Kodi Mwakonzekera Tsiku la Yehova?
“Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.”—ZEFANIYA 1:14.
1. Kodi Malemba amalifotokoza motani tsiku la Yehova?
‘TSIKU lalikulu ndi loopsa’ la Yehova lidzafika padongosolo loipali la zinthu posachedwapa. Malemba amafotokoza kuti tsiku la Yehova lidzakhala lankhondo, lamdima, lamkwiyo, lansautso, lodetsa nkhaŵa, loopsa, ndi lachipululutso. Komabe, padzakhala opulumuka, chifukwa “aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” (Yoweli 2:30-32; Amosi 5:18-20) Inde, ndi pamene Mulungu adzawononga adani ake ndi kupulumutsa anthu ake.
2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuona tsiku la Yehova kuti likufulumira?
2 Aneneri a Mulungu anasonyeza kuti tsiku la Yehova likufulumira. Mwachitsanzo, Zefaniya analemba kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.” (Zefaniya 1:14) Zinthu zikufulumirabe kwambiri lerolino chifukwa chakuti Wakupha Wamkulu wa Mulungu, Mfumu Yesu Kristu, ali pafupi ‘kudzimangira lupanga lake m’chuuno mwake ndi kuyenda kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo.’ (Salmo 45:3, 4) Kodi mwalikonzekera tsikulo?
Ankayembekezera Zinthu Zazikulu
3. Kodi Akristu ena a ku Tesalonika anali ndi ziyembekezo zotani, ndipo anali olakwa pazifukwa ziŵiri ziti?
3 Ambiri akhala ndi ziyembekezo zosakwaniritsidwa ponena za tsiku la Yehova. Akristu ena oyambirira ku Tesalonika anati, ‘Tsiku la Ambuye lafika!’ (2 Atesalonika 2:2) Koma panali zifukwa zazikulu ziŵiri zosonyeza kuti silinafike. Potchula chimodzi cha zimenezi, mtumwi Paulo anati: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.” (1 Atesalonika 5:1-6) Mu “nthaŵi ya chimaliziro” ino, ifeyo tikuyembekezera kuti mawu ameneŵo akwaniritsidwe. (Danieli 12:4) Atesalonika analibenso umboni wina wakuti tsiku lalikulu la Yehova lafika, popeza Paulo anawauza kuti: “Silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho.” (2 Atesalonika 2:3) Pamene Paulo analemba mawuwo (cha mu 51 C.E.), “chipatukocho” pa Chikristu choona chinali chisanakule kwenikweni. Lerolino, tikuchiona chili pachimake m’Dziko Lachikristu. Komabe, ngakhale kuti ziyembekezo zawo sizinakwaniritsidwe, odzozedwa okhulupirikawo mu Atesalonika, amene anapitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika mpaka imfa, analandira mfupo yakumwamba potsirizira pake. (Chivumbulutso 2:10) Ifenso tidzafupidwa ngati tikhalabe okhulupirika poyembekezera tsiku la Yehova.
4. (a) Kodi tsiku la Yehova lagwirizanitsidwa ndi chiyani pa 2 Atesalonika 2:1, 2? (b) Amene amati Abambo a Tchalitchi anali ndi malingaliro otani ponena za kubweranso kwa Kristu ndi nkhani zina zofanana?
4 Baibulo likugwirizanitsa “tsiku lalikulu la Yehova” ndi “kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Atesalonika 2:1, 2) Otchedwa kuti Abambo a Tchalitchi anali ndi malingaliro osiyanasiyana ponena za kubweranso kwa Kristu, kukhalapo kwake, ndi Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. (Chivumbulutso 20:4) M’zaka za zana lachiŵiri C.E., Papias wa ku Herapoli ankayembekezera dziko lapansi lachonde chadzaoneni m’Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Mobwerezabwereza Justin Martyr analankhula za kukhalapo kwa Yesu nayembekezera kuti Yerusalemu wobwezeretsedwa adzakhala likulu la Ufumu Wake. Irenæus wa ku Lyons anaphunzitsa kuti Ufumu wa Roma utawonongedwa, Yesu adzaonekera, kugwira Satana, ndi kulamulira ali ku Yerusalemu wa padziko lapansi.
