Kodi Malemba Amanenanji za “Umulungu wa Kristu”?
YESU KRISTU wakhala ndi chiyambukiro chachikulu chachipembedzo pa anthu. Ziri choncho chifukwa chakuti anthu mamiliyoni ambiri amadzinenera kukhala otsatira ake. Komabe, sionse amene amavomereza za amene iye ali.
Ena amene amati amalandira ziphunzitso za Yesu amamuwona kukhala Mwana wa Mulungu, osati monga Mlengi weniweniyo. Ena amakhulupirira “umulungu wa Kristu” namalingalira kuti iye alidi Mulungu. Iwo amakhulupirira kuti Yesu anakhalako nthaŵi zonse ndipo anali woposa munthu pamene anali padziko lapansi. Kodi iwo ngolondola m’nkhaniyi? Kodi Malemba amanenanji?
Kukhalako kwa Yesu Asanakhale Munthu
Yesu anachitira umboni wakuti anakhalako asanakhale munthu. Iye anati: ‘Kulibe munthu anakwera kumwamba, koma iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.’ (Yohane 3:13) Yesu ananenanso kuti: ‘Mkate wamoyo wotsika kumwamba ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.’—Yohane 6:51.
Chenicheni chakuti Yesu anali wamoyo asanadze kudziko lapansi chikuwonekera m’mawu ake aŵa: “Asanayambe kukhala Abrahamu ndipo ine ndiripo.” (Yohane 8:58) Abrahamu anakhala ndi moyo kuyambira 2018 mpaka 1843 B.C.E., pamene kuli kwakuti moyo waumunthu wa Yesu unayambira mu 2 B.C.E. mpaka 33 C.E. Imfa yake iri pafupi, Yesu anapemphera kuti: ‘Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.’—Yohane 17:5.
Otsatira a Yesu anapereka umboni wofanana. Mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu [anali mulungu, NW]. Zonse zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa. . . . Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.’ (Yohane 1:1, 3, 14) Inde, “Mawu anasandulika thupi” kukhala munthu Yesu Kristu.
Akumaloza kukukhalako kwa Yesu asanakhale munthu, mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.’ (Afilipi 2:5-7) Paulo anatcha Yesu ‘wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse.’—Akolose 1:13-16.
Sanali Waumulungu pa Dziko Lapansi
Malemba amamveketsa bwino lomwe chenicheni chakuti Yesu analidi munthu weniweni kuchokera pakubadwa kwake mpaka imfa yake. Yohane sananene kuti Mawuwo anangovekedwa thupi. Iye “anasandulika thupi” ndipo sanali thupi mbali imodzi ndi Mulungu mbali inayo. Ngati Yesu anali munthu ndi waumulungu panthaŵi imodzimodziyo, sikukananenedwa kuti ‘adamchepsa pang’ono ndi angelo.’—Ahebri 2:9; Salmo 8:4, 5.
Ngati Yesu anali ponse paŵiri Mulungu ndi munthu pamene anali padziko lapansi, kodi nchifukwa ninji anapemphera mobwerezabwereza kwa Yehova? Paulo analemba kuti: ‘Ameneyo, m’masiku a thupi lake [Kristu, NW] anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu.’—Ahebri 5:7.
Mfundo yakuti Yesu sanali mzimu mbali imodzi pamene anali padziko lapansi ikutsimikiziridwa ndi mawu a Petro akuti Kristu ‘anaphedwatu m’thupi, koma anapatsidwa moyo mumzimu.’ (1 Petro 3:18) Chifukwa chakuti anali munthu wathunthu Yesu anavutika monga mmene anthu opanda ungwiro amavutikira ndipo motero anatha kukhala mkulu wa ansembe wachifundo. Paulo analemba kuti: “Pakuti tiri naye monga mkulu wa ansembe, osati munthu amene sangachite chisoni ndi zofooka zathu, koma uyo amene wayesedwa m’mbali zonse mofanana ndi ife, koma wopanda tchimo.”—Ahebri 4:15, NW.
Pokhala ‘Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi,’ Yesu “anapereka dipo lolinganira kwa onse.” (Yohane 1:29; 1 Timoteo 2:6, NW) Mwanjirayo, Yesu anagula cholingana ndendende ndi chimene Adamu anataya—moyo waumunthu wamuyaya, ndi wangwiro. Popeza kuti chiweruzo cholungama cha Mulungu chinafuna ‘moyo kulipa moyo,’ Yesu anayenera kukhala mmene Adamu analiri poyambirira—munthu wangwiro, osati Mulungu waumunthu.—Deuteronomo 19:21; 1 Akorinto 15:22.
