“Tiuzeni, Kodi Zinthu Zimenezi Zidzachitika Liti?”
“[Kodi] chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?”—MAT. 24:3.
1. Mofanana ndi atumwi, kodi ifenso timafunitsitsa kudziwa chiyani?
YESU atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake padziko lapansi, ophunzira ake ankafunitsitsa kudziwa za tsogolo lawo. Ndiyeno kutangotsala masiku ochepa kuti aphedwe, atumwi ake anayi anamufunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:3; Maliko 13:3) Poyankha, Yesu anafotokoza ulosi umene uli pa Mateyu chaputala 24 ndi 25. Mu ulosi umenewu, Yesu anafotokoza zinthu zambiri zochititsa chidwi. Zimene iye ananena n’zofunika kwambiri kwa ife chifukwa chakuti nafenso timafunitsitsa kudziwa zam’tsogolo.
2. (a) Kodi kwa zaka zambiri takhala tikuyesetsa kuti timvetse chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso atatu ati?
2 Kwa zaka zambiri, atumiki a Yehova akhala akuphunzira mwakhama ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza. Akhala akufufuza kuti amvetse bwino nthawi imene mawu a Yesu adzakwaniritsidwe. Yehova akutithandiza mwapang’onopang’ono kuti timvetse ulosiwu, choncho zimene gulu lafotokoza pa nkhaniyi zakhala zikusintha. Kuti timvetse mfundoyi, tiyeni tikambirane mafunso atatu. Mafunsowa ndi akuti: Kodi “chisautso chachikulu” chidzayamba liti? Kodi Yesu adzaweruza liti “nkhosa” ndi “mbuzi”? Nanga Yesu ‘adzafika’ liti?—Mat. 24:21; 25:31-33.
KODI CHISAUTSO CHACHIKULU CHIDZAYAMBA LITI?
3. Kodi m’mbuyomu tinkaganiza chiyani ponena za nthawi ya chisautso chachikulu?
3 Kale tinkaganiza kuti chisautso chachikulu chinayamba mu 1914 pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba. Tinkaganizanso kuti Yehova ‘anafupikitsa masikuwo’ mu 1918 pamene nkhondoyo inatha, n’cholinga choti odzozedwa athe kulalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse. (Mat. 24:21, 22) Tinkakhulupirira kuti ntchito yolalikira ikatha, dziko la Satanali lidzawonongedwa. Choncho tinkaganiza kuti chisautso chachikulu chili ndi zigawo zitatu. Mbali yoyamba inayamba mu 1914 mpaka 1918. Kenako mbali yachiwiri inayamba mu 1918 pamene chisautsocho chinaima kaye ndipo idzatha pamene Aramagedo idzayambe. Ndipo nkhondo ya Aramagedo idzakhala mbali yomaliza.
4. Kodi ndi mfundo iti imene inathandiza kuti timvetse bwino ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza?
4 Koma titaonanso mofatsa ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza, tinazindikira kuti uyenera kukwaniritsidwa kawiri. (Mat. 24:4-22) Choyamba, ulosiwu unakwaniritsidwa ku Yudeya m’nthawi ya atumwi ndipo ukukwaniritsidwanso padziko lonse m’masiku athu ano. Zimenezi zinathandiza kuti gulu lisinthe zimene linkafotokoza m’mbuyomu zokhudza ulosiwu.a
5. (a) Kodi n’chiyani chinayamba mu 1914? (b) Kodi zimenezo zikufanana bwanji ndi zimene zinachitika m’nthawi ya atumwi?
5 Tinazindikiranso kuti mbali yoyamba ya chisautso chachikulu sinayambe mu 1914. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga osati ndi nkhondo ya mayiko. Choncho zimene zinachitika mu 1914 sizinali chiyambi cha chisautso chachikulu koma “chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.” (Mat. 24:8) “Masautso” amenewa akufanana ndi zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudeya kuyambira mu 33 C.E. mpaka mu 66 C.E.