5. Kodi akatswiri ena anenanji pankhani ya “Kudzanso” kwa Kristu ndi Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi?
5 Wolemba mbiri Philip Schaff ananena kuti chimene chinali “chinthu chapadera koposa” usanachitike Msonkhano wa ku Nicaea mu 325 C.E. chinali “chikhulupiriro chakuti ulamuliro wa zaka chikwi wa Kristu mu ulemerero padziko lapansi ndi oyera mtima oukitsidwa, chiukiriro ndi chiweruzo cha anthu onse chisanachitike, udzakhala wooneka.” A Dictionary of the Bible, yokonzedwa ndi James Hastings, imati: “Tertullian, Irenæus, ndi Hippolytus akuyembekezerabe Kudza [kwa Yesu Kristu] kwaposachedwapa; koma ndi Abambo Achialexandria tikukhala ndi malingaliro atsopano. . . . Popeza Augustine akusonyeza kuti Zaka Chikwi ndiyo nthaŵi pamene Tchalitchi chili ndi moyo padziko lapansi, Kudzanso kumeneko kukuoneka kuti kuli patali kwenikweni.”
Tsiku la Yehova ndi Kukhalapo kwa Yesu
6. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti tsiku la Yehova lili kutali kwambiri?
6 Malingaliro olakwika agwiritsa mwala, koma tisaganize kuti tsiku la Yehova lili kutali kwambiri. Kukhalapo kwa Yesu kosaoneka, kumene Malemba amagwirizanitsa ndi tsikuli, kunayamba kale. Nsanja ya Olonda ndi zofalitsa zina zogwirizana nayo za Mboni za Yehova kambiri zapereka umboni wa m’Malemba wakuti kukhalapo kwa Kristu kunayamba m’chaka cha 1914.a Komano, kodi Yesu anati chiyani ponena za kukhalapo kwake?
7. (a) Kodi mbali zina za chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu ndi mathedwe a nthaŵi ya pansi pano nzotani? (b) Kodi tingapulumuke motani?
7 Kukhalapo kwa Yesu kunadzakhala nkhani yaikulu imfa yake itayandikira kwambiri. Atamumva akuneneratu za kuwonongedwa kwa kachisi wa Yerusalemu, atumwi akewa Petro, Yakobo, Yohane, ndi Andreya anamfunsa nati: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:1-3; Marko 13:3, 4) Poyankha, Yesu ananeneratu za nkhondo, njala, zivomezi, ndi mbali zina za “chizindikiro” cha kukhalapo kwake ndi mathedwe a nthaŵi ya pansi pano. Iye anatinso: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Tidzapulumuka ngati tipirira mwachikhulupiriro mpaka kutha kwa moyo wathu umene tili nawowu kapena kutha kwa dongosolo loipali.
8. Chimaliziro cha dongosolo lachiyuda chisanafike, kodi nchiyani chinayenera kuchitika, ndipo zimenezo zikuchitika motani lerolino?
8 Mapeto asanafike, mbali yapadera kwambiri ya kukhalapo kwa Yesu idzakwaniritsidwa. Poifotokoza, iye anati: ‘Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.’ (Mateyu 24:14) Aroma asanawononge Yerusalemu ndipo dongosolo la zinthu lachiyuda lisanathe mu 70 C.E., Paulo ananena kuti uthenga wabwino ‘unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Komabe, lerolino ntchito yaikulu kwambiri yolalikira ikuchitidwa ndi Mboni za Yehova “padziko lonse lapansi.” Pazaka makumi angapo zapitazi, Mulungu watsegula njira yoperekera umboni waukulu ku Eastern Europe. Pokhala ndi nyumba zosindikizira ndi ziŵiya zina padziko lonse lapansi, gulu la Yehova nlokonzeka kuchita ntchito yowonjezereka, ngakhale mu “gawo losakhudzidwa.” (Aroma 15:22, 23, NW) Kodi mtima wanu umakusonkhezerani kuchita zonse zimene mungathe popereka umboni chimaliziro chisanafike? Ngati zili choncho, Mulungu angakulimbitseni kuti mukhale ndi phande lofupa m’ntchito ya mtsogolo.—Afilipi 4:13; 2 Timoteo 4:17.
