Mmene Kusandulika kwa Kristu Kumakuyambukirirani
Amuna anayi adangokwera kumene paphiri lalitali. Pamwambapo panachitika chinthu chozizwitsa. Pamene ophunzira atatu a Yesu Kristu odabwawo anali chipenyere, iye anasinthika pamaso pawo. Mvetserani pamene Marko, wolemba Uthenga Wabwino, akusimba chochitika chosangalatsa chimenechi:
‘YESU anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nawo pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pawo: ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai. Ndipo anawonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu. Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. Pakuti sanadziŵa chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu. Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mawu [anatuluka] m’mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani iye. Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.’—Marko 9:2-8.
Tangolingalirani! Nkhope ya Yesu inali kuwala mofanana ndi dzuŵa lenileni. (Mateyu 17:2) Zovala zake zinali kunyezimira, ‘monga ngati muomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.’ Panali mkokomo wa liwu lamphamvu la Mulungu iye mwini likulengeza za Mwana wake. Ha, chinali chochitika chodabwitsa chotani nanga!
Liwu Lachigiriki lomasuliridwa “anasandulika” limatanthauza “kusinthira ku mpangidwe wina.” Limawonekeranso pa Aroma 12:2, pamene Akristu akupatsidwa uphungu wa ‘kukhala osandulika’ mwakukonzanso kwa mtima wawo.—An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine, Volyumu IV, tsamba 148.
Inde, chochitika chodabwitsa chimenechi chinachitika pamene Yesu anasandulika pambuyo pa phwando la Paskha la 32 C.E. Kodi chinatsogolera ku chozizwitsa chimenechi nchiyani? Kodi chiri ndi chifuno chapadera? Kodi nchifukwa ninji Mose ndi Eliya anaphatikizidwamo? Ndipo kodi ndimotani mmene kusandulika kwa Kristu kumakuyambukirirani?
Zochitika Zoyambirira
Asanakwere paphiripo, Yesu ndi ophunzira ake anali pafupi ndi Kaisareya wa Filipi. Popeza kuti mzinda umenewu unali pafupifupi makilomita 25 kum’mwera koma chakumadzulo kwa Phiri la Hermoni, kusandulikako kuyenera kuti kunachitikira pa chimodzi cha zitunda zake zazitali.
Pamene anali kupita ku “phiri lalitali,” Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: ‘Kodi anthu anena kuti ine ndine yani?’ Iwo anayankha kuti: “Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.” Ndiyeno Kristu anafunsa kuti: “Koma inu munena kuti ndine yani?” Petro anayankha kuti: “Ndinu Kristu.” Pamenepo, Yesu ‘anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za iye. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zoŵaŵa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.’—Marko 8:27-31.
Yesu anapitiriza kulonjeza kuti: ‘Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalaŵa imfa konse, kufikira akawona ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.’ (Marko 9:1; Mateyu 16:28) Lonjezo limeneli linakwaniritsidwa “atapita masiku asanu ndi limodzi,” pamene Yesu anali kupemphera ndipo anasandulika pamaso pa Petro, Yakobo, ndi Yohane. Luka akunena kuti izi zinachitika “masiku asanu ndi atatu” pambuyo pake, mwachiwonekere chifukwa chakuti anaphatikizapo tsiku limene lonjezo linapangidwa ndi pamene linakwaniritsidwa.—Mateyu 17:1, 2; Marko 9:2; Luka 9:28.
Sikunali Loto Kapena Chopeka
Kusandulika kwa Yesu sikunali loto. Atumwi atatuwo sakanalota loto limodzimodzilo, ndipo Yesu anakutcha “masomphenya.” Kumeneku sikutanthauza chinthu chopeka, pakuti liwu Lachigiriki logwiritsiridwa ntchito pa Mateyu 17:9 m’malo ena limasuliridwa kukhala ‘chowoneka.’ (Machitidwe 7:31) Choncho openyererawo anali ogalamuka kotheratu, ndipo ndi maso awo ndi makutu, anawonadi ndi kumva chimene chinali kuchitika.—Luka 9:32.
Pokhala wogalamuka koma wosadziŵa choti anene, Petro anapereka lingaliro la kumanga misasa itatu—umodzi wa Yesu, wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. (Luka 9:33) Mtambo womwe unapangika pamene Petro analankhula mwachiwonekere unasonyeza kukhalapo kwa Mulungu pa phiripo, monga kunaliri pa chihema chokomanako cha Aisrayeli m’chipululu. (Eksodo 40:34-38; Luka 9:34) Ndipotu atumwiwo sakanakhala mtulo pamene “Mulungu Atate” analengeza kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani iye.’—2 Petro 1:17, 18; Luka 9:35.
Chifukwa Chake Mose Anawoneka
Pamene kusandulikako kunachitika, Mose anali ‘wosadziŵa kanthu bi,’ popeza anafa zaka mazana ambiri kalelo. (Mlaliki 9:5, 10) Mofanana ndi Davide, iye sanaukitsidwe ndipo chotero sanalipo mwaumwini. (Machitidwe 2:29-31) Koma kodi nchifukwa ninji Mose anawoneka ndi Kristu m’masomphenya ameneŵa?
