Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kudalitsidwa ndi Malangizo Owonjezereka
OPHUNZIRA angolandira kumene kalongosoledwe ka fanizo la wofesa mbewu. Koma tsopano akufuna kuphunzira zowonjezereka. “Tiuzeni ife,” iwo akufunsa, “fanizo la namsongolem’munda.”
Ndi khalidwe losiyana chotani nanga la ophunzirawo kuchokera ku lija la khamu lonse pagombe! Anthuwo akusowa chikhumbo chofunitsitsa chakuphunzira matanthauzo amafanizo, kukhala okwaniritsidwa ndi ndandanda ya zinthu zoperekedwa kwa iwo. Kusiyanitsa amvetseri a mphepete mwa nyanja amenewo ndi ophunzira ake ofunsira kufuna kudziwa, Yesu akuti:
“Ndi muyeso umene muyesera nawo, udzayesedwa kwa inu, ndipo kudzawonjezedwa kwa inu.” Ophunzirawo akuyesera kwa Yesu chikondwerero chofunitsitsa ndi kusamalitsa ndipo chotero akudalitsidwa mwakulandira malangizo owonjezereka. Chotero, mkuyankha kufunso la ophunzira ake, Yesu akulongosola:
“Wofesa mbewu yabwino ndiye Mwana wa munthu, ndipo munda ndiwo dziko lapansi, ndi mbewu yabwino ndiwo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo, ndipo mdani amene anamfesa uyu, ndiye Mdyerekezi. Ndi kututa ndicho chimariziro cha nthawi ya pansi pano, ndi otutawo ndiwo angelo.”
Pambuyo pa kuzindikiritsa mbali yonse ya fanizo, Yesu akulongosola chotulukapo chake. Pamapeto a dongosolo iri la zinthu, iye akuti, “otuta,” kapena angelo, adzasiyanitsa Akristu oyesera okhala ngati namsongole kuchokera kwa “ana enieni a ufumuwo.” “Ana a woipayo” adzaikidwa chizindikiro kaamba ka chiwonongeko, koma ana a Ufumu wa Mulungu, “olungama,“ adzawalitsa monga dzuwa mu Ufumu wa Atate wawo.
Yesu kenaka akudalitsa ophunzira ake ofunitsitsa kudziwa ndi mafanizo atatu owonjezereka. Choyamba, iye akuti: “Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika mu munda, chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo mu kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewo.”
“Ndiponso,” iye akupitirira, “ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi munthu wa pa malonda, wakufuna ngale zabwino: Ndipo mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.”
Yesu iyemwini ali monga munthu amene anapeza chuma chobisika ndi monga munthu wamalonda amene anapeza ngale ya mtengo wapatali. lye anagulitsa zonse anali nazo, monga mmene kunaliri, kusiya malo aulemerero kumwamba kudzakhala munthu wochepetsedwa. Kenaka, monga munthu pa dziko lapansi, iye akuvutika ndi kutonzedwa ndi chizunzo chaudani, kutsimikizira kukhala woyenerera kukhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu.
Chitokoso chaikidwa pamaso pa otsatira a Yesu nawonso kugulitsa chiri chonse chimene anali nacho kuti apeze mphoto ya pamwamba ya kukhala kaya olamulira anzawo ndi Kristu kapena nzika za Ufumu wa padziko lapansi. Kodi tidzalingalira kukhala ndi mbali mu Ufumu wa Mulungu monga chinthu chamtengo wapatali kuposa china chiri chonse m’moyo, monga chuma chamtengo wapatali kapena ngale ya mtengo wapatali?
Pomalizira, Yesu akuyerekeza “Ufumu wakumwamba“ ndi khoka loponyedwa m’nyanja lomwe limasonkhanitsa nsomba za mitundumitundu. Pamene nsomba zisiyanitsidwa, zosayenera zimataidwa koma zabwino zimasungidwa. Chotero, Yesu akuti, chidzatero m’nthawi ya chimaliziro cha dongosolo iri la zinthu; angelo adzasiyanitsa oipa ndi olungama, kusunga oipa kaamba ka kuwatha psiti.
Yesu iyemwini wayamba ntchito yowedza imeneyi, kuitana ophunzira ake oyambilira kukhala “asodzi a anthu.” Pansi pa chitsogozo chaungelo ntchito yowedza imeneyi ikupitirizabe mkati mwa zaka mazana. Pomalizira nthawi iima “mu khoka,“ lomwe limaimira magulu a padziko lapansi odzinenera kukhala Akristu.
Ngakhale kuti nsomba zosayenera zimataidwa ku chiwonongeko, mwachiyamikiro tingawerengedwe pakati pa ‘nsomba zabwino’ zomwe zikusungidwa. Mwakusonyeza chikhumbo chofunitsitsa monga mmene anapangira ophunzira a Yesu kaamba ka chidziwitso chowonjezereka ndi kumvetsetsa, tidzadalitsidwa osati kokha ndi malangizo koma ndi dalitso la Mulungu la moyo wosatha. Mateyu 13:36-52; 4:19; Marko 4:24, 25.
◆ Kodi ndimotani mmene ophunzira anasiyanirana ndi khamu pa gombe?
◆ Ndi ndani kapena kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi wofesa mbewu, munda, mbewu yabwino, mdani, kututa, ndi otuta?
◆Ndi mafanizo atatu owonjezera otani amene Yesu wapereka, ndipo kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku iwo?