-
Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
MUTU
Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?
1, 2. Kodi munthu angasangalale kwambiri ataitanidwa ndi ndani, nanga ndi funso liti limene tingadzifunse?
KODI ndi nthawi iti imene munasangalala kwambiri munthu wina atakuitanani kumwambo winawake? Mwina mungakumbukire nthawi imene munaitanidwa kumwambo winawake wapadera, monga ku ukwati wa mnzanu wa pamtima. Kapena mungakumbukire tsiku limene anakuitanani kuti mukayambe ntchito inayake yofunika kwambiri. Ngati munaitanidwapo ku zochitika ngati zimenezi, n’zosakayikitsa kuti munasangalala kwambiri ndiponso munamva kuti mwalemekezedwa. Komabe zoona zake n’zakuti aliyense wa ife, akuitanidwa kuti achite zinthu zinazake zofunika kwambiri kuposa zimenezi. Ndipotu zilizonse zimene tingasankhe pa nkhani imeneyi zingakhudze moyo wathu chifukwa ndi nkhani yofunika kwambiri.
2 Kodi amene akutiitana ndi ndani? Ndi Yesu Khristu, Mwana wobadwa yekha wa Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse. Mawu amene iye ananena potiitana ali m’Baibulo palemba la Maliko 10:21. Iye anati: ‘Bwera ukhale wotsatira wanga.’ Ngakhale kuti Yesu ananena mawu amenewa kwa munthu mmodzi, mawuwa akugwiranso ntchito kwa aliyense wa ife. Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Popeza Yesu akundiitana, kodi ineyo ndichite chiyani?’ Yankho la funso limeneli lingaoneke ngati losavuta chifukwa tingaganize kuti palibe amene angakane ataitanidwa ndi Yesu. Koma n’zodabwitsa kuti anthu ambiri amakana. N’chifukwa chiyani amakana?
3, 4. (a) Kodi munthu amene anapita kwa Yesu n’kufunsa zimene angachite kuti apeze moyo wosatha, anali ndi zinthu ziti zimene anthu ambiri amazisirira? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anaona makhalidwe ati abwino mwa wolamulira wachinyamata amene anali wolemera?
3 Mwachitsanzo, taganizirani munthu amene anaitanidwa ndi Yesu pamasom’pamaso zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Munthu ameneyo anali wolemekezeka kwambiri. Iye anali ndi zinthu zitatu zimene anthu ambiri amazisirira ndiponso amaziona kuti n’zofunika kwambiri. Anali ndi zinthu monga chuma, udindo ndiponso anali wachinyamata. Ponena za munthuyu, Baibulo limanena kuti anali ‘mnyamata,’ anali “wolemera kwambiri” ndiponso anali “wolamulira.” (Mateyu 19:20; Luka 18:18, 23) Komatu panali chinthu china chofunika kwambiri chokhudza mnyamatayu. Iye anamva za Mphunzitsi Waluso, Yesu, ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anamvazo.
4 M’masiku amenewo, olamulira ambiri ankalephera kulemekeza Yesu. (Yohane 7:48; 12:42) Koma wolamulira wachinyamatayu anachita zinthu mosiyana ndi olamulira enawo. Baibulo limati: “Pamene [Yesu] ankachoka kumeneko, mwamuna wina anamuthamangira n’kugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: ‘Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?’” (Maliko 10:17) Mungaone kuti munthuyu anali ndi chidwi chofuna kulankhula ndi Yesu. Iye anachita zinthu zimene munthu wosauka ndiponso wonyozeka angachite, chifukwa anathamangira Khristu anthu onse akuona. Komanso atamupeza, anagwada pamaso pake mwaulemu. Choncho, mungaone kuti wolamulira wachinyamatayu anali wodzichepetsa ndithu komanso ankazindikira zosowa zake zauzimu. Yesu anasangalala ndi makhalidwe abwinowa. (Mateyu 5:3; 18:4) Choncho n’zosadabwitsa kuti “Yesu anamuyang’ana ndipo anamukonda.” (Maliko 10:21) Kodi Yesu anayankha bwanji funso limene mnyamatayo anafunsa?
Mwayi Wapadera Kwambiri
5. Kodi Yesu anamuyankha bwanji mnyamata wolemera uja, ndipo tikudziwa bwanji kuti “chinthu chimodzi” chimene chimasoweka mwa iye sichinali choti akhale wosauka? (Onaninso mawu a m’munsi.)