Musamakhulupirira Zoposa Zimene Malemba Abaibulo Amatanthauza
Amene amanena kuti Yesu anali Mulungu waumunthu amagwiritsira ntchito malemba osiyanasiyana poyesa kutsimikizira kuti iye ali chiŵalo cha Utatu wa Chikristu Chadziko, wolingana ndi Mulungu m’mikhalidwe, mphamvu, ulemerero ndi utali wa moyo. Koma pamene tiwapenda mosamalitsa malemba ameneŵa, timapeza kuti ochirikiza “umulungu wa Kristu” amawona mavesi ameneŵa kukhala akunena zoposa zimene amanenadi.
Ena amanena kuti malemba Abaibulo m’mene Mulungu amagwiritsira ntchito mloŵa mmalo wa dzina “ife” amapangitsa Yesu (Mawuwo) asanakhale munthu kukhala wolingana ndi Yehova. Koma kugwiritsiridwa ntchito kwa mloŵa mmalo wa dzinayu sikumatanthauza kuti Mulungu anali kulankhula kwa wina wolingana naye. Kwenikweni kumapereka lingaliro lakuti pa zolengedwa zakumwamba, chimodzi chiri pamalo okwezedwa ndi Mulungu. Kwenikweni, Yesu asanakhale munthu anali tsamwali wokondedwa wa Mulungu, Mmisiri, ndi Womlankhulira.—Genesis 1:26; 11:7; Miyambo 8:30, 31; Yohane 1:3.
Zochitika zokhudza ubatizo wa Yesu sizimapereka lingaliro lakuti Mulungu, Kristu, ndi mzimu woyera ali olingana. Monga munthu, Yesu anabatizidwa kuphiphiritsira kudzipereka kwake kwa Atate ŵake wakumwamba. Pachochitika chimenecho ‘miyamba inamtsegukira,’ ndipo mzimu wa Mulungu unatsikira pa Yesu monga nkhunda. Ndiponso, ‘akuchokera kumiyamba,’ mawu a Yehova anamveka akuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.’—Mateyu 3:13-17.
Choncho pamenepo, kodi Yesu anatanthauzanji pamene anauza otsatira ake kubatiza ophunzira ‘m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera’? (Mateyu 28:19, 20) Yesu sanatanthauze kapena kunena kuti iye, Atate ŵake, ndi mzimu woyera anali olingana. Mmalomwake, amene abatizidwa amazindikira Yehova monga Mpatsi Wamoyo ndi Mulungu Wamphamvuyonse, kwa amene iwo amapereka moyo wawo. Amavomereza Yesu monga Mesiya ndi uyo mwa amene Mulungu anaperekera dipo mmalo mwa anthu okhulupirira. Ndipo amadziŵa kuti mzimu woyera ndimphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, imene ayenera kuigonjera. Komabe, opita kuubatizowo sayenera kuwona Yehova, Yesu, ndi mzimu woyera monga mulungu Wautatu.
Koma kodi zozizwitsa za Yesu sizimatsimikizira kuti iye anali Mulungu waumunthu? Ayi, pakuti Mose, Eliya, Elisa, ndi atumwiwo Petro ndi Paulo, ndi ena anachita zozizwitsa popanda kukhala Milungu yaumunthu. (Eksodo 14:15-31; 1 Mafumu 18:18-40; 2 Mafumu 4:17-37; Machitidwe 9:36-42; 19:11, 12) Mofanana nawo, Yesu anali munthu amene anachita zozizwitsa ndi mphamvu zoperekedwa ndi Mulungu.—Luka 11:14-19.
Kupyolera muulosi Yesaya anatchula Yesu Mesiyayo monga “Mulungu wamphamvu.” (Yesaya 9:6) Pa Yesaya 10:21, mneneri mmodzimodziyo analankhula za Yehova kukhala “Mulungu wamphamvu.” Ena amayesa kugwiritsira ntchito kufanana kwa mawuŵa kutsimikizira kuti Yesu ndiye Mulungu. Koma tifunikira kusamala kuti tisakhulupirire zoposa zimene mavesiŵa amanena. Liwu Lachihebri lomasuliridwa “Mulungu wamphamvu” silimasonya kwa Yehova yekha monga limachitira liwulo “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Kunena zowona, pali kusiyana pakati pa kukhala wamphamvu ndi kukhala wamphamvuyonse, popanda wamkulu.
