Kodi Mapemphero Anu ‘Amakonzedwa Ngati Chofukiza’?
“Pemphero langa liikike [“likonzedwe,” NW] ngati chofukiza pamaso panu.”—SALMO 141:2.
1, 2. Kodi kuwotcha chofukiza kunaimira chiyani?
YEHOVA MULUNGU analamula mneneri wake Mose kukonza chofukiza chopatulika kuti azichigwiritsa ntchito m’chihema cha Israyeli polambira. Mulungu anapereka malangizo akuti popanga asanganize zonunkhira zamitundu inayi. (Eksodo 30:34-38) Fungo lake linakhala lokoma zedi.
2 Pangano la Chilamulo limene Israyeli analoŵamo linalola kuwotcha chofukiza chimenechi masiku onse. (Eksodo 30:7) Kodi kugwiritsa ntchito chofukiza kunali ndi tanthauzo lapadera? Inde, pakuti wamasalmo anaimba kuti: “Pemphero langa liikike [likonzedwe] ngati chofukiza pamaso panu [Yehova Mulungu]; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.” (Salmo 141:2) M’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane akufotokoza kuti amene azungulira mpando wachifumu wakumwamba wa Mulungu ali ndi mbale zagolidi zodzala zofukiza. “Ndipo,” imatero nkhani youziridwa imeneyo, “zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.” (Chivumbulutso 5:8) Pamenepa, kuwotcha zofukiza zonunkhira bwino kunaimira mapemphero ovomerezeka operekedwa ndi atumiki a Yehova usana ndi usiku womwe.—1 Atesalonika 3:10; Ahebri 5:7.
3. Kodi chingatithandize n’chiyani ‘kukonza mapemphero athu ngati chofukiza pamaso pa Mulungu’?
3 Kuti Mulungu alandire mapemphero athu, tiyenera kupemphera kwa iye m’dzina la Yesu Kristu. (Yohane 16:23, 24) Koma kodi tingachite chiyani kuti mapemphero athu akhale abwino? Eya, kupenda zitsanzo zina za m’Malemba kudzatithandiza kukonza mapemphero athu ngati chofukiza pamaso pa Yehova.—Miyambo 15:8.
Perekani Mapemphero ndi Chikhulupiriro
4. Kodi chikhulupiriro chikugwirizana motani ndi pemphero lolandirika?
4 Kuti mapemphero athu apite kwa Mulungu ngati chofukiza chonunkhira, tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro. (Ahebri 11:6) Akulu achikristu akapeza kuti munthu wodwala mwauzimu walandira thandizo lawo la m’Malemba, “pemphero [lawo] la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo.” (Yakobo 5:15) Mapemphero operekedwa ndi chikhulupiriro amakondweretsa Atate wathu wakumwamba, ngakhalenso kuphunzira Mawu a Mulungu mwapemphero. Wamasalmo anaonetsa mtima wabwino pamene anaimba kuti: “Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda; ndipo ndidzalingalira pa malemba anu. Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.” (Salmo 119:48, 66) ‘Tikwezetu manja athu’ modzichepetsa m’pemphero ndi kusonyeza chikhulupiriro mwa kutsata malamulo a Mulungu.
5. Kodi tiyenera kuchita chiyani ikatisoŵa nzeru?
5 Tinene kuti ikutisoŵa nzeru yochitira ndi chiyeso. Mwinamwakenso tikukayikira ngati ulosi wina wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa. M’malo molola zimenezi kutikhwethemula mwauzimu, tiyeni tipempherere nzeru. (Agalatiya 5:7, 8; Yakobo 1:5-8) Zoona, sitingayembekezere Mulungu kutiyankha mwanjira yodabwitsa. Tiyenera kuonetsa kuti mapemphero athu akuchokera mumtima mwa kuchita zimene iye afuna kwa anthu ake onse. Tifunikira kuchita ntchito yolimbitsa chikhulupiriro yophunzira Malemba mothandizidwa ndi zofalitsa zoperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Yoswa 1:7, 8) Tifunikiranso kuwonjeza chidziŵitso chathu mwa kutengamo mbali m’misonkhano ya anthu a Mulungu mokhazikika.—Ahebri 10:24, 25.
