Mutu 7
Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
1. Kodi ndichifuno chachikulu chotani chimene Mulungu ali nacho kaamba ka anthu?
HA chikakhala chitonthonzo chotani nanga kuwona nkhondo, upandu ndi kuipitsa kwa dziko lapansi zikuthetsedwa! Ha kukakhala kokondweretsa chotani nanga kukhala pansi pa boma lolungama kwenikweni, mmene mungakhale kusangalala ndi chisungiko chokwanira kaamba ka munthu mwini ndi banja lake! Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzapangitsa zinthu zimenezi kukhala zenizeni. Koma liti?
2. (a) Pamene “tsiku la Yehova” lifika, kodi ndani amene adzagwidwa modzidzimutsa? (b) Kodi tingapewe motani zimenezo kutichitikira?
2 Ponena za chiwonongeko cha dziko chimene chikulambulira njira Dongosolo Latsopano la Mulungu, mtumwi Paulo akuti: “Tsiku la Yehova likudza kwenikweni monga mbala usiku.” Iye akuwonjeza kuti: “Koma inu, abale simuli m’mdima, kotero kuti tsiku limenelo liyenera kukufikirani modzidzimutsa ngati mbala.” (1 Atesalonika 5:2, 4, NW) Chotero pamene “tsiku la Yehova” lifika, awo amene akulephera kulabadira machenjezo adzakhala ngati nyama yogwidwa mwadzidzidzi m’msampha. Koma zimenezo siziyenera kukuchitikirani. Monga momwe lembalo likulongosolera, pali anthu amene ‘saali m’mdima.’ Chifukwa chake nchakuti iwo amafufuza ndi kulabadira chimene Mawu a Mulungu amanena ponena za tsiku lathu.—Luka 21:34-36.
3, 4. (a) Kodi nkuti kumene tanthauzo lokwanira la zochitika za zaka za zana la20 zikulongosoledwa? (b) Kodi ndimfundo zisanu ziti zondandalikidwa mu ulosi Wabaibulo zimene tidzapenda?
3 Baibulo limalongosola momvekera bwino zochitika za m’zaka za zana la20 zino. Koma linachita zimenezi zaka zokwanira zikwi ziŵiri pasadakhale! Pamene kuli kwakuti zambiri za zochitika zenizenizo ziri zofala, Baibulo limasonyeza tanthauzo lake lokwanira.
4 Chidziŵitso cholosera m’Baibulo chonena za tsiku lathu chiri monga zotsatirapozi: (1) Chaka chenicheni chimene Mulungu akapereka “ufumu wa anthu” kwa “aliyense iye afuna.” (2) Zochitika zapadera zimene zikachitika mkati mwa nyengo yodziŵika kukhala “mapeto a dongosolo lazinthu.” (3) Zochitika zachipembedzo zodziwika panthawiyo. (4) Kupulumuka kwa anthu ena ambadwo umene unawona kuyamba kwa “mapeto a dongosolo lazinthu.” (5) Chochitika chochititsa nthumanzi m’zochitika za dziko monga chizindikiro chotsiriza chakuti chiwonongeko cha dziko chatsala pang’ono kuyamba. Tiyeni tipende mfundo zimenezi.
(1) Chaka Chosonyezedwa—1914 C.E.
5. Kodi Mboni za Yehova zinadziŵiratu liti kuti Baibulo linasonya 1914 C.E. kukhala chaka chapadera?
5 Kalekale mu 1876, Mboni za Yehova zinazindikira kuti ulosi Wabaibulo unasonyeza chaka cha 1914 C.E. kukhala nthawi pamene zochitika zazikulu zikachitika zimene zikakhala ndi ziyambukiro zofika patali pa zochitika za anthu. Zinachititsa chenicheni chimenecho kufalitsidwa kwambiri.
6. (a) Kodi nchiyani chimene chafotokozedwa pa Danieli 4:2, 3, 17? (b) Kodi ndani amene ali “uyo” amene Yehova akumpatsa “ufumu”?
6 Ngati mutsegula Baibulo lanu pa Danieli mutu 4, mudzapeza ulosi umene umavumbula chifuno cha Mulungu chonena za kuchita kwake ufumu padziko lapansi. Chifuno cha kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewo chalongosoledwa kukhala “kuti amoyo adziŵe kuti Wam’mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense iye afuna.” (vesi 2, 3, 17) ‘Uyu’ amene Wam’mwambamwambayo ampatsa “ufumu” ndiye Kristu Yesu. Ndipo bukhu lotsirizira la Baibulo limalongosola nthawi imene “ufumu wa dziko” ukuperekedwa kwa iye monga Mfumu yakumwamba. (Chivumbulutso 11:15; 12:10, NW) Pamenepa, zimenezi zikutanthauza kuti, ulosi wa Danieli ukunena za nthawi pamene Mulungu akalowera m’zochitika za anthu mwa kupereka “ufumu wa dziko” kwa Yesu Kristu. Kodi ulosiwu umasonyeza kuti imeneyi ikakhala liti?
7. (a) Kodi ndiloto lolosera lotani limene lalongosoledwa pa Danieli 4:10-16? (b) Kodi linagwira ntchito motani kwa mfumu Nebukadinezara?
