Wolembedwa ndi Luka
18 Ndiyeno Yesu anawauza fanizo pofuna kuwasonyeza kufunika koti azipemphera nthawi zonse komanso kuti asamataye mtima.+ 2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweruza amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu. 3 Mumzindawo munalinso mkazi wamasiye amene ankapitapita kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene ndili naye pa mlandu, kuti pachitike chilungamo.’ 4 Kwa kanthawi ndithu woweruzayo sankafuna, koma pambuyo pake ananena mumtima mwake kuti, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu aliyense, 5 ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu chifukwa choti akundivutitsa. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kubwera nʼkunditopetsa ndi zimene akupemphazo.’”+ 6 Kenako Ambuye anati: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! 7 Ndiye kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulira kwa iye masana ndi usiku,+ pamene akuwalezera mtima?+ 8 Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga. Kodi Mwana wa munthu akadzafika, adzapezadi chikhulupiriro ngati chimenechi* padziko lapansi?”
9 Yesu ananenanso fanizo lotsatirali kwa ena amene ankadziona ngati olungama, amenenso ankaona anthu ena ngati opanda pake. Iye anati: 10 “Anthu awiri anapita mʼkachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi ndipo winayo anali wokhometsa msonkho. 11 Mfarisi uja anaimirira nʼkuyamba kupemphera mumtima mwake kuti, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ndine wosiyana ndi anthu ena onse. Iwo ndi achifwamba, osalungama komanso achigololo. Ndinenso wosiyana ndi wokhometsa msonkho uyu. 12 Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’+ 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Iye ankangodziguguda pachifuwa nʼkumanena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima* munthu wochimwa ine.’+ 14 Ndithu ndikukuuzani, munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Mfarisi uja.+ Chifukwa aliyense wodzikweza adzachititsidwa manyazi, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”+
15 Ndiyeno anthu ankamubweretsera ana awo kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo ataona zimenezo anayamba kuwakalipira.+ 16 Komabe Yesu anaitana anawo. Iye anati: “Asiyeni anawo abwere kwa ine, musawaletse. Chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu ngati amenewa.+ 17 Ndithu ndikukuuzani, aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono sadzalowa nʼkomwe mu Ufumuwo.”+
18 Tsopano wolamulira wina anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 19 Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 20 Iwe umadziwa malamulo akuti: ‘Musachite chigololo,+ musaphe munthu,*+ musabe,+ musapereke umboni wabodza+ ndiponso lakuti, muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’”+ 21 Ndiyeno iye anati: “Zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamngʼono.” 22 Yesu atamva zimenezo, anamuuza kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene chikusowekabe mwa iwe: Ukagulitse zinthu zonse zimene uli nazo ndipo ndalamazo ukagawe kwa anthu osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 23 Atamva zimenezi, anamva chisoni kwambiri, chifukwa anali wolemera kwambiri.+
24 Yesu anamuyangʼana nʼkunena kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu a ndalama adzalowe mu Ufumu wa Mulungu!+ 25 Kunena zoona, nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 26 Amene anamva zimenezi anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+ 27 Iye anawauza kuti: “Zinthu zosatheka kwa anthu nʼzotheka kwa Mulungu.”+ 28 Koma Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu nʼkukutsatirani.”+ 29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe amene wasiya nyumba, mkazi, azichimwene, makolo kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu+ 30 amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi mu nthawi ino, ndipo mu nthawi* imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.”+
31 Kenako anatengera pambali ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Tamverani! Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo zonse zimene zinalembedwa ndi aneneri zokhudza Mwana wa munthu zikakwaniritsidwa.+ 32 Mwachitsanzo, akamupereka kwa anthu a mitundu ina+ ndipo akamuchitira chipongwe,+ kumunyoza komanso kumulavulira.+ 33 Akakamaliza kumukwapula akamupha,+ koma pa tsiku lachitatu iye adzauka.”+ 34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la chilichonse cha zimenezi chifukwa mawu amenewa anabisika kwa iwo ndipo sanamvetse zimene zinanenedwazo.
35 Tsopano pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona anakhala pansi mʼmphepete mwa msewu nʼkumapemphapempha.+ 36 Atamva gulu la anthu likudutsa chapomwepo, anafunsa chimene chinkachitika. 37 Iwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” 38 Atamva zimenezo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!” 39 Ndiyeno anthu amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula nʼkumamuuza kuti akhale chete. Koma akatero mʼpamenenso iye ankafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!” 40 Choncho Yesu anaima nʼkulamula kuti munthuyo apite naye kwa iye. Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti: 41 “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti: “Ambuye, ndithandizeni kuti ndiyambe kuona.” 42 Choncho Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ 43 Nthawi yomweyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatira+ akulemekeza Mulungu. Komanso anthu onse ataona zimenezi, anatamanda Mulungu.+