6. (a) Kodi tonsefe tiyenera kuzindikira chiyani ponena za tsiku lathu ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo? (b) Kuwonjeza pa kupemphera kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, tiyenera kuchita chiyani?
6 Lerolino, Akristu ena akutsata zinthu ndi ntchito zimene zikuonetsa kuti iwo aiŵala kuti tili mkati mwenimweni mwa “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) Okhulupirira anzawo moyenerera angapemphere kuti iwo adzutse kapena kulimbitsa chikhulupiriro chawo mu umboni wa m’Malemba wakuti kukhalapo kwa Kristu kunayamba mu 1914 pamene Yehova anamuika kukhala Mfumu yakumwamba ndi kuti akulamulira pakati pa adani ake. (Salmo 110:1, 2; Mateyu 24:3) Tonsefe tiyenera kuzindikira kuti zochitika zimenezo zoloseredwa monga kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga—‘Babulo Wamkulu’—kuukira anthu a Yehova kwausatana kwa Gogi wa ku Magogi, ndiponso kulanditsidwa kwawo ndi Mulungu Wamphamvuyonse pankhondo ya Armagedo, zingachitike mwadzidzidzi ndiponso panthaŵi yochepa chabe. (Chivumbulutso 16:14, 16; 18:1-5; Ezekieli 38:18-23) Chotero tiyeni tipempherere thandizo la Mulungu kuti tikhale ogalamuka mwauzimu. Tonsefe tipemphere ndi mtima wonse kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, Ufumu wake udze, ndi kufuna kwake kuchitike padziko lapansi monga kumwamba. Inde, tipitirize kusonyeza chikhulupiriro ndi kupereka umboni wakuti mapemphero athu amachokera pansi pa mtima. (Mateyu 6:9, 10) Inde, onse okonda Yehova afunefune Ufumu choyamba ndi chilungamo chake ndipo achite zonse zotheka kuti alalikire nawo uthenga wabwino mapeto asanafike.—Mateyu 6:33; 24:14.
Tamandani ndi Kuyamika Yehova
7. Kodi n’chiyani chimene mukuchita nacho chidwi m’pemphero la Davide limene mbali yake yalembedwa pa 1 Mbiri 29:10-13?
7 Njira yofunika imene ‘tingakonzere mapemphero athu ngati chofukiza’ ndiyo kutamanda ndi kuyamika Mulungu kuchokera mumtima. Mfumu Davide anapereka pemphero lotero pamene iye ndi Aisrayeli anapereka chuma chothandizira kumanga kachisi wa Yehova. Davide anapemphera kuti: “Wolemekezedwa inu, Yehova Mulungu wa Israyeli, Atate wathu ku nthaŵi zomka muyaya. Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m’dzanja lanu. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.”—1 Mbiri 29:10-13.
8. (a) Kodi ndi mawu ati achiyamiko m’Masalmo 148 mpaka 150 amene akukhudzani mtima kwambiri? (b) Ngati ifenso tili ndi malingaliro osonyezedwa pa Salmo 27:4, kodi tidzachita chiyani?
8 Ati mawu amenewa achitamando ndi chiyamiko kukoma kwake! Mwina sitingalongosole zinthu bwino chonchi m’mapemphero athu, koma atha kukhalabe ochokera mumtima. Buku la Masalmo n’lodzala ndi mapemphero achitamando ndi chiyamiko. Mawu okoma achitamando akupezeka m’Masalmo 148 mpaka 150. Masalmo ambiri amanena za kuyamika Mulungu. “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,” anaimba Davide. “Ndidzachilondola ichi: kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’Kachisi wake.” (Salmo 27:4) Tichite mogwirizana ndi mapemphero amenewo mwa kutengamo mbali mokangalika m’ntchito zonse za makamu osonkhana a Yehova. (Salmo 26:12) Kuchita zimenezi ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kudzatipatsa zifukwa zambiri zopitira kwa Yehova ndi chitamando ndi chiyamiko chochokera mumtima.
