Miyambo
1 Miyambi ya Solomo+ mwana wa Davide,+ mfumu ya Isiraeli:+
2 Yothandiza munthu kuti apeze* nzeru+ ndi malangizo.*
Kuti amvetse mawu anzeru.
3 Kuti apeze malangizo+ amene amathandiza munthu kuti akhale wozindikira,
Wachilungamo,+ wochita zinthu mwanzeru*+ komanso woona mtima.
4 Yothandiza munthu wosadziwa zinthu kuti akhale wozindikira.+
Yothandiza wachinyamata kuti akhale wodziwa zinthu komanso kuti aziganiza bwino.+
5 Munthu wanzeru amamvetsera ndipo amaphunzira zinthu zambiri.+
Munthu womvetsa zinthu amapeza malangizo anzeru+
6 Omuthandiza kumvetsa mwambi komanso mawu ovuta kuwamvetsa,*
Mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko yawo.+
7 Kuopa Yehova ndi chiyambi cha kudziwa zinthu.+
Zitsiru zokha ndi zimene zimanyoza nzeru komanso malangizo.+
9 Malangizowa ali ngati nkhata ya maluwa yokongola pamutu pako+
Komanso mkanda wokongola mʼkhosi mwako.+
10 Mwana wanga, anthu ochimwa akayesa kukunyengerera, usavomere.+
11 Akanena kuti: “Tiye tipitire limodzi.
Tiye tikabisalire anthu kuti tikakhetse magazi.
Tikabisale nʼkumadikirira anthu osalakwa kuti tiwaphe popanda chifukwa.
13 Tiye tikawalande zinthu zawo zonse zamtengo wapatali.
Tidzaza nyumba zathu ndi zinthu zimene talanda anthu.
15 Mwana wanga, usawatsatire.
Mapazi ako asayende panjira yawo,+
16 Chifukwa mapazi awo amathamangira kukachita zoipa,
Amapita mofulumira kukakhetsa magazi.+
17 Ndithudi, kutchera ukonde mbalame ikuona nʼkopanda phindu.
18 Nʼchifukwa chake anthu ochimwawa amabisala kuti akhetse magazi a anthu.
Amabisala kuti achotse miyoyo ya anthu ena.
19 Izi ndi zimene anthu ofuna kupeza phindu mwachinyengo amachita,
Ndipo phindu limene apezalo lidzachotsa moyo wawo.+
20 Nzeru yeniyeni+ ikufuula mumsewu.+
Ikufuula mokweza mawu mʼmabwalo a mzinda.+
21 Ikufuula pamphambano ya* misewu yodutsa anthu ambiri.
Pamageti olowera mumzinda, ikunena kuti:+
22 “Inu anthu osadziwa zinthu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa zinthu mpaka liti?
Inu anthu onyoza, kodi mupitiriza kusangalala ndi kunyoza anthu mpaka liti?
Ndipo anthu opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+
23 Mverani kudzudzula kwanga.*+
Mukatero ndidzakukhuthulirani mzimu wanga.
Ndidzachititsa kuti mudziwe mawu anga.+
24 Chifukwa ine ndinaitana, koma inu munapitiriza kukana,
Ndinatambasula dzanja langa, koma palibe amene anafuna kuti ndimuthandize.+
25 Munapitiriza kunyalanyaza malangizo anga onse,
Komanso nditakudzudzulani munakana kusintha.
26 Inenso ndidzaseka tsoka likadzakugwerani.
Ndidzakunyogodolani zimene mumaopa zikadzabwera,+
27 Zimene mumaopa zikadzabwera ngati mvula yamkuntho,
Tsoka likadzafika ngati mphepo yamkuntho,
Ndiponso masautso ndi mavuto zikadzakugwerani.
28 Pa nthawi imeneyo azidzangondiitana koma sindidzayankha.
Adzayesetsa kundifunafuna koma sadzandipeza,+
29 Chifukwa chakuti anadana ndi kudziwa zinthu,+
Ndipo sanasankhe kuopa Yehova.+
30 Anakana malangizo anga.
Sanalemekeze mawu anga onse pamene ndinawadzudzula.
31 Choncho adzakumana ndi zotsatira* za zochita zawo,+
Ndipo mapulani awo adzawabweretsera* mavuto ambiri.
32 Chifukwa kupanduka kwa anthu osadziwa zinthu kudzawaphetsa,
Ndipo mphwayi za anthu opusa zidzawawonongetsa.