Pitirizani Kulalikira Ufumu
“Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—MATEYU 24:14, NW.
1, 2. (a) Ndi ntchito iti imene iri yofunika koposa ya m’zana lino, ndipo ndi kuutali wotani kumene iyo ikuchitidwira? (b) Ndi chitsimikizo chotani chimene chiripo cha dalitso la Yehova pa ntchito imeneyi?
KULALIKIRA mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu iri ntchito yofunika koposa ya m’zana lino. Iri imene Mulungu Wamphamvuyonse amafuna kuti ichitidwe tsopano, ndipo ikukwaniritsidwa m’kukwaniritsa Mawu ake aulosi. Chivomerezo chanu ku iyo chidzayambukira mtsogolo mwanu mosatha.—1 Akorinto 9:16, 23.
2 Chiri chosangalatsa kuwona kuti unyinji wa ogawana m’ntchito yolalikira imeneyi ukupitiriza kuwonjezereka, tsopano wokhala ndi oposa mamiliyoni atatu akutengamo mbali. Ziŵerengero zokulira kuposa ndi kalelonse zikulowa mu utumiki wa nthaŵi zonse. Ndipo anthu ambiri okondwerera akuvomereza phunziro la Baibulo ndi kuika kuyesetsa koyenerera kwa kuphunzira chifuno cha Mulungu.
3. Nchiyani chimene ena anganene ponena za chifuno cha kupitirizabe ndi kulalikira mbiri yabwino?
3 Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, ena “amaleka kuchita chabwino” ndi “kutopa” m’chigwirizano ndi ntchito yolalikira. (Agalatiya 6:9; Ahebri 12:3) Iwo anganene kuti mbiri yabwino yalalikidwa kale mokulira m’magawo awo ndipo kuti anthu atenga kaimidwe kawo ndipo tsopano akuipidwa pamene tiitanira pa nyumba zawo. Awo amene amachita ntchito yolalikira kumeneko amapeza zotulukapo zochepa kwambiri mwinamwake popanda chotulukapo nkomwe. Chotero, mwinamwake iwo amadzimva kuti, ntchito yachitidwa kale mokulira, ndipo palibe chifuno cha kupitirizira. Nchiyani chimene chiri cholakwika ndi kalingaliridwe kotereka?
Nchifukwa Ninji Kuumirira?
4. Nchiyani chimene chiyenera kutisonkhezera ife kupitiriza kulalikira ngakhale m’gawo limene chivomerezo chiri choipa?
4 Choyamba, kupirira kwathu mokhulupirika m’ntchito yolalikira sikuyenera kudalira pa kaya anthu adzamvetsera kwa ife kapena ayi. Yeremiya analalikira kwa zaka 40 m’Yerusalemu ngakhale kuti ochepa kwambiri anamvetsera ndipo ambiri mwachiwawa anamutsutsa iye. Nchifukwa ninji iye anaumirira? Chifukwa iye anali kuchita ntchito imene Yehova anailamulira ndiponso chifukwa chakuti chidziŵitso chake cha ulosi wa zomwe zinayenera kudzachitika ku Yerusalemu chinamukakamiza iye kupitirizabe kulankhula. (Yeremiya 1:17-19) Iye ananena kuti: “M’mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:7-10) Mkhalidwe wathu uli wofanana. Ali Yehova, kupyolera mwa Yesu Kristu, yemwe analamulira kuti “mbiri yabwino” iyenera kulalikidwa padziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. (Mateyu 24:14) Pamene anthu akana kumvetsera, ichi chimatipatsa ife mwaŵi wa kusonyeza kuzama kwa chikondi chathu ndi kudzipereka kwa Yehova mwa kuumirira kuchita chimene chiri chabwino. (1 Yohane 5:3) Pambali pa icho, pamene tisinkhasinkha pa zimene mtsogolo moyandikiramo mwasunga kaamba ka mtundu wa anthu, ndimotani mmene tingadziletsere ife eni kuyesetsa kuchenjeza anansi athu?—2 Timoteo 4:2.
