Kuchiritsa kwa Chikhulupiriro Kodi Kuli Kochokera kwa Mulungu?
MUNTHUYU wakhala akudwala kwa zaka 38. “Ufuna kuchiritsidwa kodi?” anafunsa tero Yesu. Ngati munali munthu ameneyu, kodi mofunitsitsa simukanayankha kuti inde? Yesu anamuuza iye kuti: “Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.” Chotulukapo cha mawu amenewo? “Ndipo pomwepo munthuyo anachira, nayalula mphasa yake, nayenda.”—Yohane 5:5-9.
Mbali iyi ya kuchiritsa kwaumulungu inali kokha imodzi ya zambiri zimene Yesu anachita mkati mwa utumiki wake wa padziko lapansi. (Mateyu 11:4, 5) Ochiritsa mwachikhulupiriro lerolino amadzinenera kuti Mulungu adakachitabe kuchiritsa koteroko, ndipo iwo akuchirikizidwa ndi maumboni zikwi zingapo omwe amadzinenera kuti anachiritsidwa ndi iwo.
Kusiyana Kwakukulu
Phunziro la Baibulo limavumbula kusiyana kwakukulu kochuluka pakati pa kuchiritsa kosimbidwa m’Baibulo ndi kuja kosimbidwa ndi ochiritsa mwachikhulupiriro a lerolino. Yesu ndi ophunzira ake, mwachitsanzo, sanalipiritse kaamba ka kuchiritsa kwawo. “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere,” anaphunzitsa tero Yesu. (Mateyu 10:8) Chotero iwo anatsatira chitsanzo chokhazikitsidwa ndi Elisa, amene anakana mphatso kuchokera kwa munthu wotchedwa Namani amene Elisa anamchiritsa khate lake. (2 Mafumu 5:1, 14-16) Chotero, pamene ochiritsa mwachikhulupiriro alipiritsa kaamba ka mautumiki awo, iwo amanyalanyaza lamulo la m’Malemba limeneli.
Chirinso chodziŵikiratu kuti kuchiritsidwa kochitidwa m’nthaŵi za Baibulo kunali kaya kwa panthaŵi yomweyo kapena kunakwaniritsidwa mkati mwa nyengo yochepa yanthaŵi. Pamene mtumwi Petro anawona mwamuna “wopunduka chibadwire,” iye anauza munthuyo: “M’dzina la Yesu Kristu M’nazarayo, yenda!” Mbiriyo ikuvumbulutsa kuti: “Ndipo pomwepo mapazi ake [a mwamuna wopundukayo] ndi mfundo za kumapazi zinalimbitsidwa. Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda.” (Machitidwe 3:1-8) Dziŵerengereni nokha zitsanzo zina pa Machitidwe 5:15, 16 ndi 14:8-10.
Kuchiritsa kwachikhulupiriro kwa masiku ano, ngakhale kuli tero, kaŵirikaŵiri kumatenga masiku, milungu, ndipo ngakhale miyezi kuti kugwire ntchito! Chodziŵika, kachiŵirinso, chiri nsonga yakuti ochiritsa mwachikhulupiriro amayedzamira ku kulunjikitsa chidwi pa matenda ogwira ntchito, monga ngati khungu, kufa miyendo, kapena kugontha—matenda amene nthaŵi zina amakhala ndi maziko a za malingaliro. Akuwona tero dokotala wotumbula anthu Paul Brand: “Mwamsanga pamene vuto la ziwalo likhala losachiritsika—kusowa miyendo, maso, kapena ziboo motuluka tsitsi—zozizwitsa sizimawonekawoneka.” Yesu, ngakhale kuli tero, anachiritsa “nthenda iriyonse ndi zofooka zonse,” kuphatikizapo kupunduka kumene mwachiwonekere kunali kwa kuthupi mwa chibadwa, monga ngati dzanja lopuwala.—Mateyu 9:35; Marko 3:3-5.