6. Kodi chisautso chachikulu chidzayamba bwanji?
6 Kodi chisautso chachikulu chidzayamba bwanji? Yesu analosera kuti: “Mukadzaona chinthu chonyansa chowononga chimene chinanenedwa kudzera mwa mneneri Danieli chitaimirira m’malo oyera, (wowerenga adzazindikire,) amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.” (Mat. 24:15, 16) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba mu 66 C.E. pamene asilikali achiroma, omwe ankaimira “chinthu chonyansa,” anaukira Yerusalemu pamodzi ndi kachisi wake, yemwe Ayuda ankaona kuti ndi ‘malo oyera.’ Apa zinali ngati ‘chinthu chonyansa chaimirira m’malo oyera.’ Ulosiwu udzakwaniritsidwa kachiwiri padziko lonse pamene bungwe la United Nations lidzaukira matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Bungweli likuimira “chinthu chonyansa” ndipo matchalitchiwo akuimira ‘malo oyera.’ chifukwa chakuti anthu ena amawaona choncho. Bungweli lidzaukiranso zipembedzo zonse zomwe ndi mbali ya Babulo Wamkulu. Zimenezi zafotokozedwanso pa Chivumbulutso 17:16-18, ndipo zidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu.
7. (a) Kodi anthu ‘anapulumuka’ bwanji m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi pa chisautso chachikulu padzachitika zotani?
7 Yesu analoseranso kuti: “Masikuwo adzafupikitsidwa.” Ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba mu 66 C.E. pamene asilikali achiroma ‘anafupikitsa masiku’ oukira Yerusalemu. Kenako Akhristu odzozedwa anathawa mu Yerusalemu ndi Yudeya n’cholinga choti ‘apulumuke.’ (Werengani Mateyu 24:22; Mal. 3:17) Ndiyeno, kodi pa chisautso chachikulu padzachitika zotani? Yehova ‘adzafupikitsa masiku’ amene bungwe la United Nations lidzaukire chipembedzo chonyenga n’cholinga choti chipembedzo choona chisawonongedwe nawo. Izi zidzapereka mpata kuti anthu a Mulungu apulumuke.
8. (a) N’chiyani chidzachitike mbali yoyamba ya chisautso chachikulu ikadzatha? (b) Kodi zikuoneka kuti Mkhristu womalizira wa m’gulu la 144,000 adzalandira mphoto yake kumwamba pa nthawi iti? (Onani mawu akumapeto.)
8 Nanga n’chiyani chidzachitike ikadzatha mbali yoyamba ya chisautso chachikulu? Mawu a Yesu aja akusonyeza kuti nkhondo ya Aramagedo isanayambe, padzachitika zinthu zina. N’chiyani chidzachitike pa nthawi imeneyi? Yankho lake lili pa Ezekieli 38:14-16 ndi Mateyu 24:29-31. (Werengani.)b Kenako Aramagedo idzayamba ndipo apa padzakhala pachimake pa chisautso chachikulu. Nkhondoyi idzafanana ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. (Mal. 4:1) Chimake cha chisautso chachikulu chidzakhala Aramagedo. Choncho tingati chisautsocho chidzakhala chinthu “chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano.” (Mat. 24:21) Nkhondoyi ikadzatha, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu udzayamba.
9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ulosi wa Yesu wonena za chisautso chachikulu umalimbikitsa anthu a Yehova?
9 Ulosi wonena za chisautso chachikuluwu ndi wolimbikitsa kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti ukutitsimikizira kuti kaya tikumana ndi mavuto otani, gulu la anthu a Yehova lidzapulumuka chisautso chachikulu. (Chiv. 7:9, 14) Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti pa nkhondo ya Aramagedo, Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira ndiponso adzayeretsa dzina lake lopatulika.—Sal. 83:18; Ezek. 38:23.
KODI YESU ADZAWERUZA LITI NKHOSA NDI MBUZI?
10. Kodi m’mbuyomu tinkaganiza chiyani zokhudza nthawi ya kuweruza nkhosa ndi mbuzi?
10 Tiyeni tsopano tikambirane mbali ina ya ulosi wa Yesu yonena za kuweruza nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:31-46) Kodi zimenezi zidzachitika liti? M’mbuyomu, tinkaganiza kuti kuweruza nkhosa ndi mbuzi kwakhala kukuchitika m’masiku otsiriza ano kuyambira mu 1914. Tinkaganizanso kuti anthu amene akukana kumva uthenga wa Ufumu n’kumwalira chisautso chachikulu chisanayambe ndi mbuzi ndipo sadzaukitsidwa.
11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanayambe kuweruza nkhosa ndi mbuzi mu 1914?
11 M’chaka cha 1995, Nsanja ya Olonda inafotokozanso lemba la Mateyu 25:31, lomwe limati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.” Magaziniyi inafotokoza kuti Yesu anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914 koma sanakhale “pampando wake wachifumu waulemerero” kuti aweruze “mitundu yonse ya anthu.” (Mat. 25:32; yerekezerani ndi Danieli 7:13.) Koma fanizo la nkhosa ndi mbuzi limafotokoza za udindo wa Yesu monga Woweruza. (Werengani Mateyu 25:31-34, 41, 46.) Yesu anali asanayambe kuweruza mitundu yonse ya anthu mu 1914. Choncho iye sanayambe kuweruza nkhosa ndi mbuzi m’chaka chimenecho.c Ndiyeno kodi Yesu adzayamba liti kuweruza?
