Ufumu wa Mulungu Umaposa Mafumu Onse
YESU KRISTU anaphunzitsa omutsatira ake kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Pemphero limeneli, lomwe ambiri amalitcha Pemphero la Ambuye, limafotokoza cholinga cha Ufumu wa Mulungu.
Kudzera mu Ufumu umenewu, dzina la Mulungu lidzayeretsedwa. Chipongwe chonse chimene chakhala chikuchitidwa pa dzinali chifukwa cha kupanduka kwa Satana ndi anthu chidzachotsedwa. Izi n’zofunika kwambiri chifukwa chakuti anthu ndi angelo angakhale mosangalala ngati nthawi zonse akuona dzina la Mulungu kukhala loyera ndi kuvomereza mosanyinyirika za ufulu wake wolamulira.—Chivumbulutso 4:11.
Kuwonjezera pamenepa, Ufumuwu unakhazikitsidwa n’cholinga choti “kufuna [kwa Mulungu] kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” Ndiyeno, kodi chifuniro chimenecho n’chotani? N’chobwezeretsa ubwenzi, umene Adamu anataya, wa pakati pa Mulungu ndi anthu. Ufumuwu udzakwaniritsanso cholinga cha Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova, chobweretsa paradaiso padziko lapansi, momwe anthu abwino adzakhalemo kwamuyaya. Zoonadi, Ufumu wa Mulungu udzabwezeretsa m’malo mwake zinthu zimene zinasokonekera chifukwa cha tchimo loyambirira ndipo udzakwaniritsa cholinga chabwino kwambiri chomwe Mulungu ali nacho chokhudza dziko lapansili. (1 Yohane 3:8) Ndipotu, Ufumu umenewu ndiponso zinthu zomwe udzachite, ndizo uthenga waukulu wa m’Baibulo.
Umaposa Mafumu Onse M’njira Zotani?
Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni, lamphamvu kwambiri. Mneneri Danieli anatipatsako chithunzithunzi cha mphamvu za Ufumu umenewu. Iye analosera kale kwambiri, kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu [onse a anthu].” Ndiponso, mosiyana ndi maboma a anthu, omwe amakhalapo kenako n’kutha m’kupita kwanthawi, Ufumu wa Mulungu “sudzawonongeka ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Komatu si zokhazi ayi. Ufumuwu umaposa boma lililonse la anthu pa chinthu chilichonse.
Ufumu wa Mulungu uli ndi Mfumu yoposa mafumu onse.
Taonani kuti Mfumu imeneyi ndani. ‘M’maloto ndi masomphenya’ omwe Danieli anapatsidwa, iye anaona Wolamulira mu Ufumu wa Mulungu ngati “mwana wa munthu” atabwera naye pamaso pa Mulungu Wamphamvuyonse n’kupatsidwa “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu” wamuyaya. (Danieli 7:1, 13, 14) Mwana wa munthu ameneyu sangakhalenso wina koma Yesu Kristu, Mesiya. (Mateyu 16:13-17) Yehova Mulungu anaika Mwana wake, Yesu, kuti akhale Mfumu ya Ufumu Wake. Nthawi yomwe anali padziko lapansi pano, Yesu anauza Afarisi oipa kuti: “Ufumu wa Mulungu uli m’kati mwa inu,” kutanthauza kuti iyeyo, Mfumu yam’tsogolo ya Ufumuwo, anali pakati pawo.—Luka 17:21.
Kodi ndi munthu uti angafanane ndi Yesu monga Wolamulira? Yesu anasonyeza kale kuti ndi Mtsogoleri wolungama, wokhulupirika, ndiponso womvera ena chisoni. Mauthenga Abwino amasonyeza kuti ndi munthu wopanda ulesi, wachikondi ndi wachifundo kwambiri. (Mateyu 4:23; Marko 1:40, 41; 6:31-34; Luka 7:11-17) Komanso, popeza kuti tsopano Yesu anaukitsidwa n’kupita kumwamba, iye sangafe kapena kulephera kuchita zinthu zina ngati mmene zimakhalira ndi anthu.—Yesaya 9:6, 7.
Yehova anaika Yesu Kristu kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake
Yesu ndi mafumu anzake akulamulira ali pamalo apamwamba.