5. (a) Ndi kaamba ka chifukwa china chiti chimene tiyenera kupirira m’ntchito yolalikira? (b) Ndimotani mmene ntchito yolalikira iliri maziko kaamba ka chiweruzo?
5 Ndiponso, kulalikira kwa Yeremiya kunalidi ntchito ya chiweruzo. Mu 607 B.C.E., palibe ndi mmodzi yense wa awo amene anavutika ndi imfa kapena kuikidwa m’ndende pamene Yerusalemu anagwa anakhoza kudzinenera kuti iwo sanadziŵa nchifukwa ninji ichi chinali kuchitika kwa iwo. Kwa zaka 40 kumayambiriro, Yeremiya anali atawachenjeza iwo za chotulukapo choterocho ngati iwo akapitiriza kukhala owukira motsutsana ndi Yehova. (Yerekezani ndi Ezekieli 2:5.) Mofananamo lerolino, kulalikira kwa mbiri yabwino monga “umboni kwa mitundu yonse” kuli maziko kaamba ka chiweruzo. Mtumwi Paulo amachimveketsa bwino chimenechi pamene iye ananena kuti Kristu Yesu adzabweretsa chilango pa “iwo osadziŵa Mulungu ndi iwo osamvera mbiri yabwino ya Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:8, 9) Anthu adzaweruzidwa ndi chivomerezo chawo ku mbiri yabwino. Chotero, ntchito yolalikira iyenera kupitiriza mofuula ndi momvekera kufikira kumapeto. (Chivumbulutso 14:6, 7) Palibe chirichonse chimene chiyenera kuletsa kubweretsedwa kwa uthenga wofunika umenewu kwa anthu mobwerezabwereza monga mmene kungathekere. Ichi chimaika thayo lalikulu pa onse a atumiki odzipereka a Yehova.
6. Ngakhale kuti uthenga wathu ungadziŵidwe mofalikira, nchifukwa ninji timafunikira kupitirizabe kulalikira?
6 Zowona, tingakhale titalalikira kale mbiri yabwino mokuliradi m’gawo lathu. Koma pali zinthu zambiri zimene zikuchitika m’dziko chakuti ngakhale kuti anthu ambiri anamva kale uthenga wathu, iwo mwamsanga adzaiwala iwo ngati tileka kulalikira. Tangolingalirani za kuwukira boma, machitachita a uchigawenga, kuleka kugwira ntchito, kugwiritsira molakwa maudindo, ndi zochitika zina zomwe zimafalitsidwa mokulira. Ndiponso pali mitundu yambiri ya zosangulutsa zofala ndi zochewutsa zina. Tiyenera kupitiriza kulalikira kuika uthenga wathu pamaso pa anthu mosasamala kanthu za kudzinenera konse koteroko kwa zinthu zina pa chisamaliro chawo.
7. Ndimotani mmene chivomerezo cha ambiri lerolino chiri chofanana ndi chija cha Aisrayeli ku kunenera kwa Yesaya, koma ndimotani mmene ichi sichiyenera kutitsekerezera ife kulalikira?
7 Pamene ambiri ayesera kutinyalanyaza ife, tiyenera kukumbukira mtundu wa anthu umene mneneri Yesaya anayenera kulalikirako. Yehova anamuuza iye: “Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova. Amene amati kwa alauli, ‘Mtima wanu usapenye,’ ndi kwa aneneri, ‘Musanenere kwa ife zinthu zowona. Munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga. Chokani inu m’njira, patukani m’bande. Tiletsereni Woyera wa Israyeli pamaso pathu.’” Mosasamala kanthu za chimenecho, Yesaya mokhulupirika anauza anthuwo kuti: “Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro. Odala ali onse amene amdikira iye.” (Yesaya 30:9-11, 18) Tiyenera kuchita chofananacho. Kokha ngati tipitiriza kuumirira, uthenga wathu udzazama kumlingo winawake. Ena adzalabadira ndipo ena sadzatero. Koma onse adzakhala ndi mwaŵi wa kumva.
‘Kodi Adzamva Bwanji?’
8. Ngakhale kuti anthu angawoneke kukhala atatenga kaimidwe kawo motsutsana ndi chowonadi, ndi nsonga zotani zimene zingasinthe malingaliro awo?
