Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Fanizo la Matalente?
“Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, wachiwiri anam’patsa matalente awiri, ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi.”—MAT. 25:15.
1, 2. N’chifukwa chiyani Yesu anapereka fanizo la matalente?
YESU anapereka fanizo la matalente pofuna kusonyeza bwino udindo umene odzozedwa ali nawo. Tiyenera kumvetsa bwino tanthauzo la fanizoli chifukwa likukhudza tonsefe, kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi.
2 Iye anapereka fanizoli poyankha funso la ophunzira ake lokhudza “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3) Choncho fanizoli likukwaniritsidwa m’nthawi yathu ndipo ndi mbali ya chizindikiro chakuti Yesu akulamulira.
3. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa fanizo la (a) kapolo wokhulupirika (b) anamwali 10 (c) matalente (d) nkhosa ndi mbuzi?
3 Mu lemba la Mateyu 24:45 mpaka 25:46, Yesu anafotokoza mafanizo okwana 4. Anafotokoza fanizo la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, la anamwali 10, la matalente ndiponso la nkhosa ndi mbuzi. Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo onsewa poyankha funso lokhudza chizindikiro cha kukhalapo kwake. M’mafanizowa, anafotokozanso makhalidwe amene otsatira ake enieni ayenera kukhala nawo masiku otsiriza ano. Mafanizo onena za kapolo, anamwali ndiponso matalente amakhudza odzozedwa. Mwachitsanzo, mu fanizo la kapolo wokhulupirika, Yesu anasonyeza kuti odzozedwa, amene ali mu kagulu kopereka chakudya m’masiku otsiriza, ayenera kukhala okhulupirika ndiponso anzeru. Mu fanizo la anamwali, anasonyeza kuti odzozedwa onse ayenera kukhala okonzeka ndiponso atcheru. Ayenera kuchita zimenezi chifukwa choti sakudziwa nthawi imene Yesu adzafike. Mu fanizo la matalente, Yesu anasonyeza kuti odzozedwa ayenera kuchita khama pa ntchito yomwe anapatsidwa. Kenako iye anapereka fanizo la nkhosa ndi mbuzi pofuna kuthandiza anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. Anasonyeza kuti iwo ayenera kukhala okhulupirika pothandiza odzozedwa apadzikoli, omwe ndi abale ake.a Tsopano tiyeni tikambirane fanizo la matalente.
AMBUYE ANAPEREKA NDALAMA ZAMBIRI KWA AKAPOLO AKE
4, 5. Kodi mbuye wotchulidwa mu fanizoli akuimira ndani ndipo talente imodzi inali yofanana ndi madinari angati?
4 Werengani Mateyu 25:14-30. Mabuku athu akhala akufotokoza kuti munthu kapena mbuye wotchulidwa mu fanizoli akuimira Yesu. Amafotokozanso kuti iye atapita kumwamba mu 33 C.E., zinali ngati wapita kudziko lina. Mu fanizo lina, Yesu ananena kuti cholinga chopitira kudziko lina chinali ‘kukalandira ufumu.’ (Luka 19:12) Koma iye sanalandire Ufumu atangopita kumene kumwambako.b M’malomwake, ‘anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambira pamenepo, anayembekezera kufikira pamene adani ake anaikidwa monga chopondapo mapazi ake.’—Aheb. 10:12, 13.
5 Mbuye wa mu fanizoli anali ndi matalente 8. Pa nthawiyo, zimenezi zinali ndalama zambiri zedi.c Asanapite kudziko lina, mbuyeyo anapereka ndalamazo kwa akapolo ake kuti achite malonda. Mofanana ndi mbuyeyo, Yesu anali ndi chuma chamtengo wapatali asanapite kumwamba. Chumacho chinkaimira ntchito yolalikira chifukwa ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri.
6, 7. Kodi matalente akuimira chiyani?
6 Tanena kale zoti Yesu ankaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. (Werengani Luka 4:43.) Zinali ngati anatsegula munda umene ungakhale ndi zokolola zambiri. Pa nthawi ina, anauza ophunzira ake kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35-38) Iye ananena izi pofuna kusonyeza kuti padzakhala ntchito yaikulu yosonkhanitsa anthu amitima yabwino kuti akhale ophunzira ake. Mofanana ndi zimene mlimi angachite, Yesu sanasiye munda wake popanda antchito oti azikolola. Iye atangoukitsidwa anauza ophunzira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:18-20) Choncho Yesu asanapite kumwamba anapereka ntchito yolalikira kwa ophunzira ake. Izi zinali ngati kuwapatsa chuma chamtengo wapatali.—2 Akor. 4:7.
7 Ndiyeno kodi matalente a mu fanizo la Yesu ankaimira chiyani? Pamene Yesu ankapereka ntchito yolalikira kwa ophunzira ake, tinganene kuti anawasungitsa “chuma chake” kapena kuti matalente. (Mat. 25:14) Mwachidule tingati matalente akuimira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa.
