Kodi Mukudziwa?
Kodi “woyang’anira kachisi” anali ndani, ndipo ntchito yake inali yotani?
“Woyang’anira kachisi” anali mmodzi wa atsogoleri achipembedzo chachiyuda amene analamula kuti mtumwi Petulo ndi Yohane aikidwe m’ndende chifukwa cholalikira. (Machitidwe 4:1-3) Baibulo silimanena ntchito imene woyang’anira kachisi ankagwira. Koma mabuku ena a mbiri yakale amatchula mfundo zina zochititsa chidwi pa nkhani imeneyi.
Zikuoneka kuti panthawi imene Yesu anali padziko lapansi, udindo woyang’anira kachisi unali m’manja mwa wansembe amene anali wachiwiri kwa mkulu wa ansembe. Woyang’anira kachisi ankakhazikitsa mtendere panja ndiponso mkati mwa kachisi wa ku Yerusalemu. Iye ankayang’anira zochitika zokhudza kulambira pakachisipo komanso gulu la alonda apakachisi. Oyang’anira ena omwe iye amawatsogolera ankayang’anira alonda amene ankatsegula ndiponso kutseka mageti apakachisi, m’mawa ndi madzulo. Alondawa ankaonetsetsa kuti anthu sakulowa kumalo oletsedwa komanso ankalondera chuma chapakachisipo.
Ansembe ndiponso Alevi ogwira ntchito pakachisi anali m’magulu 24 ndipo gulu lililonse linkatumikira kwa mlungu umodzi ndipo pachaka gulu lililonse linkatumikira kawiri. Zikuoneka kuti gulu lililonse linali ndi woyang’anira wake.—1 Mbiri 24:1-18.
Oyang’anira kachisi amenewa anali anthu olemekezeka. Anthuwa amatchulidwa pamodzi ndi ansembe aakulu amene anakonza chiwembu chopha Yesu komanso amene analamula anthu kuti akagwire Yesu.—Luka 22:4, 52.
Pa Mateyo 3:4 pamati Yohane Mbatizi ankadya “dzombe ndi uchi.” Kodi ndiye kuti anthu nthawi imeneyi ankakonda kudya dzombe?
Anthu ena amakayikira kuti Yohane ankadyadi dzombe ndipo amati lembali limatanthauza kuti Yohane ankadya zipatso zam’tchire, nthanga za zipatso kapena nsomba. Komabe, mawu achigiriki omwe Mateyo anagwiritsa ntchito, amatanthauza ziwala za mtundu wa dzombe. Ku Isiraeli kunkapezeka dzombe linalake limene limakonda kupezeka m’chipululu. Dzombeli limawononga kwambiri mbewu ndipo limakhala m’chigulu.—Yoweli 1:4, 7; Nahumu 3:15.
Kale, Asuri ndiponso Aitiopiya ankakonda kudya dzombe. Ndipo masiku ano, Aluya a mtundu wa Bedouin ndi Ayuda a ku Yemen amakonda kudya dzombe. Ku Isiraeli dzombe linkaonedwa kuti ndi chakudya cha anthu osauka. Akafuna kudya dzombe ankalichotsa mutu, miyendo ndi mimba ndipo ankadya chidale chake chosaphika. Koma nthawi zina ankakazinga kapena kuumitsa padzuwa. Nthawi zina ankalithira mchere kapena kuliviika muviniga kapenanso mu uchi.
Popeza Yohane ankalalikira m’chipululu, ayenera kuti ankapeza dzombe mosavuta. (Maliko 1:4) Dzombe limakhala ndi mapuloteni ambiri, choncho dzombe lodyera uchi chinali chakudya chopatsa thanzi kwambiri.
[Chithunzi patsamba 28]
Antchito a ku Suriya atanyamula dzombe ndi zipatso
[Mawu a Chithunzi]
From the book Discoveries Among the Ruins of Nineveh and Babylon (1853)