‘Umboni kwa Anthu a Mitundu Yonse’
“Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.”—MACHITIDWE 1:8.
1. Kodi nthawi yoyamba imene ophunzira anamva ulosi wa pa Mateyu 24:14 ndi liti ndipo anali kuti?
MAWU a Yesu pa Mateyu 24:14 ndi odziwika kwambiri, moti ambiri ife tinawaloweza pamtima. Ulosi umenewu ndi wapadera kwambiri. Kaya nthawi yoyamba imene ophunzira ake anamva ulosi umenewu anaganiza chiyani kaya. Ulosi wakewu unanenedwa chaka cha 33 C.E. Ophunzirawo anali atakhala ndi Yesu pafupifupi zaka zitatu, ndipo apa anali atabwera naye Yesuyo ku Yerusalemu. Anali ataona zozizwitsa zimene iye anachita ndi kumvetsera zimene iye anaphunzitsa. Ngakhale kuti iwo anasangalala ndi mfundo za choonadi chamtengo wapatali zimene Yesu anawaphunzitsa, anali kudziwa kuti si onse amene anasangalala nazo. Yesu anali ndi adani amphamvu.
2. Kodi ophunzira anali kudzakumana ndi zoopsa ndi mavuto otani?
2 Ali khale pamodzi ndi Yesu pa phiri la Azitona, ophunzira anayi anamvetsera mwachidwi pamene iye analankhula za zoopsa ndi mavuto amene iwo adzakumane nawo m’tsogolo. Tsiku lina m’mbuyomo, Yesu anali atawauza kuti iye adzaphedwa. (Mateyu 16:21) Koma ulendo uno anawauza mosabisa kuti iwonso anthu adzawavutitsa koopsa. Iye anati: “Adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” Koma si zokhazo ayi. Aneneri onyenga adzasocheretsa ambiri. Ena adzakhumudwa ndipo adzaperekana ndi kudana. Ndiponso, “anthu aunyinji,” adzalola chikondi chawo pa Mulungu ndi Mawu ake kuzirala.—Mateyu 24:9-12.
3. N’chifukwa chiyani mawu a Yesu pa Mateyu 24:14 ali odabwitsa kwambiri?
3 Yesu atatchula zinthu zofoola ngati zimenezi, m’pamene anauza ophunzira ake mawu amene iwo ayenera kuti anadabwa nawo. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Inde, ntchito imene Yesu anayambitsa mu Israyeli, ‘yochita umboni ndi choonadi,’ idzapitiriza mpaka itafika padziko lonse lapansi. (Yohane 18:37) Uwutu ndi ulosi wodabwitsa kwambiri! Kufikitsa ntchitoyo kwa “anthu a mitundu yonse” n’kovuta. Ndipotu kuchita zimenezo kwinaku ‘akudedwa ndi anthu a mitundu yonse,’ n’kozizwitsa ndithu. Ntchito yaikulu imeneyi ikadzachitika, sidzangokweza chabe ulamuliro ndi mphamvu za Yehova, koma idzakwezanso chikondi chake, chifundo, ndi kuleza mtima kwake. Ndipo ntchito imeneyi idzapatsa atumiki ake mpata woonetsa chikhulupiriro chawo ndi kudzipereka kwawo.
4. Kodi ndani amene anauzidwa kuchita ntchito ya umboni, ndipo Yesu anawalimbikitsa motani?
4 Yesu sanawabisire ophunzira ake kuti anali ndi ntchito yaikulu yoti iwo achite. Asanapite kumwamba, anaonekera kwa iwo ndipo anawauza kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) N’zoona kuti posapita nthawi, ena anayamba kuchita nawo ntchitoyi. Ngakhale zinatero, ophunzirawo anali ochepa kwambiri. Ayenera kuti zinawalimbikitsa kwambiri atamva kuti mzimu woyera wa Mulungu, womwe uli wamphamvu, udzawathandiza kuchita ntchito imeneyi.
