Ekisodo
23 “Musafalitse nkhani yabodza.+ Musamagwirizane ndi munthu woipa pokhala mboni yokonzera wina zoipa.+ 2 Musamachite zoipa pongotsatira gulu la anthu. Musamalepheretse kuti chilungamo chichitike popereka umboni wabodza chifukwa chofuna kusangalatsa anthu ambiri.* 3 Mukamaweruza mlandu wa munthu wosauka musamamukondere chifukwa choti ndi wosauka.+
4 Mukapeza ngʼombe kapena bulu wa mdani wanu atasochera, muzimubweza ndithu kwa mwiniwake.+ 5 Mukaona bulu wa munthu wodana nanu atagona pansi chifukwa cholemedwa ndi katundu, munthu wodana nanuyo musamamusiye yekha. Muzimuthandiza kumasula katunduyo.+
6 Musamapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+
7 Musamagwirizane ndi anthu amene akuneneza munthu mlandu wabodza.* Musamaphe munthu wosalakwa komanso wolungama, chifukwa woipa sindidzamuona kuti ndi wolungama.*+
8 Musamalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amene amaona bwinobwino, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+
9 Musamapondereze mlendo amene akukhala nanu. Inu mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+
10 Kwa zaka 6, muzidzala mbewu mʼminda yanu nʼkukolola mbewuzo.+ 11 Koma chaka cha 7 musamaulime, muziusiya kuti ugonere. Osauka amene ali pakati panu azidya zimene zili mʼmundamo ndipo zimene iwo asiya, nyama zakutchire zidzadya. Muzichita zimenezi ndi munda wanu wa mpesa komanso wa maolivi.
12 Muzigwira ntchito masiku 6. Koma tsiku la 7 musamagwire ntchito, kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu azipuma, komanso kuti mwana wa kapolo wanu wamkazi ndi mlendo apezenso mphamvu.+
13 Muzichita zonse zimene ndakuuzanizi mosamala,+ ndipo musatchule mayina a milungu ina. Asamveke pakamwa panu.+
14 Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 pa nthawi imene inaikidwa mʼmwezi wa Abibu*+ mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi umenewu. Ndipo palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+ 16 Komanso muzichita Chikondwerero cha Zokolola.* Muzikondwerera zipatso zoyamba kucha za mbewu zimene munadzala mʼminda yanu, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+ Muzichitanso Chikondwerero cha Kututa* kumapeto kwa chaka, mukamatuta zipatso zamʼmunda, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+ 17 Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+
18 Mukamapereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. Ndipo nsembe za mafuta zimene mwapereka pazikondwerero zanga zisamagone mpaka mʼmawa.
19 Muzibweretsa kunyumba ya Yehova Mulungu wanu zipatso zoyamba kucha zamʼminda yanu zomwe ndi zabwino kwambiri.+
Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+
20 Ndikukutumizirani mngelo patsogolo panu+ kuti azikutetezani mʼnjira komanso kukakulowetsani mʼdziko limene ndakukonzerani.+ 21 Muzimumvera ndi kuchita zimene wanena. Musamupandukire, chifukwa sadzakukhululukirani zolakwa zanu,+ popeza dzina langa lili mwa iye. 22 Koma mukamveradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanene, ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzalimbana ndi olimbana nanu. 23 Chifukwa mngelo wanga adzakutsogolerani nʼkukulowetsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi ndipo ine ndidzawawononga.+ 24 Musadzaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo musadzatengere zochita zawo.+ Mʼmalomwake, mudzawononge mafano awo komanso kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ 25 Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndidzachotsa matenda pakati panu.+ 26 Mʼdziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku a moyo wanu.*
27 Inu musanafike, ndidzawachititsa kuti azindiopa.+ Ndidzasokoneza anthu onse amene mudzakumane nawo. Ndipo ndidzachititsa kuti adani anu onse agonje nʼkuthawa.*+ 28 Inu musanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso panu.+ 29 Sindidzawathamangitsa pamaso panu mʼchaka chimodzi, kuti dzikolo lisakhale bwinja ndiponso kuti zilombo zakutchire zisachuluke nʼkukuvutitsani.+ 30 Ndidzawathamangitsa pamaso panu pangʼonopangʼono mpaka mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+
31 Dziko limene ndidzakupatsani lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita zimenezi chifukwa anthu okhala mʼdzikomo ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo inu mudzawathamangitsa pamaso panu.+ 32 Musamachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33 Asamakhale mʼdziko lanu kuti asakuchititseni kuti mundichimwire. Mukadzatumikira milungu yawo, udzakhala msampha ndithu kwa inu.”+