M’masomphenya omwe Danieli anaona m’maloto, anaonanso kuti ‘ufumu, ndi ulamuliro, . . . zinapatsidwa kwa anthu a opatulika.’ (Danieli 7:27) Yesu sakulamulira yekha. Ali ndi anthu ena omwe akulamulira naye ngati mafumu ndi kutumikira monga ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Pofotokoza za anthu amenewa, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi . . . ogulidwa kuchokera kudziko.”—Chivumbulutso 14:1-3.
Mwanawankhosayu ndi Yesu Kristu ataikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Yohane 1:29; Chivumbulutso 22:3) Phiri la Ziyoni limene latchulidwali likuimira kumwamba.a (Ahebri 12:22) Yesu ndi mafumu anzake, okwana 144,000, akulamulira kuchokera kumwamba. Awatu ndi malo apamwamba kwambiri! Popeza ali kumwamba, iwo amaona zambiri. Chifukwa chakuti likulu lake lili kumwamba, “Ufumu wa Mulungu” umatchedwanso kuti “Ufumu wa Kumwamba.” (Luka 8:10; Mateyu 13:11) Palibe chida chilichonse, ngakhale kuphulitsa zida za nyukiliya, chomwe chingaopseze ndi kuwononga boma lakumwamba limeneli. Boma limeneli ndi losagonjetseka ndipo lidzakwaniritsa cholinga chomwe Yehova analikhazikitsira.—Ahebri 12:28.
Ufumu wa Mulungu uli ndi anthu okhulupirika amene akuuimira padziko lapansi pano.
Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Lemba la Salmo 45:16 limati: ‘Udzaika . . . mafumu [“akalonga,” NW] m’dziko lonse lapansi.’ Mu ulosiwu, amene akuuzidwa kuti ‘udzaika’ ndi Mwana wa Mulungu. (Salmo 45:6, 7; Ahebri 1:7, 8) Motero, Yesu Kristu mwiniwakeyo adzaika akalonga omuimira. Sitikukayikira kuti anthu amenewa adzatsatira bwinobwino malangizo ake. Ngakhale panopa, amuna oyenerera amene ali akulu m’mipingo yachikristu amaphunzitsidwa kuti aziteteza, kutsitsimula, ndi kulimbikitsa Akristu anzawo, osati ‘kukhala ambuye awo.’—Mateyu 20:25-28; Yesaya 32:2.
Ufumuwu uli ndi anthu olungama.
Mulungu amawaona kuti ndi oongoka mtima ndiponso angwiro. (Miyambo 2:21, 22) Baibulo limatiuza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Anthu a mu Ufumuwu ndi ofatsa, kutanthauza kuti ndi ophunzitsika, odzichepetsa, ndiponso odekha. Pamoyo wawo, zinthu zofunika kwambiri ndi zinthu zauzimu. (Mateyu 5:3) Amayesetsa kuchita zabwino ndipo amatsatira malangizo a Mulungu.
Ufumu wa Mulungu umayendera malamulo apamwamba kwambiri.
Malamulo komanso mfundo zoyendetsera Ufumuwu n’zochokera kwa Yehova Mulungu mwiniwake. Timapindula ndi mfundo ndi malamulowa, osati kuponderezedwa nawo ayi. (Salmo 19:7-11) Tikunena pano, anthu ambiri ayamba kale kupindula chifukwa chotsatira zofuna za Yehova zolungama. Mwachitsanzo, kumvera malangizo a m’Baibulo opita kwa amuna, akazi, ndi ana kumatithandiza kukhala ndi mabanja abwino. (Aefeso 5:33–6:3) Tikamvera lamulo lakuti ‘tikhale achikondi,’ timakhala bwino ndi anthu ena. (Akolose 3:13, 14) Tikamatsatira mfundo za m’Malemba, sitikhala anthu aulesi ndiponso sitikhala okonda ndalama. (Miyambo 13:4; 1 Timoteo 6:9, 10) Kupewa kuledzera, chiwerewere, fodya, ndi mankhwala osokoneza ubongo kumatithandiza kukhala athanzi.—Miyambo 7:21-23; 23:29, 30; 2 Akorinto 7:1.
