Chaputala 7
Kulongosola Nkhani za Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Ndalama za Kristu
1. Kodi ndiboma liti limene liribe mavuto alionse azachuma, ndipo kodi ndani amene tsopano ayenera kuŵerengerana ndi boma limeneli?
KUSIYAPO limodzi lokha, palibe boma limene liribe mavuto azachuma. Maboma ambiri ali ndi ngongole yaikulu. Boma limodzi lokha limene silikuphatikizidwa ndilo “ufumu wakumwamba” limene tsopano likulengezedwa kwambiri. (Mateyu 25:1) Pakali chikhalirebe mamembala oyembekezeredwa amenewo a ufumu Wakumwamba umenewo amene ali muutumiki wa boma limenelo. Mkati mwanyengo yovutitsa koposa m’mbiri yonse yaumunthu imeneyi, atumiki a “ufumu wakumwamba” ameneŵa akuŵerengeredwa. Iwo afunikira kudziyankhira kuboma ponena za mmene agwiritsirira ntchito zinthu zamtengo wapatali zoikiziridwa kwa iwo.
2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okondwerera kwambiri fanizo lina monga momwe linasimbidwira ndi “Kalonga wa Mtendere”?
2 Kufotokoza mwafanizo nkhani imeneyi, kalekale woimira wamkulu koposa wa “ufumu wakumwamba” umenewo anasimba fanizo. Limeneli liyenera kutikondweretsa lerolino, chifukwa chakuti “Kalonga wa Mtendere” analiphatikiza muulosi wake wautali wonena za “chizindikiro” chimene chikasonyeza “kukhalapo” kwake mu Ufumu limodzi ndi mphamvu yokwanira ya kulamulira. (Mateyu 24:3) Ife lerolino tikuphatikizidwa mosapeŵeka ndi zotulukapo zimene zimatsatira kukwaniritsidwa kwa fanizo lolosera, chifukwa chakuti kupitirizabe kukhalapo kwathu, moyo wathu weniweniwo, zikuphatikizidwa. Motero nayi njira imene “Kalonga wa Mtendere” anasimba nayo fanizo kwa atumwi ake masiku ochepekera imfa yake yopereka nsembe pa Golgota isanachitike.
Fanizo la Matalente
3. Kodi akapolo amene analandira matalente kuchokera kwa mbuye wawo asanachoke anawasamalira motani mkati mwa kusakhalapo kwake?
3 “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake. Pakuti monga munthu, wakumka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu,a ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira ndalama zisanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu. Chimodzimodzinso uyo wa ziŵirizo, anapindulapo zina ziŵiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, nabisa ndalama ya mbuye wake.
4. Kodi nchiyani chimene mbuye wawo adanena kwa akapolo amene anawonjezera chiŵerengero cha matalente?
4 “Ndipo itapita nthaŵi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi. Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente zisanu, wonani ndapindulapo ndalama zisanu zina. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; loŵa iwe m’chikondwerero cha mbuye ŵako. Ndipo wandalama ziŵiriyo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine ndalama ziŵiri; wonani, ndapindulapo ndalama zina ziŵiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; loŵa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.
5, 6. Kodi ndichodzikhululukira chotani chimene kapolo wachitatu anapereka cha kubisira talente, ndipo kodi mbuyake anachitanji kwa iye?
5 “Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziŵani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wa kututa kumene simunafesa, ndi wa kusonkhanitsa kumene simunawaza; ndinawopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: wonani, siiyi yanu. Koma mbuye wake anayakha nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziŵa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake.
6 “Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”—Mateyu 25:13-30.
7. Kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi matalente?
7 M’fanizo limeneli, kodi matalente amaimira chiyani? Chinthu chamtengo wapatali, osati m’lingaliro la ndalama, koma m’lingaliro lauzimu. Matalente amaimira lamulo la kukapanga ophunzira a Kristu lamulo limeneli limayendera limodzi ndi mwaŵi wapamwamba wa kukhala nthumwi za Kristu, Mfumuyo, kuimira Ufumuwo kumitundu yonse ya dziko.—Aefeso 6:19, 20; 2 Akorinto 5:20.
8. (a) Kodi ndimumdima wotani umene kagulu ka kapolo “waulesi” kaponyedwamo mkati mwa ‘mapeto a dongosolo lino la zinthu’? (b) Kodi nchifukwa ninji dziko la mtundu wa anthu silikusangalala ndi kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso?
8 Mosakaikira konse, ife lerolino tafika kumapeto kwa kukwaniritsidwa kwa fanizo lolosera limeneli! Pa mbadwo uno pafika nyengo ya mdima wa ndiwe yani kuposa mbiri yonse ya anthu! Ndithudi, kuli mdima waukulu kunja kwa mbali yowoneka ya gulu la Yehova kumene “kagulu ka kapolo waulesi” ndi “wopanda pake” kangaponyeredweko molamulidwa ndi Ambuye. “Mdima wakunja” umenewo umatanthauza mkhalidwe wa mdima wa anthu, makamaka m’lingaliro lachipembedzo. Anthu alibe kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso. Saali m’kuunika kwa kudziŵa Ufumu wa Mulungu. Likulamulidwa ndi “mulungu wanthaŵi ino ya pansi pano,” amene ‘wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawaŵalire.’—2 Akorinto 4:4.