7 Loto lolosera m’Danieli limalongosola mtengo waukulu umene unalikhidwa ndi kumangidwa mkombero wachitsulo ndi mkuwa mpaka zitaupitira “nthawi zisanu ndi ziŵiri.” Mkati mwa nthawi imeneyo, ukapatsidwa “mtima wonga wa nyama.” (Danieli 4:10-16) Kodi uwu unatanthauzanji? Mulungu anachititsa Danieli kulongosola kuti: Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, ikachita misala ndi kuchotsedwa pampando wake wachifumu ndi kuingitsidwa pakati pa anthu kukhala monga chirombo. Pambuyo pa zaka zisanu ndi ziŵiri misala ya mfumuyo ikatha. Izi zinachitikadi kwa mfumuyo, ndipo inabwezeretsedwa pampando wake wachifumu monga munthu amene anavomereza kupambana kwa ulamuliro wa Mulungu. (Danieli 4:20-37) Komabe, zonsezi zinali ndi tanthauzo lalikulu kwambiri, ndipo kaamba ka chifukwa chimenecho zalembedwa m’Baibulo.
8. (a) Kodi tanthuzo lokulirapo la ulosiwo likunena za ufumu uti? (b) M’kukwaniritsidwa kokulirapo, kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi kudulidwa kwa mtengowo, ndipo ndimotani mmene ‘mtima wonga wa chirombo unaperekedwera’?
8 Tanthauzo lokulirapolo limanena za ulamuliro wamphamvu kwambiri umene zamoyo zonse padziko lapansi zikapindula nawo. Mu uwo, ulosiwo ukunena kuti, mudzakhala “zakudya zofikira onse” ndi tchinjirizo ngakhale kwa zinyama ndi mbalame. (Danieli 4:12) Ulamuliro wokha umene ungaperekedi mapindu amenewa ndiwo Ufumu wa Mulungu. Malamulo a makhalidwe abwino a boma lolungama limeneli anasonyezedwa mwa mbiri ya Yuda, limodzi ndi mafumu ake mu Yerusalemu. Koma chifukwa cha kusakhulupirika, Yehova analola Yuda kugonjetsedwa ndi Babulo mu 607 B.C.E. Kunali monga ngati kuti mtengo wa m’loto unali utalikhidwa ndi chitsacho kuzengenezedwa ndi mikombero. Maboma autundu achita ulamuliro padziko lonse chiyambire nthawiyo popanda chidodometso cha Mulungu. Popeza kuti maufumu autundu amenewa akuimiriridwa m’Baibulo kukhala “zirombo,” kunali ngati kuti mngelo wochokera kumwambayo anali atalengeza kuti: “Apatsidwe mtima wonga nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziŵiri.” (Danieli 4:16; 8:1-8, 20-22) Koma potsirizira pake, “nthawi zisanu ndi ziŵiri” zimenezo zaulamuliro wochitidwa ndi maboma onga zirombo zikatha. Pamenepo ‘mikombero’ ikachotsedwa, ndipo “mtengo” ukayambiranso kuphuka pamene ulamuliro wa dziko lonse unayamba kuchitidwa ndi uyo amene Yehova akampatsa “ufumu wa dziko.”
9, 10. (a) M’kuŵerengera utali wa “nthawi zisanu ndi ziŵiri,” kodi “nthawi” iriyonse ikutsimikizira kukhala yautali wotani, ndipo ndimotani mmene Baibulo limasonyezera izi? (b) Kodi ndiliti pamene “nthawi zisanu ndi ziŵiri” zinayamba, kodi izo zikulowetsamo zaka zingati, ndipo zikutha liti?
9 Kodi “nthawi zisanu ndi ziŵiri” zimenezo zikakhala zautali wotani? Zazitali kwambiri koposa zaka zisanu ndi ziŵiri zenizeni chifukwa chakuti zaka mazana ambiri pambuyo pake Yesu Kristu anasonyeza kuti “nthawi zoikidwiratu za amitundu” zimenezi zinali kupitirizabe. Zinali ndi ulamuliro wa dziko lonse kuyambira pa kugonjetsa Yerusalemu kwa Babulo mu 607 B.C.E. ndipo zinali kudzapitirizabe kutero kwa nthawi inabe.—Luka 21:24, NW.
10 Dziwonereni mmene Baibulo likutchulira “nthawi” zoloserazo. Chivumbulutso 11:2, 3 chikusonyeza kuti masiku 1 260 akupanga miyezi 42, kapena zaka zitatu ndi theka. Chivumbulutso 12:6, 14 chikutchula chiwerengero chofananacho cha masiku (1 260) koma chikuwatchula kukhala “nthawi [1] ndi zinthawi [2] ndi nusu lanthawi,” kapena “nthawi” zitatu ndi theka. Iriyonse ya “nthawi” zimenezo iri masiku 360 (3 1/2 × 360 = 1 260). Tsiku lirilonse la “nthawi” zolosera zimenezi limaimira chaka chathunthu mogwirizana ndi lamulo lakuti, “tsiku limodzi kuŵerenga chaka chimodzi.” (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Motero “nthawi zisanu ndi ziŵiri” zikwanira zaka 2 520 (7 × 360). Poŵerengera kuyambira m’mphakasa ya 607 B.C.E., pamene ufumu wophiphiritsira wa Mulungu wa Yuda unatsitsidwa ndi Babulo, zaka 2 520 zikutifikitsa kumphakasa ya 1914 C.E. (606 1/4 + 1913 3/4 = 2 520) Ndicho chaka chimene “ufumu wa dziko” unayenera kuperekedwa kwa Yesu Kristu.