5. Kodi ophunzira sanadziwe chiyani za ntchito ya umboni?
5 Ophunzirawo anali kudziwa kuti anayenera kulalikira uthenga wabwino ndi ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19, 20) Koma sanadziwe kuti umboniwo udzaperekedwa kufika potani, ndipo sanadziwe kuti mapeto adzafika liti. Ifenso sitikudziwa. Amene akudziwa zimenezi ndi Yehova yekha. (Mateyu 24:36) Yehova atakhutira ndi umboni umene waperekedwa, adzawononga dongosolo ili loipa la zinthu. Apo m’pamene Akristu adzazindikira kuti ntchito yolalikira yachitika kufika pamene Yehova anali kufuna. Zinali zosatheka kwa ophunzira oyambirira aja kudziwa kuti umboni udzaperekedwa kufika pati m’nthawi ya mapeto ino.
Umboni M’nthawi ya Atumwi
6. Kodi chinachitika pa Pentekoste mu 33 C.E. n’chiyani, nanga chinachitika n’chiyani patangodutsa nthawi yochepa?
6 M’nthawi ya atumwi, ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira inali ndi zotsatirapo zabwino zosayembekezeka. Tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., ophunzira pafupifupi 120 anali m’chipinda cha pamwamba ku Yerusalemu. Tsiku limenelo, mzimu woyera wa Mulungu unatsanulidwa pa iwo, ndipo mtumwi Petro anakamba nkhani yogwira mtima pofotokoza tanthauzo la chozizwitsa chimenecho. Mapeto ake, anthu pafupifupi 3,000 anakhulupirira ndipo anabatizidwa. Zimenezo zinali chiyambi chabe. Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo anayesa umu ndi umu kuletsa ntchito yolalikira uthenga wabwino, “Ambuye anawonjezera [kwa ophunzira] tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.” Sipanapite nthawi ndipo “chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.” Kenako, “anawonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi.”—Machitidwe 2:1-4, 8, 14, 41, 47; 4:4; 5:14.
7. N’chifukwa chiyani nkhani ya kutembenuka kwa Korneliyo inali yapadera kwambiri?
7 Chaka cha 36 C.E. kunachitikanso nkhani inayake yapadera kwambiri. Korneliyo, amene sanali Myuda, anatembenuka n’kubatizidwa. Potsogolera mtumwi Petro kwa munthu woopa Mulungu ameneyu, Yehova anasonyeza kuti lamulo la Yesu lakuti ‘aphunzitse anthu a mitundu yonse’ silinakhudze Ayuda okha amene anali kukhala m’mayiko osiyanasiyana. (Machitidwe 10:44, 45) Kodi amene anali kutsogolera ntchitoyi anatani atamva zimenezi? Atumwi ndi akulu ku Yudeya atazindikira kuti uthenga wabwino uyeneranso upite kwa anthu a mitundu—amene sanali Ayuda—analemekeza Mulungu. (Machitidwe 11:1, 18) Nthawi imeneyo, ntchito yolalikira inapitiriza kubala zipatso mwa Ayuda. Patapita zaka zambiri, mwina kufika mu 58 C.E., panali anthu ‘okhulupirira ambirimbiri mwa Ayuda’ kuwonjezera pa anthu okhulupirira amene sanali Ayuda.—Machitidwe 21:20.
8. Kodi uthenga wabwino umawakhudza bwanji anthu?
8 Ngakhale kuti n’zosangalatsa kumva za kuchuluka kwa Akristu oyambirira, tisaganize kwambiri za nambalayo koma za anthuwo. Uthenga wa m’Baibulo umene iwo anamva unali wamphamvu. (Ahebri 4:12) Unasinthiratu moyo wa anthu amene anaulandira. Anthuwo anayeretsa moyo wawo, kuvala umunthu watsopano, ndipo anayanjanitsidwanso ndi Mulungu. (Aefeso 4:22, 23) Ndi mmenenso zilili masiku ano. Ndipo onse amene akulandira uthenga wabwino ali ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chokhala ndi moyo kosatha.—Yohane 3:16.
