NKHANI YOPHUNZIRA 41
Tidzakhalebe Okhulupirika pa “Chisautso Chachikulu”
“Kondani Yehova, inu nonse okhulupirika ake. Yehova amateteza okhulupirika.”—SAL. 31:23.
NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi maboma adzalengeza za chiyani posachedwapa? (b) Kodi tiyenera kupeza mayankho a mafunso ati?
TANGOYEREKEZERANI kuti maboma alengeza zimene takhala tikuziyembekezera kwa nthawi yaitali zakuti “bata ndi mtendere.” Mwina alengezanso kuti akwanitsa kubweretsa mtendere padziko lonse. Pa nthawiyo, maboma adzafuna kuti tiziganiza kuti apeza njira yothetsera mavuto amene anthu akukumana nawo. Koma zoona zake n’zakuti sadzakhala ndi mphamvu zoti asinthe zimene zidzachitike pambuyo pake. Zili choncho chifukwa ulosi wa m’Baibulo umanena kuti: “Chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo . . . ndipo sadzapulumuka.”—1 Ates. 5:3.
2 Koma pali mafunso ofunika kwambiri pa nkhani imeneyi. Mafunso ake ndi akuti: N’chiyani chidzachitike pa nthawi ya “chisautso chachikulu”? Kodi Yehova adzafuna kuti tidzachite chiyani? Nanga kodi tingakonzekere bwanji kuti tidzakhalebe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu?—Mat. 24:21.
N’CHIYANI CHIDZACHITIKE PA NTHAWI YA “CHISAUTSO CHACHIKULU”?
3. Malinga ndi Chivumbulutso 17:5, 15-18, kodi Mulungu adzawononga bwanji “Babulo Wamkulu”?
3 Werengani Chivumbulutso 17:5, 15-18. Baibulo limanena kuti “Babulo Wamkulu” adzawonongedwa. Monga tanena kale, maboma sadzatha kusintha zimene zidzachitike pa nthawiyo. Tikutero chifukwa chakuti ‘Mulungu adzaika m’mitima yawo kuti achite mogwirizana ndi maganizo ake.’ Maganizo amenewa ndi akuti awononge zipembedzo zonse zonyenga, kuphatikizapo matchalitchi amene amati ndi achikhristu.b Mulungu adzaika maganizo akewa m’mitima ya “nyanga 10” za ‘chilombo chofiira.’ Nyanga 10 zikuimira maboma onse amene amathandiza “chilombocho,” chomwe ndi bungwe la United Nations. (Chiv. 17:3, 11-13; 18:8) Mabomawa akadzayamba kuukira zipembedzo zonyenga, chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Zimenezi zidzakhala zoopsa kwambiri padziko lonse lapansi.
4. (a) Kodi mwina maboma adzafotokoza bwanji chifukwa chake akuukira zipembedzo zonyenga? (b) Kodi n’kutheka kuti anthu amene anali m’zipembedzozo adzachita chiyani?
4 Sitikudziwa zimene maboma adzanene pofotokoza chifukwa chake akuwononga Babulo Wamkulu. Mwina adzanena kuti zipembedzo ndi zimene zikusokoneza mtendere ndipo zimakonda kulowerera ndale. Apo ayi, anganene kuti zipembedzo zili ndi chuma chochuluka kwambiri. (Chiv. 18:3, 7) Zikuoneka kuti powononga zipembedzo sikuti adzawononga anthu onse a m’zipembedzozo. M’malomwake, zikuoneka kuti maboma adzawononga mabungwe a zipembedzozo. Mabungwewo akadzawonongedwa, anthu ake adzazindikira kuti atsogoleri a zipembedzo zonyengazi alephera kuwathandiza. Ndipo n’kutheka kuti anthuwo adzayesetsa kusonyeza kuti sakugwirizana ndi zipembedzozo.
5. Kodi Yehova walonjeza chiyani zokhudza chisautso chachikulu, nanga n’chifukwa chiyani wachita zimenezi?
5 Baibulo silinena nthawi yeniyeni imene kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzatenge koma chomwe tikudziwa n’chakuti sikudzatenga nthawi yaitali. (Chiv. 18:10, 21) Yehova walonjeza kuti ‘adzafupikitsa masiku’ a chisautsocho n’cholinga choti apulumutse ‘osankhidwa’ ake komanso kuti chipembedzo choona chisadzawonongedwe. (Maliko 13:19, 20) Nanga kodi Yehova adzafuna kuti tizidzachita chiyani chisautso chachikulu chitayamba koma nkhondo ya Aramagedo isanayambe?
