Danieli
4 “Uwu ndi uthenga wochokera kwa ine Mfumu Nebukadinezara wopita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana amene akukhala padziko lonse lapansi: Mukhale ndi mtendere wochuluka. 2 Ndine wosangalala kukuuzani zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wamʼmwambamwamba wandichitira. 3 Zizindikiro zake nʼzazikulu ndipo zochita zake nʼzamphamvu. Ufumu wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ulamuliro wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
4 Ine Nebukadinezara ndinkakhala mwabata mʼnyumba mwanga ndipo zinthu zinkandiyendera bwino mʼnyumba yanga yachifumu. 5 Ndiyeno ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Nditagona pabedi langa ndinaona zithunzithunzi ndi masomphenya zimene zinandichititsa mantha.+ 6 Choncho ndinalamula kuti amuna onse anzeru a mʼBabulo awabweretse kwa ine kuti adzandimasulire malotowo.+
7 Pa nthawi imeneyo ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine. Nditawafotokozera malotowo, sanathe kundiuza kumasulira kwake.+ 8 Kenako Danieli, amene ndinamupatsa dzina lakuti Belitesazara+ potengera dzina la mulungu wanga,+ amenenso mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera,+ anabwera kwa ine ndipo ndinamuuza malotowo kuti:
9 ‘Iwe Belitesazara mkulu wa ansembe ochita zamatsenga,+ ndikudziwa bwino kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe+ ndipo palibe chinsinsi chimene ndi chovuta kwambiri kwa iwe.+ Choncho ndiuze zinthu zimene ndinaona mʼmaloto anga komanso kumasulira kwake.
10 Ine nditagona pabedi langa ndinaona masomphenya. Ndinaona mtengo+ wautali kwambiri uli pakati pa dziko lapansi.+ 11 Mtengowo unakula ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Nsonga yake inafika kumwamba ndipo umaonekera mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi. 12 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri, moti anthu ndi nyama ankapezamo chakudya chokwanira. Nyama zakutchire zinkakhala mumthunzi wake ndipo mbalame zamumlengalenga zinkakhala munthambi zake. Zamoyo zonse zinkapeza chakudya mumtengowo.
13 Ndikuona masomphenyawo ndili pabedi langa, ndinaona mlonda, mthenga woyera akutsika kuchokera kumwamba.+ 14 Mlondayo analankhula mofuula kuti: “Gwetsani mtengowo+ ndipo mudule nthambi zake. Yoyolani masamba ake ndipo mumwaze zipatso zake. Nyama zithawe pansi pake ndipo mbalame zichoke panthambi zake. 15 Koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo komanso wakopa.* Chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chikhalenso pakati pa nyama zakutchire ndi udzu wapadziko lapansi.+ 16 Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu nʼkukhala mtima wa nyama ndipo padutse+ nthawi zokwana 7.+ 17 Alonda ndi amene alamula zimenezi.+ Amithenga oyera ndi amene apempha zimenezi nʼcholinga chakuti anthu adziwe kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso adziwe kuti iye amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa ndipo amaika ngakhale munthu wonyozeka kwambiri kuti azilamulira.”
18 Amenewa ndi maloto amene ine Mfumu Nebukadinezara ndinalota. Tsopano iwe Belitesazara umasulire malotowa, chifukwa amuna ena onse anzeru a mu ufumu wanga alephera kundiuza kumasulira kwake.+ Koma iwe ungathe kuwamasulira chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.’
19 Pa nthawi imeneyo Danieli, amene dzina lake ndi Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.
Mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, usachite mantha ndi malotowa komanso kumasulira kwake.’
Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.
20 Inu munaona mtengo umene unakula kwambiri ndipo unakhala wamphamvu. Nsonga ya mtengowo inakafika mpaka kumwamba ndipo unkaoneka padziko lonse lapansi.+ 21 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira anthu ndi nyama zonse. Nyama zakutchire zinkakhala pansi pake ndipo mbalame zamumlengalenga zinkakhala munthambi zake.+ 22 Mtengowo ndi inuyo mfumu, chifukwa mwakula ndipo mwakhala wamphamvu. Ulemerero wanu wakula mpaka kukafika kumwamba+ ndipo ulamuliro wanu wafika kumalekezero a dziko lapansi.+
23 Ndiyeno inu mfumu munaona mlonda,+ mthenga woyera akutsika kuchokera kumwamba, ndipo ankanena kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo muuwononge, koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo ndi wakopa.* Chitsacho chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chizikhala limodzi ndi nyama zakutchire mpaka patadutsa nthawi zokwana 7.”+ 24 Kumasulira kwake ndi kumeneku inu mfumu. Zimene zidzakuchitikireni inu mbuyanga mfumu ndi lamulo la Mulungu Wamʼmwambamwamba. 25 Inuyo adzakuthamangitsani pakati pa anthu ndipo muzidzakhala ndi nyama zakutchire. Muzidzadya udzu ngati ngʼombe ndipo muzidzanyowa ndi mame akumwamba.+ Ndiyeno padzadutsa+ nthawi zokwana 7+ mpaka mutadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.+
26 Koma chifukwa ananena kuti asiye chitsa cha mtengowo ndi mizu yake,+ inu mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu mutadziwa kuti Mulungu ndi amene akulamulira kumwamba. 27 Choncho inu mfumu, mverani malangizo anga. Musiye kuchita machimo ndipo muzichita zinthu zabwino. Musiyenso kuchita zinthu zoipa ndipo muzichitira chifundo anthu osauka. Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+
28 Zonsezi zinachitikiradi Mfumu Nebukadinezara.
29 Patapita miyezi 12 Nebukadinezara ankayenda padenga la nyumba yachifumu ya ku Babulo. 30 Mfumuyo inkanena kuti: “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu kuti kukhale nyumba yachifumu nʼcholinga choti ulemerero wa ufumu wanga uonekere?”
31 Mfumuyo ili mkati molankhula mawu amenewa, kumwamba kunamveka mawu akuti: “Tamvera iwe Mfumu Nebukadinezara! ‘Ufumu wachoka mʼmanja mwako,+ 32 ndipo akuthamangitsa pakati pa anthu. Uzikhala ndi nyama zakutchire ndipo uzidya udzu ngati ngʼombe. Ndiyeno padutsa nthawi zokwana 7 mpaka utadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.’”+
33 Nthawi yomweyo mawuwa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara. Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo anayamba kudya udzu ngati ngʼombe komanso thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba. Tsitsi lake linatalika kwambiri ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.+
34 “Nthawi imeneyi itatha,+ ine Nebukadinezara ndinayangʼana kumwamba ndipo nzeru zanga zinabwerera. Ndinatamanda Wamʼmwambamwamba ndipo amene adzakhalepo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza, chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo kumibadwomibadwo.+ 35 Anthu onse okhala padziko lapansi ndi opanda pake poyerekezera ndi Mulungu. Iye amachita zinthu mogwirizana ndi zofuna zake pakati pa magulu akumwamba ndi anthu okhala padziko lapansi. Palibe aliyense amene angamulepheretse kuchita zimene akufuna+ kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
36 Pa nthawi imeneyo nzeru zanga zinabwerera ndipo ndinalandiranso ufumu wanga ndi ulemerero wake wonse komanso ulemu.+ Nduna zanga zikuluzikulu ndi anthu olemekezeka anayamba kufunsiranso malangizo kwa ine. Ndinabwezeretsedwa pampando wanga wachifumu ndipo anthu anayamba kundipatsa ulemu waukulu.
37 Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndi zogwirizana ndi choonadi, njira zake ndi zolungama+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+