Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Mkristu angachitenji pamene aitanidwa kukatumikira paupo wa ajuli (bungwe logamula mlandu)?
M’maiko ena, poweruza milandu amasankha maupo ogamula mlandu otchedwa juli osankhidwa pa nzika za m’chitaganya. Kumene amachita zimenezi, Mkristu ayenera kusankha mmene angachitire pamene aitanidwa kukatumikira paupo wa ajuli. Akristu ambiri aganiza ndi chikumbumtima choyera kuti mapulinsipulo a Baibulo samaletsa kukaonekera, monga momwe anachitira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego pamene boma la Babulo linawaitana kukaonekera ku chidikha cha Dura ndi mmene Yosefe ndi Mariya anapitira ku Betelehemu atalamulidwa ndi boma la Roma. (Danieli 3:1-12; Luka 2:1-4) Ngakhale ndi choncho, pali mfundo zina zimene Akristu ayenera kuzilingalira.
Si konse kumene amagwiritsira ntchito maupo ajuli. M’maiko ena, milandu ya m’khoti yaing’ono ndi ya m’khoti yaikulu imagamulidwa ndi woweruza kapena upo wa oweruza. M’maiko ena, amagwiritsira ntchito lotchedwa lamulo la anthu, ndipo maupo a juli amakhalapo poŵeruza mlandu. Chikhalirechobe, anthu ambiri samadziŵa kwenikweni mmene maupo a juli amasankhidwira ndi zimene amachita. Choncho kukhala ndi chithunzi kungathandize kaya mupatsidwa ntchito ya ujuli kapena ayi.
Anthu a Mulungu amadziŵa kuti Yehova yekha ndiye Woweruza Wamkulu. (Yesaya 33:22) Mu Israyeli wakale, amuna achidziŵitso, olungama ndi opanda tsankho ndiwo anatumikira monga oweruza kuthandiza kuthetsa mikangano ndipo anapereka mayankho pa mafunso okhudza chilamulo. (Eksodo 18:13-22; Levitiko 19:15; Deuteronomo 21:18-21) Pamene Yesu anali padziko lapansi, milandu inali kuweruzidwa ndi Sanhedrin, khoti lalikulu la Ayuda. (Marko 15:1; Machitidwe 5:27-34) Myuda wamba sanaloledwe ngakhale kukhala pa upo woweruza milandu yaing’ono.
Maiko ena anagwiritsira ntchito maupo a juli a anthu wamba. Socrates anaweruzidwa ndi upo wa ajuli okwanira 501. Kuweruza mlandu kwa ajuli kunalikonso m’Boma la Roma, ngakhale kuti kunachotsedwa m’nthaŵi ya kulamulira kwa mafumu. Pambuyo pake, Mfumu Henry III wa England anapereka lamulo lakuti woimbidwa mlandu ayenera kuweruzidwa ndi anansi ake. Anaganiza kuti popeza kuti anansiwo anamdziŵa wamlanduyo, chiweruzo chawo chidzakhala choyenera kuposa njira zozunza munthu poyesa kuona ngati munthuyo ndi maliwongo kapena ayi. M’kupita kwa nthaŵi, upo wa ajuli unasintha ndi kukhala wa nzika zimene zimamvetsera mlandu ndi kupereka chigamulo malinga ndi umboni wopezeka. Woweruza waukatswiri anawatsogolera pamfundo zopereka umboni.
Maupo a ajuli amasiyanasiyana m’mitundu yake, chiŵerengero cha ajuli, ndi zoloŵetsedwamo kuti afike pachigamulo. Mwa chitsanzo, ku United States, upo waukulu wa ajuli wa anthu 12 mpaka 23 umanena ngati pali umboni wokwanira kuti munthu aimbidwe mlandu waukulu; sumagamula kuti ali ndi liwongo kapena ali wopanda liwongo. Mofananamo, pa upo wa juli wofufuza, ajuli amapenda umboni kuona ngati munthuyo anachita upandu.
