Kumbukirani Maprinsipulo Achikristu
PAMENE mwana ayamba kupezeka kusukulu, pakati pa zinthu zoyamba zimene iye amaphunzira pali kuŵerenga ndi kulemba. Mbali zokulira zimenezi zimamukonzekeretsa iye kaamba ka zinthu zopita patsogolo kwenikweni, zonga ngati maphunziro zamayanjano, sayansi, ndi zinenero. Ngati mwana alephera kutenga kugwiririra kwakuya kwa kuŵerenga ndi kulemba, mtsogolo mwake monse mwamaphunziro mumayambukiridwa moipa.
Kuphunzira mmene tingalambirire Mulungu kuli mwanjira ina kofanana. Pamene tiphunzira Baibulo, timapeza kuti pali maziko a chowonadi ochulukira, kapena maprinsipulo, omwe afunikira kuzoloweredwa. Mwamsanga titagwiririra amenewa, tingapitirizebe ku zinthu zakuya. Ngati, ngakhale kuli tero, sitimvetsetsa mwakuya ndi kukhulupirira maprinsipulo oyambirira amenewa, kulambira kwathu kudzakhala m’ngozi. Sitidzakhala okhoza kupanga zigamulo zabwino, ndipo chikhulupiriro chathu chidzakhala chogwedezeka mopepuka.
Maprinsipulo okulira a Baibulo sali ovuta kuwamvetsetsa. (Onani charti.) Komabe, iwo sali osakondweretsa kapena nkhani za chikondwerero cha luntha. Iwo ali amoyo, zowonadi zofunika, ndipo Akristu anzeru amaphunzira kuwakonda iwo. Yehova akunena kuti: “tamvera mawu anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako; uwasunge mkati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse.”—Miyambo 4:20-22; Ezekieli 18:19, 20, 23.
Ngakhale ndi tero, mosasamala kanthu za kufunika kwa maprinsipulo amenewa, Yesu anachenjeza kuti kokha ochepera akakhoza kugwirira ku iwo ndi kukhala ndi moyo mwa iwo. Iye ananena kuti: “Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:14) Ichi sichiri chifukwa chakuti maprinsipulowo ali obisika. Yehova amafuna amuna ndi akazi kukhala ndi moyo mwa iwo ndipo chotero kulandira moyo. (2 Petro 3:9) Iye wapangitsa nzeru, chidziŵitso, ndi kuzindikira kulembedwa m’Baibulo, lomwe liri lopezeka mofala kwa onse. Ndipo Mboni zake zimalimbikitsa anansi awo kufunafuna kaamba ka chidziŵitso chopatsa moyo chimenechi. Mwanjirayi, m’chenicheni, “nzeru ifuula panja; imveketsa mawu ake pabwalo.” (Miyambo 1:20; 2:1-9) Koma pali magwero ena omwe akugwira ntchito.
Satana waphimba maso a anthu ochulukira ku maprinsipulo owona. (2 Akorinto 4:4) Mowonjezereka, mzimu wa munthu wa kudziimira payekha umampangitsa iye kukhumba kupita m’njira yake m’malo mwa kuyang’ana ku Mphamvu Zokulira kaamba ka chitsogozo. M’tsiku la mtumwi Paulo, ngakhale ena omwe anaphunzira maprinsipulo okulira anaphonya iwo. Ndiponso, iye analemba kuti: “Muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu.”—Ahebri 5:12.
Ndiponso, Yesu anachenjeza kuti: “Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?’ Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo: Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Nchifukwa ninji anthu omwe maganizira kuti akutumikira Yesu amadzipeza iwo eni okanidwa? Chifukwa chakuti “ntchito zawo zokulira” siziri zozikidwa pa maprinsipulo a Baibulo. Chiri monga ngati akuyesera kuphunzira mbiri yakale kapena sayansi popanda choyamba kuphunzira kuŵerenga. Ntchito zawo ziri pangozi, zosazikidwa m’chowonadi. Chotero, iwo ali “akuchita kusayeruzika.”
Kodi Kulanbira Kwanu Kuli Kolandirika?
Kodi tinagakhale otsimikizira kuti Yesu tsiku lina sadzanena kwa ife kuti, ‘Chokani kwa ine, inu akuhita kusayeruzika’? Inde, ngati kulambira kwathu kuli kozikidwa kotheratu pa maprinsipulo a Baibulo. Chingakhale tero ngati tinsanthula mosamalitsa Baibulo, makamaka mawu a Yesu. Yesu anayenda m’chipata chopapatiza, njira yopapatiza yopita kumoyo—m’chenicheni, iye anali “njira ndi chowonadi ndi moyo.” (Yohane 14:6) Ngati tigwiritsira ntchito zonena zake ndi kutsatira mosamalitsa mapazi ake, tidzakhala panjira yofananayo.—Yohane 6:68; 1 Petro 2:21.