Antchito Anzake a Mulungu
9. Kodi Akristu oyambirira anazindikira kuti anali ndi mwayi ndiponso udindo wotani?
9 Akristu oyambirira sananene kuti zimene anali kuchitazo anazichita ndi mphamvu yawo. Iwo anali kudziwa kuti ntchito yawo ya utumiki inatheka chifukwa cha “mphamvu ya Mzimu Woyera.” (Aroma 15:13, 19) Yehova ndiye amene anakulitsa zonse mwauzimu. Komanso, Akristu amenewa anadziwa kuti anali ndi mwayi ndi udindo wokhala “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akorinto 3:6-9) N’chifukwa chake iwo, potsatira langizo la Yesu, anachita khama pantchito imene anapatsidwayo.—Luka 13:24.
10. Kodi Akristu ena oyambirira anachita zotani kuti apereke umboni kwa anthu a mitundu yonse?
10 Paulo, pokhala “mtumwi wa anthu amitundu,” anayenda maulendo ataliatali pamtunda ndi nyanja ndipo anakhazikitsa mipingo yambiri m’chigawo cha Roma cha Asiya ndi Girisi. (Aroma 11:13) Anapitanso ku Roma ndipo mwina mpaka anakafika ku Spain. Pamene Paulo anali kuchita zimenezi, mtumwi Petro, amene anali ndi udindo wolalikira ‘Uthenga Wabwino kwa amdulidwe,’ anapita kum’mawa ku Babulo, kumene kunali Ayuda ambiri. (Agalatiya 2:7-9; 1 Petro 5:13) Ena mwa anthu ambiri amene analimbikira ntchito ya Ambuye anali akazi monga Trufena ndi Trufosa. Mkazi wina, dzina lake Persida, akuti ‘anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.’—Aroma 16:12.
11. Kodi Yehova anawadalitsa bwanji ophunzira chifukwa cha khama lawo?
11 Anthu amenewa Yehova anawadalitsa kwambiri limodzi ndi antchito ena achangu chifukwa cha khama lawo. Patadutsa zaka zosakwana 30 kuchokera pamene Yesu analosera zoti umboni udzaperekedwa kwa anthu a mitundu yonse, Paulo analemba kuti “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo” chinali chitalalikiridwa “Uthenga Wabwino.” (Akolose 1:23) Kodi chimaliziro chinafika? Tingatero kuti chinafika. Chinafika pa dongosolo la zinthu la Chiyuda m’chaka cha 70 C.E. pamene magulu a nkhondo a Roma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake. Ngakhale zinatero, Yehova anafuna kuti pachitike ntchito yaikulu ya umboni asanawononge dongosolo lonse la zinthu la Satana.
Umboni wa Masiku Ano
12. Kodi Ophunzira Baibulo oyambirira analimva bwanji lamulo la kulalikira?
12 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kulambira koyera kunayambiranso patadutsa nthawi yaitali imene mpatuko wa zipembedzo unali wofala. Ophunzira Baibulo, limene linali dzina la Mboni za Yehova nthawi imeneyo, analimvetsa bwinobwino lamulo la kupanga ophunzira padziko lonse lapansi. (Mateyu 28:19, 20) Pofika chaka cha 1914, panali anthu pafupifupi 5,100 amene anali kuchita ntchito yolalikira mwachangu, ndipo uthenga wabwino unali utafika m’mayiko 68. Komabe, Ophunzira Baibulo oyambirirawo sanalimvetse tanthauzo lonse la lemba la Mateyu 24:14. Kumapeto kwa zaka za m’ma 1800, mabungwe oona za Baibulo anali atamasulira Baibulo, buku limene muli uthenga wabwino, m’zinenero zambiri ndi kulifalitsa padziko lonse. Ndiye kwa zaka zambiri, Ophunzira Baibulo anaganiza kuti umboni kwa anthu a mitundu unali utaperekedwa kale.
13, 14. Kodi ndi mfundo yomveka iti yokhudza chifuniro cha Mulungu ndi cholinga chake imene inafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya mu 1928?
13 Pang’ono ndi pang’ono, Yehova anathandiza anthu ake kumvetsa chifuniro chake ndi cholinga chake. (Miyambo 4:18) Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya December 1, 1928, inati: “Kodi tingati kufalitsidwa kwa Baibulo kunakwaniritsa ntchito yolalikira uthenga wa ufumu imene inaloseredwa? Ayi ndithu! Ngakhale kuti Baibulo lafalitsidwa kwambiri, kagulu kochepa ka Mulungu ka mboni zake padziko lapansi kakufunikabe kusindikiza mabuku ofotokoza [cholinga] cha Mulungu ndi kupita kunyumba za anthu amene ali ndi Mabaibulo. Apo ayi, anthu sangadziwe kuti boma la Mesiya linakhazikitsidwa m’nthawi yathu ino.”