8 Mwinamwake timadzimva kuti anthu m’dera lina atenga kaimidwe kolimba ndipo kuti agamulapo kukana uthenga wathu kapena ngakhale kutsutsa iwo. Koma kumbukirani, mkhalidwe m’miyoyo ya anthu ukusintha mokhazikika. Iwo angayang’anizane ndi mavuto atsopano kapena mikhalidwe m’mawa, mlungu wotsatira kapena mwezi wotsatira yomwe idzawapanga iwo kukhala ovomereza ku chowonadi. Iwo angamve nkhani zosokoneza maganizo m’dziko kapena mwinamwake kuvutika chifukwa cha kusowa kwa chuma, matenda, kapena imfa m’banja. Zinthu zoterozo zingawapangitse iwo kugalamuka ndi kufuna kuphunzira choyambitsa cha nsautso yawo. Ngati tipitiriza kulalikira, iwo adzadziŵa kumene akayenera kutembenukira.
9. Ndimotani mmene ntchito yathu yolalikira ingayerekezedwere ndi ija ya antchito opulumutsa m’gawo la tsoka?
9 Mkhalidwe wathu ungayerekezedwe ndi uja wa antchito opulumutsa m’dera la tsoka, monga ngati pambuyo pa chivomezi. Ena angakhale akumagwira ntchito m’gawo limene opulumuka oŵerengeka anapezeka, koma chenicheni chakuti ogwira ntchito anzawo anali kupeza opulumuka ambiri m’gawo lina sichidzawapangitsa iwo kumva ulesi ndi kusiya. M’malomwake, ogwira ntchito yopulumutsa onse mosatopa amapitiriza ngakhale pamene amadzimva kuti sipangakhale opulumuka owonjezereka aliwonse m’gawo lawo logawiridwa. Ndipo, kenaka, nthaŵi zina iwo amadzapeza wopulumuka wina. Kufufuzako kumasiidwa kokha pamene nthaŵi imene yapita imavumbulutsa kuti palibe chiyembekezo china chirichonse. Chabwino, kufufuza kwathu sikunaletsedwe, ndipo tidakapezabe zikwi ndi zikwi zofuna kupulumutsidwa kuchokera kudziko iri lakale ndi kupulumuka “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 14) Ngakhale m’madera amene anagwiridwa kale ntchito mokwanira ndipo kumene anthu ambiri samavomereza, kukupezekabe zotulukapo zina. Ndipo pali zifukwa zowonjezereka za kupitirizira kulalikira.
10. Ndimotani kokha mmene anthu adzadziŵira kumene angatembenukire ngati iwo akufuna kupeza chowonadi, mogwirizana ndi Aroma 10:13, 14?
10 Anthu amafunikira kukumbutsidwa mopitiriza kuti “aliyense woitanira pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” Komabe, monga mmene Paulo akupitirizira m’kalata yake kwa Aroma, “ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:13, 14) Mawu awa ayenera kusindikiza pa aliyense wa ife kufunika kwa kuumirira m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.
11. Ndi thayo lotani limene tiri nalo kulinga kwa achichepere omwe akukula kufikira uchikulire?
11 Pamene nthaŵi yotsiriza yapitiriza, ana abadwa ndipo akula kufikira ku uchikulire kapena ku msinkhu wa thayo. Kaŵirikaŵiri anthu achichepere amenewa sanapereke chisamaliro chirichonse ku chowonadi. Makolo awo angakhale anakana uthengawo ndipo ngakhale kulankhula motsutsana ndi iwo. Koma tsopano achichepere amenewa akula mokwanira kuti alingalire mosamalitsa kaamba ka iwo eni ponena za mikhalidwe ya dziko, ponena za mtsogolo, ndi ponena za chifuno chawo m’moyo. Iwo nawonso amafuna kuitanira pa dzina la Yehova ngati ati adzapulumutsidwe. Koma “adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye?” (Aroma 10:14) M’nkhani zambiri a zaka za pakati pa 13 ndi 19 amenewa ndi achichepere amakhala ovomereza ku chowonadi, chotero tifunikira kuwafunafuna ndi kulalikira kwa iwo.