Pamene anthu ambiri aganiza za upo wa juli, amaganiza za upo wa nzika 12 pakuweruza mlandu—kaya kukangana kwa anthu kapena mlandu wa upandu—amene amamvetsera umboni kuti agamule kuti ali ndi mlandu kapena ali wopanda mlandu. Umenewu ndi upo wa juli yaing’ono, umasiyana ndi juli yaikulu. Kaŵirikaŵiri, bwalo la milandu limatumiza zidziŵitso zokatumikira pa upo wa juli kwa anthu osankhidwa pampambo wa oyenerera kuponya voti, oyendetsa galimoto okhala ndi laisensi, kapena ena otero. Ena sangasankhidwe nkomwe, monga aja omwe anachita milandu yaikulu ndi odwala maganizo. Malinga ndi lamulo lakumaloko, ena—monga madokotala, atsogoleri achipembedzo, maloya, kapena eni mabizinesi aang’ono—angapemphe kuti asawaphatikizepo. (Ena angasiyidwe chifukwa chakuti chikumbumtima chawo sichiwalola konse kuchita ntchito yaujuli.) Komabe, boma likuyesa kusasiyapo ena kotero kuti onse azikhala ndi thayo la kutumikira pa upo wa juli, mwina mobwerezabwereza m’kupita kwa zaka.
Sikuti onse amene amaitanidwa ku ntchito yaujuli amakhalapo paupo wa juli poweruza mlandu. Mwa gulu la anthu oitanidwa kuntchito yaujuli, ena amasankhidwa amene angakhale paupo wa juli pamlandu wakutiwakuti. Ndiyeno woweruza amadziŵikitsa woimba wina mlandu ndi woimbidwa mlandu ndi maloya awo kenako nafotokoza mtundu wake wa mlanduwo. Iye ndi maloyawo amapenda mmodzi ndi mmodzi wa ajuliwo kuona amene angayenere. Iyi ndiyo nthaŵi yolankhula ngati wina chikumbumtima chake sichikumulola kutumikirapo chifukwa cha mtundu wake wa mlanduwo.
Gululo liyenera kuchepetsedwa mpaka pa chiŵerengero cha omwe afunikira kukhalapo poweruza mlanduwo. Woweruzayo amatchotsa aliyense amene angasonyeze mzimu wa kukondera chifukwa cha kufunapo kanthu kena pamlanduwo. Ndiponso, maloya a mbali iliyonse ali ndi mphamvu ya kuchotsa ajuli angapo. Aliyense amene amachotsedwa pa upo wa juli amabwerera kugulu la ajuli kukayembekeza kusankha kwina pamilandu ina. Akristu ena okhala mumkhalidwe umenewu agwiritsira ntchito nthaŵi imeneyi kuchita umboni wamwamwaŵi. Patapita masiku angapo, ntchito ya wajuli aliyense imatha, kaya anakhalapo paupo kapena ayi.
Akristu amayesa ‘kuchita za iwo eni,’ osati ‘kududukira’ nkhani za ena. (1 Atesalonika 4:11; 1 Petro 4:15) Pamene Myuda anapempha Yesu kuweruza nkhani yonena za choloŵa, iye anayankha kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugaŵira inu?” (Luka 12:13, 14) Yesu anadza kudzalengeza uthenga wabwino wa Ufumu, osati kudzaweruza milandu. (Luka 4:18, 43) Mwina yankho la Yesu linasonkhezera munthuyo kugwiritsira ntchito njira yomwe inali m’Chilamulo cha Mulungu yothetsera mikangano. (Deuteronomo 1:16, 17) Ngakhale kuti mfundo zotero nzomveka, kupita ku ntchito yaujuli nkosiyana ndi kududukira nkhani za ena. Nzofananako ndi mkhalidwe wa anzake a Danieli atatu aja. Boma la Babulo linalamula kuti akaonekere ku chidikha cha Dura, ndipo pamene iwo anatero sanaswe Chilamulo cha Mulungu. Zimene anachita pambuyo pake ndi nkhani ina, monga momwe Baibulo limasonyezera.—Danieli 3:16-18.
Atumiki a Mulungu atamasuka ku Chilamulo cha Mose, anafunikira kupita ku makhoti a boma m’maiko osiyanasiyana. Mtumwi Paulo analangiza “oyera mtima” m’Korinto kuthetsa mikangano mumpingo momwemo. Pamene anatcha oweruza a m’makhoti a boma kuti “osalungama,” Paulo sananene kuti amenewo sanayenere kuweruza nkhani za anthu. (1 Akorinto 6:1) Ananena chodzikanira m’khoti la Roma, mpaka anachita apilu mlandu wake kwa Kaisara. Sikuti makhoti a boma ali olakwa m’zonse.—Machitidwe 24:10; 25:10, 11.