12. (a) Kodi Yesu adzayamba liti kuweruza mitundu yonse ya anthu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zafotokozedwa pa Mateyu 24:30, 31 ndi Mateyu 25:31-33, 46?
12 Ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza umasonyeza kuti iye adzayamba kuweruza mitundu yonse ya anthu chipembedzo chonyenga chikadzawonongedwa. Monga tanenera m’ndime 8, zinthu zina zimene zidzachitike pa nthawiyo zafotokozedwa pa Mateyu 24:30, 31. Mukaona bwinobwino mavesiwa, muona kuti Yesu ankalosera zinthu zofanana ndi zimene anatchula m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Mwachitsanzo, pali mawu akuti Mwana wa munthu adzafika mu ulemerero wake limodzi ndi angelo ake ndiponso kuti mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye. Palinso mawu akuti anthu amene adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa ‘adzatukula mitu yawo’ podziwa kuti adzalandira “moyo wosatha.”d Komanso pali mawu akuti anthu amene adzaweruzidwa kuti ndi mbuzi “adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni” podziwa kuti akupita ku “chiwonongeko chotheratu.”—Mat. 25:31-33, 46.
13. (a) Kodi Yesu adzaweruza liti nkhosa ndi mbuzi? (b) Kodi mfundoyi ikutithandiza kuona bwanji utumiki wathu?
13 Choncho Yesu adzaweruza anthu a mitundu yonse kuti ena ndi nkhosa ndipo ena ndi mbuzi akadzabwera pa nthawi ya chisautso chachikulu. Kenako pa Aramagedo, yomwe ndi chimake cha chisautso chachikulu, anthu amene ali ngati mbuzi adzapita “ku chiwonongeko chotheratu.” Mfundo imeneyi ikutithandiza kuona kuti ntchito yathu yolalikira ndi yofunika kwambiri. Popeza kuti chisautso chachikulu sichinayambe, anthu adakali ndi mpata wosintha n’kuyamba kuyenda pa ‘msewu wopanikiza wolowera ku moyo.’ (Mat. 7:13, 14) N’zoona kuti ngakhale panopa anthu akhoza kuchita zinthu ngati nkhosa kapena mbuzi. Komabe tizikumbukira kuti anthu adzaweruzidwa kuti ndi nkhosa kapena mbuzi pa nthawi ya chisautso chachikulu. Chotero tiyenera kupitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu mwakhama kuti anthu ambiri akhale ndi mpata womvetsera uthengawu.
KODI YESU ADZABWERA LITI?
14, 15. Tchulani malemba anayi onena za nthawi imene Yesu adzabwere kudzaweruza anthu.
14 Kodi pali zinanso zokhudza ulosi wa Yesu umenewu zomwe tinkakhulupirira m’mbuyomu zimene tiyenera kusintha? Tiyeni tionenso ulosiwu kuti tipeze yankho.
15 Zimene Yesu analosera pa Mateyu 24:29 mpaka 25:46, kwenikweni zikuchitika m’masiku otsiriza ano ndipo zina zidzachitika pa chisautso chachikulu. Pa machaputala amenewa, Yesu ananena maulendo 8 za ‘kubwera’ kwake kapena kuti ‘kufika’ kwake.e Ponena za chisautso chachikulu, iye anati: “Adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba.” Ananenanso kuti: “Simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.” Komanso anati: “Pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu ananena kuti: ‘Mwana wa munthu adzafika mu ulemerero wake.’ (Mat. 24:30, 42, 44; 25:31) Malemba anayiwa akunena za nthawi imene Khristu adzabwere kudzaweruza anthu. Nanga malemba ena anayi otsala amene amanena za kubwera kwa Yesu ndi ati?
16. Kodi ndi malemba ena ati amene amanena za kubwera kwa Yesu?
16 Ponena za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yesu anati: “Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo.” M’fanizo la anamwali 10, Yesu anati: “Atanyamuka kupita kukagula, mkwati anafika.” M’fanizo la matalente, Yesu ananena kuti: “Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwera.” M’fanizo lomwelo, mbuyeyo ananena kuti: “Ine pobwera ndikanalandira ndalama zangazo.” (Mat. 24:46; 25:10, 19, 27) Kodi malemba amenewa akunena za kubwera kwa Yesu pa nthawi iti?