Malinga ndi Yesaya 43:10, Yehova anati: “Ndisanakhale ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.” Koma mawuwo samatsimikizira kuti Yesu ndiye Mulungu. Mfundo njakuti panalibe amene anatsogola kwa Yehova, kuti panalibe mulungu amene anakhalako iye asanakhale, pakuti ngwamuyaya. Sipadzakhala mulungu pambuyo pa Yehova chifukwa iye adzakhalakobe ndipo sadzakhala ndi womloŵa mmalo popeza ali Mfumu Yaikulu. Chikhalirechobe, Yehova anapanganso ena amene iye mwiniwake anawatcha milungu, monga momwe Malemba amasonyezera ponena za anthu ena kuti: “Ndinati ine, Inu ndinu milungu, ndi ana a Wam’mwambamwamba nonsenu. Komatu mudzafa monga anthu, ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.” (Salmo 82:6, 7) Mofananamo, Mawuwo anali mulungu wolengedwa ndi Yehova, koma zimenezo sizinampange Yesu kukhala wolingana ndi Mulungu Wamphamvuyonse panthaŵi iriyonse.
Malo Enieni a Yesu
Amene amanena kuti Mulungu anakhala munthu monga Mulungu waumunthu ayenera kudziŵa kuti Baibulo silimapereka lingaliro lirilonse lakuti Yesu mwiniyo anadziwona motero. Mmalomwake, limasonyeza mosasintha kuti Yesu nthaŵi zonse ngwochepa kwa Atate ŵake. Pamene anali padziko lapansi, Yesu sanadzinenere kukhala wina aliyense koma Mwana wa Mulungu. Ndiponso, Kristu anati: ‘Atate ali wamkulu ndi ine.’—Yohane 14:28.
Paulo anasiyanitsa Yehova ndi Yesu mwakunena kuti: ‘Koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa iye, ndi ife kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.’ (1 Akorinto 8:6) Paulo anatinso: “Koma inu ndinu a Kristu; ndi Kristu ndiye wa Mulungu.” (1 Akorinto 3:23) Ndithudi, monga momwe Akristu aliri a Mbuye wawo, Yesu Kristu, chotero iye ali wa Mutu wake, Yehova Mulungu.
Akumatchula mfundo yofanana, Paulo analemba kuti: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Unansi umenewu pakati pa Mulungu ndi Kristu udzapitirizabe, pakuti pambuyo pa Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Yesu, iye “adzapereka ufumu kwa Mulungu ndi Atate” ndipo “Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”—1 Akorinto 15:24, 28; Chivumbulutso 20:6.
Kupenda Malemba Ena
Ponena za kubadwa kwa Yesu, Mateyu analemba kuti: ‘Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi [Yehova, NW] mwa mneneri [pa Yesaya 7:14], ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.’ (Mateyu 1:22, 23) Yesu sanatchedwe ndi dzina laumwini lakuti Emanueli, koma ntchito yake monga munthu inakwaniritsa tanthauzo lake. Kukhalapo kwa Yesu padziko lapansi monga Mbewu Yaumesiya ndi Woloŵa mpando wachifumu wa Davide kunatsimikizira olambira a Yehova kuti Mulungu anali nawo, kumbali yawo, kumawachirikiza m’zochita zawo.—Genesis 28:15; Eksodo 3:11, 12; Yoswa 1:5, 9; Salmo 46:5-7; Yeremiya 1:19.
