Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu ndi Wolamulira Wachichepere Wachuma
PAMENE Yesu akuyendabe kudutsa m’boma la Pereya kulinga ku Yerusalemu, mwamuna wachichepere akumuthamangira ndi kugwada pamaso pake. Mwamunayo akutchedwa wolamulira, mwinamwake kutanthauza kuti iye ali ndi malo otchuka m’sunagoge ya kumaloko kapena ngakhale kuti iye ali chiŵalo cha Bwalo la Milandu Lalikulu Lachiyuda. Ndiponso, iye ali wachuma kwambiri. “Mphunzitsi wabwino,” iye akufunsa tero, “ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
“Unditcha ine wabwino bwanji?” Yesu akuyankha tero. “Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.” Mwachiwonekere mwamuna wachichepereyo akugwiritsira ntchito “wabwino” monga dzina laulemu, chotero Yesu akumulola iye kudziŵa kuti dzina laulemu loterolo liri kokha la Mulungu.
“Koma ngati,” Yesu akupitiriza tero, “ufuna kuloŵa m’moyo, sunga malamulo.”
“Otani?” mwamunayo akufunsa tero.
Akutchula asanu a Malamulo Khumi, Yesu akuyankha kuti: “Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.” Ndipo akuwonjezera ngakhale lamulo lofunika koposa, Yesu akunena kuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”
“Zonsezi ndinasunga kuyambira ndiri mwana,” mwamunayo akuyankha tero ndi kuwona mtima konse. “Ndisowanso chiyani?”
Pomvetsera ku pempho la mwamunayo lofunitsitsa, lowona mtima, Yesu akumva chikondi kaamba ka iye. Koma Yesu akuzindikira kudzi gwirizanitsa kwake ku chuma chakuthupi, ndipo chotero akusonyeza chosoŵa chake kuti: “Chinthu chimodzi chisoŵeka: Pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphwawi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsane ine.”
Yesu akupenyerera, mosakaikira ndi chifundo, pamene mwamunayo akunyamuka ndi kutembenuka napita wachisoni kwambiri. Chuma chake chikumuchititsa khungu ku phindu la chuma chenicheni. “Ndi chovuta chotani nanga,” Yesu akumva chisoni tero, “mmene chidzakhalira kwa achuma kuloŵa ufumu wa Mulungu!”
Mawu a Yesu azizwitsa ophunzirawo. Koma iwo akudabwa ngakhale mowonjezereka pamene iye akupitiriza kulongosola lamulo lachisawawa lakuti: “Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano koposa kuti mwini chuma aloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
“Ndipo angathe kupulumuka ndani?” ophunzirawo akufuna akudziŵa.
Akuwayang’ana molunjika, Yesu akuyankha kuti: “Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”
Atawona kuti iwo apanga chosankha chosiyana kwambiri ndi chija cha wolamulira wachichepere wachuma, Petro akunena kuti: “Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata inu.” Chotero iye akufunsa kuti: “Nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?”
“M’kubadwanso,” Yesu akulonjeza tero, “pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri, kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” Inde, Yesu akusonyeza kuti padzakhala kubadwanso kwa mikhalidwe pa dziko lapansi kotero kuti zinthu zidzakhala monga mmene zinaliri m’munda wa Edene. Ndipo Petro ndi ophunzira ena adzalandira mphoto ya kulamulira ndi Kristu pa Paradaiso ya dziko lapansi imeneyi. Motsimikizirika, mphoto yaikulu yoteroyo iri yoyenera kudzipereka kulikonse!
Ngakhale kuli tero, ngakhale tsopano pali mphoto, monga mmene Yesu molimba mtima akunenera kuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi irinkudza, moyo wosatha.”
Monga mmene Yesu akulonjezera, kulikonse padziko kumene ophunzira ake apitako, iwo amasangalala ndi unansi ndi Akristu anzawo umene uli wathithithi ndi wa mtengo wapatali kuposa uja wosangalalidwa ndi ziŵalo za banja lakuthupi. Wolamulira wachichepere wachumayo mwachiwonekere walephera ponse paŵiri pa mphoto iyi ndi ija ya moyo wosatha mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu.
Pambuyo pake Yesu akuwonjezera kuti: “Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.” Kodi iye akutanthauza chiyani?
Iye akutanthauza kuti anthu ambiri amene ali “oyamba” kusangalala ndi mwaŵi wachipembedzo, onga ngati wolamulira wachichepere wachumayu, sadzaloŵa Ufumu. Iwo adzakhala “akuthungo.” Koma ambiri, kuphatikizapo ophunzira a Yesu odzichepetsa, omwe akusulizidwa ndi Afarisi odzilungamitsa mwaumwini kukhala monga “akuthungo”—monga anthu a kudziko, kapena ‛am ha·’aʹrets—adzakhala “oyamba.” Kukhala kwawo “oyamba” kumatanthauza kuti iwo adzalandira mwaŵi wakukhala olamulira anzake a Kristu mu Ufumuwo. Marko 10:17-31; Mateyu 19:16-30; Luka 18:18-30.
◆ Mwachiwonekere, mwamuna wachichepere wachumayo ali wolamulira wa mtundu wanji?
◆ Nchifukwa ninji Yesu akukana kutchedwa wabwino?
◆ Ndimotani mmene chokumana nacho cha wolamulira wachichepereyo chikuchitira fanizo ngozi ya kukhala wachuma?
◆ Kodi ndi mphoto zotani zomwe Yesu akulonjeza ophunzira ake?
◆ Kodi ndimotani mmene woyambirira akukhalira wakuthungo, ndi wakuthungo kukhala woyambirira?