Kutsegula Njira Yobwerera ku Paradaiso
“[Yesu] anati kwa iye: ‘Zowonadi ndikuwuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’”—LUKA 23:43, “NW.”
1, 2. (a) Kodi nchiyani chomwe “paradaiso” imatanthauza, ndipo munda wa Edene uyenera kukhala unafanana ndi chiyani? (b) Kodi ndimotani mmene liwu la Chihebri kaamba ka “munda” latembenuzidwira mu Malemba Achikristu Achigriki?
BANJA la munthu linayambira mu Paradaiso. Ponena za chilengedwe cha mwamuna, timaŵerenga m’bukhu loyamba la Malemba Oyera kuti: “Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo. Ndipo Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakum’mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.” (Genesis 2:7, 8) Dzina lakuti “Edene” limatanthauza “Chisangalalo,” ndipo chotero munda wa Edene unali paki yaikulu ya chisangalalo, yokhala ndi mbali zambiri zosiyanasiyana ndipo zokongola.
2 Liwu lakuti “paradaiso” latengedwa kuchokera ku chinenero cha Chigriki, ndipo m’chinenero chimenecho limatanthauza munda wonga paki. Liwu la Chigriki logwiritsiridwa ntchito kutembenuza nauni ya Chihebri gan, lotanthauza “munda,” liri pa·raʹdei·sos. Malemba kuchokera ku Mateyu kufikira ku Chibvumbulutso analembedwa m’chinenero cha Chigriki, ndipo liwu la Chigriki limeneli linagwiritsiridwa ntchito m’kulemba mawu a Ambuye Yesu Kristu pamene iye anali kuvutika ndi chilango cha imfa pa mtengo wozunzirapo pa Kalivali pa Nisani 14 ya chaka cha 33 C.E.
Lonjezo la Yesu la Paradaiso kwa Munthu Wochita Zoipa
3. (a) Kodi nchiyani chomwe wochita zoipa womvera chifundo anapempha Yesu? (b) Kodi pempho la wochita zoipayo limasonyeza chiyani m’chigwirizano ndi chikhulupiriro chake ponena za Yesu?
3 Pa nthaŵi imeneyo, ochita zoipa aŵiri anapachikidwa limodzi ndi Yesu. Mmodzi wa iwo anali ataleka kulankhula monyoza kwa Yesu m’njira imene wachifwamba wachiŵiri wopachikidwa ku mbali ina ya Yesu anapitirizira kuchita. Wochita zoipa womvera chifundoyo anatembenuka ndi kunena kuti: “Yesu, ndikumbukireni pamene mulowa Ufumu wanu,” mwa kutero kulongosola chikhulupiriro chakuti Yesu, ngakhale kuti anapachikidwa limodzi naye, anali m’mzera wa ufumu wa kutsogolo. (Luka 23:42; Marko 15:32) Mmene chimenecho chingakhalire chinakhudzira mtima wa Ambuye Yesu! Mpandu waubwenzi ameneyo anakhulupirira kuti Yesu Kristu anali wopanda liwongo ndipo kuti sanayenerere chilango choipitsitsa choterocho chonga kupachikidwa m’kuchititsidwa manyazi kwapoyera. (Luka 23:41) Iye anasonyeza mwa pempho lake kuti anakhulupirira kuti Yesu akawukitsidwa kuchokera kwa akufa ndipo akaloŵa mu ufumu. Wochita zoipayo anasonyezanso chikhulupiriro chakuti iyemwini akawukitsidwa ndi kuti Yesu akakhala Mmodzi yemwe akamuitana kuchoka kwa akufa ndi kumuyanja iye ndi moyo watsopano pa dziko lapansi.
