Lingaliro la Baibulo
Kodi Nkotheka Kupulumutsa Ukwati Mnzanu Atachimwa?
“Ndinena kwa inu, amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.”—MATEYU 19:9.
NDI mawu amenewo Yesu Kristu anapereka chilolezo kwa Mkristu chakuti akhoza kusudzula mnzake wochimwa.a Komabe, bwanji ngati wosachimwayo wasankha kuusunga ukwati wawo ndipo munthu ndi mkazi wake nkutsimikiza kuti adzaumanganso unansiwo? Kodi ndi mavuto otani omwe iwo adzakumana nawo, ndipo kodi angawathetse motani? Tiyeni tione mmene Baibulo limatithandizira kuyankha mafunso ameneŵa.
Nyumba Yopasuka
Choyamba tiyenera kuzindikira kukula kwake kwa zimene kusakhulupirika kwawononga. Monga momwe Yesu Kristu anafotokozera, Woyambitsa ukwati anafuna kuti mwamuna ndi mkazi ‘asakhalenso aŵiri, koma thupi limodzi.’ Anawonjeza kuti: “Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” Inde, ukwati unalinganizidwa kuti ugwirizanitse anthu mosalekanitsika. Pamene munthu aswa lumbiro la ukwati mwa kuchita chigololo, pamakhala zotsatirapo zopweteka kwenikweni.—Mateyu 19:6; Agalatiya 6:7.
Umboni wa zimenezi ndiyo nsautso yomwe wosachimwayo amakhala nayo. Zotsatirapo za chigololo zingafanizidwe ndi za mkuntho umene umapasula nyumba. Dr. Shirley P. Glass anati: “Anthu angapo amene ndawapima anandiuza kuti chikanawakhalira chopepukako ngati mnzawo anachita kumwalira.” Zoona, ena omwe anafedwa anzawo angakane zimenezo. Komabe, nzachionekere kuti chigololo chimapweteka mtima kwabasi. Anthu ena samaiŵaliratu chinyengocho.
Polingalira nsautso yoteroyo, wina angafunse kuti, ‘Kodi chigololo chiyenera kuthetsa ukwati?’ Mwinamwake. Mawu a Yesu ponena za chigololo amasonyeza kuti wosachimwayo ali ndi ufulu wa m’Malemba wa kusudzula mnzake koma sali wokakamizika kutero. Amuna ena ndi akazi awo amamvana kumanganso ndi kulimbitsa chimene chinaswekacho mwa kusintha zimene zifunikira kusintha—ngakhale kuti palibe chimene chimalungamitsa chigololo.
Inde, nkwabwino kusintha zimene zifunikira kusintha mu ukwati pamene onse ali okhulupirika kwa wina ndi mnzake. Komabe, ngakhale pamene wina wachimwa, ena osachimwa amasankha kuusungabe ukwatiwo. M’malo mwa kusankha kuchita zimenezo akumaganiza kuti zonse zidzakhala bwino, wosachimwayo ayenera kulingalira zotsatirapo zake. Adzalingalira zofuna za ana ake ngakhalenso zimene iye afuna mwauzimu, mumtima mwake, kuthupi, ndi m’zandalama. Angachitenso mwanzeru kulingalira ngati kuli kotheka kuupulumutsa ukwati wake.
Kodi Ukwatiwo Ngwotheka Kuupulumutsa?
Womanga asanayese kumanganso nyumba yomwe mkuntho unagwetsa, ayenera kuona ngati nkotheka kuibwezeretsa pakale paja. Mofananamo, asanayese kumanganso ukwati umene kusakhulupirika kunapasula, mwamuna ndi mkazi wake—makamaka wosachimwayo—angafune kupenda moona mtima ngati chikondi ndi chidaliro zingakhalemonso mu ukwatiwo.
Chinthu china choyenera kuchilingalira ndiko kuona kuti kodi wolakwayo akusonyeza kulapa koona mtima kapena akuchitabe chigololo “mumtima mwake.” (Mateyu 5:27, 28) Ngakhale akulonjeza kuti adzasintha, kodi akuzengereza kuthetsa unansi wake wachisembwere? (Eksodo 20:14; Levitiko 20:10; Deuteronomo 5:18) Kodi adakali wachimasomaso? Kodi amaimba mlandu mnzake pachigololo chake? Ngati zili choncho, zoyesayesa za kubwezeretsa chidaliro mu ukwatiwo sizingaphule kanthu. Komabe, ngati athetsa chibwenzi chamsericho, ndi kuvomereza mlandu wa kulakwa kwake, ndi kusonyeza kuti watsimikiza kuumanganso ukwatiwo, mnzakeyo angaone maziko oyembekezera kuti tsiku lina angabwezeretse chidaliro chenicheni.—Mateyu 5:29.
Ndiponso, kodi wosachimwayo angakhululukedi? Izi sizikutanthauza kuti sayenera kudandaula kaamba ka kupweteka mtima pa zimene zinachitika kapena kuti ayenera kungofera mkati monga kuti palibe zinachitika. Zikutanthauza kuti adzayesetsa kuti m’kupita kwa nthaŵi, asasungebe chakukhosi. Kukhululuka koteroko kumatenga nthaŵi koma kungathandize kukhazikitsa maziko olimba omangiraponso ukwatiwo.
