Danieli
7 Mʼchaka choyamba cha ulamuliro wa Mfumu Belisazara+ ya Babulo, Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake.+ Ndiyeno analemba zimene analotazo+ ndipo anafotokoza nkhani yonseyo. 2 Iye anati:
“Mʼmasomphenya usiku, ndinaona mphepo 4 zakumwamba zikuvundula nyanja yaikulu.+ 3 Ndipo zilombo 4 zikuluzikulu+ zinatuluka mʼnyanjayo. Chilombo chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake.
4 Chilombo choyamba chinali chooneka ngati mkango+ ndipo chinali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Ndinapitiriza kuchiyangʼana mpaka pamene mapiko ake anathotholedwa. Ndiyeno anachitukula panthaka nʼkuchiimiriritsa ndi miyendo iwiri ngati munthu. Kenako anachipatsa mtima wa munthu.
5 Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi ndipo mʼkamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+
6 Kenako ndinapitiriza kuyangʼana ndipo ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku+ koma chinali ndi mapiko 4 pamsana pake ooneka ngati a mbalame. Chilombochi chinali ndi mitu 4+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro.
7 Ndinapitiriza kuona masomphenya usiku umenewo ndipo ndinaona chilombo cha nambala 4. Chilombocho chinali choopsa kwambiri, chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri ndipo chinali ndi mano akuluakulu achitsulo. Chinkadya komanso kuphwanyaphwanya chilichonse chimene chinali nacho pafupi ndipo zotsala chinkazipondaponda ndi mapazi ake.+ Chilombochi chinali chosiyana ndi zilombo zina zonse zimene ndinaona poyamba ndipo chinali ndi nyanga 10. 8 Pa nthawi imene ndimayangʼanitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaingʼono+ yamera pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaingʼonoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.*+
9 Ndinapitiriza kuyangʼana mpaka pamene mipando yachifumu inaikidwa ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pampando wake wachifumu.+ Zovala zake zinali zoyera kwambiri+ ndipo tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera. Mpando wake wachifumu unkaoneka ngati malawi a moto ndipo mawilo a mpandowo ankaoneka ngati moto umene ukuyaka.+ 10 Mtsinje wa moto unkayenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana 1 miliyoni* amene ankatumikira nthawi zonse ndi atumiki enanso 100 miliyoni* amene ankatumikira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linayamba kuzenga mlandu ndipo mabuku anatsegulidwa.
11 Pa nthawi imeneyo, ndinapitirizabe kuyangʼana chifukwa ndinkamva mawu odzitukumula* amene nyanga ija inkalankhula.+ Ndinapitiriza kuyangʼana mpaka pamene chilombocho chinaphedwa ndipo thupi lake linaponyedwa pamoto nʼkuwonongedwa. 12 Koma zilombo zinazo+ anazilanda ulamuliro, ndipo anazilola kuti zikhalebe moyo kwa kanthawi komanso nyengo yoikidwiratu.
13 Ndinapitiriza kuona masomphenya usikuwo ndipo ndinaona winawake wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo. Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri+ uja ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Wamasiku Ambiriyo. 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemu+ ndi ufumu kuti anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
15 Koma ineyo Danieli, ndinavutika kwambiri mumtima chifukwa masomphenya amene ndinaona ankandichititsa mantha.+ 16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anaimirira pamenepo kuti ndimufunse tanthauzo la zimenezi. Choncho iye anandifotokozera kumasulira kwa zinthu zimenezi. Iye anati:
17 ‘Zilombo zikuluzikulu zimenezi, zomwe zilipo 4,+ zikuimira mafumu 4 amene adzalamulire padziko lapansi.*+ 18 Koma oyera a Mulungu Wamkulu+ adzalandira ufumu+ ndipo ufumuwo udzakhala wawo+ mpaka kalekale, inde kwamuyaya.’
19 Ndiyeno ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza chilombo cha nambala 4 chija, chimene chinali chosiyana ndi zina zonse. Chilombo chimenechi chinali choopsa kwambiri. Mano ake anali achitsulo, zikhadabo zake zinali zakopa* ndipo chinkadya komanso kuphwanyaphwanya zinthu zimene zinali nacho pafupi. Zotsala chinkazipondaponda ndi mapazi ake.+ 20 Ndinkafunanso kudziwa za nyanga 10+ zimene zinali pamutu pake ndi nyanga ina imene inamera nʼkuchititsa kuti nyanga zitatu zija zigwe.+ Nyanga imeneyi inali ndi maso ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula* ndipo inkaoneka yaikulu kuposa zina zija.
21 Ndinapitirizabe kuyangʼana pamene nyangayo inkachita nkhondo ndi oyera ndipo inkapambana pankhondoyo,+ 22 mpaka pamene Wamasiku Ambiri+ anabwera ndipo anapereka chiweruzo chokomera oyera a Mulungu Wamkulu.+ Ndipo nthawi yomwe inaikidwiratu yoti oyerawo atenge ufumu inakwana.+
23 Ndiyeno iye anandiuza kuti: ‘Ponena za chilombo cha nambala 4 chimenechi, pali ufumu wa nambala 4 umene udzakhalepo padziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu ena onse ndipo udzadya dziko lonse lapansi komanso udzalipondaponda nʼkuliphwanyaphwanya.+ 24 Ponena za nyanga 10 zija, mu ufumuwo mudzatuluka mafumu 10. Pambuyo pa mafumu amenewa padzatulukanso mfumu ina imene idzakhale yosiyana ndi oyambawa ndipo idzagonjetsa mafumu atatu.+ 25 Idzalankhula mawu otsutsana ndi Mulungu Wamʼmwambamwamba+ ndipo idzapitiriza kuzunza oyera a Mulungu Wamkulu. Idzafuna kuti isinthe nthawi ndi lamulo ndipo oyerawo adzaperekedwa mʼmanja mwake kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri ndi hafu ya nthawi.*+ 26 Koma Bwalo la milandu linayamba kuzenga mlandu ndipo linachotsa ulamuliro wa mfumuyo nʼcholinga choti mfumuyo aiwonongeretu.+
27 Ufumu, ulamuliro, ndi ulemerero wa maufumu apadziko lonse lapansi zinaperekedwa kwa anthu amene ndi oyera a Mulungu Wamkulu.+ Ufumu wawo udzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo maulamuliro onse adzawatumikira ndi kuwamvera.’
28 Nkhani imeneyi yathera pamenepa. Ineyo Danieli, ndinachita mantha kwambiri moti nkhope yanga inasintha. Koma nkhaniyi ndinaisunga mumtima mwanga.”