PITIRIZANI KULAMBIRA YEHOVA NDI MTIMA WONSE
6. N’chifukwa chiyani kungochoka mu Babulo Wamkulu si kokwanira?
6 Munkhani yapita ija, tinaphunzira kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azipewa chilichonse chokhudza Babulo Wamkulu. Koma tiyenera kuchita zambiri osati kungochoka mu Babulo Wamkuluyo. Tiyeneranso kuyesetsa kumalambira Yehova ndi mtima wonse. Tiyeni tione zinthu ziwiri zimene zingatithandize kuchita zimenezi.
7. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizitsatirabe mfundo zachilungamo za Yehova? (b) Kodi lemba la Aheberi 10:24, 25 limasonyeza bwanji kufunika kosonkhana pamodzi, makamaka panopa?
7 Choyamba, tiyenera kumayesetsa kutsatira mfundo zachilungamo za Yehova. Sitiyenera kuyamba kuona kuti makhalidwe a anthu am’dzikoli ndi abwino. Mwachitsanzo, tiyenera kuona kuti chiwerewere chamtundu uliwonse ndi cholakwika. Izi zikuphatikizapo kukwatirana kapena kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Mat. 19:4, 5; Aroma 1:26, 27) Chachiwiri, tiyenera kupitiriza kulambira limodzi ndi Akhristu anzathu. Tiyenera kuchita zimenezi kulikonse kumene tingakwanitse, kaya m’Nyumba za Ufumu, m’nyumba za abale kapenanso mobisa. Mulimonse mmene zingakhalire, sitiyenera kusiya kusonkhana limodzi ndi Akhristu anzathu kuti tizilambira Yehova. Kunena zoona, tiyenera ‘kuwonjezera kuchita zimenezi, makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’—Werengani Aheberi 10:24, 25.
8. Kodi zikuoneka kuti uthenga wathu udzasintha bwanji m’tsogolo?
8 Pa nthawi ya chisautso chachikulu, uthenga wathu uyenera kuti udzasintha. Panopa timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo timayesetsa kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Koma pa nthawiyo n’kutheka kuti tizidzalalikira uthenga wamphamvu wokhala ngati matalala. (Chiv. 16:21) Mwina tizidzalengeza kuti dziko la Satanali latsala pang’ono kwambiri kuwonongedwa. Pa nthawi yoyenera, tidzadziwa uthenga umene tidzalalikire komanso njira zolalikirira. Koma panopa sitikudziwa ngati tidzagwiritsa ntchito njira zimene takhala tikuzigwiritsa ntchito mu utumiki kwa zaka zambirimbiri, kapena tidzagwiritsa ntchito njira zina. Mulimonse mmene zidzakhalire, zikuoneka kuti tidzakhala ndi mwayi wolengeza molimba mtima uthenga wa chiweruzo cha Yehova.—Ezek. 2:3-5.
9. Kodi maboma adzachita chiyani akadzamva uthenga wathu, nanga sitiyenera kukayikira za chiyani?
9 Uthenga wathu uyenera kuti udzachititsa maboma kuganiza zoletsa ntchito yathu. Ndipo tidzafunika kupitiriza kudalira Yehova kuti azitithandiza. Sitiyenera kukayikira kuti Mulungu wathu adzatipatsa mphamvu kuti tichite zimene akufuna.—Mika 3:8.
TIZIKONZEKERA KUUKIRIDWA
10. Malinga ndi Luka 21:25-28, kodi anthu ambiri adzatani pa nthawi ya chisautso chachikulu?
10 Werengani Luka 21:25-28. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, anthu adzadabwa kwambiri kuona zinthu zimene ankaganiza kuti ndi zokhalitsa zitayamba kusokonekera. Iwo adzasowa mtengo wogwira ndipo adzaona kuti moyo wawo uli pa ngozi. (Zef. 1:14, 15) Pa nthawi imeneyo, zinthu ziyenera kuti zidzakhala zovuta ngakhale kwa anthu a Yehova. Popeza timapewa kukhala mbali ya dzikoli, tidzakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ndipo mwina tidzafika posowa zinthu zina zofunika.
11. (a) N’chifukwa chiyani maboma adzayamba kuganizira kwambiri za Mboni za Yehova? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa chisautso chachikulu?