Mulungu anauza Mose kuti: ‘Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale awo, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mawu anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nawo zonse ndimuuzazi.’ (Deuteronomo 18:18) Petro mwachindunji anagwirizanitsa ulosiwu ndi Yesu Kristu. (Machitidwe 3:20-23) Pambali pa Yesu, Mose anali mneneri wamkulu koposa amene Mulungu anatumizira mtundu wa Israyeli.
Pali zofanana pakati pa Mose ndi Mose Wamkulu, Yesu Kristu. Mwachitsanzo, pamene iwo anali makanda, miyoyo yawo onse aŵiri inaikidwa pachiswe ndi olamulira ankhanza, koma Mulungu anatsimikizira kuti makandawo anapulumuka. (Eksodo 1:20–2:10; Mateyu 2:7-23) Amuna aŵiriwo anatha kusala kudya masiku 40 kuchiyambi kwa ntchito zawo monga atumiki apadera a Yehova. (Eksodo 24:18; 34:28; Deuteronomo 9:18, 25; Mateyu 4:1, 2) Ndipo Mose ndi Yesu anachita zozizwitsa mwa mphamvu ya Mulungu.—Eksodo 14:21-31; 16:11-36; Salmo 78:12-54; Marko 4:41; Luka 7:18-23; Yohane 14:11.
Mulungu anagwiritsira ntchito Mose kulanditsa Israyeli kuukapolo wa ku Igupto, mongadi momwe Yesu akudzetsera chimasuko chauzimu. (Eksodo 12:37–14:31; Yohane 8:31, 32) Mose anapatsidwa mwaŵi wa kukhala nkhoswe ya pangano la Chilamulo pakati pa Mulungu ndi Aisrayeli, pamene kuli kwakuti Yesu ndiye Nkhoswe ya pangano latsopano. (Eksodo 19:3-9; 34:3-7; Yeremiya 31:31-34; Luka 22:20; Ahebri 8:3-6; 9:15) Yehova anagwiritsiranso ntchito Mose kudzipangira dzina Lake pamaso pa Aisrayeli, Aigupto, ndi ena, mongadi momwe Yesu Kristu walemekezera dzina loyera la Yehova. (Eksodo 9:13-17; 1 Samueli 6:6; Yohane 12:28-30; 17:5, 6, 25, 26) Mwakuchititsa Mose kuwonekera ndi Yesu wosandulikayo, Mulungu anasonyeza kuti Kristu akatumikira m’maudindo ameneŵa kumlingo waukulu koposa.
Chifukwa Chake Eliya Anawonekera
Ngakhale kuti mneneri Eliya wakufayo sanaukitsidwe, kunali koyenerera kuti awonekere m’masomphenya akusandulikawo. Eliya anachita ntchito yaikulu m’kubwezeretsa kulambira kowona ndi kuyeretsa dzina la Yehova pakati pa Aisrayeli. Yesu Kristu anachita zofananazo pamene anali pa dziko lapansi ndipo adzachitadi zoposa kuti abwezeretse chipembedzo chowona ndi kulemekeza Atate wake wakumwamba kupyolera mwa Ufumu Waumesiya.
Mneneri Malaki anasonyeza kuti ntchito ya Eliya inachitira chithunzi ntchito ya mtsogolo. Kupyolera mwa Malaki, Mulungu anati: ‘Tawonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate awo; kuti ndisafike ndi kukantha dziko liwonongeke konse.’—Malaki 4:5, 6.
Ulosi umenewu unali ndi kukwaniritsidwa kwake kochepa m’ntchito ya Yohane Mbatizi. Yesu anasonyeza chimenechi pambuyo pa kusandulikako, pamene ophunzira ake anafunsa chifukwa chake alembi ananena kuti Eliya ayenera kudza choyamba—Mesiya asanabwere. Yesu ananena kuti: ‘Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziŵa iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo.’ Nkhaniyo ikuwonjezera kuti: ‘Ndipo chonchonso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo. Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nawo za Yohane Mbatizi.’—Mateyu 17:10-13.
Yohane anachita ntchito yonga ya Eliya pamene anabatiza Ayuda amene analapa machimo awo motsutsana ndi pangano la Chilamulo. Chofunika koposa nchakuti, Yohane anali kalambula bwalo wa Mesiya ndipo anadziŵikitsa Yesu Kristu. (Mateyu 11:11-15; Luka 1:11-17; Yohane 1:29) Koma kodi nchifukwa ninji ntchito ya Yohane inali kukwaniritsidwa kochepa kwa ulosi wa Malaki?
