2 Mbiri
20 Kenako Amowabu,+ Aamoni+ ndi Aamonimu* ena anabwera kudzamenyana ndi Yehosafati. 2 Choncho anthu anapita kukauza Yehosafati kuti: “Kwabwera chigulu cha anthu kuchokera kuchigawo chakunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu ndipo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+ 3 Yehosafati atamva zimenezi anachita mantha ndipo anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.+ Choncho analengeza kuti Ayuda onse asale kudya. 4 Ndiyeno Ayudawo anasonkhana kuti afunsire kwa Yehova.+ Iwo anachokera mʼmizinda yonse ya Yuda kuti afunsire kwa Yehova.
5 Kenako Yehosafati anaimirira pamaso pa gulu la anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, mʼnyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 nʼkunena kuti:
“Inu Yehova Mulungu wa makolo athu, kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Mʼdzanja lanu muli mphamvu ndipo palibe amene angalimbane nanu.+ 7 Inu Mulungu wathu, kodi si paja munathamangitsa anthu amene ankakhala mʼdzikoli pamaso pa anthu anu Aisiraeli nʼkulipereka kwa mbadwa* za Abulahamu, bwenzi lanu, kuti likhale lawo mpaka kalekale?+ 8 Iwo anayamba kukhala mʼdzikolo ndipo anakumangirani malo opatulika a dzina lanu+ nʼkunena kuti, 9 ‘Tsoka likatigwera, kaya lupanga, chiweruzo chowawa, mliri kapena njala, tiziima patsogolo pa nyumbayi ndi pamaso panu (popeza dzina lanu lili mʼnyumbayi)+ nʼkufuulira inu kuti mutithandize pa mavuto athu, ndipo inu muzitimva nʼkutipulumutsa.’+ 10 Tsopano Aamoni, Amowabu ndi anthu akudera lamapiri la Seiri+ abwera. Inu simunalole kuti Aisiraeli alowe mʼdziko lawo pamene ankachokera ku Iguputo ndipo sanawaphe.+ 11 Tsopano akutibwezera pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene munatipatsa kuti likhale cholowa chathu.+ 12 Inu Mulungu wathu kodi simuwaweruza?+ Ifeyo tilibe mphamvu zotha kulimbana ndi gulu lalikulu limene likudzamenyana nafeli ndipo sitikudziwa chochita,+ koma maso athu ali pa inu.”+
13 Pa nthawiyi Ayuda onse anali ataimirira pamaso pa Yehova, limodzi ndi akazi awo, ana awo ngakhalenso ana awo angʼonoangʼono.
14 Kenako mzimu wa Yehova unafika pa Yahazieli yemwe anali pagulu la anthuwo. Iye anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Benaya, Benaya anali mwana wa Yeyeli, Yeyeli anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali Mlevi, mmodzi wa ana a Asafu. 15 Choncho Yahazieli anati: “Tamverani Ayuda nonsenu, anthu a ku Yerusalemu ndi inu Mfumu Yehosafati! Yehova akukuuzani kuti, ‘Musaope kapena kuchita mantha ndi gulu lalikululi chifukwa nkhondoyi si yanu, ndi ya Mulungu.+ 16 Mawa mupite kukakumana nawo. Iwo adzabwera kudzera pampata wa Zizi. Mudzawapeza kumapeto kwa chigwa musanafike kuchipululu cha Yerueli. 17 Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Aliyense angoima pamalo ake+ nʼkuona mmene Yehova angakupulumutsireni.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+
18 Nthawi yomweyo Yehosafati anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi, ndipo Ayuda onse ndi anthu a ku Yerusalemu anawerama pamaso pa Yehova kuti alambire Yehovayo. 19 Kenako Alevi omwe anali mbadwa za Kohati+ ndi za Kora anaimirira nʼkuyamba kutamanda Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mawu okweza kwambiri.+
20 Mʼmawa wa tsiku lotsatira, anthuwo ananyamuka nʼkupita kuchipululu cha Tekowa.+ Ali mʼnjira, Yehosafati anaimirira nʼkunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu! Khulupirirani Yehova Mulungu wanu kuti mukhale olimba.* Khulupirirani aneneri ake+ kuti zinthu zikuyendereni bwino.”