Funani Thandizo la Yehova Modzichepetsa
9. Kodi Mfumu Asa inapemphera motani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
9 Ngati tikutumikira Yehova ndi mtima wonse monga Mboni zake, tili otsimikiza kuti iye amamva mapemphero athu opempha thandizo. (Yesaya 43:10-12) Talingalirani Mfumu Asa ya Yuda. Zaka zoyambirira 10 za ulamuliro wake wazaka 41 (977-937 B.C.E.) zinali zamtendere. Ndiyeno gulu lankhondo la Zera Mkusi la anthu zikwi chikwi chimodzi linaukira Yuda. Ngakhale kuti anali ochepa, Asa ndi anthu ake anatuluka kukakumana nawo oukirawo. Komabe, asanayambe nkhondo, Asa anapemphera ndi mtima wonse. Anazindikira kuti Yehova ndiye ali ndi mphamvu yakupulumutsa. Pochonderera thandizo, mfumuyo inati: “Titama Inu, tatulukira aunyinji awa m’dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakulakeni.” Panatsatira chilakiko chotheratu pamene Yehova anapulumutsa Yuda chifukwa cha dzina lake lalikululo. (2 Mbiri 14:1-15) Kaya Mulungu atilanditsa pa mayesero kapena kutilimbitsa kuti tiwapirire, m’posakayikitsa kuti amamva kudandaula kwathu popempha thandizo lake.
10. Pamene sitikudziŵa chochita ndi vuto linalake, kodi pemphero la Mfumu Yehosafati lingatithandize motani?
10 Ngati sitikudziŵa chochita ndi vuto linalake, tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzamva mapembedzero athu ofuna thandizo. Zimenezi zinasonyezedwa m’masiku a Mfumu Yehosafati ya Yuda, imene ulamuliro wake wazaka 25 unayamba mu 936 B.C.E. Pamene magulu ankhondo a Moabu, Amoni, ndi a kuphiri la Seiri anadza kudzaukira Yuda, Yehosafati anadandaula motere: “Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nawo aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziŵa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.” Yehova anayankha pemphero lodzichepetsa limenelo, namenyera nkhondo Yuda mwa kusokoneza adaniwo kotero kuti anaphana. Chifukwa chake, mitundu yowazungulira inagwidwa ndi mantha, ndipo m’Yuda munakhala mtendere. (2 Mbiri 20:1-30) Ikatisoŵa nzeru yofunika polimbana ndi vuto, tingapemphere monga Yehosafati kuti: ‘Sitikudziŵa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa inu, Yehova.’ Mzimu woyera ungatikumbutse mfundo za m’Malemba zofunika kuthetsera vutolo, kapenanso Mulungu angatithandize mwa njira imene ife anthu sitingaimvetse.—Aroma 8:26, 27.
11. Kodi tingaphunzirepo chiyani ponena za pemphero pa zimene Nehemiya anachita zokhudzana ndi linga la Yerusalemu?
11 Tingafunikire kulimbikira kupempherera thandizo la Mulungu. Nehemiya anasonyeza chisoni chachikulu, kulira misozi, kusala kudya, ndi kupemphera masiku ambiri m’malo mwa linga lowonongeka la Yerusalemu ndi nsautso ya nzika za Yuda. (Nehemiya 1:1-11) Ndithudi mapemphero ake anakwera kwa Mulungu ngati chofukiza chonunkhira. Tsiku lina Mfumu Aritasasta ya Perisiya inafunsa Nehemiya wachisoniyo kuti: “Ufunanji iwe?” “Pamenepo,” akutero Nehemiya, “ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.” Pemphero lachidule limenelo komanso lamumtima linayankhidwa, popeza Nehemiya analoledwa kukachita chokhumba mtima wake mwa kupita ku Yerusalemu kukamanganso linga lake lopasukalo.—Nehemiya 2:1-8.
Lolani Kuti Yesu Akuphunzitseni Kupemphera
12. Mwa mawu anuanu, kodi mwachidule mungazifotokoze motani mfundo zazikulu za m’pemphero la Yesu lachitsanzo?
12 Pa mapemphero onse olembedwa m’Malemba, lophunzitsa kwambiri ndi pemphero lachitsanzo loperekedwa ndi Yesu Kristu monga chofukiza chonunkhira. Uthenga Wabwino wa Luka umati: “Wina wa ophunzira [a Yesu] anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake. Ndipo anati kwa iwo, Mmene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze; tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.” (Luka 11:1-4; Mateyu 6:9-13) Tiyeni tilipende pemphero limeneli, limene cholinga chake sikumalilakatula koma chitsanzo chabe.
