Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Wophunzira Wosiyanako
NDI chowoneka chochititsa mantha chotani nanga pamene Yesu afika ku gombe! Amuna awiri amawonekedwe woopsya kwambiri akutuluka kuchokera ku manda achapafupipo ndi kuthamangira kwa iye. Iwo ali ogwidwa ndi ziwanda. Popeza m’modzi wa iwo ali mwinamwake waukali kwambiri kuposa winayo ndipo wakhala akuvutika kwa nthawi yaitali pansi pa ulamuliro wa ziwanda iye akukhala maziko achidwi.
Kwanthawi yaitali munthu womvetsa chisoni ameneyu wakhala akukhala wamaliseche pakati pa manda. Mopitiriza, usana ndi usiku, iye amalira mofuula ndi kudzitematema ndi miyala. lye ali waukali kotero kuti palibe wina aliyense ali ndi kulimba mtima kwakupitira panjira imeneyo. Kuyesayesa kunachitidwa kumumanga iye, koma iye anali kumwetula maunyolo ndi kuduladula matangadza mu mapazi ake. Palibe aliyense ali ndi mphamvu ya kumfuya iye.
Pamene mwamunayo akuyandikira kwa Yesu ndi kugwa pansi pa mapazi ake, ziwanda zomulamulira iye zimpangitsa kufuula: “Ndiri ndi chiyani ndi inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.”
“Turuka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu,” Yesu akupitiriza kunena. Koma kenaka Yesu afunsa: “Dzina lako ndani?”
“Dzina langa ndine Legio, chifukwa tiri ambiri,” ndiro yankho. Ziwanda zimasangalala mkuwona kuvutika kwa awo amene zimakhoza kuwagwira, mwachiwonekere kusangalala mkuwapangitsa iwo kukhala ndi mzimu wamantha wa gulu. Koma zitakumanizidwa ndi Yesu, zikupempha kuti zisapititsidwe kuphompho. Pano tikuwonanso mphamvu yaikulu yomwe Yesu anali nayo ya kulaka ngakhale ziwanda zochititsa mantha. Ichi chikuvumbulanso kuti ziwanda ziri zozindikira kuti kuponyedwa kuphompho limodzi ndi mtsogoleri wawo, Satana Mdyerekezi chiri chiweruzo chotsimikizirika cha Mulungu kaamba ka iwo.
Gulu la nkhumba chifupifupi 2, 000 zinali kudya pafupipo pa phiri. Chotero ziwandazo zikuti: “Titumizeni ife mu nkhumbazo kuti tilowe mu izo.” Mwachiwonekere ziwandazo zimapeza mtundu wina wake wosakhala wa chibadidwe, wa chikondwerero cha chikhumbo cha kukhala waukali m’kulowa mu matupi a zolengedwa zathupi. Pamene Yesu akuzilola izo kulowa mu nkhumbazo, 2, 000 zonse za izo zikutsika ndi liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja.
Pamene oweta nkhumbazo anawona ichi, iwo akuthamanga kukasimba nkhaniyi m’mzinda ndi kuminda. Pa chimenecho, anthu atuluka kudzawona chomwe chachitika. Pamene afika, iwo akuwona munthu amene kuchokera mwa iye ziwandazo zinatuluka, atavala ndi wa nzeru zake zabwino, akukhala pa mapazi a Yesu!
Mboni zowona ndi maso zikusimba kwa anthuwo ndimotani mmene munthuyo anachiritsidwira. Iwo akunenanso ponena za chochitika chodabwitsa cha imfa ya nkhumbazo. Pamene amva ichi, ma ntha aakulu awagwira anthuwo, ndipo ayamba ku pempha Yesu kuti achoke mu malire awo. Chotero iye akugonjera ndi kukwera ngalawa. Munthu amene anali ogwidwa ndi ziwandayo amupempha Yesu kumulola iye kupita naye. Koma Yesu akumuuza iye: “Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu akuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.”
Yesu kawirikawiri amalangiza awo amene waachiritsa kusauza aliyense, popeza iye sakufuna kuti anthu adzifikira pa maziko a maripoti m’maganizo athumanzi. Koma kupatulidwa uku kuli koyenera chifukwa munthu yemwe anali ndi ziwandayo adzachitira umboni pakati pa anthu amene Yesu tsopano mwinamwake sadzakhala ndi mwawi wakuwafikira. Kuwonjezerapo, kukhalapo kwa munthuyo kudzapereka umboni ponena za mphamvu ya ntchito yabwino ya Yesu, kuletsa maripoti ena alionse osayenerera omwe angakhale akuzungulira ponena za kutaidwa kwa nkhumbazo.
Mkusunga malangizo a Yesu, munthu yemwe anali wa ziwandayo achoka. lye ayamba kulalikira kuzungulira mu Dekapoli zinthu zonse zimene Yesu anachita kwa iye; ndipo anthu onse anazizwa. Mateyu 8:28-34; Marko 5:1-20; Luka 8:2639; Chivumbulutso 20:1-3.
◆ Nchifukwa ninji, mwinamwake, chidwi chakokedwera kwa munthu m’modzi wogwidwa ndi ziwanda pamene analipo awiri a iwo?
◆ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ziwanda zimadziwa ponena za kuponyedwa kuphompho kwa mtsogolo?
◆ Nchifukwa ninji, mwachiwonekere, ziwanda zimakonda kugwira anthu ndi zinyama?
◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu anapanga kupatulidwa kwa munthu yemwe anali wogwidwa ndi ziwanda, kumlangiza iye kuuza ena ponena za zimene iye anachita kwa iye?