Polankhula kwa Yesu woukitsidwayo, mtumwi Tomasi anadzuma kuti: “Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.” (Yohane 20:28) Cholembedwachi ndi zina ‘zinalembedwa kuti [ife] tikhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu.’ Ndipo Tomasi sanali kutsutsa Yesu, amene anatumiza mawu kwa ophunzira ake kuti: “Ndikwera kunka kwa . . . Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17, 30, 31) Chotero Tomasi sanalingalire kuti Yesu anali Mulungu Wamphamvuyonse. Tomasi ayenera kuti anatcha Yesu “Mulungu wanga” m’lingaliro lakuti Kristu anali “mulungu,” koma osati ‘Mulungu wowona yekha.’ (Yohane 1:1; 17:1-3) Kapena mwakunena kuti “Mulungu wanga,” Tomasi angakhale anazindikira Yesu monga Wolankhulira wa Mulungu ndi Womuimira, monga momwe ena anatchera mthenga waungelo monga ngati anali Yehova.—Yerekezerani ndi Genesis 18:1-5, 22-33; 31:11-13; 32:24-30; Oweruza 2:1-5; 6:11-15; 13:20-22.
Pamenepa, malinga ndi Baibulo, Yesu anakhalako monga Mawu asanakhale munthu. Pamene anali padziko lapansi, sanali Mulungu waumunthu. Anali munthu weniweni, ngakhale kuti anali wangwiro, monga momwe Adamu analiri poyambirira. Chiyambire chiukiriro cha Yesu, iye wakhala mzimu wosakhoza kufa wokwezedwa koma wamng’ono kwa Mulungu nthaŵi zonse. Chifukwa chake, mowonekera bwino, Malemba samachirikiza lingaliro la “umulungu wa Kristu.”
[Bokosi patsamba 23]
Kodi Angelo Amamlambira Yesu?
MATEMBENUZIDWE ena a Ahebri 1:6 amati: “Angelo onse a Mulungu amlambire [Yesu].” (King James Version; The Jerusalem Bible) Mwachiwonekere mtumwi Paulo anagwira mawu Septuagint, imene imati pa Salmo 97:7: “Mlambireni [Mulungu] angelo Ake nonsenu.”—C. Thomson.
Liwu Lachigiriki lakuti pro·sky·neʹo, lomasuliridwa “kulambira” pa Ahebri 1:6, lagwiritsiridwa ntchito pa Salmo 97:7 mu Septuagint mmalo mwa liwu Lachihebri lakuti, sha·chahʹ, lotanthauza “kugwada.” Kameneka kangakhale kachitidwe kovomerezeka ka ulemu kwa anthu. (Genesis 23:7; 1 Samueli 24:8; 2 Mafumu 2:15) Kapena kangasonyeze kulambiridwa kwa Mulungu wowona kapena koperekedwa molakwa kwa milungu yonama.—Eksodo 23:24; 24:1; 34:14; Deuteronomo 8:19.
Kaŵirikaŵiri pro·sky·neʹo woperekedwa kwa Yesu amalingana ndi kulamba koperekedwa kwa mafumu ndi ena. (Yerekezerani ndi Mateyu 2:2, 8; 8:2; 9:18; 15:25; 20:20 ndi 1 Samueli 25:23, 24; 2 Samueli 14:4-7; 1 Mafumu 1:16; 2 Mafumu 4:36, 37.) Kaŵirikaŵiri nkwachiwonekere kuti kulamba kumaperekedwa kwa Yesu osati monga Mulungu koma monga “Mwana wa Mulungu” kapena “Mwana wa munthu” Waumesiya.—Mateyu 14:32, 33; Luka 24:50-52; Yohane 9:35, 38.
Ahebri 1:6 amatchula malo a Yesu pansi pa Mulungu. (Afilipi 2:9-11) Panopa matembenuzidwe ena amamasulira pro·sky·neʹo “kuchitira . . . ulemu” (The New English Bible), “kulamba kwa” (New World Translation), kapena “kugwada pamaso pa” (An American Translation). Ngati munthu wina akonda kumasulira kwa “kulambira,” kulambira koteroko nkocheperapo, pakuti Yesu anauza Satana kuti: “[Yehova, NW] Mulungu wako udzamgwadira [mpangidwe wa pro·sky·neʹo], ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.”—Mateyu 4:8-10.
Ngakhale kuti Salmo 97:7, limene limanena za kulambira Mulungu, linagwiritsiridwa ntchito kwa Kristu pa Ahebri 1:6, Paulo anasonyeza kuti Yesu woukitsidwayo ali ‘chinyezimiro cha ulemerero [wa Mulungu], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.’ (Ahebri 1:1-3) Chotero “kulambira” kulikonse kumene angelo apatsa Mwana wa Mulungu nkocheperapo ndipo kumalunjikitsidwa kwa Yehova kupyolera mwa iye.