13. Kodi mungalifotokoze motani tanthauzo la mawu akuti, “Atate, Dzina lanu liyeretsedwe”?
13 “Atate, Dzina lanu liyeretsedwe.” Kuitana Yehova Atate ndi mwayi wapadera umene atumiki odzipatulira ali nawo. Monga mmene ana amathamangira kwa atate wachifundo ndi nkhaŵa iliyonse, tiyenera nthaŵi zonse kutayira nthaŵi tikupemphera kwa Mulungu mwaulemu. (Salmo 103:13, 14) Mapemphero athu ayenera kuonetsa kuti chachikulu kwa ife ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova chifukwa timalakalaka kuliona litayeretsedwa chitonzo chonse chimene chaikidwa pa ilo. Inde, tikufuna kuti dzina la Yehova lipatulidwe komanso liyeretsedwe.—Salmo 5:11; 63:3, 4; 148:12, 13; Ezekieli 38:23.
14. Kodi kumatanthauzanji kupemphera kuti, “Ufumu wanu udze”?
14 “Ufumu wanu udze.” Ufumuwo ndiwo ulamuliro wa Yehova umene amachita mwa boma lakumwamba la Mesiya limene lili m’manja mwa Mwana wake ndi “opatulika” anzake a Yesu. (Danieli 7:13, 14, 18, 27; Chivumbulutso 20:6) ‘Udzadza’ posachedwa kuwononga adani onse apadziko lapansi a uchifumu wa Mulungu, kuwachotseratu onse. (Danieli 2:44) Kenako kufuna kwa Yehova kudzachitika padziko lapansi, monganso kumwamba. (Mateyu 6:10) Zimenezo zidzazisangalatsa kwambiri zolengedwa zokhulupirika zotumikira Mfumu ya Chilengedwe Chonse!
15. Kodi kupempha Yehova kuti ‘atipatse chakudya chathu cha patsiku’ kumaonetsa chiyani?
15 “Tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.” Kupempha Yehova chakudya “cha patsiku” kumasonyeza kuti sitipempha zochulukitsa koma zosoŵa zathu za tsiku ndi tsiku zokha. Ngakhale kuti tikhulupirira kuti Mulungu adzatipatsa, timagwiranso ntchito ndi kugwiritsa ntchito njira iliyonse yoyenera imene ilipo kuti tipeze chakudya ndi zofunika zina. (2 Atesalonika 3:7-10) Komanso, tiyenera kuyamika Mgawiri wathu wakumwamba chifukwa chikondi chake, nzeru, ndi mphamvu n’zimene zimatheketsa zinthu zimenezi.—Machitidwe 14:15-17.
16. Kodi tingalandire motani chikhululukiro cha Mulungu?
16 “Mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu.” Pokhala opanda ungwiro ndi ochimwa, sititha kukwaniritsa malamulo angwiro a Yehova. Ndiye chifukwa chake tifunikira kupemphera kuti atikhululukire pamaziko a nsembe ya dipo la Yesu. Koma ngati tikufuna kuti “Wakumva pemphero” agwiritse ntchito mapindu a nsembe imeneyo pa machimo athu, tiyenera kukhala olapa ndi ofunitsitsa kulandira chilango chilichonse chimene atipatsa. (Salmo 65:2; Aroma 5:8; 6:23; Ahebri 12:4-11) Ndiponso, tingayembekeze Mulungu kutikhululukira kokha ngati ifenso “takhululukira amangawa athu,” aja amene amatilakwira.—Mateyu 6:12, 14, 15.