Otsatira achifupi a Yesu anayendanso m’njira yochepayo, yopapatiza yopita ku moyo. Chotero, pamene Yesu anamwalira iye anaika m’manja mwawo ntchito ya kuphunzitsa ena mmene angalambirire Mulungu. Iye anachenjezanso kuti akabwerera ndi kuyembekeza kufufuza iwo ponena za mmene anadzisungira iwo eni mkati mwa kusakhalapo kwake.—Mateyu 24:46; 25:14-23; 28:19, 20.
Potsirizira pake, chiŵerengero cha awo odzinenera kutsatira Kristu chinakwera ku mazana a mamiliyoni. Koma m’nkhani zambiri, kulambira kochitidwa ndi makamu ochulukira amenewa sikunazikidwe pa maprinsipulo a Baibulo. Chotero, pamene Yesu anakhazikitsidwa monga Mfumu ya kumwamba mu 1914 ndipo kenaka ‘kudza’ kudzaweruza awo odzinenera kukhala atsatiri ake, kodi iye anapezanji? Mamiliyoni odzinenera kukhala Akristu anali odzilowetsa mu nkhondo zoipitsitsa kotheratu m’mbiri yakale ya mtundu wa anthu kufika kumlingo umenewo.
Inde, unyinji wokulira wa “Akristu” unkachita mosiyana kotheratu ndi maziko a maprinsipulo a Baibulo. Komabe, panali gulu la Akristu enieni oyesera mwamphamvu kutsatira maprinsipulo aumulungu ndiponso kuphunzitsa iwo kwa aliyense yemwe akamvetsera m’dziko lopenga ndi nkhondoli. Awa anasonkhana pamodzi ndipo m’kupita kwanthaŵi anatsagana ndi khamu lalikulu la anthu a mitima yowongoka. (Mateyu 24:31; Chivumbulutso 7:4, 9, 10) Iwo akali kutsatirabe maprinsipulo opatsa moyo, kuuza ena ponena za chifuno chokulira cha Mulungu, kusonkhana pamodzi monga gulu la nkhosa limodzi, ndi kuyesera zolimba kusinthira ku “chifuno changwiro cha Mulungu.”—Aroma 12:2.
Prinsipulo la m’Malemba Lofunika Koposa
Ichi sichinakhale chopepuka. Kaamba ka chinthu chimodzi, Akristu owona amenewa anafunikira kumenyera kupanda ungwiro kwawo, chibadwa cha uchimo. Ndipo amafunikira kukhala m’dziko lomwe iri lotsutsidwa kotheratu m’mapindu ndi maprinsipulo omwe iwo akuyesera kukhala ndi moyo nawo. M’chenicheni, mtumwi Yohave ananena kuti: “Dziko lonse ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Chimenecho ndicho chifukwa chake alambiri owona a Mulungu lerolino ayenera kusunga mwathithithi m’malingaliro prinsipulo lofunika kwambiri lolongosoledwa ndi Yesu: “Sali [Akristu] mbali yadziko.”—Yohane 17:16.
Yehova sakukakamiza anthu kumtumikira iye, koma awo omwe amasankha kuchita tero afunikira kupanga kugamulapo kosamalitsa. Mwachitsanzo, iwo afunikira kugwirizanitsidwa ku chenicheni chakuti sangakhale otchuka m’dziko iri. (Mateyu 24:9) Mtumwi Yakobo anachenjeza kuti: “Iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Ndipo mtumwi Paulo ananena kuti: “Pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama?” ndi “Wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?” Kenaka anagwira mawu a Yehova iyemwini kuti: “Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, . . . ndipo musakhudze kanthu kosakonzeka.”—2 Akorinto 6:14-17; Aefeso 5:11.
Ndimotani mmene ‘tingadzipatulire ife eni’? Ndithudi, osati mwa kudzichotsa ife eni mwakuthupi kuchoka m’dziko. Koma tingapewe kukhala ‘oikidwa mgoli ndi osakhulupirira.’ Tingapewe ‘mayanjano oipa omwe amaipitsa makhalidwe okoma.’ (1 Akorinto 15:33) Ndipo tingadzipatule ife eni kuchoka ku mzimu wadziko, mzimu wakufunafuna zaumwini, kusawona mtima, kukondetsa zinthu zakuthupi, ndi kukhumba kopenga kaamba ka zosangalatsa. (2 Timoteo 3:1-5) Chitsimikiziritso chotenthetsa mtima chapatsidwa kwa awo omwe amadzipatula iwo eni ku zokhumba zadziko iri: “Wakuchita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Yohane 2:15-17.