11. Kodi olemba mbiri akunenanji ponena za tanthauzo la chaka cha 1914?
11 Zitazindikira kuti Baibulo linasonyadi ku 1914, Mboni za Yehova zinayenera kuyembekezera kwa zaka makumi ambiri zisanawone chotulukapo chake. Kuchiyambiyambi mu 1914 mkhalidwe wamtendere wa dziko unapangitsa kuwonekera kwa ochuluka kuti palibe chirichonse chimene chikachitika. Koma chilimwe chisanathe, chidaliro cha Mboni chinalungamitsidwa pamene dziko linalowetsedwa m’nkhondo imene inalibe yofanana nayo. Popenda bukhu lakuti 1914, wolemba mbiri A. L. Rowse analemba kuti: “Ngati panali chaka chirichonse chimene chinasonyeza mapeto anyengo ndi chiyambi cha ina, chinali 1914. Chaka chimenecho chinathetsa dziko lakale limodzi ndi lingaliro lake lachisungiko ndi kuyambitsa nyengo yamakono, imene mkhalidwe wake uli kupanda chisungiko kumene kuli gawo lathu la tsiku ndi tsiku.”44 Lipoti lina lonena za katswiri wandale zadziko Wachibritishi Winston Churchill linati: “Chipolopolo chimene chinaombedwa pa June 28, 1914, mu Sarajevo, chinaphwanya dziko lachisungiko ndi kulingalira kwanzeru . . . Dziko silinakhale konse malo amodzimodziwo chiyambire panthawi imeneyo. . . . Panali posinthira, ndipo dziko labwino kwambiri, labata ndi lokondweretsa ladzulo linali litazimiririka, losadzawonekanso.”45 Chaka chimenecho, chosonyezedwa ndi ulosi wa Baibulo zaka zikwi zingapo pasadakhale, chinatsimikiziradi kukhala posinthira m’mbiri.
12. Kodi nchiyani chimene chinali chochititsa kusintha kwakukulu m’zochika za anthu mu 1914 ndi pambuyo pake?
12 Poyamba kungawonekere kukhala kwachilendo kuti kulongedwa pampando wachifumu kwa Kristu kungasonyezedwe ndi nkhondo imene inalibe yofanana nayo padziko lapansi. Koma musaiŵale kuti “wolamulira wa dziko” ndiye Satana Mdyerekezi. (Yohane 14:30, NW) Iye sanafune kuwona ufumu wa Mulungu ukutenga ulamuliro wa zochitika za dziko lapansi. Kuti achotse chisamaliro ku Ufumuwo, iye anachititsa anthu kuloŵa m’nkhondo yochirikiza kunena kwawo kwakuti ali ndi ulamuliro. Ndiponso, Baibulo limasonyeza kuti Satana ndi ziwanda zake anayesayesa kulikwira boma la Ufumu panthawi yake yakubadwa. Nchotulukapo chotani? “Munali nkhondo m’mwamba . . . chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene amasokeretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, chinaponyedwa pansi kudziko lapansi ndipo angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Popeza Satana anali atatsaliridwa ndi “kanthaŵi” chabe, mkwiyo wake unali waukulu. (Chivumbulutso 12:3-12, NW) Zaka mazana khumi ndi asanu ndi anayi pasadakhale Baibulo linapereka kulongosola kolondola konena za chotulukapo.
(2) Zochitika Zokhala ndi Tanthauzo Lapadera
13. Kodi nchiyani chimene chinachititsa kufotokoza kwa Yesu ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dongosolo lazinthu’?
13 M’chaka cha 33 C.E., Yesu analongosola mwatsatanetsatane ‘chizindikiro cha kukhala kwake pafupi ndi chamapeto adongosolo la zinthu.’ Chimenechi chalembebwa m’Baibulo m’Mateyu chaputala 24 ndi 25, Marko 13, ndi Luka 21. Pamene anali ndi kagulu ka ophunzira ake m’Yerusalemu, Yesu anali ataneneratu za chiwonongeko cha kachisi kumeneko. Ndiyeno ophunzira ake anafunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti, ndipo nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi chamapeto a dongosolo la zinthu?”—Mateyu 24:1-3, NW.
14. Tchulani zina za zochitika zapadera zimene Yesu anaphatikiza mu “chizindikiro.”
14 Poyankha Yesu anati: “Inu mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo; wonani kuti simukuwopsedwa. Pakuti zinthu zimenezi ziyenera kuchitika, koma mapeto sanafike. Pakuti mtundu udzaukira mtundu wina ndi ufumu kuukira ufumu wina, ndipo padzakhala kupereŵera kwa zakudya ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Zinthu zonsezi ndichiyambi cha zoŵaŵa za nsautso.” Monga momwe Luka 21:11 akusonyezera, iye anatchulanso ‘miliri m’malo osiyanasiyana.’ Iye anachenjeza za “kuwonjezeka kwa kusayeruzika.” Ndipo chifukwa chakumeneko, iye anati “Chikondi cha chiŵerengero chokulirapo chidzazirala.” Ndiponso, kwakukulukulu, iye ananeneratu kuti: “Mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:4-14, NW.