4. Kodi ndimotani mmene Yesu anayankhira pempho la wochita zoipayo, chikumasonyeza chiyani?
4 Pamene Yesu ananena kwa iye kuti: “Zowonadi ndikuwuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso,” iye analoza ku chiwukiriro cha wochita zoipa womvera chifundo ameneyo. Chimenecho chiyenera kukhala chinali chitonthozo chenicheni kwa mpandu yemwe anasonyeza chikhulupiriroyo. Kuti chiwukiriro cha mwamunayo chichitike, Yesu anafunikira kuwukitsidwa choyamba. Kenaka, kusonyeza mphamvu yake yopatsidwa ndi Mulungu ya kuwukitsa, Yesu akaitana wochita zoipa ameneyu kuchoka kwa akufa pa tsiku la chiwukiriro cha dziko la mtundu wa anthu.—Luka 23:43; Yohane 5:28, 29; 1 Akorinto 15:20, 23; Ahebri 9:15.
5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene Bwanamkubwa Pontiyo Pilato analemba pamwamba pa Yesu wopachikidwa? (b) Kodi ndi m’chinenero chiti chimene Yesu mwachidziŵikire analankhula kwa wochita zoipayo?
5 Kodi Yesu anapereka lonjezo limenelo m’chinenero chiti? Zambiri zinkagwiritsidwa ntchito kumeneko pa nthaŵiyo. Ichi chikusonyezedwa ndi mawu amene Bwanamkubwa Pontiyo Pilato anapangitsa kuti alembedwe pamwamba pa mutu wa Yesu Kristu wopachikidwa, kumuzindikiritsa iye kwa oyenda m’njira onse kuti aŵerenge. Cholemberacho pa Yohane 19:19, 20 chikunena kuti: “Koma Pilato analemba lembo, naliika [pa mtengo wozunzirapo, NW]. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA. Ndipo lembo ilo analiŵerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m’Chihebri, ndi m’Chiroma, ndi m’Chihelene.”
6 Mwa kubadwa kwake mu Betelehemu kwa mayi wake namwali, Mariya, Yesu anabadwa Myuda, kapena m’Hebri. Mogwirizanamo, m’kulalikira kwake kwa zaka zitatu ndi theka m’dziko lobadwirako, iye mwachiwonekere analalikira m’chinenero cha panthaŵiyo cha Chiyuda, kapena Chihebri. Chotero, pamene iye anapanga ndemanga zotsimikizira kwa wochita zoipa womvera chifundoyo, iye mwachidziŵikire analankhula m’Chihebri. Chotero iye angakhale anagwiritsira ntchito liwu la Chihebri gan pamene anali kulozera ku Paradaiso—liwu lopezeka pa Genesis 2:8. Pamenepo, kufalitsidwa kwa Septuagint ya Chigriki kwa Malemba Opatulika kumagwiritsira ntchito liwu lakuti pa·raʹdei·sos pamene likutembenuza liwu loyambirira lakuti gan.
7. Kodi ndimotani mmene Yesu analemekezedwera pamene anawukitsidwa?
7 Yesu anawukitsidwa kwa akufa pa tsiku lachitatu lotsatira kupachikidwa kwake, kapena pa Nisani 16 ya kalenda ya Chihebri. Masiku makumi anayi pambuyo pake iye anabwerera kumwamba, mudzi wake woyambirira, kokha tsopano m’malo okwezeka kwenikweni. (Machitidwe 5:30, 31; Afilipi 2:9) Iye tsopano anavekedwa ndi kusafa kwa moyo, mkhalidwe wogawanidwa ndi Atate wake wakumwamba. Yehova Mulungu anali Wokhala ndi kusafa kwa moyo wamkulu kufikira kuwukitsidwa kwa Yesu kuchoka kwa akufa pa Sande limenelo, Nisani 16.—Aroma 6:9; 1 Timoteo 6:15, 16.
Dipo Litsegula Njira
8. Kodi nchiyani chimene chinali chifuno choyambirira cha Yehova m’chigwirizano ndi dziko lapansi, ndipo kodi nchiyani chomwe chimasonyeza kuti iye amamamatira ku chifuno chimenecho?
8 Zonsezi zinali njira m’chifuno cha Mulungu cha kukhalira ndi dziko lonse lapansi lovekedwa ndi kukongola kwa paradaiso, inde, kukhala paradaiso wa chiwunda chonse. (Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11) Pa 1 Akorinto 15:45, mtumwi Paulo akulozera kwa Yesu kukhala “Adamu wotsiriza.” Ichi chimasonyeza kuti Mulungu wasungirira ku chifuno chake choyambirira m’chigwirizano ndi dziko lapansi ndi kuti winawake adzakwaniritsa chifuno chimene Adamu woyamba analephera kuchita.