9. Kodi Yesu anatchula mfundo yotani, monga kwalembedwa pa Mateyu 24:36?
9 Ntchito yolalikira Ufumu yomwe ananeneratu ndi mbali zina za chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu zikukwaniritsidwa tsopano lino. Chifukwa chake, mapeto a dongosolo la zinthu loipali ali pafupi. Nzoona kuti Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:4-14, 36) Koma ulosi wa Yesu ungatithandize kukonzekera “tsiku ilo ndi nthaŵi yake.”
Anakonzekera
10. Tikudziŵa motani kuti nkotheka kukhala odikira mwauzimu?
10 Kuti tipulumuke tsiku lalikulu la Yehova, tiyenera kukhalabe odikira mwauzimu ndi kuchirimika pa kulambira koona. (1 Akorinto 16:13) Tikudziŵa kuti chipiriro chotere nchotheka, popeza banja lina loopa Mulungu linatero nilipulumuka Chigumula chomwe chinawononga anthu oipa mu 2370 B.C.E. Poyerekezera nyengoyo ndi kukhalapo kwake, Yesu anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.
11. Kodi Nowa anatsatira njira yotani mosasamala kanthu za chiwawa chomwe chinaliko m’tsiku lake?
11 Monga ifeyo, Nowa ndi banja lake anali m’dziko lachiwawa. “Ana aamuna a Mulungu” osamva anasanduka anthu nadzitengera akazi mwa amene anabala Anefili oipawo—anthu a ndewu amene mosakayika anawonjezera chiwawa. (Genesis 6:1, 2, 4; 1 Petro 3:19, 20) Komabe, “Nowa anayendabe ndi Mulungu” mwachikhulupiriro. Anali “wangwiro m’mibadwo yake”—mbadwo woipa wa m’tsiku lake. (Genesis 6:9-11) Mwa kudalira Mulungu mwapemphero, tingachite mofananamo m’dziko lachiwawa loipali pamene tikuyembekezera tsiku la Yehova.
12. (a) Kusiyapo kumanga chingalaŵa, kodi Nowa anachita ntchito yanji? (b) Kodi anthu anatani ndi ulaliki wa Nowa, ndipo nchiyani chinawatsatira?
12 Nowa amadziŵika bwino lomwe monga womanga chingalawa chopulumukiramo zamoyo pa Chigumula. Iye analinso “mlaliki wa chilungamo,” koma anthu apanthaŵiyo “sanadziŵa kanthu” ponena za uthenga wake wopatsidwa ndi Mulungu. Iwo anadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, kukhala ndi mabanja, ndi kuchitabe zinthu zamasiku onse m’moyo mpaka Chigumula chinawapululutsa iwo onse. (2 Petro 2:5; Genesis 6:14) Iwo sanafune kumva za kalankhulidwe kowongoka ndi khalidwe lowongoka, monga momwenso mbadwo woipa walerowu sumafuna kumva zimene Mboni za Yehova zimanena pankhani ya “kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu,” chikhulupiriro mwa Kristu, chilungamo, ndi “chiweruziro chilinkudza.” (Machitidwe 20:20, 21; 24:24, 25) Palibe zolembedwa zosonyeza kuti panali anthu angati padziko lapansi pamene Nowa anali kulengeza uthenga wa Mulungu. Koma chinthu chimodzi nchotsimikizika, chiŵerengero cha anthu padziko lapansi chinatsika kwambiri mu 2370 B.C.E.! Chigumula chinasesa oipa onse, kungosiyapo awo amene anakonzekera chochita cha Mulungu chimenecho—Nowa ndi enanso asanu ndi aŵiri a m’banja lake.—Genesis 7:19-23; 2 Petro 3:5, 6.