11 Pa nthawiyo, anthu amene anali m’zipembedzo zimene zawonongedwa adzakwiya kuona kuti a Mboni za Yehova akulambirabe Mulungu. Ayenera kuti adzasonyeza mkwiyo wawo m’njira zosiyanasiyana monga kuuza anthu ena pa intaneti. Maboma komanso Satana adzadana nafe kwambiri chifukwa chipembedzo chathu chokha n’chimene chidzatsale. Adzaona kuti sanakwaniritse cholinga chawo choti awononge zipembedzo zonse padzikoli. Choncho adzayamba kuganizira kwambiri za atumiki a Yehovafe. Kenako mabomawo adzagwirizana n’kukhala Gogi wakudziko la Magogic ndipo adzatiukira ndi mphamvu zawo zonse. (Ezek. 38:2, 14-16) Popeza sitikudziwa zonse zimene zidzachitike pa nthawiyo, mwina tingachite mantha tikaziganizira. Koma sitiyenera kuopa chisautso chachikulu chifukwa Yehova adzatipatsa malangizo otithandiza kuti tidzapulumuke. (Sal. 34:19) Tidzatha ‘kuimirira chilili ndi kutukula mitu yathu’ podziwa kuti ‘chipulumutso chathu chikuyandikira.’d
12. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wachita chiyani potithandiza kuti tidzakhalebe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu?
12 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala akutithandiza kuti tidzakhalebe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu. (Mat. 24:45) Mwachitsanzo, wachita zimenezi pogwiritsa ntchito misonkhano yachigawo ya 2016 mpaka 2018. Pa misonkhano imeneyi, tinalimbikitsidwa kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tidzapulumuke pa tsiku la Yehova. Tiyeni tikambirane makhalidwe amenewa mwachidule.
TIZIYESETSABE KUKHALA OKHULUPIRIKA, OPIRIRA KOMANSO OLIMBA MTIMA
13. N’chiyani chingatithandize kukhala okhulupirika kwa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi panopa?
13 Kukhulupirika: Mutu wa msonkhano wa 2016 unali wakuti “Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova.” Pamsonkhanowu tinaphunzira kuti tikhoza kukhala okhulupirika kwa Yehova ngati tili naye pa ubwenzi wolimba. Tinakumbutsidwa kuti tikhoza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova tikamapemphera kuchokera mumtima komanso kuphunzira Mawu ake mwakhama. Tikamachita zimenezi tingakhale ndi mphamvu zotithandiza kuthana ndi vuto lililonse. Pamene dziko la Satanali latsala pang’ono kuwonongedwa, tingayesedwe pa nkhani yokhala okhulupirika kwa Mulungu komanso Ufumu wake. Anthu am’dzikoli akhozanso kupitiriza kutinyoza. (2 Pet. 3:3, 4) Izi zikhoza kuchitika makamaka chifukwa chakuti sitikhala mbali ya dziko. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tikhale okhulupirika panopa kuti tidzathe kukhalabe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu.
14. (a) Kodi n’chiyani chidzasinthe pa nkhani ya abale amene amatsogolera zinthu padzikoli? (b) N’chifukwa chiyani tidzafunika kukhala okhulupirika pa nthawiyo?
14 Pa nthawi ya chisautso chachikulu, abale amene amatsogolera zinthu padzikoli adzasintha. Pa nthawi inayake, odzozedwa onse adzapita kumwamba kuti akamenye nawo nkhondo ya Aramagedo. (Mat. 24:31; Chiv. 2:26, 27) Choncho abale a m’Bungwe Lolamulira sadzakhalanso nafe padzikoli. Koma a khamu lalikulu adzapitiriza kuchita zinthu mwadongosolo. Ndipo abale ena oyenerera a m’khamu lalikululi ndi amene azidzatsogolera zinthu. Tidzayenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika pochita zinthu mogwirizana ndi abalewa komanso pomvera malangizo awo ochokera kwa Mulungu. Izi n’zimene zidzathandize kuti tipulumuke.
15. Kodi tingatani kuti tikhale opirira, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi panopa?
15 Kupirira: Mutu wa msonkhano wa 2017 unali wakuti “Musafooke.” Msonkhanowu unatithandiza kuti tizipirira mayesero. Tinaphunzira kuti tingakwanitse kupirira ngakhale kuti zinthu sizili bwino pa moyo wathu. Tingachite zimenezi tikamadalira Yehova. (Aroma 12:12) Tisaiwale zimene Yesu analonjeza kuti: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Lonjezoli likusonyeza kuti tiyenera kukhalabe okhulupirika zivute zitani. Tikamapirira mavuto athu panopa tidzakhala amphamvu chisautso chachikulu chikadzayamba.
16. Kodi timakhala olimba mtima chifukwa chiyani, nanga tingatani kuti tikhale olimba mtima panopa?
16 Kulimba mtima: Mutu wa msonkhano wachigawo wa 2018 unali wakuti “Limbani Mtima.” Msonkhanowu unatikumbutsa kuti munthu sakhala wolimba mtima chifukwa cha luso lake. Mofanana ndi kupirira, munthu amakhala wolimba mtima akamadalira Yehova. Ndiye kodi tingatani kuti tizimudalira kwambiri? Tingachite zimenezi tikamawerenga Mawu ake tsiku lililonse n’kumaganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ake m’mbuyomu. (Sal. 68:20; 2 Pet. 2:9) Gogi akadzatiukira pa chisautso chachikulu, tidzafunika kukhala olimba mtima n’kumadalira Yehova kuposa kale lonse. (Sal. 112:7, 8; Aheb. 13:6) Koma kuti tidzakhale olimba mtima pa nthawi imeneyo, tiyenera kudalira Yehova panopa.e
TIZIYEMBEKEZERA KUPULUMUTSIDWA
17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa nkhondo ya Aramagedo? (Onani chithunzi chapachikuto.)