5 Poyankha, Yesu anasonyeza kuti Atate wake anali atapereka kale mfundo zofunika zothandiza anthu kuti adzalandire moyo wosatha. Yesu anauza mnyamatayo mfundo za m’Malemba zimene ankayenera kutsatira, koma iye ananena motsimikiza kuti amatsatira mfundo za m’Chilamulo cha Mose mokhulupirika. Komabe, chifukwa choti Yesu anali ndi nzeru zakuya, anaona zimene zinali mumtima mwa wolamulirayo. (Yohane 2:25) Iye anaona kuti wolamulirayo anali ndi vuto linalake lalikulu lokhudza ubwenzi wake ndi Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe.” Kodi ‘chinthu chimodzicho’ chinali chiyani? Yesu anati: “Pita ukagulitse zinthu zimene uli nazo ndipo ndalama zake ukapatse osauka.” (Maliko 10:21) Kodi Yesu ankatanthauza kuti munthu ayenera kukhala wosauka kuti azitumikira bwino Mulungu? Ayi.a Apa, Khristu ankaphunzitsa munthuyu mfundo ina yofunika kwambiri.
6. Kodi Yesu anaitana wolamulira wachinyamata amene analinso wolemera, kuti achite chiyani, nanga zimene wachinyamatayo anachita zinasonyeza kuti anali ndi vuto lotani mumtima mwake?
6 Pofuna kusonyeza chimene chinkasowa mwa mnyamatayo, Yesu anam’patsa mwayi wapadera kwambiri pomuuza kuti: ‘Bwera ukhale wotsatira wanga.’ Wolamulirayo anali ndi mwayi waukulu chifukwa Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba anamuitana pamasom’pamaso kuti azimutsatira. Kuwonjezera pamenepa, Yesu anamulonjeza madalitso osaneneka chifukwa anamuuza kuti: “Udzakhala ndi chuma kumwamba.” Kodi wolamulira wachinyamatayu, amene analinso wolemera, anavomera mwayi wapadera kwambiriwu? Nkhaniyi imati: “Iye atamva mawu amenewo anakhumudwa ndipo anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.” (Maliko 10:21, 22) Choncho, zimene Yesu ananena zomwe mnyamatayo sankaziyembekezera, zinachititsa kuti vuto limene linali mumtima mwake lionekere. Iye ankakonda kwambiri chuma chake ndiponso ankasangalala ndi udindo umene anali nawo komanso ulemu umene anthu ankamupatsa chifukwa cha zimenezi. N’zomvetsa chisoni kuti ankakonda kwambiri zinthu zimenezi kuposa mmene ankakondera Khristu. Choncho “chinthu chimodzi” chimene chinkasowa mwa iye chinali chakuti iye sankakonda Yesu ndiponso Yehova ndi mtima wake wonse. Chifukwa chakuti wachinyamatayu analibe chikondi chimenechi, anakana mwayi wapadera wokhala wotsatira wa Yesu. Komano, kodi inuyo nkhaniyi ikukukhudzani bwanji?
7. N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti mawu amene Yesu ananena poitana wolamulira uja akukhudzanso ifeyo masiku ano?
7 Mawu amene Yesu ananena poitana munthu uja, sakukhudza wolamulira yekhayo kapenanso anthu ochepa chabe. Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, . . . apitirize kunditsatira.” (Luka 9:23) Palembali, mawu akuti “munthu” akutanthauza kuti aliyense angakhale wotsatira wa Khristu ngati “akufuna.” Mulungu amakokera kwa Mwana wake anthu oona mtima ngati amenewo. (Yohane 6:44) Aliyense ali ndi mwayi woti angakhale wotsatira wa Yesu, kaya ndi wolemera, wosauka ngakhalenso wochokera mu fuko kapena mtundu uliwonse wa anthu. Choncho, mawu amene Yesu ananenawa sakukhudza anthu okhawo amene analipo pa nthawi imene iye ananena zimenezi. Mawu a Yesu onena kuti, ‘bwera ukhale wotsatira wanga’ akukhudzanso inuyo. N’chifukwa chiyani muyenera kutsatira Khristu? Nanga munthu ayenera kuchita chiyani kuti asonyeze kuti ndi wotsatira wa Khristu?
-
-
Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
a Yesu sanauze aliyense amene ankamutsatira kuti asiye chuma chake chonse. Ngakhale kuti iye ananenapo kuti n’zovuta kwambiri kuti munthu wachuma akalowe mu Ufumu wa Mulungu, ananenanso kuti: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Maliko 10:23, 27) Ndipotu anthu angapo olemera anakhala otsatira a Khristu. Iwo anapatsidwa malangizo apadera mumpingo wa Chikhristu okhudza chumacho koma sanauzidwe kuti apereke chuma chawo chonse kwa anthu osauka.—1 Timoteyo 6:17.
-