Awo Omwe Amatsatira Maprinsipulo Okulira
Kodi chiri chothekera lerolino kutsatira maprinsipulo a Baibulo ndi kuyenda m’njira yopapatiza yomwe imatsogolera ku moyo? Inde, ngakhale ana angachite tero. Mwachitsanzo, ana achichepere aŵiri mu Brazil anali amakhalidwe abwino kwambiri pa sukulu kotero kuti mphunzitsi wawo anafunsa mayi wawo kudza kudzakambitsirana chifukwa chake. Mayiyo analongosola kuti chinali chifukwa chakuti iwo anali kutsatira maprinsipulo a Baibulo onena za chimvero kulinga kwa makolo ndi ena mu ulamuliro. (Aefeso 6:1-3) Pamapeto a nyengo ya sukulu, iwo anapatsidwa mwaŵi wa kulongosola ku kalasi lonse mapindu omwe amadza kuchokera ku kachitidwe kaumulungu koteroko.
Yesu analongosola prinsipulo: “Chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Dokotala wopita patsogolo mu Japan anaphunzira chimenechi ndipo, kukuzizwitsidwa kwa anzake, anachiika icho m’kugwira ntchito. Iye anasiya malo ake athayo lotchuka ndi kupita kunja kwa mzinda wochepera kumene iye akakhala wa chithandizo chauzimu kwa anthu a mumzindawo. Kudzipereka nsembe kwa mapindu a zakuthupi kumeneku sikunamuchotsere iye chimwemwe. M’malomwake, onse aŵiri iye ndi mkazi wake akupeza chimwemwe chokulira m’kubweretsa Mawu a moyo kwa ena.
Baibulo limanena kuti: “Pakuti wakuimwaimwa ndi wosusukayo adzasauka.” (Miyambo 23:21) Iri liri chenjezo lowonekera bwino molimbana ndi kumwerekera. Tikuchenjezedwanso molibana ndi kugwiritsira ntchito molakwa kwa anamgoneka: “Ntchito zathupi zomwe ziri . . . kupembedza mafano, kuchita ula [phar·ma·kiʹa, “matsenga” m’chinenero choyambirira cha Chigriki].” (Agalatiya 5:19, 20) Kuwonjezerapo, mtumwi Paulo akulimbikitsa kuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse chathupi ndi chamzimu.”—2 Akorinto 7:1.
Kusuta fodya ndi kugwiritsira ntchito anamgoneka omwerekeretsa ena mwachiwonekere kumapita motsutsana ndi maprinsipulo a Baibulo amenewa ndipo chotero kuli “kusayeruzika.” (Mateyu 7:23) Mtumiki aliyense wa Mulungu yemwe amadziipitsa iyemwini ndi zinthu zoterozo adzapeza kuti kulambira kwake sikuli kolandiridwa kwa Mulungu. Chotero, mazana angapo a zikwi atenga sitepi ya kuleka kugwiritsira ntchito anamgoneka amenewa, ndipo monga chotulukapo, alandira ponse paŵiri mapindu auzimu ndi akuthupi. Ndithudi, sichiri nthaŵi zonse chopepuka kupatuka ku zizoloŵezi zosayera zimenezi.
Mwamuna wachichepere mu Michigan, U.S.A., anaphunzira ponena za Mulungu ndi maprinsipulo ake kuchokera kwa atumiki ena omwe anaitanira pa chitseko chake. Anakonda chimene anamva koma anazindikira kuti chizoloŵezi chake cha kusuta mbanje ndi fodya sichinali chogwirizana ndi kulambira Yehova. Iye akunena kuti: “Sindinakhale ndi vuto lirilonse la kuleka anamgoneka, omwe ndinasangalala nawo. Koma chinanditenga ine chifupifupi miyezi isanu ndi umodzi kuti ndileke kusuta ndudu.” Iye anathandizidwa ndi Akrsitu anzake ndi pemphero. Tsopano, pokhala ndi moyo woyera mogwirizana ndi maprinsipulo a Baibulo, iye akusangalala ndi chikumbumtima choyera, unansi ndi Mulungu, iye kuyanjana Kwachikristu. M’chenicheni, iye akunena kuti kufikira pamene ankhala Mkristu, sanadziŵe chimene ubwenzi unali.
Kutsatira maprinsipulo olungama kuli mowonadi njira yanzeru. Ndipo nzeru iri yamtengo wapatali kwambiri ngakhale kuposa golidi woyengeka. Tengani njira imeneyi inueni, ndipo chidzabweretsa chitamando kwa Yehova ndi kugwira ntchito ku madalitso osatha a inueni.—Salmo 19:7, 10; Miyambo 16:16.
[Bokosi patsamba 27]
Maprinsipulo ali zowonadi zenizeni kapena malamulo ofunika kuchokera ku amene zowonadi zina kapena malamulo angatengedwe. Zotsatirazi ziri zitsanzo zina:
□ “Udzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.”—Mateyu 22:37.
□ “Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu inunso muwachitire iwo zotero.”—Mateyu 7:12.
□ “Ubwenzi ndi dziko lapansi uli udani ndi Mulungu.”—Yakobo 4:4.
□ “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.
□ “Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.”—Aroma 15:1.
□ “Potero mwa iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”—Ahebri 13:15.
□ “Ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.”—Ahebri 10:24, 25.
□ “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa [Yehova].”—Mateyu 4:4.