8. Kodi mbuyeyo ankayembekezera chiyani ngakhale kuti akapolowo anapatsidwa matalente osiyana?
8 Fanizoli likusonyeza kuti mbuyeyo anapereka matalente 5 kwa kapolo wina, matalente awiri kwa wina ndipo winayo anangomupatsa talente imodzi. (Mat. 25:15) Ngakhale kuti akapolowa analandira matalente osiyana, mbuyeyo ankayembekezera kuti onse achita khama. Choncho tinganene kuti Khristu ankafuna zoti ophunzira ake achite zonse zimene angathe pa ntchito yolalikira. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Akhristu akhala akuchita malonda ndi matalente. Buku la Machitidwe limasonyeza kuti iwo ankachita khama kwambiri pa ntchito yolalikira.d—Mac. 6:7; 12:24; 19:20.
AKAPOLO AKUCHITA MALONDA NTHAWI YA MAPETOYI
9. (a) Kodi akapolo awiri okhulupirika anachita bwanji ndi matalente aja ndipo izi zikusonyeza chiyani? (b) Kodi a “nkhosa zina” ayenera kuchita chiyani?
9 M’nthawi ya mapeto ino, makamaka kuyambira mu 1919, Akhristu odzozedwa okhulupirika akhala akuchita malonda ndi matalente a Ambuye. Mofanana ndi akapolo awiri oyamba aja, Akhristuwa akhala akuchita zonse zimene angathe pa ntchito yawo. Sitinganene kuti amene analandira matalente 5 ndi ndani kapena amene analandira matalente awiri ndi ndani. Chofunika kwambiri n’chakuti mu fanizoli, onse awiri anachita khama n’kuchulukitsa kawiri matalente amene anapatsidwa. Koma kodi anthu amene adzakhale padzikoli ayenera kugwiranso ntchito imene odzozedwa apatsidwa? Fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi limasonyeza kuti anthu amenewa ali ndi mwayi waukulu wothandiza abale a Khristu pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. M’masiku otsiriza ano, magulu awiriwa ali ngati “gulu limodzi.” Onse akugwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu.—Yoh. 10:16.
10. Kodi mbali yaikulu ya chizindikiro chakuti Yesu akulamulira ndi iti?
10 Ambuye amayembekezera kuti tizigwira ntchito mwakhama. Tanena kale kuti Akhristu oyambirira ankachitadi zimenezi. Kodi izi n’zimene zikuchitika m’masiku otsiriza ano pamene fanizo la matalente likukwaniritsidwa? Inde. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu okhulupirika akhala akugwira mwakhama kwambiri ntchito yolalikira. Chaka chilichonse, anthu masauzande ambiri amakhala ofalitsa. Izi zachititsa kuti ntchito yolalikira ikhale mbali yaikulu ya chizindikiro chakuti Yesu akulamulira. Ambuye ayenera kuti akusangalala kwambiri.
KODI MBUYE WAWO ADZABWERA LITI?
11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu adzabwera kudzawerengera ndalama pa chisautso chachikulu?
11 Yesu adzabwera kudzawerengera ndalama chakumapeto kwa chisautso chachikulu. N’chifukwa chiyani tikunena choncho? Yesu ananena mobwerezabwereza za kubwera kapena kufika kwake mu ulosi wa pa Mateyu chaputala 24 ndi 25. Mwachitsanzo iye ananena kuti pa chisautso chachikulu anthu “adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba” kudzapereka chiweruzo. Yesu ananena kuti otsatira ake amene adzakhalepo m’masiku otsirizawo ayenera kukhala maso. Iye ananena kuti: “Simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.” Komanso anati: “Pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” (Mat. 24:30, 42, 44) Choncho pamene iye ananena kuti “mbuye wa akapolowo anabwera ndi kuwerengerana nawo ndalama,” ayenera kuti ankatanthauzanso nthawi imene adzabwere kudzaweruza anthu pamapeto a dzikoli.e—Mat. 25:19.
12, 13. (a) Kodi mbuyeyo anati chiyani kwa akapolo awiri oyambirira, ndipo n’chifukwa chiyani anatero?(b) Kodi odzozedwa adzadindidwa liti chidindo chomaliza? (Onani bokosi lakuti “Nanga Amene Amamwalira Chisautso Chachikulu Chisanayambe?” pamwambapa.) (c) Kodi anthu amene adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa adzalandira mphoto iti?
12 Fanizo lija limanena kuti mbuye wawo atabwera anapeza kuti amene anapatsidwa matalente 5 ndiponso amene anapatsidwa awiri anali okhulupirika. Woyambayu anapeza 5 enanso pomwe wachiwiri anapeza awiri ena. Mbuyeyo anagwiritsa ntchito mawu ofanana poyamikira akapolo awiriwa. Anati: “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri.” (Mat. 25:21, 23) Kodi izi zikusonyeza kuti Yesu adzachita chiyani akadzabwera kudzaweruza anthu m’tsogolomu?