9. Kodi nchiyani chomwe Yesu anapereka kutsegula njira yobwerera ku Paradaiso?
9 Mogwirizana ndi Paulo, Yesu anapereka “dipo lolingana.” (1 Timoteo 2:6, NW) Yesu Kristu iyemwini anali atanena kuti: “Monga Mwana wa munthu sanadza kukutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Ichi chinachipangitsa kukhala chothekera kwa awo osonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu kupeza moyo wosatha.—Mateyu 20:28; Yohane 3:16.
10. (a) Kodi nchiyani chomwe Mulungu anagamulapo m’chigwirizano ndi chiŵerengero chokhala ndi polekezera cha anthu oyanjidwa? (b) Kodi ndi liti pamene kusankhidwa kwa “kagulu ka nkhosa” kunayamba, ndipo kochitidwa ndi ndani?
10 Pamene Yesu anakwera kumwamba pambuyo pa kuwukitsidwa kwake kuchokera kwa akufa, iye akakhoza kupereka ubwino wa nsembe ya dipo yake kwa Mulungu m’malo mwa banja la munthu. Ngakhale kuli tero, chinali chifuno cha Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu, kutenga mwa amitundu ya dziko lapansi “anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Mogwirizana ndi Chibvumbulutso 7:4 ndi 14:1-4, awa ayenera kufika ku chiŵerengero cha kokha anthu 144,000, “kagulu ka nkhosa,” oitanidwa ku Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Luka 12:32) Kusankhidwa kwa oyanjidwa mwapadera a Yehova Mulungu kunayamba ndi kusankhidwa kwa atumwi 12 a Yesu Kristu. (Mateyu 10:2-4; Machitidwe 1:23-26) Yesu ananena kwa ziŵalo zomwe zinali maziko a mpingo wake kuti: “Inu simunandisankha ine, koma ine ndinakusankhani inu.” (Yohane 15:16) Awa akakhoza kupititsa patsogolo ntchito ya kulengeza Paradaiso wa chiwunda chonse womadzayo pansi pa kulamulira kwa Ufumu.
Kuyandikira kwa Ufumuwo
11. Kodi ndi liti pamene Ufumu wa Umesiya unafunikira kukhazikitsidwa?
11 M’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ife lerolino tikupitiriza kupereka pemphero kwa Yehova kaamba ka Ufumu Wake kuti udze. (Mateyu 6:9, 10; Yohane 14:13, 14) Ufumu wa Umesiya unafunikira kukhazikitsidwa pamapeto pa “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu.” (Luka 21:24) Nthaŵi za Akunja zimenezo zinakwaniritsidwa pofika chaka cha 1914.a
12. Kodi nchiyani chomwe chinachitika mu 1914 m’chigwirizano ndi ulosi wa Yesu wa zinthu zozizwitsa zomwe zikazindikiritsa kukhalapo kwake kosawoneka ndi maso?
12 Chaka chimenecho chinazindikiritsidwa ndi nkhondo yoyamba ya dziko ya mu mbiri yakale ya anthu. Ichi chinali m’chigwirizano ndi ulosi wa Yesu wonena za zinthu zozizwitsa zomwe zikazindikiritsa kukhalapo kwake kosawoneka ndi maso mu mphamvu ya Ufumu pa dziko lapansi. Ophunzira ake anali atamufunsa iye funso iri: “Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” M’kuyankha Yesu ananena kuti: “Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m’malo akuti akuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba. Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimariziro.”—Mateyu 24:3, 7, 8, 14; Marko 13:10.
13. (a) Kodi ndi m’njira yotani mmene kulalikira kwa Ufumu wa Mulungu kuliri mbiri yabwino? (b) Kodi ndi kwa utali wotani mmene mapemphero kaamba ka kudza kwa Ufumu wa Mulungu akhala akuperekedwa, ndipo kodi mboni zake pa dziko lapansi sizitopa konse ndi kupereka mapemphero amenewa?
