Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kudziperekeranji kaamba ka Ena?
“KODI ndi zikondwerero zayani zimene zimatenga malo oyamba m’moyo wanu?” Mtolankhani wa Galamukani! anafunsa funso limeneli kwa gulu la achichepere pa khwalala la anthu ambiri. “Za inemwini,” anatero Mike. “Ndimafuna ‘choyamba’ poyamba, pothera, ndipo nthaŵi zonse.” Susie wazaka zakubadwa khumi ndi zisanu mphambu ziŵiri anati: “Ngati ndinafunikira kusankha kaya ubwino wa banja langa kapena wanga, wanga ukanakhala woyamba.”
Nzachisoni kuti, malingaliro oterowo ngofala. Bukhu lotchedwa The Postponed Generation likusimba za phunziro la ophunzira okwanira 1,125 mwa amene akatswiri a mayanjano a anthu aŵiri anayesera kupeza kaya achichepere anali odera nkhaŵa kwakukulukulu ponena za iwo okha kapena ponena za chitaganya. Zotulukapo? Pafupifupi 80 peresenti anatsimikizira kukhala “ofuna za iwo okha, popanda nkhaŵa iriyonse kapena kudzimva athayo ku chitaganya.”
Pamenepa, nzosadabwitsa kuti ngochepa omwe ngofunitsitsa kudzipereka kaamba ka ena, kuvutitsidwa kapena kuchita zimene angathe m’malo mwa ena. Mabuku onga ngati The Art of Selfishness ndi Looking Out for Number One amakhala ogulidwa koposa, akutumikira monga zitsanzo zolembedwa za kuyambika kwa mkhalidwe wodzikonda. Monga mmene Baibulo linaloserera, anthu lerolino ali “odzikonda.”—2 Timoteo 3:1, 2.
Motero, kodi ndimotani mmene inu mumachitira ku zosoŵa za ena? Mwachitsanzo, ngati mwakonzekera kukhala pansi kuti mupenyerere programu ya pa wailesi yakanema yapamtima ndiyeno Amayi kapena Atate akupemphani kupita ku sitolo, kodi mumakwiya kapena kuipidwa? Kodi mumakana kuchita ntchito zapanyumba, kubwerekana zovala kapena kusiira malo mbale kapena mlongo, kapena kungochitira winawake chabwino pamene ‘sikuli koyenera’? Pamenepo ndiyo nthaŵi yakuti mupange masinthidwe. Koma kodi nchifukwa ninji? Ndipo chofunika koposa, motani?
Magwero a Dyera
Lamulo la Mulungu kwa anthu ake nlakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Ichi chitanthauza kuti tiri ndi thayo lakukhala osamalira, opanda dyera, odera nkhaŵa ku zosoŵa za ena. Ngakhale ndi tero, nthaŵi zonse sitimafikira muyezo wabwino umenewu, ndipo Baibulo limatithandiza kumvetsa chifukwa chake. Pa Genesis 8:21 pamati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata [wake].”
Tate wathu woyambirira Adamu sanasamale mmene kachitidwe kake kachipanduko kakayambukirira ena. Pamenepa, siziyenera kutidabwitsa kuti, ifeyo, mbadwa zake, tinabadwa ndi chilema cha dyera. (Yerekezerani ndi Salmo 51:5.) Ichi chimawonekera modabwitsa m’nthaŵi zoyambirira m’moyo. Magazine a Parents amanena kuti: “Ana onse ngodzikonda. . . . Iwo amakukondani komabe kokha pamene mukuwachitira chinachake.” Ngati silamuliridwa, dyera lingakhale mkhalidwe wawo waumunthu.
Mkhalidwe wina umene umalepheretsa wina kudzipereka mmalo mwa ena ndiwo ulesi. (Miyambo 21:25) Ndithudi, pamene ulesi ulamulira, wina amapanga zodzikhululukira zopeka kupeŵa kuchita zinthu. Miyambo 22:13 imati: “Waulesi ati, Pali mkango panjapo, ndidzaphedwa pamakwalalapo.”
