Tikukulandirani ku Moyo Wabwino Koposa!
“Kaya tikhala ndi moyo kapena tifa, ndife a Yehova.”—AROMA 14:8.
1. Pankhani ya moyo wabwino koposa, kodi Yesu anaphunzitsa chiyani?
YEHOVA amafuna kuti tikhale ndi moyo wabwino koposa. Anthu angakhale ndi moyo m’njira zosiyanasiyana, koma njira imodzi yokha ndiyo yabwino koposa. Chofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo wabwino ndicho kukhala mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena ndiponso kuphunzira kwa Mwana wake Yesu Khristu. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kulambira Mulungu ndi mzimu ndi choonadi, ndipo anawalamula kuti apange ophunzira. (Mat. 28:19, 20; Yoh. 4:24) Tikamachita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yesu, timasangalatsa Yehova ndipo Iye amatidalitsa.
2. M’nthawi ya atumwi, kodi anthu ambiri anatani atamva uthenga wa Ufumu, ndipo kutsatira “Njirayo” kunkatanthauza chiyani?
2 Anthu amene ali ndi “maganizo oyenerera moyo wosatha” akayamba kukhulupirira n’kubatizidwa, timakhala ndi zifukwa zomveka zowauzira kuti, “Tikukulandirani ku moyo wabwino koposa!” (Mac. 13:48) M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri a mitundu yosiyanasiyana anaphunzira choonadi ndipo anasonyeza poyera kuti anadzipereka kwa Mulungu mwa kubatizidwa. (Mac. 2:41) Ophunzira oyambirira amenewo ankatsatira “Njirayo.” (Mac. 9:2; 19:23) Mawu akuti kutsatira “Njirayo,” anali oyenerera chifukwa anthu amene anakhala otsatira Khristu ankachita zinthu mosonyeza kuti akukhulupirira Yesu Khristu ndiponso kuti akutsatira chitsanzo chake.—1 Pet. 2:21.
3. Kodi anthu a Yehova amabatizidwa chifukwa chiyani, ndipo ndi angati amene abatizidwa pa zaka 10 zapitazo?
3 Ntchito yopanga ophunzira yapita patsogolo mofulumira m’masiku otsiriza ano ndipo panopa ikugwiridwa m’mayiko oposa 230. Pazaka 10 zapitazi, anthu oposa 2,700,000 anasankha kutumikira Yehova ndipo anabatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa iye. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu oposa 5,000 ankabatizidwa mlungu uliwonse. Anthu amasankha kubatizidwa chifukwa chokonda Mulungu, kudziwa Malemba ndiponso kukhulupirira zimene Malembawo amanena. Ubatizo ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu, chifukwa pamenepa m’pamene munthu amayambira kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Umasonyezanso kuti tikukhulupirira zoti Yehova atithandiza kumutumikira mokhulupirika, ngati mmene anathandizira atumiki ake akale kuyenda m’njira yake.—Yes. 30:21.
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kubatizidwa?
4, 5. Tchulani madalitso amene munthu amapeza akabatizidwa.
4 N’kutheka kuti inuyo mwaphunzira za Mulungu, mwasintha moyo wanu, ndipo panopa ndinu wofalitsa wosabatizidwa. Zimenezi zili bwino kwambiri. Koma kodi munapemphera kwa Mulungu kuti mukufuna kudzipereka kwa iye, ndipo kodi mukufuna mutabatizidwa? N’kutheka kuti pa zimene mwaphunzira m’Baibulo, tsopano mwaona kuti cholinga chanu chachikulu chiyenera kukhala kutamanda Yehova, osati kungodzisangalatsa kapena kufunafuna chuma. (Werengani Salmo 148:11-13; Luka 12:15.) Ndiyeno kodi ndi madalitso otani amene munthu amapeza akabatizidwa?
5 Mukadzakhala Mkhristu wodzipereka ndi wobatizidwa, moyo wanu udzakhala waphindu kwambiri. Mudzasangalala kwambiri chifukwa chochita zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:1, 2) Mzimu woyera wa Mulungu udzakuthandizani kukhala ndi makhalidwe abwino monga mtendere ndi chikhulupiriro. (Agal. 5:22, 23) Mulungu adzayankha mapemphero anu ndipo adzakudalitsani pamene mukuyesetsa kusintha moyo wanu kuti zochita zanu zigwirizane ndi Mawu ake. Mudzasangalala ndi utumiki wanu ndipo kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kudzathandiza kuti chiyembekezo chanu cha moyo wosatha chilimbe. Komanso kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa kudzasonyeza kuti mukufunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova.—Yes. 43:10-12.