13 Mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu wa Yehova tsopano ikulalikidwa m’maiko oposa 200, ndipo kuyesayesa kukupangidwa kufutukula iyo m’magawo owonjezereka. Iridi mbiri, osati ya boma la dziko lomwe likudzalo, koma ya ufumu womwe tsopano uli m’mphamvu, uwo womwe wayamba kale kulamulira. Ufumu umenewo unakhazikitsidwa mu 1914. Iwo unayambitsa maziko kaamba ka yankho ku pemphero limene Yesu anandandalitsa zoposa zaka 1,900 zapitazo. Pemphero limenelo lakhala likuperekedwa kwa Muyambitsi wa Ufumuwo chiyambire pamene yemwe anati akhale Mfumu ya boma limenelo anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kaamba ka uwo. Chotero Mkonzi wa Ufumu umenewo wakhala akumvetsera pempho kaamba ka iwo kwa nthaŵi yaitali kwenikweni. Iye wakhala wosangalatsidwa kumva pemphero loperekedwa kwa iye ndi mboni zake pa dziko lapansi mkati mwa nthaŵi yonseyo, popeza kuti chinasonyeza kuti iwo anasungirira ku chikhulupiriro chawo m’kudza kwa Ufumu umenewo. Iwo sanatope ndi kupereka pemphero limenelo kwa “Atate wakumwamba,” ngati kuti chinakhala chinachake chothodwetsa kwa iwo.—Mateyu 6:9, 10.
14. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimawumirira m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu?
14 Pamene kuli kwakuti Mboni za Yehova zimakhulupirira ndi kulengeza kuti Ufumuwo unakhazikitsidwa m’mwamba mu 1914, iwo amawumirira m’kulalikira mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu. Iwo amachita tero chifukwa chakuti Ufumu wokhazikitsidwawo sunatengebe kulamulira kotheratu kwa dziko lapansi koma walola maufumu a dziko iri kupitirizabe kusonyeza mphamvu zawo ndi ulamuliro pa mitundu yonse ndi mafuko a mtundu wa anthu. (Aroma 13:1) Uyenera chotero kubwera m’lingaliro lokwanira, uko ndiko kuti, ku mlingo wakuti liri boma lokha lomwe lidzagonjetsa padziko lonse lapansi.—Danieli 2:44.
15. Kodi nchiyani chomwe chakhala chikuchitika chiyambire Pentekoste wa 33 C.E. chomwe chiri pa mlingo wokulira kuposa pamene mafumu a Israyeli anadzozedwa?
15 Ngakhale kuti waikidwa monga Mfumu ya Ufumu umenewo, Yesu sakulamulira yekha. Yehova Mulungu waika atsatiri 144,000 a Mwana wake wachifumu kukhala oloŵa nyumba anzake mu Ufumu Waumesiya wa Mulungu. (Danieli 7:27) Monga mmene mafumu akale a Israyeli anadzozedwa ndi mafuta oyera odzozera ndi mkulu wansembe, chotero chiyambire pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E., Yehova walola a 144,000 oloŵa nyumba anzake a Yesu Kristu kudzozedwa ndi mzimu woyera Wake, kuwabala iwo ku moyo wauzimu m’mwamba ndi “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.”—Chibvumbulutso 19:16; yerekezani ndi 1 Mafumu 1:39.
Paradaiso Yemwe Adzabwezeredwanso ndi “Adamu Wotsiriza”
16. Kodi nchiyani chomwe chinali kayang’anidwe ka Ufumu pa kupachikidwa kwa Yesu, koma nchifukwa ninji iye sanali mlengezi wa mbiri yoipa?
16 Pa kupachikidwa kwa Yesu mu 33 C.E., chinawonekera kukhala chokaikiritsa kuti pakakhala kuthekera kwakuti iye akakhala ndi ufumu nkomwe. Koma m’kulalikira kwake kwa Ufumu wa Mulungu, iye sanakhale mlengezi wa mbiri yoipa. Pa tsiku lachitatu pambuyo pa kupachikidwa kwake, Muyambitsi wa Ufumuyo anatsimikizira kuti ophunzira a Yesu sakhala akupereka mapemphero kaamba ka boma lomwe silinali lothekera. Yehova anawukitsa Yemwe anafunikira kudzamuimira Iye mu Ufumu wopemphereredwawo ndi kumuveka iye ndi kusafa kwa moyo.