Zoloŵetsedwamo m’Kuthandiza Ena
Fanizo la Msamariya wachifundo lolembedwa pa Luka 10:29-37 limasonyeza kuti kuthandiza ena kungaloŵetsemo kudzipereka nsembe kwenikweni. Poyankha funso lakuti, “Ndipo mnansi wanga ndani?” Yesu anasimba za Myuda yemwe anamenyedwa ndi achifwamba ndikusiidwa wofuna kufa. Mosasamala kanthu za kusamvana kwautundu kokhala pakati pa Ayuda ndi Asamariya, munthu Wachisamariya anasonkhezeredwa kudzipereka kaamba ka mnkhole wa upanduyo. Iye anasamalira zironda za munthuyo, mogwiritsira ntchito vinyo ndi mafuta ake. Kenaka ananyamula munthuyo mosamalitsa namuika pa nyama yake nampereka ku nyumba ya alendo. Iye analipira kwa mwininyumba ya alendoyo malipiro a masiku aŵiri ndikulonjeza kulipira zowonongedwa zowonjezereka zirizonse.
Fanizo logwira mtima iri limanena mwa gogogo za chimene chimatanthauza kudzipereka kaamba ka ena: kukhala woyambirira, kudzipanga mnansi kwa ena. Kumaphatikizapo kukhala wofuna kupereka nthaŵi, nyonga, ndi ndalama. Tiyeni tikambitsirane njira zina zochitira zimenezi.
Kudzipereka kaamba ka Banja Lanu
Anansi anu apondapo nane mpondepo ndiwo ziŵalo za banja lanu—makolo, abale, alongo. Komabe, mungalingalire kuti awo oyandikana nanu kwenikweni ayenera kumvetsetsa moyo wanu wotanganitsidwa ndi kusafuna zopambanitsa kwa inu. Komabe, Baibulo limalangiza kuti: ‘Mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula.’ (1 Petro 4:9) Yesani kuwona zosokoneza zimene zingatulukepo, osati monga zokwiitsa, koma monga mwaŵi wolimbitsira chomangira cha banja.
Eddie akukumbukira kuti: “Ndandanda ya amayi kaŵirikaŵiri inkawasiya otoperatu. Ko-ma sindidzaiŵala konse chimwemwe chowoneka pankhope pawo atatsegula chitseko ndikupeza kuti mbale nzotsukidwa, pansi mpokolopedwa, ndi thebulo yokonzedwa kaamba ka chakudya chamadzulo. Ndiyenera kuvomereza kuti ndikadakonda kuseŵera mpira m’nthaŵiyo, koma kudzipereka kunathandiza kumangirira banja lathu pamodzi.” Kodi mungalingalire njira zina za kudzipereka kaamba ka ziŵalo za banja lanu?
Kukhala Wachifundo kwa Akristu Anzanu
Mtumwi Paulo anati: ‘Chifukwa chake, monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Chimwemwe chochuluka chimatulukapo pamene mudzipereka nokha m’malo mwa Akristu anzanu.—Machitidwe 20:35.
Mwachitsanzo, Chris wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi zakubadwa, ali mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye amasangalala ndi kutumikira chiŵalo cha mpingo chokalamba. Nthaŵi ina mlongoyu anamtumira foni kuti adzamthandize. Chikepe cha m’nyumba yake chinaleka kugwira ntchito, ndipo pokhala wosakhoza kukwera masitepe a nyumba zisanu zosanja, anasowa chochita. Chris atafika, anati: “Kwerani kumsana kwanga ndipo ndidzakuberekani kunka pamwamba ngati ziribwino kwa inu.” Iwo anakwera nafika panyumba yachisanu! Kodi nzotopetsa? Mosakaikira. Koma Chris anafupidwa osati ndi chiyamikiro cha bwenzi lake lokalamba chokha komanso ndi kudziŵa kuti kachitidwe kake kanakondweretsa Mulungu!