17 Monga tinaphunzirira munkhani yapita ija, ambirife takhala moyo wathu wonse m’masiku otsiriza ano. Koma tilinso ndi mwayi wodzapulumuka pa chisautso chachikulu. Nkhondo ya Aramagedo idzakhala chimake cha mapeto a dziko loipali. Koma sitiyenera kuchita mantha chifukwa nkhondoyi ndi ya Mulungu. (Miy. 1:33; Ezek. 38:18-20; Zek. 14:3) Yehova akadzangolamula, Yesu adzatsogolera odzozedwa komanso angelo ambirimbiri pomenya nkhondoyi. Iwo adzamenyana ndi Satana, ziwanda komanso anthu amene ali kumbali ya Satana.—Dan. 12:1; Chiv. 6:2; 17:14.
18. (a) Kodi Yehova walonjeza chiyani? (b) Kodi lemba la Chivumbulutso 7:9, 13-17 limakuthandizani bwanji kuyembekezera zam’tsogolo molimba mtima?
18 Yehova watilonjeza kuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” (Yes. 54:17) “Khamu lalikulu” la atumiki a Yehova okhulupirika lidzapulumuka ‘n’kutuluka m’chisautso chachikulu.’ Ndipo lidzapitiriza kuchitira Mulungu utumiki wopatulika. (Werengani Chivumbulutso 7:9, 13-17.) Kunena zoona, Baibulo limatithandiza kuti tiziyembekezera zam’tsogolo molimba mtima. Sitikayikira kuti “Yehova amateteza okhulupirika.” (Sal. 31:23) Anthu onse amene amamukonda ndiponso kumutamanda adzasangalala kwambiri iye akadzayeretsa dzina lake.—Ezek. 38:23.
19. Kodi tidzakhala ndi mwayi wotani m’tsogolomu?
19 Tangoganizani mmene lemba la 2 Timoteyo 3:2-5 lingamvekere pofotokoza mmene anthu am’dziko latsopano adzakhalire popanda kusokonezedwa ndi Satana. (Onani bokosi lakuti “Mmene Anthu Adzakhalire M’tsogolo.”) M’bale George Gangas,f yemwe anali m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti: “Dzikoli lidzakhala labwino kwambiri pa nthawi imene aliyense adzakhala m’bale komanso mlongo. Posachedwapa mudzakhala m’dziko latsopano ndipo mudzakhala ndi moyo wamuyaya ngati Yehova.” Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
a Tikudziwa kuti posachedwapa, padzikoli padzachitika “chisautso chachikulu.” Kodi n’chiyani chidzatichitikire ifeyo pa nthawiyo? Nanga kodi Yehova adzafuna kuti tidzachite chiyani? Kodi ndi makhalidwe ati amene tiyenera kuyesetsa kukhala nawo panopa n’cholinga choti tidzakhalebe okhulupirika? Munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa.
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Matchalitchi amene amati ndi achikhristu saphunzitsa anthu kuti azilambira Yehova mogwirizana ndi mfundo zake.
c TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu oti Gogi wakudziko la Magogi (komanso dzina lachidule lakuti Gogi) akunena za mgwirizano wa mayiko umene udzaukire atumiki a Yehova pa nthawi ya chisautso chachikulu.
d Kuti mudziwe bwinobwino zimene zidzachitike nkhondo ya Aramagedo isanayambe, onani mutu 21 m’buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira. Kuti mudziwe zambiri zokhudza kuukira kwa Gogi wakudziko la Magogi komanso mmene Yehova adzatetezere anthu ake pa Aramagedo, onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2015, tsamba 14-19.
e Msonkhano wachigawo wa 2019 wa mutu wakuti “Chikondi Sichitha” watitsimikizira kuti tidzakhala otetezeka tikamadalira Yehova.—1 Akor. 13:8.
f Onani nkhani yakuti “Zochita Zake Zimtsata” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1994.
g MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa nthawi ya chisautso chachikulu, kagulu ka abale ndi alongo kalimba mtima n’kukachita misonkhano yawo m’nkhalango.
h MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Khamu lalikulu la atumiki a Yehova okhulupirika lidzatuluka m’chisautso chachikulu likusangalala.