17, 18. (a) Kodi nchiyani chomwe chiri kupatulika kwa kutchedwa kwa Yesu “Adamu wotsiriza”? (b) Kodi nchiyani chomwe zochitika za dziko chiyambire 1914 zimasonyeza?
17 Yesu anadziŵa kuti Mlengi wa Paradaiso yoyambirira pa dziko lapansi akaika pa iye thayo la kukonzanso Paradaiso kukhala watsopano ndi kuwona kudzazidwa ndi anthu kwa munda wa chiwunda chonse. Pa 1 Akorinto 15:45, 47, timaŵerenga kuti: “Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo. Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiŵiri ali wakumwamba.” Adamu wachiŵiri anabwera pansi pano kuchokera kumwamba ndipo ali yemwe Yehova akugwiritsira ntchito kukhazikitsanso Paradaiso pano pa dziko lapansi. Panali pa maziko amenewa pamene Ambuye Yesu ananena kwa wochita zoipa womvera chifundoyo kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Kuchokera pa kukambitsirana kumeneku chiri chowonekeranso kuti Paradaiso idzakhazikitsidwa pa dziko lapansi pansi pa Ufumu wakumwamba m’manja a Yesu Kristu wolemekezedwa, “Adamu wotsiriza.”
18 Zochitika za dziko chiyambire 1914 zimagwirizana ndi maulosi onenedwa ndi Yesu Kristu ndipo chotero kutsimikizira kuti Yesu wakhala m’mphamvu kuyambira pamenepo. Kwa zaka zoposa makumi asanu ndi aŵiri tsopano, anthu a mbadwo uno wa zana la 20 okhala ndi moyo chiyambire 1914 akumana ndi kukwaniritsidwa kwa zochitika zondandalitsidwa mu ulosi wa Yesu wopezeka pa Mateyu mutu 24. Chotero, nyengo ino ya nthaŵi ikuyandikira mapeto ake, ndi kubwezeretsedwanso kwa Paradaiso pa dziko lapansi kokhala pafupi kwenikweni.—Mateyu 24:32-35; yerekezani ndi Salmo 90:10.
Nyengo ya Dziko Latsopano Yosangalatsa Iri Patsogolo
19, 20. (a) Pamapeto pa Armagedo, kodi Yehova adzaloŵetsa okondedwa ake m’chiyani? (b) Kodi nchiyani chomwe chidzafunikira kuchitidwa mwamsanga pamapeto pa Armagedo?
19 Silidzakhala dongosolo la zinthu losungulumwa, logwetsa ulesi mu limene Yehova adzaloŵetsa okondeka ake pambuyo pa kuyeretsa ulamuliro wake wa chilengedwe chaponseponse kupyola pa kukaikira kulikonse pa nkhondo ya Armagedo. Nyengo yomwe ikudzayo kaamba ka banja la munthu pansi pa ulamuliro wabwino wa Mfumu Yaumesiya, Yesu, Mwana wa Mulungu, idzakhala yosangalatsa kwenikweni. Eya, padzakhala zochulukira chotani nanga zodzafunikira kuchitidwa za mtundu wopindulitsa! Zipsyera zirizonse ndi zonse zosiyidwa pankhope ya dziko lapansi kuchokera ku kukangana kozungulira chiwunda chonse pakati pa makamu a kumwamba a Yehova ndi mphamvu zogwetsedwa za kuipa zidzachotsedwa. Palibe chikumbutso chomwe chidzasiyidwa.
20 Koma bwanji ponena za zida zonse zankhondo zimene mitundu idzasiya kumbuyo? M’chiyang’aniro cha chisonyezero chophiphiritsira cha utali wa nthaŵi yomwe chidzatenga kuthetsa mbali zowotcheka za izo, unyinjiwo udzakhala wokulira. (Ezekieli 39:8-10) Opulumuka Armagedo angadzakhale okhoza kusinthira zida zomenyera nkhondo zotsalira zirizonse za mitundu ku zifuno zothandiza.—Yesaya 2:2-4.