‘Mulibe Chikhulupiriro’
Momvetsa chisoni, anthu ambiri odwalitsa amapezeka pa ‘maulendo ochiritsa’ kokha kubwerera kunyumba odwala monga mmene analiri. Ochiritsa mwachikhulupiriro amalongosola kulephera kumeneku mwakunena kuti, ‘Iwo alibe chikhulupiriro!’ Uku, ngakhale kuli tero, kuli kunyenga. Monga mmene Dr. William Nolen anawonera kuti: “Mosiyana ndi dokotala wa chiorthodox, wochiritsa malingaliro sayenera kutenga thayo pamene kuchiritsa kwake kulephera. Ndiyenera kudzinenera kuti ndingakonde kusankha ku chodzikhululukira chotero pamene ndikumana ndi wodwala yemwe sindingathe kumuchiritsa.”
Kulibe aneneri a Mulungu, Yesu, osatinso ophunzira a Yesu amene anali ndi chifuno ndi kalelonse cha kuperekera chodzikhululukira kuti wopundukayo sanachiritsidwe chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro. Zowona, kusoweka kwa chikhulupiriro kungakhale kunachepetsa chiŵerengero cha anthu omwe anabwera kuti adzachiritsidwe. Koma kwa awo amene anabweradi, kuchiritsa kotheratu nthaŵi zonse kunachitika!—Marko 6:5, 6.
Ndithudi, m’nkhani zina anthu omwe mwachiwonekere analibe chikhulupiriro anachiritsidwa. Namani, mkulu wa gulu la nkhondo la Asuri, mwachitsanzo, sanakhulupirire mokwanira kuti iye akhoza kuchiritsidwa ku khate lake m’njira imene mneneri Elisa anamtsogozera. Kunali kokha pambuyo pa kuchiritsidwa kwake kuti iye anavomereza kuti: “Tawonani, tsopano, ndidziŵa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi koma kwa Israyeli ndiko.” (2 Mafumu 5:11-13, 15) Chodzikhululukira chopanda pake cha ochiritsa mwachikhulupiriro chotero chimakhala chosanunkha kanthu.
Kuchiritsa—Mphatso Yomwe Inatha
Koma kodi sichiri chowona kuti mphatso zozizwitsa za kuchiritsa zinali zofala pakati pa Akristu oyambirira? (1 Akorinto 12:9) Inde, koma panali chifukwa chabwino kaamba ka zozizwitsa zimene zinachitika nthaŵi ya kumbuyo imeneyo. Kwa zaka chikwi ndi theka, mtundu wa Israyeli wakuthupi unali anthu osankhidwa ndi Mulungu; koma m’zana loyamba la Nyengo Yathu, Israyeli anakanidwa chifukwa cha kusowa kwake chikhulupiriro ndi kulowedwa m’malo ndi mpingo watsopano Wachikristu. Akristu oyambirira amenewo anafunikira thandizo lopambana kulimbikitsa chikhulupiriro ndi kupereka umboni ku dziko la kunja kuti iwo anali ndi chirikizo la Yehova Mulungu.
Chotero, mphatso zozizwitsa, kuphatikizapo kuchiritsa, zinaperekedwa ku mpingo Wachikristu waubwana. Izi zinatumikira monga “chizindikiro” kwa osakhulupirira ndiponso monga njira yomangirira chikhulupiriro cha okhulupirira. (1 Akorinto 14:22) Komabe, chifupifupi zaka zikwi ziŵiri pambuyo pake, Chikristu sichirinso mu mkhalidwe wake waubwana. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 13:9-13.) Baibulo linamalizidwa kale kwambiri ndipo lakhala likufalitsidwa m’mamiliyoni a makope. Chotero Akristu owona lerolino mopepuka angatsogoze osakhulupirira ku masamba ake ku kuchirikiza zimene akuphunzitsa. Ziwonetsero zozizwitsa sizikufunikiranso tsopano.