14 Nsanja ya Olonda imeneyo inapitiriza kunena kuti: “Mu 1920, . . . Ophunzira Baibulo anamvetsa molondola ulosi umene Ambuye wathu ananena pa Mateyu 24:14. Nthawi imeneyo anazindikira kuti ‘uthenga uwu wabwino’ umene unayenera kulalikidwa padziko lonse kuti ukhale umboni kwa anthu osakhala Ayuda kapena anthu a mitundu yonse, si uthenga wabwino wonena za ufumu umene unali kubwera m’tsogolo koma uthenga wabwino wonena kuti Mfumu Mesiya wayamba kulamulira dziko.”
15. Kodi ntchito yopereka umboni yakula kufika pati chiyambire zaka za m’ma 1920?
15 “Kagulu kochepa ka mboni” ka m’ma 1920 kameneko sikanapitirize kukhala kochepa. M’tsogolo mwake, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” linadziwika ndipo linayamba kusonkhanitsidwa. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Lero, pali alaliki a uthenga wabwino okwanira 6,613,829 m’mayiko 235. Ulosi umenewu wakwaniritsidwa modabwitsa kwambiri. Sizinachitikepo kuti “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” n’kulalikidwa mpaka pamene wafikapa. Ndipo sizinachitikepo kuti padziko lapansi n’kukhala ndi atumiki a Yehova okhulupirika ambiri ngati mmene zilili panopa.
16. Kodi tinachita zotani m’chaka chautumiki chathachi? (Onani tchati pamasamba 27 mpaka 30.)
16 M’chaka chautumiki cha 2005, khamu limeneli la Mboni linagwira ntchito molimbika. Linathera maola oposa wani biliyoni polalikira uthenga wabwino m’mayiko 235. Linapanga maulendo obwereza mamiliyoni ambiri, ndipo linachititsa maphunziro a Baibulo mamiliyoni. Mboni za Yehova n’zimene zachita ntchito imeneyi mwa kufuna kwawo. Zachita zimenezi mwa kupatula nthawi ndi kupereka chuma chawo kuti zithe kuuza ena za Mawu a Mulungu. (Mateyu 10:8) Ndipo Yehova akupitiriza kuthandiza atumiki ake kuchita chifuniro chake kudzera mwa mzimu wake woyera wamphamvu.—Zekariya 4:6.
Kuchita Khama Kuti Umboni Uperekedwe
17. Kodi anthu a Yehova akulabadira motani mawu a Yesu okhudza kulalikira uthenga wabwino?
17 Ngakhale kuti padutsa zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene Yesu ananena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa, changu cha anthu a Mulungu pantchitoyi sichinachepe. Tikudziwa kuti tikamapirira pochita zabwino, timaonetsa makhalidwe a Yehova monga chikondi, chifundo, ndi kuleza mtima. Mofanana ndi iye, sitikufuna kuti ena awonongeke koma tikufuna kuti anthu alape nayanjanitsidwenso ndi Yehova. (2 Akorinto 5:18-20; 2 Petro 3:9) Chifukwa chodzazidwa ndi mzimu wa Mulungu, Mboni za Yehova zikupitiriza kulalikira mwachangu uthenga wabwino mpaka kumalekezero a dziko lapansi. (Aroma 12:11) Mapeto ake, anthu kulikonse akulandira choonadi ndi kutsatira malangizo a Yehova achikondi. Nazi zitsanzo zina.
18, 19. Tafotokozani nkhani za amene analabadira uthenga wabwino.