Ufumu wa Mulungu ndi boma lokonzedwa ndi Mulungu. Mulungu wapatsa udindo Mfumu yake, yomwe ndi Mesiya, Yesu Kristu, limodzi ndi anzake onse olamulira naye woonetsetsa kuti malamulo Ake olungama limodzi ndi mfundo Zake zabwino zikutsatiridwa. Anthu a Ufumuwu, kuphatikizapo anthu ouimira padziko lapansi pano, amasangalala kutsatira malamulo a Mulungu pamoyo wawo. Motero, anthu olamulira ndiponso olamulidwa ndi Ufumuwu amaona Mulungu kukhala wofunika kwambiri pamoyo wawo. N’chifukwa chake Ufumuwu ulidi ulamuliro wa Mulungu. Palibe chomwe chidzaulepheretse kukwaniritsa cholinga chomwe anaukhazikitsira. Komano kodi Ufumu wa Mulungu, womwe umatchedwanso kuti Ufumu wa Mesiya, unayamba liti kulamulira?
Ufumu Uyamba Kulamulira
Mfundo yodziwira nthawi yomwe Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira imapezeka m’mawu a Yesu. Iye anati: “Mapazi a anthu akunja adzapondereza [Yerusalemu, NW] kufikira kuti nthawi [zoikika, NW] za anthu akunja zakwanira.” (Luka 21:23, 24) Padziko lonse lapansi, mzinda wa Yerusalemu wokha ndiwo unkagwirizanitsidwa ndi dzina la Mulungu. (1 Mafumu 11:36; Mateyu 5:35) Mzindawu unali likulu la ufumu wa padziko lapansi wovomerezedwa ndi Mulungu ndipo Mulunguyo ankauthandiza. Mzinda umenewu unadzaponderezedwa ndi amitundu, kutanthauza kuti maboma a anthu anadzasokoneza ulamuliro wa Mulungu pa anthu ake. Kodi zimenezi zinayamba liti?
Mfumu yomaliza kukhala pampando wachifumu wa Yehova ku Yerusalemu inauzidwa kuti: “Chotsa chilemba, vula korona, . . . sudzakhalanso [wa munthu, NW] kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.” (Ezekieli 21:25-27) Mfumuyi inauzidwa kuti ivule korona, ndipo ulamuliro wa Mulungu pa anthu Ake udzasokonezedwa. Izi zinachitika m’chaka cha 607 B.C.E., Ababulo atawononga Yerusalemu. M’kati mwa “nthawi zoikika” zomwe zinatsatirapo, Mulungu sanakhale ndi boma loimira ulamuliro wake padziko lapansi pano. Koma kumapeto kwa nthawi zimenezo m’pamene Yehova anadzapereka mphamvu zolamulira kwa “mwini chiweruzo,” yemwe ndi Yesu Kristu. Kodi nthawi imeneyi inali yaitali motani?
Ulosi wina wa m’buku la m’Baibulo la Danieli umati: “Likhani mtengowo ndi kuuwononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi [wa] mkuwa, . . . mpaka zitam’pitira nthawi zisanu ndi ziwiri.” (Danieli 4:23) Malinga ndi zimene tione, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zomwe atchulazi ndi zofanana kutalika kwake ndi “nthawi zoikika za anthu akunja.”
M’mavesi ena, Baibulo limagwiritsa ntchito mitengo kuimira anthu, olamulira, ndiponso maufumu. (Salmo 1:3; Yeremiya 17:7, 8; Ezekieli, chaputala 31) Mtengo wophiphiritsawo ‘unali kuonekera mpaka malekezero a dziko lonse lapansi.’ (Danieli 4:11) Motero ulamuliro woimiridwa ndi mtengowu, womwe unadzalikhidwa n’kuikidwa mikombero, unakula ‘kufika ku malekezero a dziko lapansi,’ n’kuphatikiza ufumu wonse wa anthu. (Danieli 4:17, 20, 22) Motero, mtengowu ukuimira ulamuliro wamphamvu wa Mulungu, makamaka padziko lapansi. Ulamuliro umenewu unakhalapo ndi mphamvu kwa kanthawi, kudzera mu ufumu womwe Yehova anakhazikitsa pa mtundu wa Israyeli. Mtengo wophiphiritsawo unalikhidwa, ndipo chitsa chake chinamangidwa mikombero yachitsulo ndi mkuwa n’cholinga choti chisaphuke. Izi zinasonyeza kuti ufumu womwe Mulungu anali kugwiritsa ntchito kulamulira nawo dziko lapansi udzasiya kugwira ntchito, zomwe zinachitika m’chaka cha 607 B.C.E., koma osati kwamuyaya. Mtengowo unakhala womangidwa mikombero mpaka “nthawi zisanu ndi ziwiri” zitatha. Pamapeto pa nthawizi, Yehova anadzapereka ulamuliro kwa woyenera kulowa ufumuwo, yemwe ndi Yesu Kristu. N’zoonekeratu kuti Baibulo likamatchula za “nthawi zisanu ndi ziwiri” ndi “nthawi zoikika za anthu akunja,” limakhala likunena za nthawi imodzimodzi yomweyo.