15, 16. (a) Kodi alionse a maulosi a Yesu anakwaniritsidwa Yerusalemu asanawonongedwe mu 70 C.E.? (b) Kodi tikudziŵa motani kuti payeneranso kukhala kukwaniritsidwa kwina, kofunikadi kwambiri?
15 Koma funso lingafunsidwe kuti: ‘Kodi ena a maulosi amenewo sanakwaniritsidwe m’chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma m’chaka cha 70 C.E. chisanachitike?’ Inde, ena anakwaniritsidwa. Koma zochuluka zinalinkudza, monga momwe maulosi enieniwo akusonyezera. Ndithudi, Yesu anali kuyankha funso limene linali nkhawa yapanthawiyo ya ophunzira ake. Koma iye anagwiritsira ntchito mwaŵiwo kupereka chidziŵitso cholongosola zambiri ponena za nthawi pamene “Mwana wa munthu” akadza “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” ndi pamene “ufumu wa Mulungu” ukakhala utayandikira.—Luka 21:27, 31.
16 Ndithudi, zinthu zimenezi sizinachitike pofika chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. Bukhu lotsirizira la Baibulo, lolembedwa pafupifupi 96 C.E., limasonyeza kuti zochitika zonena za Ufumu zimenezi zinali chikhalirebe mtsogolo. (Chivumbulutso 1:1; 11:15-18; 12:3-12) M’chinenero chophiphiritsira Chivumbulutso chimasonyeza kuti nkhondo, kuperewera kwa zakudya, ndi miliri zimene Yesu anali atazineneratu zikakhalabe zochitika zamtsogolo, ndipo pamlingo wosafanana ndi wina uliwonse. Zikasonyeza nthawi pamene Kristu akayamba ndi kumaliza kugonjetsa kwake adani onse a Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 6:1-8) Chenicheni chakuti mbali zina za ulosi wa Yesu zinakwaniritsidwa m’zaka za zana loyamba chikumtsimikizira kukhala wowona, chikumapereka chifukwa chabwino cha kukhalira ndi chidaliro m’zina zimene Yesu ananena kuti zikachitika.
17. Kodi mikhalidwe m’dziko lerolino njosiyana kwambiri ndi mmene inaliri 1914 isanakhale?
17 Kodi maulosi amenewa akhala ndi kukwaniritsidwa kokulirapo ndi kotheratu kumeneku zaka za zana la20 zino? Anthu osadziwa ausinkhu wakubadwa wa zaka zosakwanira 70 angalingalire kuti nthawi zathu siziri zapadera chifukwa chakuti iwo sakukumbukira nthawi pamene zinthu zinali zosiyana. Koma anthu achikulire ndi amenenso ali odziŵa zochitika za m’mbiri amadziwa kuti siziri choncho. Monga momwe bukhu lina la mbiri limalongosolera ponena za zochitika za 1914 kuti: “Maiko khumi ndi asanu okha sanalowe m’nkhondo . . . Koma pakati pawo panalibe dziko lalikulu limene likanakhala ndi mphamvu yakuchita monga mtetezi. Izi sizinachitikepo chiyambire m’mbiri ya dziko; palibe nkhondo iriyonse imene inakhala yaikulu motero. Ulosi wa Baibulo Loyera wakuti: ‘Mtundu udzaukira mtundu wina ndi ufumu kuukira ufumu wina,’ unakwaniritsidwa kwenikweni.”46
18. Kodi nchifukwa ninji tikakhala olakwa ngati tikadanena kuti nkhondo yofalikirayo ndiyo yokha imene inali “chizindikiro”?
18 Koma zinthu zotero sizinali mbali zokha za chimene Yesu analongosola kukhala “chizindikiro.” Pogwiritsira ntchito fanizo, iye anati: “Wonani mkuyu, ndi mitengo yonse: pamene iphukira, muipenya nimuzindikira panokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuwona zinthu izi zirinkuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika.” (Luka 21:29-32) Ngati inu mukanawona mtengo umodzi wokha ukuphuka masamba mosakhala m’nyengo yake, simukanalingalira kuti dzinja linali pafupi. Koma pamene muwona mitengo yonse ikuphuka masamba panyengo yake, mumadziŵa chimene kukutanthauza. Momwemonso, Yesu ananeneratu kuti “kukhala pafupi” kwake ndi “mapeto a dongosolo la zinthu” zikasonyezedwa osati ndi nkhondo yokha, koma ndi zinthu zingapo zonse zikumachitika m’mbadwo umodzi.
19. (a) Monga momwe kwasonyezedwera pa tchati chotsatirapochi, kodi ndimotani mmene mbali zosiyanasiyana za “chizindikiro” zakwaniritsidwira chiyambire 1914? (b) Kodi nchifukwa ninji nkhondo zakale, kupereŵera kwa zakudya, zivomezi, ndi zina zotero, sizikupanga “chizindikiro” chimene Yesu ananena?