13. Kodi nchilengezo cha Mulungu chachiweruzo chotani chimene Nowa anakhulupirira kwambiri?
13 Mulungu sanamuuziretu Nowa tsiku ndi ola lenileni la Chigumula zaka zambirimbiri icho chisanachitike. Komabe, pamene Nowa anali ndi zaka 480, Yehova analengeza kuti: “Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthaŵi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi aŵiri.” (Genesis 6:3) Nowa anakhulupirira kwambiri chilengezo cha Mulungu cha chiweruzo chimenechi. Atakwanitsa zaka 500, iye “anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti,” ndipo mwambo wa panthaŵiyo ukusonyeza kuti panapita zaka 50 mpaka 60 ana ake asanakwatire. Pamene Nowa anauzidwa kumanga chingalawa chopulumukiramo pa Chigumula, zikuoneka kuti ana ake amenewo ndi akazi awo anamthandiza ntchitoyo. Kumanga chingalawa kuyenera kuti kunachitikira pamodzi ndi utumiki wa Nowa monga “mlaliki wa chilungamo,” kumtanganitsa zaka 40 mpaka 50 Chigumula chisanachitike. (Genesis 5:32; 6:13-22) Pazaka zonsezo, iye ndi banja lake anachita zinthu ndi chikhulupiriro. Ifenso tiyeni tisonyeze chikhulupiriro pamene tilalikira uthenga wabwino ndi kuyembekezera tsiku la Yehova.—Ahebri 11:7.
14. Kodi nchiyani chimene Yehova anauza Nowa pomalizira pake, ndipo chifukwa ninji?
14 Pamene chingalawa chinali pafupi kumalizidwa, Nowa ayenera kuti analingalira kuti Chigumula chili pafupi, ngakhale kuti sanadziwe nthaŵi yake yeniyeni pamene chidzachitika. Yehova anamuuzadi pomalizira pake kuti: “Akapita masiku asanu ndi aŵiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.” (Genesis 7:4) Zimenezo zinapatsa Nowa ndi banja lake nthaŵi yokwanira yoloŵetsa mitundu yonse ya zinyama m’chingalawa ndi kuloŵamo iwo eni Chigumula chisanayambe. Sitifunikira kudziŵa tsiku ndi ola pamene chiwonongeko cha dongosolo ili chidzayamba; sitinapatsidwe thayo la kupulumutsa zinyama, ndipo anthu oyembekezera kupulumuka ayamba kale kuloŵa m’chingalawa chophiphiritsira, paradaiso wauzimu wa anthu a Mulungu.
“Dikirani”
15. (a) M’mawu anuanu, kodi mungafotokoze motani mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 24:40-44? (b) Kusadziŵa nthaŵi yeniyeni ya kudza kwa Yesu kudzachita kubwezera kwa Mulungu kuli ndi chotsatirapo chotani?
15 Ponena za kukhalapo kwake, Yesu anafotokoza kuti: “Pomwepo adzakhala [akugwira ntchito] aŵiri m’munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: aŵiri adzakhala opera [dzinthu] pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Koma dziŵani ichi, kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi iti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:40-44; Luka 17:34, 35) Kusadziŵa nthaŵi yeniyeni ya kudza kwa Yesu kudzabwezera chilango m’malo mwa Mulungu kumatigalamutsa ndipo kumatipatsa mpata tsiku ndi tsiku wa kusonyeza kuti sitikutumikira Yehova ndi zolinga zadyera.
16. Kodi nchiyani chidzachitikira awo ‘osiyidwa’ ndi awo ‘otengedwa’?
16 Awo ‘osiyidwa’ kuchiwonongeko pamodzi ndi oipa adzaphatikizapo aja amene aona kuunika koma amene aloŵerera m’moyo wadyera. Tikhaletu pakati pa ‘otengedwa,’ awo odzipereka kotheratu kwa Yehova ndi oyamikiradi zogaŵira zake zauzimu kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Mpaka chimaliziro chenichenicho, tiyeni titumikire Mulungu ndi “chikondi chochokera mumtima woyera ndi m’chikumbumtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga.”—1 Timoteo 1:5.