Baibulo limatithandiza kudziwa kutalika kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri.” Limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa masiku 1,260 ndi “nthawi [nthawi imodzi], ndi zinthawi [nthawi ziwiri], ndi nusu [kapena kuti theka] la nthawi,” zomwe zonse pamodzi zimakwana “nthawi” zitatu ndi theka. (Chivumbulutso 12:6, 14) Kuwirikiza chiwerengerochi kawiri, timapeza nthawi zisanu ndi ziwiri, zimene ndi masiku 2,520.
Tikawerengetsera masiku enieni 2,520 kuchokera m’chaka cha 607 B.C.E. timapeza kuti masikuwa amatha m’chaka cha 600 B.C.E. Koma nthawi zisanu ndi ziwiri zinali nthawi yaitali kwambiri kuposa nyengo imeneyi. Masiku amenewa anali asanathe pomwe Yesu analankhula za “nthawi zoikika za anthu akunja.” Motero, nthawi zisanu ndi ziwirizi ndi nthawi zaulosi. N’chifukwa chake tiyenera kugwiritsa ntchito lamulo la m’Malemba lakuti: “Tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi.” (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Motero, nthawi zisanu ndi ziwiri zomwe anthu akunja anakhala akulamulira dziko popanda Mulungu kuwasokoneza zimakwana zaka 2,520. Tikawerengetsera zaka 2,520 kuchokera m’chaka cha 607 B.C.E. timapeza kuti zakazi zimatha m’chaka cha 1914 C.E. Ichi ndiye chaka chimene “nthawi zoikika za anthu akunja,” kapena kuti nthawi zisanu ndi ziwiri, zinatha. Izi zikutanthauza kuti Yesu Kristu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914.
“Ufumu Wanu Udze”
Popeza kuti Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa kale kumwamba, kodi tiyenera kupitiriza kuupempherera kuti udze, mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa m’pemphero lachitsanzo lija? (Mateyu 6:9, 10) Inde. Mpaka pano, kupempha zimenezi n’koyenera. Posachedwapa, dziko lapansili liyamba kulamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu.
Zimenezi zikadzachitika, anthu okhulupirika adzadalitsidwa kwambiri. Baibulo limati: “Mulungu yekha adzakhala nawo, . . . ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Nthawi imeneyo, “wokhalamo [m’dzikoli] sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Anthu omwe akukondweretsa Yehova adzakhala ndi moyo kwamuyaya. (Yohane 17:3) Poyembekezera kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa limodzi ndi maulosi enanso osangalatsa opezeka m’Baibulo, tiyeni tipitirize “kufuna Ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu].”—Mateyu 6:33, NW.
a Kale, Mfumu Davide ya Israyeli inalanda Ajebusi phiri la Ziyoni la padziko lapansi pano, n’kulisandutsa likulu la ufumu wake. (2 Samueli 5:6, 7, 9) Inasamutsanso Likasa lopatulika n’kupita nalo komweko. (2 Samueli 6:17) Popeza Likasa linkaimira kukhalapo kwa Yehova, Ziyoni ankatchedwa malo omwe Mulungu ankakhala, zomwe zinachititsa kuti malowa akhale oyenera kuimira kumwamba.—Eksodo 25:22; Levitiko 16:2; Salmo 9:11; Chivumbulutso 11:19.