19 Kodi zinthu zimenezo zachitika? Pamene mupenda tchati chotsatirapochi chimene chiri ndi mutu wakuti “Kodi Nchiyani Chimene Chidzakhala Chizindikiro?” mungakumbukire kukhala mutaŵerenga zankhondo za zaka mazana ambiri zapitazo. Koma “Nkhondo Yadziko I njapadera pakati pa zina zonse, monga posinthira m’mbiri. Mungakumbukirenso, kuti, kupereŵera kwa zakudya, miliri, zivomezi, nthawi za kusayeruzika ndi zoyesayesa zapadera za kupititsa patsogolo mtendere ndi chisungiko zachitika 1914 isanakhale. Komabe, palibe nthawi ina iriyonse m’mbiri imene zinthu zonsezi zinachitika m’mbadwo umodzi kumlingo waukulu wotero. Kunena mowonadi mtima, ngati zochitikazo chiyambire 1914 sizikukwaniritsa chizindikirocho, kodi nchiyaninso china chimene chikufunika? Mosakaikira, tikukhala ndi moyo panthawi ya “kukhala pafupi” kwa Yesu m’mphamvu ya Ufumu.
20, 21. Kodi ndimotani mmene zochitika zogwirizanitsidwa ndi Nkhondo Yadziko I zimatsimikizirira kukhala chabe “chiyambi cha zoŵaŵa za nsautso,” monga momwe Yesu ananeneratu?
20 Kuwonekera kwa mbali za “chizindikiro” sikunatanthauze kuti Ufumu wa Mulungu ukachotsa panthawi yomweyo kuipa konse padziko lapansi. Monga momwe Yesu ananeneratu, “zinthu zonsezi ziri chiyambi cha zoŵaŵa za nsautso.” (Mateyu 24:8, NW) Zina zinali kudzalondola. The World Book Encyclopedia ikulongosola kuti: “Nkhondo Yadziko I ndi zotsatirapo zake inatsogolera ku vuto landalama lalikulu kopambana m’mbiri mkati mwa zaka zoyambirira za m’ma1930. Zotulukapo zankhondoyo ndi mavuto akubwerera ku mtendere zinachititsa kupanda mpumulo pafupifupi mu mtundu uliwonse.”47 Zaka zoŵerengeka pambuyo pake Nkhondo Yadziko II inaulika. Inali yowopsa kuwirikiza nthawi zambiri yoyamba ija. Chiyambire panthawi imeneyo, kusalemekeza moyo ndi chuma kwakula, ndipo kuwopa upandu kwakhala mbali yamoyo watsiku lirilonse. Makhalidwe abwino akankhiridwa pambali. Kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu kukupereka mavuto amene asakuthetsedwa. Kuipitsidwa kwa malo kukuipitsa mkhalidwe wa moyo ndipo ngakhale kuuwopseza. Ndipo palinso chiwopsezo chachipiyoyo cha nyukliya.
21 Kodi ndiliti pamene “zoŵaŵa za nsautso” zimenezi zinayamba? London Star inati: “Olemba mbiri ena m’zaka za zana lirinkudzalo angadzanene bwino lomwe kuti tsiku limene dziko linapenga linali . . . [mu] 1914.”48 Chaka chimenecho, cha 1914, chinali chitasonyezedweratu kalekale ndi ulosi wa Baibulo.
(3) Zochitika Zapadera Zachipembedzo
22. (a) Kodi Yesu anagwirizanitsa nchiyani ulosi wake wonena za kuwonjezereka kwa kusayeruzika ndi kuzirala kwa chikondi? (b) Kodi ndimotani mmene ziphunzitso za atsogoleri achipembedzo zathandizira mkhalidwe umenewu?
22 Ndiponso pakati pa zochitika zapadera zimene Yesu ananena kuti zikasonyeza “mapeto a dongosolo lazinthu” nzotsatirapozo: “Aneneri onyenga ambiri adzauka ndi kusokeretsa ambiri; ndipo chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusayeruzika chikondi cha chiŵerengero chokulirapo chidzazirala.” (Mateyu 24:11, 12, NW) Yesu anagwirizanitsa kusayeruzika kowonjezereka ndi kuzirala kwa chikondi ndi chisonkhezero cha aneneri onyenga—aphunzitsi achipembedzo amene monyenga amadzinenera kukhala akunenera Mulungu. Poyamba, bukhu lino linapereka maumboni osonyeza kuti atsogoleri achipembedzo achirikiza nkhondo za amitundu, anyalanyaza miyezo Yabaibulo ya makhalidwe abwino kukhala yachikale, ndipo atcha mbali za Baibulo kukhala zonama. Nchotulukapo chotani? ‘Kuzirala’ m’kukonda Mulungu ndi malamulo ake. Kumeneku kwakhala chochititsa chachikulu chakuwonongeka kwa makhalidwe abwino, limodzi ndi kusalemekeza ulamuliro ndi kusadera nkhawa ndi munthu mnzawo.—2 Timoteo 3:1-5.
23, 24. Kodi nchiyani chimene chakhala chikuchitika ku chipembedzo m’zaka zaposachedwapa?