Komabe, simuyenera kuyembekezera mikhalidwe yovuta iyi kuti musonyezere ena nkhaŵa yanu. Mwachitsanzo, misonkhano Yachikristu isanayambe ndi pambuyo pake, achichepere ena amakonda kusonkhana pamodzi, ndi kupatula okalamba. Ichi nchosemphana ndi uphungu wa Baibulo wa ‘kuchitira ulemu’ okalamba. (Levitiko 19:32) Nthaŵi zina, moni waubwenzi kapena kukambitsirana kwachidule ndizo zokha zofunika kusangalatsa wokalamba. ‘Koma nzovuta kwa ine kulankhula kwa okalamba,’ inu mungatsutse tero. ‘Tiri ndi zolankhuzana zochepa.’
Doug, yemwe tsopano akutumikira monga mkulu mumpingo Wachikristu, akukumbukira izi mokondwa: “Pamsinkhu wa zaka 19 mabwenzi anga apamtima anali okalamba mokhoza kukhala makolo kapena agogo anga. Iwo anathandizira ku kukula kwanga kwauzimu chotani nanga!” Bwanji osadzipereka pang’ono ndi kupanga mfundo ya kupalana ubwenzi ndi okalamba, mwinamwake pa msonkhano wanu Wachikristu wotsatira? Kaŵirikaŵiri mudzapeza kuti muli ndi zambiri zokambirana kuposa ndi zimene munaganiza poyamba! Ndipo mofanana ndi Doug, mudzapeza kuti mungaphunzire kuchokera ku zokumana nazo zawo zopindulitsa m’moyo.
Kuthandiza “Iwo Akunja”
Pa Akolose 4:5 mtumwi Paulo anati: ‘Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthaŵi ingatayike.’ Mboni za Yehova zimasonyezera ena nkhaŵa mwakulalikira uthenga wa Baibulo. (Mateyu 24:14) Achichepere amene amatenga thayo lawo mosamalitsa pamaso pa Mulungu akusonkhezeredwa kukhala ndi phande mokwanira m’ntchito imeneyi monga mmene kungathekere.
Tamitha akuti: “Ndimadzipereka m’ntchito yolalikira chifukwa cha kukonda kwanga Yehova.” Ngakhale kuti ngwazaka 11 zakubadwa, iye amathera maola ambiri mwezi uliwonse m’ntchito yolengeza. “Kulalikira kumandipatsanso mwaŵi wosonyeza chikondi kwa anansi anga.” M’malo mofuna ntchito zapamwamba, zikwi za Akristu achichepere asankha ntchito yotumikira ena monga alengezi anthaŵi zonse, kaŵirikaŵiri akumagwira ntchito yapambali kudzichirikiza okha. Ena adzipereka mwaufulu kukhala amishonale kapena antchito pa maofesi anthambi osiyanasiyana a Watch Tower Society.
Mumapindula mwa Kupatsa
“Anthu amafunikira anthu ena kaamba ka thanzi lawo,” anatero magazine a American Health. Ofufuza akunenadi kuti anthu amene amadzipereka kaamba ka ena amapeza mapindu a thanzi. Komabe, Yesu Kristu anasonya ku phindu linanso, mwakumati: “Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu.” (Luka 6:38) Munthu wooloŵa manja amakondedwa ndi ena; mosalephera iyenso amalandira kowoloŵa manja!—Yerekezerani ndi Miyambo 11:25.
Motero khalani wopatsa, kudzipereka nokha kaamba ka ena. Nthaŵi zonse pamene chilema chanu chadyera chiwonekera, kumbukirani kuti Mawu a Mulungu amati: ‘Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.’ (1 Akorinto 10:24) Mwakutero mudzapeza osati ubwenzi wa ena wokha komanso chivomerezo cha Mulungu Wam’mwambamwamba.
[Chithunzi patsamba 18]
Kudzipereka kaamba ka ena kumabweretsa chimwemwe chachikulu