21 Atakambirana ndi anthuwo, iye anasankha anthu oti aziimbira+ Yehova ndiponso kumutamanda atavala zovala zokongola ndi zopatulika ndipo ankayenda patsogolo pa amuna onyamula zida. Iwo ankanena kuti: “Yamikani Yehova, chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”+
22 Anthuwo atayamba kuimba nyimbo zotamanda Mulungu mosangalala, Yehova anakonza zoti Aamoni, Amowabu ndi anthu akudera lamapiri la Seiri, omwe ankapita ku Yuda, aukiridwe mwadzidzidzi ndipo iwo anayamba kuphana okhaokha.+ 23 Aamoni ndi Amowabu anaukira anthu okhala kudera lamapiri la Seiri+ ndipo anayamba kuwapha mpaka kuwamaliza. Atatha kupha anthu a ku Seiri, iwo anaphana okhaokha.+
24 Ayuda atafika pansanja ya mlonda yamʼchipululu+ nʼkuyangʼana chigulu cha anthu chija, anangoona mitembo yokhayokha ili pansi+ popanda wopulumuka. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukatenga zinthu za adani awowo ndipo anapeza zinthu zambiri, zovala ndi zinthu zina zamtengo wapatali. Iwo anayamba kutenga zinthuzo mpaka zina zinawakanika kunyamula.+ Zinthuzo zinalipo zambiri moti anatuta kwa masiku atatu. 26 Pa tsiku la 4 anasonkhana kuchigwa cha Beraka ndipo anatamanda* Yehova kumeneko. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti chigwa cha Beraka*+ mpaka lero.
27 Kenako Ayuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu ndipo Yehosafati ankawatsogolera. Anabwerera akusangalala chifukwa Yehova anawathandiza kugonjetsa adani awo.+ 28 Choncho anafika ku Yerusalemu akuimba ndi zoimbira za zingwe,+ azeze+ ndi malipenga ndipo anapita kunyumba ya Yehova.+ 29 Maufumu onse amʼdzikolo atamva kuti Yehova wagonjetsa adani a Isiraeli, anakhala ndi mantha ochokera kwa Mulungu.+ 30 Choncho ufumu wa Yehosafati unalibe chosokoneza chilichonse, ndipo Mulungu wake anapitiriza kumupatsa mpumulo kuti adani ake onse asamamuvutitse.+
31 Yehosafati anapitiriza kulamulira ku Yuda. Iye anali ndi zaka 35 pamene ankakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili.+ 32 Yehosafati anapitiriza kuyenda mʼnjira za Asa,+ bambo ake. Sanasiye kuyenda mʼnjirazo ndipo anachita zoyenera pamaso pa Yehova.+ 33 Komabe sanachotse malo okwezeka+ ndipo anthu anali asanakonze mitima yawo kuti atsatire Mulungu wa makolo awo.+
34 Nkhani zina zokhudza Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, zikupezeka mʼzinthu zimene Yehu+ mwana wa Haneni+ analemba ndipo zinaphatikizidwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli. 35 Kenako Yehosafati mfumu ya Yuda anachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Isiraeli amene ankachita zoipa.+ 36 Choncho anayamba kugwira naye ntchito yopanga zombo zopita ku Tarisi.+ Zombozo anazipangira ku Ezioni-geberi.+ 37 Koma Eliezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa analosera zinthu zotsutsana ndi Yehosafati kuti: “Chifukwa chakuti mwachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova awononga ntchito yanu.”+ Choncho zombozo zinasweka+ ndipo sizinathenso kupita ku Tarisi.