M’masomphenya ameneŵa, Eliya anawoneka akulankhula ndi Yesu. Izi zinali pambuyo pa imfa ya Yohane Mbatizi, chotero zinasonyeza kuti ntchito yonga ya Eliya ikachitidwa mtsogolo. Ndiponso, ulosiwo unasonyeza kuti ntchitoyo ikachitidwa lisanadze ‘tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.’ Chochitika chomadza mofulumira chimenecho chimaphatikizapo ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ pa Har–Magedon, kapena Armagedo. (Chibvumbulutso 16:14-16) Zimenezi zimatanthauza kuti kukhazikitsidwa kwa Ufumu wakumwamba wa Mulungu kukatsatira ntchito yolingana ndi zochita za Eliya ndi womloŵa m’malo wake, Elisa. Ndipo kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni zamakono za Yehova zakhala zikuchita ntchito yoloŵetsamo kubwezeretsa kulambira kowona ndi kukweza dzina la Mulungu.—Salmo 145:9-13; Mateyu 24:14.
Chifuno Chake
Kusandulikako kunamlimbitsa Yesu kaamba ka kuvutika ndi imfa zomwe anali pafupi kukumana nazo. Kumva Atate wake wakumwamba akulankhula za iye kukhala Mwana Wake wovomerezedwa kunalimbitsa chikhulupiriro cha Yesu. Koma kodi nchiyani chimene kusandulika kunachita kwa ena?
Kusandulika kwa Yesu kunalimbitsanso chikhulupiriro cha openyerera. Kunakhomereza m’maganizo awo mfundo yakuti Yesu Kristu ndiye Mwana wa Mulungu. Ndithudi, popeza kuti Wolankhulira Wamkulu wa Yehova, Mawuyo, anali pakati pawo, iwo anamva mawu enieni a Mulungu mwiniyo akulengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Ngakhale kuti Yehova anachitira umboni wofananawo pamene Yesu anali kubatizidwa, pa kusandulikako, Mulungu anawonjezera kuti ophunzirawo ayenera kumvera Mwana Wake.—Mateyu 3:13-17; 17:5; Yohane 1:1-3, 14.
Kusandulikako kunalimbitsa chikhulupiriro mwanjira inanso. Mkati mwa masomphenyawo, Yesu, “Mose,” ndi “Eliya” analankhula za ‘kumuka kwake kumene [Kristu] ati adzatsiriza ku Yerusalemu.’ (Luka 9:31) Liwu lakuti “kumuka” latembenuzidwa kuchokera ku liwu Lachigiriki lakuti eʹxo·dos. Eksodo ameneyu, kapena kumuka, mwachiwonekere anaphatikizapo ponse paŵiri imfa ndi chiukiriro cha kumoyo wauzimu cha Yesu chochitidwa ndi Mulungu. (1 Petro 3:18) Choncho kusandulika kunalimbitsa chikhulupiriro m’kuuka kwa Kristu. Iko makamaka kunakulitsa chikhulupiriro mwakupereka umboni wogomeka maganizo wakuti Yesu akakhala Mfumu ya Ufumu Waumesiya wa Mulungu. Ndiponso, masomphenyawo anasonyeza kuti Ufumuwo ukakhala waulemerero.
Kusandulikako kunalimbitsanso chikhulupiriro muulosi wa m’Malemba. Zaka 32 pambuyo pake (pafupifupi 64 C.E.), Petro anakumbukirabe chokumana nacho chimenechi nalemba kuti: ‘Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziŵitsani mphamvu ndi mawonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ine ndikondwera naye; ndipo mawu aŵa ochokera kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m’phiri lopatulika lija. Ndipo tiri nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu.’—2 Petro 1:16-19.
Tanthauzo Lake kwa Inu
Inde, Petro anawona kusandulika kwa Yesu kukhala chitsimikiziritso cha mawu aulosi a Mulungu. Mtumwi Yohane nayenso angakhale analoza ku masomphenya ameneŵa pamene ananena kuti: ‘Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.’ (Yohane 1:14) Mofananamo, kusandulikako kungakulitse chikhulupiriro chanu m’mawu aulosi a Yehova.
Kusandulika ndi zochitika zogwirizana nako zingalimbitse chikhulupiriro chanu chakuti Yesu Kristu ndiye Mwana wa Mulungu ndi Mesiya wolonjezedwa. Kungakhwimitse chikhulupiriro chanu m’kuuka kwa Yesu kunka kumwamba ku moyo wauzimu. Masomphenya ozizwitsa ameneŵa ayeneranso kukulitsa chikhulupiriro chanu m’boma la Mulungu, popeza kuti kusandulikako kunali kusonyezeratu ulemerero ndi mphamvu Yaufumu za Kristu.
Kuli makamaka kolimbitsa chikhulupiriro kudziŵa kuti kusandulika kwa Kristu kunasonya ku tsiku lathu, pamene kukhalapo kwa Yesu kuli kwenikweni. (Mateyu 24:3-14) Chiyambire 1914 iye wakhala akulamulira kumwamba monga Mfumu yoikidwa ndi Mulungu. Ulamuliro ndi mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu zidzagwiritsiridwa ntchito posachedwapa motsutsana ndi adani onse a ulamuliro waumulungu, kutsegulira njira dziko latsopano. (2 Petro 3:13) Mukhoza kusangalala ndi madalitso ake osatha ngati mumasonyeza chikhulupiriro m’zinthu zodabwitsa zosonyezedwa m’kusandulika kwa Yesu Kristu.