9. (a) M’kukwaniritsidwa kwa fanizo, kodi ndani amene anaphiphiritsiridwa ndi “mwamuna,” ndipo anapita kutali motani? (b) Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wosonyeza kubwera kwake?
9 Lerolino pali umboni waukulu wakuti wophiphiritsiridwa ndi “munthu,” amene anali ndi matalente a siliva okwanira asanu ndi atatu, wabwera kuchokera kumaulendo ake akutali. “Munthu” ameneyo ndiye Kristu Yesu. Ulendo wake kudziko lakwinawo unamfikitsa pamaso pa Mlengi wa dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi za chilengedwe chathu. Kusonyeza kubwera kwake, nkhondo ziŵiri zadziko, tsopano zotsagana ndi nkhondo zina zambiri pamlingo wocheperapo, zakhathamiritsa dziko lathu lapansi ndi magazi. Monga momwe kudanenedweratu, zimenezi zatsagana ndi njala, miliri, ndi zivomezi, ndiponso ndi kuwonjezereka kwa kusayeruzika ndi kulalikidwa kwa “mbiri yabwino” m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Zimenezi zakwaniritsa maumboni a zimene Yesu adanena kuti zikakhala “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.”—Mateyu 24:3-15, NW.
10. (a) Kodi nchifukwa ninji mwamunayo anapita kudziko lakutali? (b) Kodi nchifukwa ninji kunali kwakuti dziko lamtundu wa anthu kwenikweni silinawone kubwera kwake?
10 Ngakhale kuli kwakuti sikunasonyezedwe molunjika m’fanizo la Yesu, munthu wopita kudziko lakutali, wochoka kwanthaŵi yaitali, kwenikweni ulendo wake unali wokalandira “ufumu wakumwamba,” wotchulidwa kuchiyambiyambi m’Mateyu 25:1. Mosasamala kanthu za kuulika kwa Nkhondo Yadziko I, Yehova Mulungu, amene ufumu wake pa Israyeli unagubuduzidwa mu 607 B.C.E., anakhazikitsa pampando wachifumu Woloŵa nyumba wa Ufumu wokhala ndi kuyenera mu 1914 C.E., imene inali nthaŵi ya kutha kwa kuponderezedwa kwake. Ayi, mitundu Yachikunja sinawone ndi maso awo enieni kuikidwa pampando wachifumu kwa Uyo amene Mfumu Davide anamtcha “Ambuye wanga.” (Salmo 110:1) Iwo sakanamuwona chifukwa chakuti mwamuna wa m’fanizo limenelo, Yesu Kristu, anali atauza ophunzira ake, asanayende ulendo wopita kutaliwo kuti: “Katsala kanthaŵi, ndipo dziko lapansi silidzandiwonanso ine.”—Yohane 14:19.
11. (a) Kodi nchiyani chimene chikakhala mbali ya chizindikiro chosonyeza kubwera kwake ndi kukhalapo kwake? (b) Kodi ndiliti pamene zimenezi zikachitika?
11 Popeza kudza m’mphamvu ya Ufumu wakumwamba kochitidwa ndi Kristu kunali kosawoneka ndi maso aumunthu, iye anafunikira kusonyeza kukhalapo kwake mu Ufumu wakumwamba mwa chizindikiro chimene atumwi anapempha kwa iye masiku atatu imfa yake yophedwera chikhulupiriro isanachitike. Mbali ya chizindikiro chokhutiritsa maganizo chimenecho inali kudzakhala yakuti mwamunayo akabwerera kuchokera ku ulendo ndi kuŵerengera ndi akapolo ake amene anaikizirako matalente ake amtengo wapatali. Popeza zimenezi zinali choncho, kuŵerengera kumeneko kwa okhala ndi mwaŵi wa kugwiritsira ntchito matalente kunali kudzachitika pambuyo pa 1914.
12. (a) Kodi ndani amene ali ndi thayo la kutsogolera kuperekedwa kwa umboni wa Ufumu? (b) Kodi chipulumutso chawo potsirizira pake chimadalira pa chiyani?
12 Zimenezi zikatanthauza kuŵerengerana ndi awo amene anali oloŵa nyumba a “ufumu wakumwamba.” Zimenezi zikatanthauza kuŵerengerana ndi otsalira a kagulu Kachikristu kameneko, kamene kanabalidwa ndi mzimu wa Mulungu kuyambira patsiku la Pentekoste wa chaka cha 33 C.E. (Machitidwe, chaputala 2) Pakakhala otsalira a ameneŵa padziko lapansi mkati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” kuyambira 1914 kumkabe mtsogolo. Ameneŵa akakhala amene thayo likagwera pa iwo la kutsogolera kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wa panthaŵi imeneyo wakuti: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Ameneŵa ali ndi thayo la kukhala okhulupirika kufikira mapeto, kotero kuti apulumutsidwe kuloŵa mu Ufumu wakumwamba. (Mateyu 24:13) Pokhala ndi lingaliro la chipulumutso chawo chomalizira, Mulungu Wamphamvuyonse wawalimbikitsa kupirira kufikira tsopano, mosasamala kanthu za chizunzo cha padziko lonse. Chenicheni chimenecho chikuchitira umboni kuti akuwavomereza!