23 Chifukwa cha mikhalidwe yotero, mamiliyoni ambiri achoka m’magulu achipembedzo, ena akutembenukira ku Baibulo ndipo akugwirizanitsa miyoyo yawo ndi njira zake. Ena akungosiya mogwiritsidwa mwala ndi monyansidwa. Ambiri akukhala adani achipembedzo. Mkonzi wina anati: “Munthuwe sungachitire mwina kusiyapo kuchita kakasi ndi mmene vuto la dziko lino liriri lochokera m’chipembedzo. Pali mikangano yoŵerengeka yandale imene imachititsa kusonkhezera nkhondo yokhetsa mwazi mofanana ndi nkhondo yachipembedzo.” Chifukwa cha ichi, iye anafunsa kuti: “Bwanji osathetsa chipembedzo?”49
24 Kunyonyotsoka kwa zipembedzo zazikulu kuli kotsimikiziridwa bwino lomwe. Mwachitsanzo, lipoti lina lonena za Italiya limasonyeza kuti pamene kuli kwakuti 95 peresenti ya anthu imazidziŵikitsa kukhala Akatolika, “ofika m’tchalitchi pa Sande akuyerekezeredwa pa osakwanira 20 peresenti.”50 Lipoti lina likuvumbula kuti chiŵerengero cha ansembe padziko lonse lapansi chinachepa ndi 25 000 m’zaka khumi.51 Mu United States mafufuzidwe a patchalitchi ananeneratu “kutsika kwina kofikira pa 50 peresenti kwa ansembe Achikatolika Achimereka podzafika chaka cha 2000.”52 U.S.News & World Report inanena “kutsika kwakukulu m’chiŵerengero cha amuna oloŵa maseminale Achikatolika” mu United States, kuchokera pa chiŵerengero chapamwamba cha 48 992 kufika pa 11 262 m’zaka zosakwanira 20.53 The New York Times inasimba kuti “Chiŵerengero cha avirigo chatsika kuchoka pa 181 421 kufika pa 121 370” padziko lonse lapansi m’zaka 15.54 Mkhalidwewu ngwofanana mu zipembedzo zochuluka.
25. (a) Mosemphana ndi zimenezo, kodi Baibulo limasonyeza kuti nchiyani chimene chikakhala chikuchitikira kulambira kowona panthawi ino? (b) Kodi kusonkhanitsidwa kwa olambira Mulungu wowona kumeneku kukuchitika motsogozedwa ndiyani, ndipo pamaziko otani? (c) Kodi anthu amitundu yonse akuyang’anizana ndi nkhani yotani?
25 Mosemphana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti “khamu lalikulu” lochokera m’mitundu yonse likasonkhanitsiridwa kukulambiridwa kowona kwa Yehova m’nthawi ino yamapeto. Yesu ananeneratu za kusonkhanitsidwa uku, akumanena kuti akalekanitsa anthu wina ndi mnzake, kaya kaamba ka kusungidwa kupyola “chisautso chachikulu,” kapena “kudulidwa kosatha.” (Chivumbulutso 7:9, 10, 14; Yesaya 2:2-4; Mateyu 25:31-33, 46) Kodi nchiyani chimene chimalekanitsa anthu kaamba ka kupulumuka? Baibulo limayankha kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.” (1 Yohane 2:17) Ndipo kodi ndimotani mmene anthu akadziŵira chimene chiri chifuniro cha Mulungu? Mwa kulabadira kuntchito yophunzitsa ya padziko lonse lapansi imene Yesu ananeneratu pamene anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Kulalikira uku kumachititsa anthu a mitundu yonse kuyang’anizana ndi nkhani yakuti: Kodi iwo akuchirikiza ulamuliro wa Mulungu? Kapena, mogwirizana ndi chisonkhezero cha Satana m’Edene, kodi iwo amafuna ulamuliro woima pawokha wochitidwa ndi anthu? Yehova amapatsa anthu mwaŵi wa kusankha.
26, 27. (a) Kodi ntchito ya umboni imeneyi yachitidwa kale kumlingo wotani? (b) Kodi nchifukwa ninji kulabadira kwa munthu kuuthenga wa Ufumu kuli chinthu chofunika kwambiri?
26 Umboni wapadziko lonse lapansi wa Ufumu ukuperekedwa mwamphamvu yowonjezereka. M’maiko oposa 200, Mboni za Yehova mamiliyoni angapo zimafikira anthu m’nyumba zawo ndi kupereka mwaŵi wa kuphunzira nawo Baibulo, kwaulere. Mabukhu amene izo zimagwiritsira ntchito ali mabukhu ofotokoza Baibulo ofalitsidwa kopambana padziko lapansi. Kwenikweni, iwo ali pakati pa mabukhu ofalitsidwa kopambana amtundu uliwonse. Ndipo amenewa ngopezeka m’zinenero zokwanira 190.
27 Ntchito yolekanitsa iyi yakhala ikuchitika kwa zaka zambiri. Tsopano ikuyandikira mapeto ake. Malinga ndi kunena kwa Mawu a Mulungu, awo amene akana ulamuliro wa Ufumu wake, kudzanso awo amene mwamphwayi akulekerera mwaŵi wa kuphunzira za iye, adzadulidwa. (Mateyu 25:34, 41, 46; 2 Atesalonika 1:6-9) Kwa ena amene amadzidziŵikitsa kukhala ochirikiza Ufumu wa Mulungu, imeneyi idzasonyeza kukhala nthawi ya mpumulo waukulu. Koma kodi ndiliti pamene chiweruzochi chidzadza?