21. Mofanana ndi chokumana nacho cha opulumuka Chigumula, kodi ndi mkhalidwe wotani womwe udzayang’anizana ndi opulumuka Armagedo, koma ndi kusiyana kokulira kotani?
21 Anzawo amakono odalitsidwa a Nowa ndi banja lake monga opulumuka mozizwitsa a Chigumula cha chiwunda chonse adzayang’anizana ndi mkhalidwe wa dziko lapansi wofanana ndi umene banja la Nowa linapeza. Ngakhale kuli tero, Satana Mdyerekezi ndi magulu ake a ziwanda sadzavutitsanso miyamba yosawoneka yozungulira dziko lapansi koma adzakhala atayikidwa ku kusagwira ntchito kotheratu kwa zaka mazana khumi. (Chibvumbulutso 20:1-3) Opulumuka Armagedo adzakhala ndi ntchito ya chitokoso ya kugonjetsa dziko lapansi lomwe lapyola “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” akumayang’anizana ndi chiyambukiro chirichonse chomwe ichi chidzasiya pa pulaneti limeneli.—Chibvumbulutso 16:14.
22. Kodi ndimotani mmene opulumuka Armagedo adzachitira ku chitokoso chofutukula Paradaiso pa dziko lonse lapansi?
22 Pokhala ochepera m’chiŵerengero, opulumuka amenewa a nkhondo ya Armagedo mwachibadwa angayembekezeredwe kukhala otopetsedwa pamene adzapatsidwa ntchito yokulira ya kufutukula Paradaiso pa dziko lonse. Koma m’malomwake, atasangalatsidwa mopambanitsa, iwo adzapanga chiyambi champhamvu ndi chomvera ku iyo. Iwo amazindikira mokwanira kuti dziko lapansi iri liri chopondapo mapazi chophiphiritsira cha Mulungu, ndipo mowona mtima amafuna kukhala ndi malo amenewa akubweretsedwa mu mkhalidwe wabwino kwambiri ndi wokongola woyenerera mapazi ake kukhala pa ilo.
23. Kodi ndi chirikizo lotani limene opulumuka Armagedo adzakhala nalo monga chitsimikiziro chakuti ntchito yawo ya kubwezeretsa Paradaiso idzapambana?
23 Chiri chosangalatsa ndi cholimbikitsa kudziŵa kuti iwo sadzasiyidwa okha ndi opanda chithandizo pambuyo pa kutenga ntchito yosangalatsa imeneyi m’kukwaniritsa lamulo laumulungu lonena za dziko lapansi. (Yerekezani ndi Yesaya 65:17, 21-24.) Iwo adzakhala ndi chinjirizo lokwanira, lopanda polekezera la Uyo yemwe anapanga lonjezo la kubwezeredwa kwa Paradaiso ndi yemwe ananena pa tsiku la kukwera kwake kumwamba kuti: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Iye adakali ndi mphamvu zimenezo, ndipo ali wokhoza kukwaniritsa lonjezo lake lodabwitsa kwa wochita zoipa womvera chifundo uja, monga momwe tidzawonera kuchokera m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka tsatanetsatane, onani bukhu lakuti “Let Your Kingdom Come,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 135-9. Onaninso Ezekieli 21:27.
Mafunso a Kubwereramo
◻ Kodi nchiyani chimene lonjezo la Yesu pa Kalivali limatsimikizira kaamba ka mtundu wa anthu ndi mpandu mmodzi?
◻ Kodi nchiyani chomwe chiri maziko a kutsegulira njira yobwerera ku Paradaiso?
◻ Kodi nchiyani chomwe Adamu woyamba analephera kuchita, koma kodi nchiyani chimene “Adamu wotsiriza” adzakwaniritsa?
◻ Pamapeto pa Armagedo, kodi ndi mu mtundu wotani wa dongosolo la zinthu mmene Yehova adzalowetsa okondedwa ake?
[Chithunzi patsamba 13]
Nkhani yakuti “Mapeto a Maufumu Onse mu 1914” inawonekera mu “The World Magazine” ya August 30, 1914