Odzinenera Monyenga Kukhala ndi Matalente
13. (a) Kodi ndani amene amanena kuti analandira matalente? (b) Kodi ndichiweruzo chake chotani chimene timafikira?
13 Dziko Lachikristu limadzinenera kuti liri ndi chiyanjo cha kuikiziridwa matalente a munthu wachuma wa m’fanizo la Yesu. Koma pamene tipenda njira yake chiyambire 1914, kodi tifika pachiweruzo chotani? Ichi: Iro silinakhale ndi moyo mogwirizana ndi zonena zake. Lakhala losakhulupirika kwa mwamuna wa m’fanizo, iro ladzigwirizanitsa ndi maufumu a dziko lino; andale zadziko amaboma audziko ndiwo atsamwali ake. Iro likali kuchirikizabe Mitundu Yogwirizana, yoloŵa m’malo mwa Chigwirizano cha Amitundu chimene tsopano chiri chakufa.
14. Kodi tikulipeza kuti Dziko Lachikristu lerolino?
14 Iro silimaphiphiritsira ngakhale kapolo wopatsidwa talente limodzi, amene anatsimikizira kukhala waulesi ndi amene sanawonjezere chuma cha mbuye wake. Motero m’nyengo ino chiyambire pachimake pa Nkhondo Yadziko I mu 1918, mosakaikira Dziko Lachikristu ladziŵikitsidwadi nthaŵi zonse kukhala mu mdima wakunja kwa nyumba ya Mbuye younikiridwa bwino lomwe. Mu mdima wa ndiwe yani kunjako ndiko kumene, m’kulankhula kophiphiritsira, likulira ndi kukukuta mano kumene kwayamba kale kuchitika. Zowonjezereka zidzachitika pamene okondedwa ake andale za dziko amtembenukira ndi kumkhalitsa wamaliseche monga wokhala ndi liwongo lalikulu koposa wa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga.
Kagulu ka “Kapolo Woipa” Kaponyedwa Kunja
15. Kodi ndani amene akwaniritsa chithunzi cha kapolo waulesi, ndipo kodi iwo akudzipeza kuti tsopano?
15 Awo amene kwenikweni akhala mbali ya otsalira odzozedwa ndi mzimu ndi amene aikiziridwa kukhala ndi chuma cha Ufumu, koma amene aleka kupanga zoyesayesa za kuwonjezera zinthu za Ambuye wobwerayo, aponyedwa kunja kwa utumiki wachifumu wa Ambuye. (Mateyu 24:48-51) Sitimapeza konse kagulu ka “kapolo woipa” ndi waulesi kali kulalikira “mbiri yabwino ya ufumu.” Mmalo mwake, iwo akudera nkhaŵa ndi chipulumutso chawo mmalo mwa zinthu za Ufumu wa Mulungu. Iwo tsopano akupezeka mu “mdima wakunja,” kumene dziko la mtundu wa anthu liri. Talente lawo lophiphiritsira lalandidwa kwa iwo ndipo lapatsidwa kukagulu kamene kasonyeza kufunitsitsa kugwiritsira ntchito talente limenelo mkati mwa nthaŵi yotsala ya ‘mapeto a dongosolo limeneli la zinthu.’
16. (a) Kodi ino iri nthaŵi yabwino kwambiri yakuti matalente ophiphiritsira tiwagwiritsire ntchito motani? (b) Kodi ndithayo lotani limene tsopano liri la “khamu lalikulu” la “nkhosa zina”?
16 Sipanakhale nthaŵi yokondweretsa kwambiri motere ya kulengeza “mbiri yabwino ya ufumu” mogwiritsira ntchito “talente,” ndiko kuti, mwaŵi wapadera, mpata, wa kukhala “nthumwi m’malo mwa Kristu,” Mfumu yolamulira, ndi kumpangira ophunzira ake. (2 Akorinto 5:20) Ndipo pamene mapeto akuyandikira mofulumira, kuli koyenerera kuti “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lithandize nthumwi zotsala zobadwa ndi mzimu pamene mwachangu likugwiritsira ntchito mokwanira “talente” la mtengo wapatali loikiziridwa kwa iwo.
[Mawu a M’munsi]
a Talente la siliva Lachigiriki linali lolemera makilogalamu 20,4.
[Chithunzi patsamba 59]
Awo osonyeza zizindikiro za kukhala kapolo woipa amachotsedwa mu utumiki wa Ambuye ndi kuponyedwa mu mdima