(4) “Mbadwo Uwu Sudzatha Kuchoka”
28. Kodi ndimkati mwa nthawi yotani mmene Yesu ananeneratu kuti chiwonongeko cha dziko chonenedweratu chikadza?
28 Ponena za “tsiku iro ndi nthaŵi yake,” Yesu anati, “sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo akumwamba kapena mwana, koma atate yekha.” Koma Yesu anaperekadi chosonyeza nthawi chothandiza pamene iye anati: “Mbadwo uwu sudzatha kuchoka kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34, 36) Chotero mbali zosiyanasiyana zonse za “chizindikiro,” kudzanso ‘chisautso chachikulu,’ ziyenera kuchitika mkati mwa nthawi ya moyo wa mbadwo umodzi—mbadwo wa 1914. Izi zitanthauza kuti anthu ena amene anawona zochitika za 1914, pamene ‘mapeto a dongosolo lazinthu’ anayamba, akakhalabe amoyo kuwona mapeto ake pamene ‘chisautso chachikulu’ chikukantha. Awo amene akukumbukira zochitika za 1914 akukalamba tsopano. Ambiri a iwo afa kale. Koma Yesu akutitsimikizira kuti “mbadwo uwu sudzatha kuchoka” chiwonongeko cha dongosolo iri lazinthu chisanadze.—Mateyu 24:21.
29. Mwakulola zochitika chiyambire 1914 kukula mpaka pamene zafikapa, kodi ndimotani mmene Mulungu wapangitsira kukhala kosavuta kwambiri kwa anthu kupanga chosankha choyenera?
29 Ha ndiwodekha motani nanga mmene Mulungu wakhalira kulola mwaŵi wowonjezereka uwu wa kulapa! (2 Petro 3:9) Kwanthawi yoyamba m’mbiri, mavuto otsatanatsatana afika pamilingo yaikulu kopambana—nkhondo, kuipitsa, kuchulukitsitsa kwa chiŵerengero cha anthu, ndi ena otero. Lirilonse la iwo lingathe kudzetsa chiwonongeko chotheratu. Mwa kulola umboni wotere kuunjikana, Mulungu wapangitsa kukhala kosavuta kwambiri kuti anthu awone kuti munthu alibe mayankho. Panthawi imodzimodziyo, kulalikidwa kwa “mbiri yabwino ya ufumu” kwathandiza anthu owona mtima kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha kaamba ka mtendere weniweni ndi chisungiko. Chotero Mulungu amawapatsa nthawi ya kudziika kumbali yake ya mkangano waukuluwo.
(5) Chizindikiro Chomaliza
30. Kodi nchizindikiro chotsirizira chotani cha kuyandikira kwa chiwonongeko cha dziko chimene Baibulo limasonyeza?
30 Pali chikhalirebe chochitika china chimodzi chimene chidzadza monga chizindikiro chosalakwika chakuti chiwonongeko cha dziko chatsala pang’ono. Ponena za chimenechi mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, . . . ndipo sadzapulumuka konse.”—1 Atesalonika 5:2, 3; Luka 21:34, 35.
31, 32. (a) Kodi “mtendere ndi chisungiko” zimene olamulira andale za dziko akulengeza zidzakhala zenizeni? (b) Kodi nchifukwa ninji kukakhala kwaupandu kusokeretsedwa nazo?
31 Atsogoleri adziko amadziŵa kuti nkhondo ya nyukliya imatanthauza kusolotseratu. Ndiponso, mavuto aakulu monga ngati kuipitsidwa kwa malo okhala, kuchuluka kwambiri kwa chiŵerengero cha anthu, ndi mavuto a m’banja amafuna chisamaliro ndi ndalama. Chotero iwo akufuna kukonza maunansi owonongedwa a pakati pa mitundu. Umboni wa ichi ndiwo chilengezo chochitidwa ndi Mitundu Yogwirizana cha 1986 kukhala ‘chaka cha mtendere ndi chisungiko cha mitundu yonse.’ Mosakaikira, ichi, chiri sitepe lomka ku kukwaniritsidwa kwa mawu ogwidwa pamwambapawa a Paulo. Ndithudi, makambitsirano andale zadziko ndi mapangano sakupanga masinthidwe enieni alionse mwa anthu kuwachititsa kukondana. Iwo sakuletsa upandu, ndiponso sakuthetsa matenda ndi imfa. Komabe ulosiwo umasonyeza kuti nthawi idzafika pamene mitundu idzalengeza kuti yapeza mlingo wakutiwakuti wa ‘mtendere ndi chisungiko.’ Pamene chimenechi chichitika, pomwepo ‘chiwonongeko cha mwadzidzidzi’ chidzadza ‘modzidzimutsa’ pa awo osokeretsa anthu, limodzi ndi onse amene amaika chidaliro chawo mwa iwo.
32 Koma padzakhala opulumuka. Kodi inu mudzakhala mmodzi wa iwo?
[Bokosi pamasamba 78, 79]
“Kodi Nchiyani Chimene Chidzakhala Chizindikiro?”
“Mtundu Udzaukira Mtundu Wina”—
“Nkhondo Yadziko I inayambitsa zaka zana za Nkhondo Yotheratu, za—m’lingaliro loyambirira kotheratu la liwulo—nkhondo yadziko lonse lapansi. . . . Ndikale lonse 1914-1918 isanakhale . . . nkhondo siinakute chigawo chachikulu kwambiri cha dziko lapansi. . . . Ndikale lonse sipanakhale kupha kwakukulu kwambiri ndi kosasankha.”—World War I Lolembedwa ndi H. Baldwin.
