Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Mikate ndi Chotupitsa
MAKAMU a akulu apita kwa Yesu mu Dekapoli. Ambiri akubwera kuchokera pa mtunda wautali kufika ku gawo iri lokhalidwa kwambiri ndi akunja kudzamva kwa iye ndi kuchiritsidwa matenda awo. Iwo abweretsa limodzi nawo mitanga yaikulu, kapena zimadengu, zimene mwamwambo amazigwiritsira ntchito kutengeramo zakudya pamene akuyenda kupyola m’madera a Akunja.
Potsirizira pake, ngakhale kuli tero, Yesu akuitana ophunzira ake ndi kunena kuti: “Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya; ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwawo osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.”
“Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m’chipululu muno?” Ophunzirawo akufunsa.
Yesu akufunsa kuti: “Muli nayo mikate ingati?”
“Isanu ndi iŵiri,” iwo akuyankha, “ndi tinsomba toŵerengeka.”
Akulangiza anthuwo kuseyama pansi, Yesu akutenga mikate ndi tinsombato, apemphera kwa Mulungu, anyema izo, ndipo ayamba kuzipereka izo kwa ophunzira ake. Iwo, kenaka, apatsa anthu, onsewo anadya nakhuta. Pambuyo pake, pamene anatola makombo otsala, panali malichero asanu ndi aŵiri odzaza, ngakhale kuti chifupifupi amuna 4,000 limodzi ndi akazi ndi ana, anali atadya!
Yesu auza makamuwo kuti amuke, akwera ngalawa ndi ophunzira ake, ndi kuwolokera ku gombe la kumadzulo kwa Nyanja ya Galileya. Kuno Afarisi, panthaŵi ino otsagana ndi ziwalo za gulu la mpatuko la chipembedzo la Asaduki, ayesera kumuyesa Yesu mwa kumufunsa iye kusonyeza chizindikiro chochokera kumwamba.
Akuzindikira zoyesayesa zawo za kumuyesa iye, Yesu akuyankha: “Madzulo munena, ‘Kudzakhala ngwe, popeza thambo liri lacheza’; ndipo m’mawa, ‘Lero nkwa mphepo, popeza thambo liri la cheza chodera.’ Mudziŵa kuzindikira za pa nkhope pa thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira.”
Ndi chimenecho, Yesu akuwatcha iwo obadwa oipa ndi achigololo ndi kuwachenjeza iwo kuti, monga mmene anauzira Afarisi poyambirirapo, chizindikiro sichidzapatsidwa kwa iwo koma chizindikiro cha Yona. Akuchoka, iye ndi ophunzira ake alowa m’ngalawa ndi kulinga ku Betsaida ku gombe la kumpoto kwa Nyanja ya Galileya. Ali pa ulendo ophunzirawo akuwona kuti aiwala kubweretsa mkate, iwo ali kokha ndi mkate umodzi pakati pawo.
Akusunga m’maganizo chokumana nacho chake ndi achirikizi a Herode Afarisi ndi Asaduki, Yesu akuchenjeza kuti: “Yang’anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi chotupitsa mkate cha Herode.” Popeza kuti ophunzirawo akukhulupirira kuti Yesu akulozera ku kuiwala kwawo kwa kubweretsa mkate, chotupitsa mkate mwachiwonekere chinabweretsa lingaliro la mkate ku malingaliro awo, iwo anayamba kutsutsana ponena za nkhaniyo. Akuzindikira kusamvana kwawo, Yesu akunena kuti: “Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate?”
Posachedwapa, Yesu wapereka mkate mozizwitsa kwa zikwi za anthu, akumachita chozizwitsa chomalizira chimenechi mwinamwake kokha tsiku limodzi kapena aŵiri pambuyo pake. Iwo ayenera kudziŵa kuti iye sali wodera nkhaŵa ponena za kusoweka kwa mikate yeniyeni. “Simukumbukira kodi,” iye akuwakumbutsa iwo, “pamene ndinagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo?”
“Khumi ndi iŵiri,” iwo anayankha.
“Pamene ndinagawira mikate isanu ndi iŵiri kwa anthu zikwi zinayi, munatola malichero angati odzala ndi makombo?”
“Asanu ndi aŵiri,” iwo akuyankha.
“Simudziŵitsa ngakhale tsopano kodi?” Yesu akufunsa. “Bwanji nanga simudziŵa kuti sindinena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”
Ophunzirawo pomalizira amvetsa nsonga. Chotupitsa, chinthu chopangitsa kusasa ndi kupanga mkate kutupa, linali liwu logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri kusonyeza kuwononga. Chotero tsopano ophunzirawo akumvetsetsa kuti Yesu akugwiritsira ntchito kuphiphiritsira, kuti iye akuwachenjeza iwo kukhala ogalamuka motsutsana ndi “chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki,” chiphunzitso chimene chiri ndi chiyambukiro chosakaza. Marko 8:1-21; Mateyu 15:32–16:12.
◆ Nchifukwa ninji anthu ali ndi mitanga ya zakudya yaikulu ndi iwo?
◆ Pambuyo pa kuchoka ku Dekapoli, ndi maulendo a pangalawa ati amene Yesu akutenga?
◆ Ndi kusamvana kotani kumene ophunzira anali nako ponena za ndemanga ya Yesu yonena za chotupitsa?
◆ Nchiyani chimene Yesu anatanthauza mwa “chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki?”