Kodi Mukudziwa?
Kodi fanizo la Yesu la “tiagalu” linali lonyoza?
Pamene Yesu anali ku Siriya, mayi wina wachigiriki anabwera kudzamupempha kuti amuchiritsire mwana wake wamkazi. Poyankha Yesu ananena fanizo ndipo m’fanizolo anayerekezera anthu omwe sanali Ayuda ndi “tiagalu.” M’Chilamulo cha Mose, agalu ankaonedwa kuti ndi nyama zodetsedwa. (Levitiko 11:27) Ndiye kodi Yesu ananena fanizoli pofuna kunyoza mayi wachigirikiyu komanso anthu ena omwe sanali Ayuda?
Ayi. Mogwirizana ndi zimene Yesu anauza ophunzira ake, apa mfundo yake inali yakuti, ntchito yake yaikulu pa nthawiyo inali kuthandiza Ayuda. N’chifukwa chake iye anauza mayiyo kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana n’kuponyera tiagalu.” (Mateyu 15:21-26; Maliko 7:26) Agiriki ndi Aroma ankaweta agalu ndipo ankawakonda kwambiri moti ankakhala nawo m’nyumba zawo komanso ana awo ankasewera ndi agaluwo. Choncho mawu a Yesu akuti “tiagalu” ayenera kuti anakumbutsa mayiyo mmene Agiriki ankakondera agalu. Ndipotu mayi ameneyu anamvetsa bwino mfundo ya Yesu moti anayankha kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.” Yesu anamuyamikira chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo anachiritsa mwana wake wamkazi.—Mateyu 15:27, 28.
Kodi malangizo amene mtumwi Paulo anapereka okhudza ulendo wawo wapanyanja anali abwino?
Ngalawa imene Paulo ndi anthu ena anakwera popita ku Italiya inakumana ndi chimphepo choopsa. Anthuwa atafika pamalo enaake, mtumwiyu analangiza oyendetsa ngalawayo kuti asapitirize ulendowo, koma ayembekeze kaye. (Machitidwe 27:9-12) Kodi malangizo amenewa anali abwino?
Kale anthu omwe ankayenda panyanja ya Mediterranean ankadziwa bwino kuti kuyenda panyanjayi m’miyezi yozizira kunali koopsa kwambiri. Kungoyambira pakati pa mwezi wa November kukafika pakati pa mwezi wa March, anthu ankaona kuti si nthawi yabwino kuyenda panyanja. Koma ulendo umene Paulo ankanenawu ankayenera kunyamuka mu September kapena mu October. Wolemba mabuku wina wa ku Roma, dzina lake Vegetius (wa m’ma 300 C.E.), analemba m’buku lake lina zokhudza kuyenda panyanja ya Mediterranean. Iye anati: “Miyezi ina ndi yabwino kwambiri kuyenda panyanjayi, ina ndi yokayikitsa pomwe ina ndi yoopsa.” (Epitome of Military Science) Vegetius ananena kuti nthawi yabwino kuyenda panyanjayo inali kuyambira pa 27 May kukafika pa 14 September. Nthawi yokayikitsa inali kuyambira pa 15 September kukafika pa 11 November. Pomwe nthawi yoopsa inali kuyambira pa 11 March kukafika pa 26 May. Choncho, popeza Paulo ankayenda panyanja kawirikawiri, n’zosakayikitsa kuti ankadziwa bwino zimenezi. Munthu amene ankayendetsa ngalawa imene Paulo anakwera komanso mwiniwake wa ngalawayo ayenera kuti ankadziwanso zimenezi, koma sanamvere malangizo a Paulo. Zotsatira zake, ngalawayo inasweka ndi chimphepo komanso mafunde amphamvu.—Machitidwe 27:13-44.