18 Charles anali mlimi kumadzulo kwa dziko la Kenya. Mu 1998 anagulitsa fodya wake wa makilogalamu oposa 8,000 ndipo anam’patsa setifiketi imene inati iye ndiye Mlimi Wodziwa Kwambiri Kulima Fodya. Nthawi imeneyo, anayamba kuphunzira Baibulo. Sipanapite nthawi ndipo anazindikira kuti munthu amene amalima fodya amaphwanya lamulo la Yesu lakuti munthu azikonda mnansi wake. (Mateyu 22:39) Atadziwa chilungamo chakuti ‘mlimi wodziwa kwambiri kulima fodya’ ndi ‘munthu amene amadziwa kwambiri kupha anthu,’ Charles anapopera mankhwala m’munda wake n’kupha fodya yense. Anapita patsogolo mpaka anadzipereka ndi kubatizidwa ndipo tikunena pano ndi mpainiya wokhazikika komanso mtumiki wothandiza.
19 Sitikukayika kuti Yehova, kudzera mu umboni umene ukuperekedwa padziko lonse, akugwedeza amitundu ndipo zinthu zofunika, kutanthauza anthu, zikufika. (Hagai 2:7) Pedro, amene amakhala ku Portugal, anapita ku seminale ali ndi zaka 13. Chimene anali kufuna ndi kukhala mmishonale kuti aziphunzitsa anthu Baibulo. Komabe atakhala kuseminale nthawi yochepa, anasiya chifukwa chakuti m’kalasi lake sanali kuphunzira Baibulo kawirikawiri. Patapita zaka zisanu ndi chimodzi, anayamba kuphunzira saikoloje payunivesite inayake ku Lisbon. Anali kukhala ndi amayi ake aang’ono a Mboni za Yehova, ndipo iwo anam’limbikitsa kuphunzira Baibulo. Nthawi imeneyo, Pedro anali kukayikira ngati kunja kuno kuli Mulungu, ndipo sanadziwe kuti kaya ayambe kuphunzira Baibulo kapena ayi. Anacheza ndi mphunzitsi wake wa saikoloje za vuto lakelo. Mphunzitsiyo ananena kuti saikoloje imati anthu amene satha kuganiza zoyenera kuchita amakhala ndi chizolowezi chochita zinthu zomwe amadzipweteka nazo. Atamva zimenezo, Pedro anasankha kuphunzira Baibulo. Anabatizidwa posachedwapa ndipo tikunena pano ali ndi maphunziro ake a Baibulo.
20. N’chifukwa chiyani tikusangalala kuti umboni ukuperekedwa kwa anthu a mitundu m’madera ochuluka?
20 Mpaka pano sitikudziwa kuti umboni udzaperekedwa kwa anthu a mitundu kufika pati, ndipo sitikudziwa tsiku ndi nthawi pamene chimaliziro chidzafike. Koma tikudziwa kuti chimalizirocho chifika posachedwapa. Tikusangalala kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino m’madera ochuluka yangokhala chimodzi mwa zizindikiro zambiri zosonyeza kuti nthawi yayandikira pamene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira m’malo mwa maboma a anthu. (Danieli 2:44) Chaka ndi chaka, anthu mamiliyoni akupatsidwa mpata wolabadira uthenga wabwino, ndipo zimenezi zimalemekeza Yehova Mulungu wathu. Tiyeni tisasiye kukhala okhulupirika. Ndipo tiyeni pamodzi ndi abale athu padziko lonse titanganidwe ndi ntchito yopereka umboni kwa anthu a mitundu yonse. Tikatero, tidzadzipulumutsa ife eni ndi iwo akutimvera.—1 Timoteo 4:16.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani ulosi wa pa Mateyu 24:14 uli wapadera kwambiri?
• Kodi Akristu oyambirira anachita zotani kuti alalikire, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
• Kodi zinatani kuti Ophunzira Baibulo adziwe kuti m’pofunika kupereka umboni kwa anthu a mitundu yonse?
• Poona ntchito imene anthu a Yehova anachita chaka chautumiki chathachi, n’chiyani chakusangalatsani?
[Tchati pamasamba 27-30]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2005 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Mapu/Zithunzi patsamba 25]
Paulo anayenda maulendo ataliatali pamtunda ndi nyanja kuti akalalikire uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 24]
Yehova anauza Petro kuti akapereke umboni kwa Korneliyo ndi banja lake