Paulo mowonjezera anasonyeza kuti mphatso za mphamvu zoposa zaumunthu “zidzaleka.” (1 Akorinto 13:8) Mphatso zoterozo zinaperekedwa kokha mwachindunji kapena m’kukhalapo kwa atumwi a Kristu Yesu. (Machitidwe 8:18-20; 10:44-46; 19:6) Pambuyo pa imfa ya atumwi, ziwonetsero zozizwitsa zinaleka.
Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature yolembedwa ndi McClintock and Strong (Volyumu VI, tsamba 320) inawona kuti chiri “lingaliro losatsutsika kuti mkati mwa zaka zana loyambirira pambuyo pa imfa ya atumwi timamva zochepa kapena sitimva chirichonse cha kugwira ntchito kwa zozizwitsa ndi Akristu oyambirira.”
Chifukwa cha Kuchenjerera
Yesu Kristu anachenjeza kuti nthaŵi idzafika imene ambiri adzanena kwa iye: “Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?” Ndipo Yesu adzawauza iwo: “Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse! Chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Nchiyani, tsopano, chimene timaŵerengera kaamba ka kupambana kwawo komawunikira m’kuchita “mphamvu zazikulu” ngati suli mzimu wa Mulungu?
M’nkhani zina, kunyenga kowonekeratu kumawonekera kukhala kutaphatikizidwa. Mwachitsanzo, The Herald, nyuzipepala ya ku Zimbabwe, inasimba pa anthu atatu omwe wochiritsa wawo wa chikhulupiriro wotchuka analengeza kukhala atawachiritsa. Pepalayo inavumbula ichi monga kunyenga: “Mwana mmodzi kufikira tsopano sangamve ndiponso sangalankhule; mwana mmodzi sanali wogontha kapena wosalankhula; ndipo mkazi yemwe anali wogontha kumene, kufikira tsopano samva.”
Nthaŵi zina, kuchiritsa kwachikhulupiriro kumawonekera kukhala ndi zotulukapo zowongokera kwa wodwalayo. M’nkhani zina—makamaka kumene nyengo yaitali ya nthaŵi imapita kuchira kusanawonekere—chimawoneka kuti dongosolo lochiritsa la thupi lachibadwa limaphatikizidwamo. Mu bukhu la Science ndi Paranormal, Dr. William Nolen akunena kuti “chifupifupi 80 peresenti ya odwala amene amabwera kwa [sing’anga wa chiorthodox] amakhala ndi matenda okhala ndi malire—kunena kuti, matenda kuchokera ku amene iwo angapeze kuchira kwa mwamsanga. Chotero, ndi kupita kwanthaŵi, wochiritsa mwachikhulupiriro angadzitengere ulemu mopepuka kaamba ka kuchiritsako.
Pomalizira, Baibulo limachenjeza kuti “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuwunika,” mkuyesayesa kwa kufuna kunyenga. (2 Akorinto 11:14) Pa 2 Atesalonika 2:9, 10, Paulo mowonjezera akulongosola kuti: “[Kudza kwa wosayeruzikayo kuli monga mwa machitidwe a Satana m’mphamvu yonse, NW] [“mitundu yonse ya zozizwitsa,” The Jerusalem Bible] ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama ndi chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka.” Chotero chenjerani! Kuchiritsa kwa chikhulupiriro kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo mphamvu zauchiwanda! “Sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda,” anachenjeza tero Paulo. “Simungathe kumwera chikho cha [Yehova, NW] ndi chikho cha ziwanda.”—1 Akorinto 10:20, 21.