Kuwola “Zogumuka”
Wosachimwayo atasankha kuupulumutsa ukwati wawo, nchiyani tsopano chimene aŵiriwo ayenera kuchita? Monga momwedi zogumuka za nyumba yowonongeka ndi mkuntho ziyenera kuchotsedwa, “zogumuka” za ukwatiwo ziyenera kuwoledwa. Zimenezo zingatheke pamlingo wakutiwakuti ngati mwamuna ndi mkazi wake auzana maganizo awo. Miyambo 15:22 imati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” Liwu lachihebri lotembenuzidwa “upo” limatanthauza kudziŵana ndipo latembenuzidwa kuti “gulu lodziŵana” pa Salmo 89:7 NW. Chotero, limaphatikizapo osati chabe kunena za pakamwa basi, koma kulankhulana kwenikweni ndi koona mtima kumene kumavumbula zakukhosi kwa onse aŵiri.—Miyambo 13:10.
Mwachitsanzo, nthaŵi zina wosachimwayo angafune kufunsa mnzake mafunso owonjezereka. Chinakhala kwa utali wotani? Ndani wina yemwe amadziŵa za icho? Zoona, zidzakhala zopweteka kwa mwamuna ndi mkazi wake kukambitsirana nkhani zimenezi. Komabe, kwa wosachimwayo chidziŵitso chimenechi chingakhale chofunika kuti akhalenso ndi chidaliro mwa mnzake. Ngati zili choncho, zingakhale bwino kwambiri kuti wochimwayo ayankhe moona mtima ndi molingalira. Ayenera kufotokoza nkhaniyo mwachikondi ndi mwachifundo, akukumbukira kuti cholinga cha kukambitsiranaku nchakuchiritsa, osati kuvulaza aliyense. (Miyambo 12:18; Aefeso 4:25, 26) Onse aŵiri afunikira kugwiritsira ntchito nzeru ndi kudziletsa, ndi kumvetsera mwachifundo pamene akufotokoza maganizo awo ponena za chimene chinachitika.b—Miyambo 18:13; 1 Akorinto 9:25; 2 Petro 1:6.
Omwe ali Mboni za Yehova angafune kupempha chithandizo kwa akulu mumpingo. Inde, kwa Akristu, machimo oopsa monga chigololo ayenera kuululidwa nthaŵi yomweyo kwa akulu, omwe amasamala za moyo wauzimu wa mwamuna ndi mkazi wake ndiponso wa mpingo. Ngati akulu aonana ndi wachigololoyo, ndipo asonyeza kulapa kwenikweni, amamlola kukhalabe mumpingo. Zitakhala choncho, akulu angapitirizebe kuthandiza aŵiriwo.—Yakobo 5:14, 15.
Kuumanganso
Aŵiriwo atakhazika mitima yawo pansi, mwamuna ndi mkazi wake angathe kumanganso mbali zofunika za ukwati wawo. Kulankhulana moona mtima kudzafunikabe. Pamene azindikira zofooka, afunikira kusintha moyenerera.
Makamaka wofunikira kusintha ndi uja wochimwa. Komabe, wosachimwayo ayenera kuchita mbali yake kulimbitsa mbali zofooka mu ukwatiwo. Izi sizikutanthauza kuti ndiye anachititsa chigololocho kapena kuti chingalungamitsidwe—palibe chilichonse chingalungamitse kuchita tchimo loterolo. (Yerekezerani ndi Genesis 3:12; 1 Yohane 5:3.) Zingangotanthauza kuti mungakhale munali mavuto m’banjamo omwe anafuna kuthetsedwa. Kumanganso ndi ntchito ya aŵiri. Kodi nkofunika kulimbitsa mikhalidwe yabwino ndi zonulirapo inu nonse? Kodi munanyalanyaza ntchito zauzimu? Njira yotulukira zofooka zazikulu ndi kusintha zimene zifunikira kusintha njofunika kwambiri pomanganso ukwati wowonongeka.
Kuusamalira
Ngakhale nyumba yomangidwa bwino imafuna kuisamalira nthaŵi zonse. Choncho, nkofunika kwambiri kuusamalira unansi womangidwanso. Mwamuna ndi mkazi wake sayenera kulola nthaŵi yopitapo kuthetsa kufunitsitsa kwawo kutsatira zolinga zawo zatsopano. M’malo molefuka atabwevuka pang’ono, monga atagweranso m’chizoloŵezi chosalankhulana, ayenera kuchitapo kanthu msanga ndi kuwongolera zinthu ndi kupitabe patsogolo.—Miyambo 24:16; Agalatiya 6:9.
Makamaka, mwamuna ndi mkazi ayenera kuika moyo wawo wauzimu patsogolo, osaulola uwo, ndi ukwati wawo womwe, kubwera m’mbuyo mwa ntchito zina. Salmo 127:1 limati: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” Ndiponso, Yesu anachenjeza kuti: “Yense akamva mawu anga ameneŵa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.”—Mateyu 7:24-27.
Inde, ngati mapulinsipulo a Baibulo anyalanyazidwa chifukwa chakuti avuta kuwatsatira, ukwati udzakhala wosalimba pokumana ndi mkuntho wotsatira wa kusakhulupirika. Komabe, ngati mwamuna ndi mkazi wake atsatira miyezo ya Baibulo pankhani zonse, ukwati wawo udzakhala ndi dalitso la Mulungu. Adzakhalanso ndi chisonkhezero champhamvu kwambiri pakukhulupirika kwawo mu ukwati—chifuno chokondweretsa Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu.—Mateyu 22:36-40; Mlaliki 4:12.
[Mawu a M’munsi]
a Pali zifukwa zabwino zimene munthu angasankhire kusudzula mnzake wachigololo. Kuti mudziŵe zochuluka pankhaniyi, onani “Lingaliro la Baibulo: Chigololo—Kukhululukira Kapena Kusakhululukira?” mu kope la Galamukani! ya August 8, 1995.
b Ngati mufuna kudziŵa zochuluka ponena za kumvetsera kwabwino, onani Galamukani! ya February 8, 1994, masamba 22-5, ndi December 8, 1994, masamba 10-13.