choonadi, Mawu enieni a Mulungu.
Paulo anatchula chiphunzitso cholimbikitsacho motere: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Liwulo “kuuka,” kapena mpangidwe wake wina, limapezeka nthaŵi zoposa 50 m’Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo Paulo akunena za ilo kukhala chiphunzitso choyambirira cha chikhulupiriro Chachikristu.—Machitidwe 24:15; Ahebri 6:1, 2.
Mwachionekere, kuuka kwa akufa kumatanthauza kuti imfa iliko. Palibe paliponse m’Baibulo pamene mudzapeza ganizo lililonse lakuti munthu ali ndi moyo wosafa. Ngati munthu anali ndi moyo wosafa umene umalekana ndi thupi pa imfa ndi kupita kumalo a moyo wamuyaya kumwamba kapena ku helo kapena umene umabadwanso, ndiye kuti sipakanafunikira chiukiriro. Komabe, malemba a Baibulo pafupifupi zana limodzi amasonyeza kuti moyo wa munthu suli wosafa, koma kuti umafa ndipo umawonongeka. Baibulo mosasintha limalankhula za imfa kukhala yosemphana ndi moyo, kutanthauza kuti, kusakhalako monga kosemphana ndi kukhalako.
Imfa, kapena kusakhalako, inali chilango cha Adamu ndi Hava kaamba ka kuchimwira Mulungu. Inali chilango, osati njira yoloŵera ku moyo wosafa kwinakwake. Mulungu momvekera bwino ananena kuti iwo akabwerera kumene anachokera—kufumbi lapansi: “M’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Iwo analibe moyo wosafa asanalengedwe ndi Mulungu ndi kuikidwa pa dziko lapansi, m’munda wa Edene, ndipo sanakhale ndi wotero atamwalira.
Kuuka kwa akufa kukuyerekezeredwa ndi kuuka m’tulo, kapena kupumula. Mwachitsanzo, Yesu anati ponena za Lazaro amene anali kupita kukamuukitsa: “Lazaro . . . ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Ponena za mneneri Danieli, timaŵerenga kuti: “Udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.”—Danieli 12:13.
Moyo Wosatha pa Dziko Lapansi
Kodi nchiyani chimene chidzakhala gawo la awo oukitsidwa kwa akufa? Baibulo limalankhula za mitundu iŵiri ya chiukiriro—cha kumwamba ndi cha padziko lapansi. Chiukiriro cha padziko lapansi chidzakhala gawo la unyinji wa awo amene akhalako ndi kufa. Oŵerengeka kwambiri ndiwo amene akhala ndi chiukiriro cha kumwamba, kukalamulira ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 14:1-3; 20:4) Kodi chiukiriro cha padziko lapansi chidzayamba liti? Chidzayamba Mulungu atawononga dongosolo loipa lilipoli ndipo “dziko latsopano,” chitaganya chatsopano cha anthu olungama, litakhazikika.—2 Petro 3:13; Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44.
Mu “dziko latsopano,” simudzakhalanso matenda kapena kuvutika. Ngakhale imfa sidzakhalakonso koma idzaloŵedwa m’malo ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Ndiponso, wamasalmo analosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Mofananamo, Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”—Mateyu 5:5.
Tayerekezerani malonjezo abwino koposa a Mulungu amenewo ndi chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo. Malinga ndi chikhulupiriro chimenecho, kumalingaliridwa kuti mumabwerera nthaŵi ndi nthaŵi kudzakhalanso m’dongosolo lakale loipa la zinthu limodzimodzili. Zimenezi zingatanthauze kuti mudzapitirizabe kuzingidwa ndi kuipa, kuvutika, matenda, ndi kumafa m’njira yoonekera kukhala yosatha. Ha, limenelo ndi lingaliro lopanda chiyembekezo chotani nanga!
Chotero, Baibulo limayankha mafunso akuti, Kodi munayamba mwakhalako? ndipo, Kodi mudzakhalakonso? mwanjira iyi: Ayi, simunakhaleko ndi moyo wina uliwonse kusiyapo wamakonowu. Koma mukhoza kuchititsa moyo wanu kukhala wosatha, inde, wamuyaya. Lerolino, mu “masiku otsiriza” ameneŵa a dongosolo lilipoli, mungathe kukhala ndi chiyembekezo cha kupulumuka mapeto a dzikoli ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu popanda kumwalira. (2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 7:9-15) Kapena ngati mumwalira dziko latsopano la Mulungu lisanadze, mungakhale ndi chiyembekezo cha kuukitsidwira ku moyo wamuyaya pa dziko lapansi laparadaiso.—Luka 23:43.
Ngati musonyeza chikhulupiriro mwa Yesu, mosasamala kanthu ndi zimene zingachitike, mawu a Yesu kwa Marita pamene mlongo wake Lazaro anamwalira amagwiranso ntchito kwa inu: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”—Yohane 11:25, 26.
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Adamu analibe moyo wosafa koma anabwerera kufumbi pamene anamwalira
[Chithunzi patsamba 24]
Mawu a Mulungu amaphunzitsa za chiukiriro, osati kubadwanso kwa moyo