17. Kodi mawuwo, “Musatitengere ife kokatiyesa,” amatanthauzanji?
17 “Musatitengere ife kokatiyesa.” Baibulo nthaŵi zina limati Yehova ndiye amachititsa zinthu pamene amangozilola. (Rute 1:20, 21) Mulungu satiyesa kuti tichite tchimo. (Yakobo 1:13) Ziyeso zakuti tichite choipa zimachokera kwa Mdyerekezi, thupi lathu lauchimo, ndi dziko lino. Satana ndiye Woyesayo amene amatisonkhezera kulakwira Mulungu. (Mateyu 4:3; 1 Atesalonika 3:5) Pamene tipereka pempho lakuti, “Musatitengere ife kokatiyesa,” timapempha Mulungu kuti asatilole kulephera pamene tiyesedwa kusamvera iye. Angatithandize kuti tisagonje ndi kuti Satana, “woipayo,” asatigonjetse.—Mateyu 6:13; 1 Akorinto 10:13.
Chitani Mogwirizana ndi Mapemphero Anu
18. Kodi tingachite motani mogwirizana ndi mapemphero athu akuti tikhale ndi ukwati ndi moyo wa banja wachimwemwe?
18 Pemphero la Yesu lachitsanzo linali ndi mfundo zazikulu zokha, koma titha kupempherera nkhani iliyonse. Mwachitsanzo, tingapemphere kuti tikukhumba kukhala ndi ukwati wachimwemwe. Kuti tikhale oyera mpaka titaloŵa mu ukwati, tingapempherere kudziletsa. Komano tichite mogwirizana ndi mapemphero athu mwa kupewa mabuku ndi zosangalatsa zachiwerewere. Titsimikizenso mtima ‘kukwatira mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 7:39; Deuteronomo 7:3, 4) Titakwatira, tidzafunikira kuchitabe mogwirizana ndi mapemphero athu akuti tipeze chimwemwe mwa kugwiritsa ntchito uphungu wa Mulungu. Ndipo tikakhala ndi ana, si kokwanira kupemphera kuti adzakhale atumiki a Yehova okhulupirika. Tiyenera kuchita zonse zotheka kukhomereza choonadi cha Mulungu m’maganizo awo kupyolera m’phunziro la Baibulo ndi mwa kupezeka nawo nthaŵi zonse pamisonkhano yachikristu.—Deuteronomo 6:5-9; 31:12; Miyambo 22:6.
19. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikupempherera utumiki wathu?
19 Kodi tikupempherera dalitso mu utumiki? Pamenepo tichite mogwirizana ndi mapemphero amenewo mwa kutengamo mbali mwatanthauzo m’ntchito yolalikira Ufumu. Ngati tipempherera mipata yothandizira ena kuti apeze njira ya kumoyo wosatha, tifunikira kukhala ndi zolembapo zabwino za amene achita chidwi ndi kukonzekera kuphatikiza pa ndandanda yathu nthaŵi yochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Nanga bwanji ngati tikufuna kuyamba ntchito yolalikira yanthaŵi zonse monga mpainiya? Pamenepo tichite mogwirizana ndi mapemphero athu mwa kuwonjeza ntchito yathu yolalikira ndi mwa kupita nawo mu utumiki apainiya. Kuchita zinthu zimenezi kudzasonyeza kuti tikuchita mogwirizana ndi mapemphero athu.
20. Kodi nkhani yotsatira idzafotokoza chiyani?
20 Ngati tikutumikira Yehova mokhulupirika, tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti adzayankha mapemphero athu ogwirizana ndi chifuniro chake. (1 Yohane 5:14, 15) Inde, tapeza mfundo zopindulitsa mwa kupenda mapemphero ena olembedwa m’Baibulo. Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza zitsogozo zina za m’Malemba za aja amene akufuna ‘kukonza mapemphero awo ngati chofukiza pamaso pa Yehova.’
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro?
◻ Kodi chitamando ndi chiyamiko ziyenera kukhala ndi mbali yotani m’mapemphero athu?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani mwachidaliro tingapemphe thandizo la Yehova m’pemphero?
◻ Kodi mfundo zina zazikulu m’pemphero lachitsanzo n’zotani?
◻ Kodi tingachite motani mogwirizana ndi mapemphero athu?
[Chithunzi patsamba 12]
Monga Mfumu Yehosafati, nthaŵi zina tifunikira kupemphera kuti: ‘Sitikudziŵa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa inu, Yehova’
[Chithunzi patsamba 13]
Kodi mumapemphera mogwirizana ndi pemphero la Yesu lachitsanzo?