12. Ndimotani mmene kupitiriza kwathu kwa kugwira ntchito ya kulalikira kuyenera kupanga mbali ya chisonyezero cha chifundo cha Yehova?
12 Chenicheni chakuti njira idakali yotseguka kaamba ka kulalikira chiri chisonyezero cha chifundo cha Yehova. Mtumwi Petro analemba kuti: “[Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo. Komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.” (2 Petro 3:9, 15) Chikhumbo cha Yehova chakuti anthu onse apulumutsidwe chikusonyezedwa osati kokha mwa kulola nthaŵi kupita moleza mtima asanapereke chiweruzo komanso mwa kupitiriza kwake kuchonderera kwa anthu onse kutembenukira kwa iye ndi kupulumutsidwa. (1 Timoteo 2:4) Pamene tipitiriza kulalikira mbiri yabwino, timawunikira chifundo cha Mulungu, ndipo m’njira iyi timamlemekeza iye.
Kupewa Liwongo la Mwazi
13, 14. (a) Ndimotani mmene ntchito yathu yolalikira ingayerekezedwere ndi ntchito ya mlonda, monga mmene yatchulidwira mu ulosi wa Ezekieli? (b) Nchifukwa ninji Paulo akananena kuti iye anali “wopanda liwongo ndi mwazi wa anthu onse,” ndipo ndimotani kokha mmene Mboni za Yehova zinganenere ichi lerolino?
13 Thayo la Mboni zodzipereka za Yehova la kuchenjeza anthu za kudza kwa chiweruzo cha Mulungu lingayerekezedwe ndi lija la Ezekieli m’nthawi yake. Iye anaikidwa monga mlonda kunyumba ya Israyeli. Ntchito yake inali kuchenjeza Aisrayeli kuti chiweruzo chinali kubwera pa iwo ngati iwo satembenuka kuchoka ku njira zawo zoipa. Ngati iye monga mlonda analephera kufuula chenjezo, chiweruzo chikanabwerabe pa anthu oipa, koma mwazi wawo ukanakhala pamutu pa mlonda wonyalanyazayo. Mu ichi Yehova anasonyeza khalidwe lake kulinga ku kupereka chiweruzo: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo. Bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferanji inu nyumba ya Israyeli?”—Ezekieli 33:1-11.
14 Mtumwi Paulo anavomereza thayo lake monga mlonda, akumanena kwa akulu ochokera ku Efeso kuti: “Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.” Nchifukwa ninji iye anakhoza kunena tero? Iye akupitiriza kuti: “Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Chotero chiri chofanana ndi gulu la mlonda lerolino, otsalira odzozedwa a atsatiri a Yesu Kristu. Onsewa, limodzi ndi anzawo oposa mamiliyoni atatu omwe ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu ndi kulandira moyo wosatha padziko lapansi, sayenera kufooka m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi kuchenjeza za kudza kwa chiweruzo chake. Mwanjira imeneyi iwo amapewa liwongo la mwazi.
15. Mogwirizana ndi Ezekieli mutu 9, ndi ndani amene anaikidwa chizindikiro, ndipo ndani amene ankaika chizindikirocho?
15 Ntchito yolalikira lerolino yalongosoledwa mwaulosi mu Ezekieli mutu 9. Pano, chilango cha Yehova chinatsimikiziridwa kaamba ka mzinda wa Yerusalemu. Kumayambiriro kwa kuperekedwa kwa chiweruzo chimenecho, munthu wovala zovala za bafuta ndi zolembera m’chuwuno mwake akuuzidwa kupita pakati pa mzinda ndi kuika chizindikiro pa mphumi pa onse omwe akuusa moyo pa zinthu zonyansa zomwe zikuchitidwa mmenemo. Pamene ntchito yoika chizindikiroyi ikatsirizidwa, onse mu mzinda kupatulapo awo amene anaikidwa chizindikiro kaamba ka chipulumutso akaphedwa. Pamapeto a chipambano cha ntchito yake yoika chizindikiro, munthuyo anasimba kuti: “Ndachita monga munandilamulira ine.” (Ezekieli 9:11) Iye mokhulupirika anachita ntchito yake kufikira kumapeto.