Nkhondo Yadziko I inapha asilikali ankhondo ndi alaiya mamiliyoni 14; Nkhondo Yadziko II inapha mamiliyoni 55. Chiyambire Nkhondo Yadziko II panali mazana ambiri a kulandidwa kwa maboma, zipanduko, ndipo nkhondo zapha miyoyo ya anthu okwanira mamiliyoni 35.
Chotero, chiyambire 1914 miyoyo yoposa mamiliyoni 100 yatayika m’nkhondo!
“Padzakhala Kupereŵera kwa Zakudya”—
Kupereŵera kwa zakudya kunakhalapo maiko ambiri pambuyo pa Nkhondo Yadziko I ndi Nkhondo Yadziko II.
Tsopano, mosasamala kanthu za zaka zambiri zakupita patsogolo kwa sayansi, pafupifupi nusu ya dziko iri ndi njala. Ana oyerekezeredwa kukhala mamiliyoni 12 chaka chirichonse amafa asanathe chaka chifukwa cha kudya kosakwanira. Ena mamiliyoni ambiri amafanso chaka ndi chaka kaamba ka chifukwa chofanana.
“Miliri”—
Palibe mliri wolembedwa umene ndikale lonse unafanana ndi uja wa fuluwenza Yasipanya ya 1918-1919. Inadwalitsa anthu okwanira mamiliyoni 500; oposa mamiliyoni 20 anafa.
Ofufuza mankhwala sanakhoze kuletsa chinthu chonga nthenda yamtima kuti isafike mlingo wa mliri. Kensa iri mliri womakulakula. Chiŵerengero cha ogwidwa ndi nthenda zopatsirana mwa kugonana chakwera kwambiri.
“Zivomezi” m’Malo Ambiri—
Modalira pa magwero ake, ziŵerengero zoyerekezeredwa za akufa zimasiyanasiyana. Koma kupereka zitsanzo zochepa: 30 000 mpaka 32 000 anafa m’chivomezi m’Italiya mu 1915; 100 000 mpaka 200 000 m’Tchayina mu 1920; 95 000 mpaka 150 000 m’Japani mu 1923; 25-000 mpaka 60 000 m’Indiya mu 1935; 12 000 mpaka 20 000 m’Iran mu 1968; 54 000 mpaka 70 000 m’Peru mu 1970; 20 000 mpaka 23 000 m’Guatemala mu 1976; 100 000 mpaka 800 000 m’Tchayina mu 1976. Kuyambira 1914 zikwi mazana ambiri za ena zafa m’zivomezi zazikulu zikwi zambiri padziko lonse lapansi.
Ziŵerengero zochokera m’magwero osiyanasiyana zimasonyeza kuti avereji ya chiŵerengero cha zivomezi zazikulu chaka chirichonse chiyambire 1914 yakhala yokulirapo kuwirikiza nthawi zambiri kuposa avereji ya chiŵerengo cha zaka 2 000 chakachi chisanafike.
“Kuwonjezeka kwa Kusayeruzika”—
Inu mudziŵa zenizeni. Kukwera kwa upandu kukuyambukira dziko lirilonse padziko lapansi. Moyo wa inu mwini wayambukiridwa. M’chitaganya chanu, kodi nchiyani chimene chakhala chikuchitika m’masukulu? Kodi m’dera lanu muli kugwiritsiridwa ntchito kosaloledwa ndi lamulo kwa mankhwala? Bwanji ponena za kusawona mtima m’bizinesi? Kodi mumawona kukhala wosungika motani m’makwalala usiku?
Kusayeruzika sikuli kokha ponena za malamulo aumunthu, koma iko kuli kwakukulukulu kotero ponena za lamulo la Mulungu. (Wonani 2 Timoteo 3:1-5, 13.)
“Ufumu wa Mulungu Ukulalikidwa pa Dziko Lonse”—
Ntchitoyi ikuchitidwa mokhazikika ndi Mboni za Yehova mamiliyoni angapo m’maiko oposa 200.
Mkati mwa zaka khumi zokha zapita, maola pafupifupi mabiliyoni anayi (mamiliyoni chikwi) awonongeredwa ndi Mboni za Yehova m’kulalikidwa kwapoyera kwa uthenga uwu. M’nyengo imodzimodzi imeneyo izo zafalitsa, m’zinenero zokwanira 190, mabukhu oposa mabiliyoni 5 osonya ku Ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo chokha cha munthu.
Kulengezedwa kwa “Mtendere ndi Chisungiko”—
Atsogoleri akuvomereza kufunika kwa mtendere kuti apewe chiwonongeko cha nyukliya ndi kusamalira mavuto ena omakulakula. Sitepe lomka kucholinga ichi ndiro chilengezo chochitidwa ndi Mitundu Yogwirizana cha 1986 kukhala chaka cha “mtendere, chisungiko cha mitundu yonse ndi kugwirizana.”—General Assembly, Agenda item 32, msonkhano wa39.
Kodi zinthu zonsezi ziri “chizindikiro” cha chiyani?
Chakuti ife tsopano tikukhala ndi moyo mu “mapeto a dongosolo la zinthu.” Chakuti Kristu wakhala pampando wake wachifumu ndipo akulekanitsa mwa anthu a mitundu yonse awo amene akufunadi kuchita chifuniro cha Mulungu. Chakuti “chisautso chachikulu” chayandikira kwambiri. Kaamba ka maumboni owonjezereka, ŵerengani Mateyu chaputala 24 ndi 25, Marko 13, ndi Luka 21.