Makhoti akunja ali ntchito ya “maulamuliro aakulu.” Iwo “aikidwa ndi Mulungu,” ndipo amapanga malamulo ndi kuona kuti akutsatiridwa. Paulo analemba kuti: “Ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.” Akristu ‘samatsutsana nawo olamulira’ pamene achita ntchito zalamulo zimenezo, pakuti sakufuna ‘kuwakaniza’ popeza angalandire chilango.—Aroma 13:1-4; Tito 3:1.
Poyesa kulinganiza bwino zinthu, Akristu ayenera kuona ngati angavomereze kapena kukana zofuna zina za Kaisara. Paulo anapereka uphungu wakuti: “Perekani kwa anthu onse [maulamuliro aakulu] mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Zimenezi nzomveka bwino ponena za msonkho wa ndalama. (Mateyu 22:17-21) Ngati Kaisara anena kuti nzika ziyenera kupereka nthaŵi yawo ndi nyonga kuyeretsa misewu kapena kuchita ntchito ina pakati pa ntchito za Kaisara, Mkristu aliyense ayenera kuona ngati angavomereze kapena kukana.—Mateyu 5:41.
Akristu ena aona ntchito yaujuli monga kupereka kwa Kaisara zake za Kaisara. (Luka 20:25) Ntchito ya ajuli ndiyo kumvetsera umboni ndi kupereka ganizo loona mtima pamfundo zoona kapena lamulo. Mwachitsanzo, pa upo wa juli yaikulu, ajuli amanena kaya umboniwo umafuna kuti munthuyo azengedwe mlandu kapena ayi; samagamula kuti ali ndi liwongo. Nanga bwanji pamlandu wa m’khoti yaing’ono? Pamlandu wotero, ajuli angagamule kuti alipiritsidwe kapena kubwezera. Pamlandu wa m’khoti lalikulu, amanena kaya umboniwo umafuna chigamulo cha liwongo kapena ayi. Nthaŵi zina amanena chilango chimene chiyenera kuperekedwa chopezeka m’lamulo. Ndiyeno boma limagwiritsira ntchito ulamuliro wake ‘kukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.’—1 Petro 2:14.
Bwanji ngati Mkristu aona kuti chikumbumtima chake sichikumulola kutumikira paupo wa juli ina? Baibulo silimatchula ntchito yaujuli, choncho sanganene kuti, ‘chipembedzo changa sichindilola kuchita ntchito yaujuli.’ Malinga ndi mlanduwo, iye anganene kuti chikumbumtima chake sichikumulola kutumikira pabungwe la ajuli pamlandu wakutiwakuti. Zingakhale choncho ngati mlanduwo uli wa chisembwere, kuchotsa mimba, kupha munthu mwangozi, kapena nkhani zina zimene kulingalira kwake ndi kwa chidziŵitso cha Baibulo, osati kwa lamulo la dziko. Komabe, nthaŵi zina mlanduwo sungaloŵetsemo nkhani zotero.
Mkristu wokhwima ayeneranso kulingalirapo kuti kodi adzagaŵana nawo thayo la chilango chomwe chidzaperekedwa ndi oweruza? (Yerekezerani ndi Genesis 39:17-20; 1 Timoteo 5:22.) Ngati chigamulo choperekedwa ncholakwika ndipo chilango cha imfa chiperekedwa, kodi Mkristu yemwe anali paupo wa juliyo adzagaŵana nawo liwongo? (Eksodo 22:2; Deuteronomo 21:8; 22:8; Yeremiya 2:34; Mateyu 23:35; Machitidwe 18:6) Pamene anali kumzenga mlandu Yesu, Pilato anafuna kumasuka ku “mwazi wa munthu uyu.” Ayudawo anati: “Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.”—Mateyu 27:24, 25.
Ngati Mkristu apita ku ntchito yaujuli, molamulidwa ndi boma, koma chifukwa cha chikumbumtima chake akana kutumikira pamlandu wina mosasamala kanthu za kuumiriza kwa woweruza, Mkristuyo ayenera kukhala wokonzekera kuyang’anizana ndi zotsatirapo—kaya zikhale faindi kapena kumangidwa.—1 Petro 2:19.
Choncho, Mkristu aliyense woitanidwa ku ntchito yaujuli ayenera kusankha njira imene ayenera kutsatira, malinga ndi chidziŵitso chake cha Baibulo ndi chikumbumtima chake. Akristu ena apita kuntchito zaujuli ndipo atumikira pamaupo a juli. Ena akakamizika kukana ngakhale kuti angalangidwe. Mkristu aliyense ayenera kusankha yekha zimene adzachita, ndipo ena sayenera kusuliza chigamulo chake.—Agalatiya 6:5.