Pamene Mkristu Akudwala
Zowona, pamene wina akudwala, kuchiritsa kozizwitsa kungawoneke chothekera chosangalatsa. Dziŵani, ngakhale kuli tero, kuti wogwira naye ntchito mnzake wa mtumwi Paulo Epafrodito anadwala pafupi kufa. (Afilipi 2:25-27) Mnzake wathithithi wa Paulo Timoteo mofananamo anavutika “m’zofooka zobwera kaŵirikaŵiri.” (1 Timoteo 5:23) Komabe, Paulo sanachiritse aliyense wa amuna amenewa mozizwitsa. Ndipo pamene Paulo anafuna chisamaliro cha mankhwala iyemwini, iye angakhale anagwiritsira ntchito mautumiki a Luka, “sing’anga wokondedwa,” yemwe anayenda naye.—Akolose 4:14.
Mofananamo lerolino, Mkristu amene akudwala angafune thandizo la sing’anga woyeneretsedwa kapena wochiritsa, mwakupewa kudziloŵetsa kulikonse mu kuchiritsa kouziridwa ndi ziwanda, kapena kunyengezera kuchiritsa matenda, komwe kuli kofala m’maiko ambiri lerolino. Iye angapempherenso, osati kaamba ka kuchiritsa kozizwitsa, koma kaamba ka nzeru ya kuchita ndi matendawo. (Yakobo 1:5) Iye angapemphenso kuti Yehova “amgwirizize pa kama wodwalira.”—Masalmo 41:3.
Chitayerekezedwa, chingakhale chokhumudwitsa kwambiri pamene sayansi ya mankhwala iri yosakhoza kuchiritsa matenda akuti akuti. Mosasamala kanthu za chimenecho, ngakhale pamene akudwala, Mkristu ayenera kukalamira “kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri,” osalola kudera nkhaŵa kwa moyo kuphiimba zodera nkhaŵa zonse kotheratu. (Afilipi 1:10) Iye angadzilimbitse iyemwini ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo pansi pa Ufumu wa Mulungu pamene “okhalamo sadzanena: ‘Ine ndidwala.’”—Yesaya 33:24; 65:17-19.
Ndithudi, chiyembekezo ichi cha dziko lapansi latsopano lolungama chiri chamtengo wapatali kwambiri kuposa malonjezo opanda pake a ochiritsa mwachikhulupiriro. Lingalirani Peter, mwamuna wa khungu wokhala mu Akumadan, mu Ghana. Iye anawononga chiwonkhetso cha zaka 26 mu matchalitchi osiyanasiyana ochiritsa mwachikhulupiriro m’chiyembekezo chakuti khungu lake lidzachiritsidwa. Koma palibe wochiritsa mwachikhulupiriro aliyense yemwe watsegula maso ake. Kenaka, pamene anali adakapezekabe ku tchalitchi cha ochiritsa mwachikhulupiriro, iye anafikiridwa ndi Mboni za Yehova.
Mbonizo zinalongosola kuchokera m’Baibulo kuti pansi pa Ufumu wa Mulungu kuchiritsa kotheratu kwa zofooka zonse kudzachitika. Ichi chinatsegula maso a Peter akumvetsetsa. Wodzazidwa ndi chiyamikiro kaamba ka zowonadi zosangalatsa za Baibulo, iye anakhala wolengeza wa nthaŵi zonse wa Ufumu wa Mulungu ndipo wakhala akutumikira tero koposa zaka zitatu! Iye akuyang’ana kutsogolo ku nthaŵi pamene, m’njira yeniyeni, “maso akhungu adzatsegulidwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.”—Yesaya 35:5, 6.
Ndi thandizo la Mawu a Mulungu, zikwi za ena mofananamo zadzipulumutsa kuchokera ku chikhulupiriro cholakwika mwa ochiritsa mwachikhulupiriro.
[Chithunzi patsamba 5]
Ochiritsa mwachikhulupiriro mochepera amachiritsa anthu okhala ndi mavuto a kuthupi
[Zithunzi patsamba 7]
Mkristu amene akudwala amapemphera kaamba ka mphamvu ya kupirira. Iye amayang’ananso kutsogolo kudziko latsopano, kumene “okhalamo sadzanena: ‘Ine ndidwala’”