13 Chisautso chachikulu chisanayambe, odzozedwa akhama amene akuimiridwa ndi akapolo awiri oyamba aja adzakhala atadindidwa chidindo chomaliza. (Chiv. 7:1-3) Ndiyeno nkhondo ya Aramagedo isanayambe, Yesu adzawapatsa mphoto yawo kumwamba. Anthu ena amene athandiza abale a Khristu pa ntchito yolalikira adzaweruzidwa kuti ndi nkhosa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala padziko lapansi n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.—Mat. 25:34.
KAPOLO WOIPA NDI WAULESI
14, 15. Kodi Yesu ankasonyeza kuti odzozedwa ambiri adzasintha n’kukhala oipa ndiponso aulesi? Fotokozani.
14 Mu fanizoli, kapolo womaliza anangobisa talente ija m’malo mochita nayo malonda kapena kusungitsa kubanki. Kapoloyo anasonyeza mtima woipa chifukwa sanayese n’komwe kuthandiza mbuye wake. N’chifukwa chake mbuyeyo anamuuza kuti ndi “kapolo woipa ndi waulesi.” Kenako mbuyeyo anamulanda talenteyo n’kuipereka kwa kapolo amene anali ndi matalente 10. Kapolo woipayo anaponyedwa ‘kunja kumdima kumene analira ndi kukukuta mano.’—Mat. 25:24-30; Luka 19:22, 23.
15 Popeza kuti kapolo mmodzi anabisa talente, kodi Yesu ankatanthauza kuti wodzozedwa mmodzi pa atatu alionse adzakhala woipa ndiponso waulesi? Ayi. Kumbukirani zimene Yesu ananena m’mafanizo ena okhudza masiku otsiriza. Mu fanizo la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, iye anafotokoza za kapolo woipa amene anayamba kumenya akapolo anzake. Pamenepa Yesu sankatanthauza kuti ena adzasintha n’kukhala kapolo woipa. Koma ankachenjeza kapolo wokhulupirika kuti asamasonyeze makhalidwe a kapolo woipa. N’chimodzimodzi ndi fanizo la anamwali 10. Yesu sankatanthauza kuti hafu ya odzozedwa adzayamba kukhala ngati anamwali opusa aja. M’malomwake, ankachenjeza abale ake zimene zingachitike ngati atasiya kukhala tcheru ndiponso kukhala okonzeka.f Choncho n’zomveka kunena kuti mu fanizo la matalente, Yesu sankatanthauza kuti m’masiku otsiriza odzozedwa ambiri adzasintha n’kukhala oipa ndiponso aulesi. Yesu anachenjeza odzozedwa kuti azichita malonda ndi matalente awo kapena kuti azichita khama pa ntchito yawo n’kumapewa makhalidwe ndiponso mtima wa kapolo woipa.—Mat. 25:16.
16. (a) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa fanizo la matalente? (b) Kodi m’nkhaniyi tasintha bwanji mmene timafotokozera fanizo la matalente? (Onani bokosi lakuti “Tanthauzo la Fanizo la Matalente” patsamba 24.)
16 Kodi tikuphunzirapo chiyani pa fanizo la matalente? Choyamba, Mbuye yemwe ndi Khristu, wapereka ntchito yamtengo wapatali kwa odzozedwa. Ntchitoyi ndi yolalikira ndi kuphunzitsa. Chachiwiri, Khristu amafuna kuti tonsefe tizichita khama pa ntchito yolalikira. Tiyeni tipitirize kugwira ntchitoyi mwakhama, kukhala okhulupirika ndiponso atcheru. Tikatero Mbuye wathu adzatidalitsa.—Mat. 25:21, 23, 34.
a Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 21 mpaka 22, ndime 8 mpaka 10, inafotokoza mfundo zotithandiza kudziwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Nkhani yapitayi yafotokoza tanthauzo la fanizo la anamwali 10. Fanizo la nkhosa ndi mbuzi linafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, tsamba 23 mpaka 28 ndiponso lifotokozedwa m’nkhani yotsatira.
b Onani bokosi lakuti “Kodi Fanizo la Matalente Likufanana Bwanji ndi la Ndalama za Mina?”
c M’nthawi ya Yesu, talente imodzi inali yofanana ndi madinari 6,000. Antchito ambiri ankalandira dinari imodzi pa tsiku. Choncho munthu ankayenera kugwira ntchito zaka 20 kuti alandire talente imodzi.
d Atumwi atamwalira, Satana anayambitsa mpatuko. Mpatukowo unasokoneza mpingo wachikhristu kwa zaka zambiri. Pa nthawiyi, palibe anthu amene ankapitiriza ntchito imene Yesu anaisiya. Koma izi zinadzasintha ‘m’nthawi yokolola’ kapena kuti m’masiku otsiriza. (Mat. 13:24-30, 36-43) Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 9 mpaka 12.