Mayendedwe Opatulika Ngofunika
17. (a) Kodi nchiyani chinanenedweratu pa 2 Petro 3:10? (b) Kodi ndi mayendedwe ndi mapembedzedwe ena ati amene 2 Petro 3:11 akulimbikitsa?
17 Mtumwi Petro analemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zammwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.” (2 Petro 3:10) Miyamba ndi dziko lapansi lophiphiritsira sizidzapulumuka kutentha kwa mkwiyo waukulu wa Mulungu. Choncho Petro akuwonjezera kuti: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.” (2 Petro 3:11) Mayendedwe ndi mapembedzedwe ameneŵa akuphatikizapo nthaŵi zonse kupezeka pamisonkhano yachikristu, kuchitira ena zabwino, ndi kukhala ndi phande latanthauzo pakulalikira uthenga wabwino.—Mateyu 24:14; Ahebri 10:24, 25; 13:16.
18. Ngati tayamba kukonda dzikoli, kodi tiyenera kuchitanji?
18 ‘Mayendedwe opatulika ndi chipembedzo’ zimafuna kuti ‘tidzisungire eni osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27) Koma bwanji ngati tayamba kukonda dzikoli? Mwinamwake tikukopeka kukhala pamalo oipa pamaso pa Mulungu mwa kufuna zosangulutsa zoipa kapena mwa kumvetsera nyimbo zimene zimasonkhezera mzimu wopanda umulungu wa dzikoli. (2 Akorinto 6:14-18) Ngati zili choncho, tiyeni tipemphe thandizo la Mulungu m’pemphero kuti tisapitire pamodzi ndi dziko koma tiime ovomerezeka pamaso pa Mwana wa munthu. (Luka 21:34-36; 1 Yohane 2:15-17) Ngati tadzipatulira kwa Mulungu, ndithudi tidzachita zonse zimene tingathe kuti timange ndi kukhala naye ndi unansi wabwino ndi kukonzekera tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
19. Kodi nchifukwa ninji makamu a olengeza Ufumu akuyembekeza kupulumuka mathedwe a dongosolo loipali la zinthu?
19 Nowayo woopa Mulungu ndi banja lake anapulumuka Chigumula chimene chinawononga dziko lakale. Anthu owongoka mtima anapulumuka mapeto a dongosolo la zinthu lachiyuda mu 70 C.E. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane anali wachangube mu utumiki wa Mulungu cha m’ma 96-98 C.E., pamene analemba buku la Chivumbulutso, nkhani yake ya Uthenga Wabwino, ndi makalata atatu ouziridwa. Pa zikwi za amene analandira chikhulupiriro chenicheni pa Pentekoste wa 33 C.E., ambiri ayenera kuti anapulumuka mapeto a dongosolo lachiyuda. (Machitidwe 1:15; 2:41, 47; 4:4) Lerolino makamu a olengeza Ufumu ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka mathedwe a dongosolo la zinthu loipa lilipoli.
20. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ‘alaliki a chilungamo’ achangu?
20 Pokhala tidzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano patsogolopa, tiyenitu tikhale ‘alaliki a chilungamo’ achangu. Ulidi mwaŵi waukulu chotani nanga kutumikira Mulungu m’masiku otsiriza ano! Ndipo nkosangalatsa chotani nanga kutsogolera anthu kupita ku “chingalawa” chamakono, paradaiso wauzimu amene anthu a Mulungu akusangalala naye! Mamiliyoni amene alimo tsopano akhaletu okhulupirikabe, odikira mwauzimu, ndi okonzekera tsiku lalikulu la Yehova. Koma kodi chidzathandiza tonsefe kukhalabe odikira nchiyani?
[Mawu a M’munsi]
a Onani mitu 10 ndi 11 ya m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ena akhala ndi ziyembekezo zotani ponena za tsiku la Yehova ndi kukhalapo kwa Kristu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Nowa ndi banja lake anakonzekera Chigumula?
◻ Kodi nchiyani chidzachitika kwa amene ‘akudikira’ ndi kwa amene sakutero?
◻ Kodi nchifukwa ninji mayendedwe opatulika ngofunika, makamaka pamene tikuyandikira kwambiri tsiku lalikulu la Yehova?