17. Kodi tinkafotokoza kuti mawu oti “pobwera” a pa Mateyu 24:46 akunena za nthawi iti?
17 M’mbuyomu, tinkafotokoza m’mabuku athu kuti kubwera kwa Yesu kotchulidwa m’malemba anayi a m’ndime 16 kunachitika mu 1918. Mwachitsanzo, taonani zimene Yesu ananena zokhudza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Werengani Mateyu 24:45-47.) Poyamba tinkaganiza kuti mawu akuti “pobwera” amene ali pa vesi 46 akunena za nthawi imene Yesu anabwera kudzayendera odzozedwa mu 1918, ndipo mu 1919 anaika kapoloyo kuti aziyang’anira zinthu zake zonse. (Mal. 3:1) Koma titaonanso bwinobwino ulosi wa Yesu umenewu, tazindikira kuti m’pofunika kusintha zinthu zina zimene tinkafotokoza m’mbuyomu. N’chifukwa chiyani tikutero?
18. Kodi kuonanso bwinobwino nkhani yonse yokhudza ulosi wa Yesu kwatithandiza kuzindikira chiyani pa nkhani ya kubwera kwake?
18 M’chaputala chomwechi, tisanafike pavesi 46, mawu onse onena za ‘kubwera’ amafotokoza za kubwera kwa Yesu kudzaweruza anthu pa chisautso chachikulu. (Mat. 24:30, 42, 44) Monga tanenera m’ndime 12, ‘kufika’ kwa Yesu kotchulidwa pa Mateyu 25:31 kudzachitikanso pa nthawi yomweyo. Chifukwa cha zimene tafotokozazi, tinganene kuti kubwera kwa Yesu kudzaika kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse, komwe kwatchulidwa pa Mateyu 24:46, 47, kudzachitika m’tsogolo pa nthawi ya chisautso chachikulu. Nkhani yonse yokhudza ulosi wa Yesu umenewu ikusonyeza kuti malemba onse 8 onena za kubwera kwake amafotokoza za nthawi imene azidzaweruza anthu pa chisautso chachikulu.
19. Kodi takambirana mfundo ziti, nanga nkhani yotsatira idzayankha mafunso ati?
19 Kumayambiriro kwa nkhaniyi, tinafunsa mafunso atatu okhudza nthawi. Tsopano tiyeni tibwereze zimene takambirana. Choyamba, takambirana kuti chisautso chachikulu sichinayambe mu 1914 koma chidzayamba pamene bungwe la United Nations lidzaukira Babulo Wamkulu. Kenako takambirana zifukwa zosonyeza kuti Yesu sanayambe kuweruza nkhosa ndi mbuzi mu 1914 koma adzachita zimenezi pa chisautso chachikulu. Pomaliza, taona umboni wakuti kubwera kwa Yesu kudzaika kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse sikunachitike mu 1919 koma zimenezi zidzachitika pa chisautso chachikulu. Mwachidule tingati zinthu zitatu zonsezi zidzachitika m’tsogolo pa chisautso chachikulu. Kodi zimene takambiranazi zikukhudza bwanji zinthu zina zimene tinkakhulupirira pa fanizo la kapolo wokhulupirika? Nanga zikukhudza bwanji zimene tinkakhulupirira pa mafanizo ena a Yesu amene akukwaniritsidwa masiku otsiriza ano? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ofunika amenewa.
a Ndime 4: Kuti mudziwe zambiri, onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1994, tsamba 8 mpaka 21 ndiponso ya May 1, 1999, tsamba 8 mpaka 20.
b Ndime 8: Chinthu chimodzi chimene chatchulidwa m’mavesi amenewa ndi ‘kusonkhanitsa osankhidwa.’ (Mat. 24:31) Choncho zikuoneka kuti odzozedwa onse amene adzakhale padzikoli mbali yoyamba ya chisautso chachikulu ikadzatha, adzatengedwa kupita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Izi zikusintha zimene zinafotokozedwa m’nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990, tsamba 30.
c Ndime 11: Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, tsamba 18 mpaka 28.
d Ndime 12: Onani nkhani yofanana ndi imeneyi pa lemba la Luka 21:28.
e Ndime 15: Mawu akuti ‘kubwera’ ndiponso ‘kufika’ anamasuliridwa kuchokera ku mawu amodzi achigiriki akuti erʹkho·mai.