16. (a) Ndi ndani amene mwamuna wovala bafutayo anaimira lerolino? (b) Ndimotani mmene nkhani ya kulemekeza ulamuliro wa Yehova imatifulumizira ife kupitirizabe kulalikira?
16 Munthu wovala batufayo anaimira otsalira odzozedwa a atsatiri a Kristu, ndipo iwo agwirizana ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” Nkhani yaikulu lerolino, monga mmene inaliri m’nthawi ya Ezekieli, iri kulemekeza ulamuliro wa Yehova. Ponena za mapeto a dongosolo iri loipa la kachitidwe ka zinthu pa nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova akuti: “Ndipo amitundu adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.” (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; Ezekieli 39:7) Popeza kuti amitundu adzadziŵa ichi, chiri choyenera kuti atumiki a Yehova padziko lapansi apitirizebe kulalikira dzina lake ndi chifuno chake monga umboni kwa mitundu yonse.
17, 18. (a) Ndimotani mmene kupitiriza kwathu kulalikira kumatithandizira ife kukhalabe ogalamuka? (b) Ndi ripoti lotani limene tonsefe timafuna kupanga kwa Yehova pamene iye abweretsa ntchito yolalikira kumapeto, ndipo ndimotani mokha mmene tingachitire ichi?
17 Mwakupitirizabe kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu, timasungilira kugalamuka kwathu. Timakhalabe ozindikira ponena za kufunika kwa dzina la Yehova ndi chifuno. Ngati tifooka, chiyembekezo chathu cha Ufumu chingafooke, ndipo tingasokeretsedwe ndi “nkhaŵa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndi kusakhwimitsa zipatso zamphumphu.” (Luka 8:14) Mwakupitirizabe mwachangu kulalikira “mbiri yabwino,” ife mokhulupirika timatsatira malamulo a Ambuye wathu, Yesu Kristu: “Yang’anirani, dikirani. Pakuti simudziŵa nthaŵi yake. Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.”—Marko 13:10, 33, 37.
18 Lolani tonse a ife, chotero, tiuumirire kufunafuna ‘awo omwe akuusa moyo’ kufikira ku utali umene Yehova adzalola nthaŵi kaamba ka icho. Lolani kuti tonse a ife, kaya otsalira odzozedwa kapena “nkhosa zina,” tipitirizebe mokhulupirika kutenga ntchito yathu yolalikira mbiri yabwino ya Ufumu m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse. (Mateyu 24:14) Pamene Yehova iyemwini adzabweretsa ntchitoyi kumapeto mwakuyambitsa “chisautso chachikulu,” lolani kuti aliyense wa ife adzakhale wokhoza kunena kwa Yehova kuti, ‘Tachita monga mmene mwalamulira.’
Kodi Mumakumbukira?
◻ Nchiyani chimene zotulukapo zikusonyeza ponena za kulalikira kwathu?
◻ Ndi ziti zomwe ziri zifukwa zina zimene tiyenera kupitirizira kulalikira?
◻ Ndimotani mmene kulalikira kwathu kuliri chisonyezero cha chifundo cha Yehova?
◻ Ndimotani mmene tingakhalire oyera ku mwazi wa anthu onse?
◻ Ndimotani mmene kulalikira kwathu kumatithandizira ife kukhala ogalamuka?
[Tchati patsamba 28]
ZOTULUKAPO ZA KULALIKIRA MKATI MWA ZAKA ZISANU NDI ZIŴIRI
Chiŵe. cha Obati. Opez. pa Chiku. Chiŵe. cha Maphu. a Baibulo
1981 119,836 5,987,893 1,475,177
1982 138,540 6,252,787 1,586,293
1983 161,896 6,767,707 1,797,112
1984 179,421 7,416,974 2,047,113
1985 189,800 7,792,109 2,379,146
1986 225,868 8,160,597 2,726,252
1987 230,843 8,965,221 3,005,048