6. Kodi ubatizo wathu umasonyeza chiyani?
6 Tikadzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa, timalengeza poyera kuti ndife a Yehova. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kunena zoona, palibe mmodzi wa ife amene amadzikhalira moyo iye yekha, ndipo palibe amene amafa mwa iye yekha; chifukwa kaya tikhale ndi moyo, tikhalira Yehova, ndipo ngati tifa, tifera Yehova. Chotero kaya tikhala ndi moyo kapena tifa, ndife a Yehova.” (Aroma 14:7, 8) Mulungu watilemekeza chifukwa chakuti watipatsa ufulu wosankha. Tikasankha kukhala ndi moyo umenewu chifukwa choti timakonda Mulungu, timasangalatsa mtima wake. (Miy. 27:11) Ubatizo wathu umasonyeza kuti tinadzipereka kwa Mulungu ndipo tinalengeza poyera kuti Yehova ndiye Wolamulira wathu. Umasonyezanso kuti tinasankha kukhala ku mbali yake pankhani ya ulamuliro wa m’chilengedwe chonse. (Mac. 5:29, 32) Zikatere, Yehova nayenso amakhala ku mbali yathu. (Werengani Salmo 118:6.) Ubatizo umachititsanso kuti tipeze madalitso auzimu ambiri panopo ndiponso m’tsogolo.
Timapeza Abale Otikonda Kwambiri
7-9. (a) Kodi Yesu anawatsimikizira chiyani anthu amene anasiya zinthu zawo zonse ndi kuyamba kum’tsatira? (b) Kodi lonjezo la Yesu lomwe lili pa Maliko 10:29, 30 likukwaniritsidwa bwanji?
7 Mtumwi Petulo anauza Yesu kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani; nanga n’chiyani chimene ife tidzapezapo?” (Mat. 19:27) Apa, Petulo ankafuna kudziwa kuti iyeyo komanso ophunzira ena a Yesu adzapeza chiyani m’tsogolo. Kuti agwire ntchito yolalikira Ufumu ndi mtima wonse, analolera kusiya zinthu zina zofunika. (Mat. 4:18-22) Kodi Yesu anawatsimikizira chiyani pa nkhaniyi?
8 Malinga ndi zimene Maliko analemba pa nkhani yomweyi, Yesu anasonyeza kuti ophunzira ake adzakhala m’gulu la abale. Iye anati: “Palibe amene anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, amene tsopano lino sadzapeza zochuluka kuwirikiza nthawi 100 m’nthawi ino, nyumba ndi abale ndi alongo ndi amayi ndi ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo, ndipo m’dongosolo la zinthu limene likubweralo, moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjezazi, m’nthawi ya atumwi, Akhristu ena anapereka “nyumba” zawo ndiponso anakhala “abale ndi alongo ndi amayi” a okhulupirira anzawo. Ena mwa Akhristu amene anachita zimenezi, anali Lidiya, Akula, Purisikila ndi Gayo.—Mac. 16:14, 15; 18:2-4; 3 Yoh. 1, 5-8.
9 Zimene Yesu ananenazi zikukwaniritsidwa kwambiri masiku ano. “Minda” imene otsatira ake amasiya ikutanthauza zinthu zimene anthu ambiri amalolera kusiya n’cholinga chopititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’mayiko osiyanasiyana. Anthu amenewa akuphatikizapo amishonale, ogwira ntchito pa Beteli, komanso atumiki amene amatumizidwa m’mayiko osiyanasiyana kukagwira ntchito zomangamanga. Abale ndi alongo ambiri asiya nyumba zawo n’cholinga choti azikhala moyo wosafuna zambiri. Timasangalala kumva zimene akumana nazo zimene zimasonyeza mmene Yehova akuwasamalirira ndiponso mmene akusangalalira chifukwa chom’tumikira. (Mac. 20:35) Popeza atumiki obatizidwa onse a Yehova ali m’gulu la padziko lonse la abale, iwo angapeze madalitso amene amabwera chifukwa cha “kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu].”—Mat. 6:33.
Timakhala Otetezeka “M’ngaka Yake”
10, 11. Kodi ‘ngaka ya Wam’mwambamwamba’ n’chiyani, ndipo tingatani kuti tikhalemo?
10 Kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa kumatibweretseranso madalitso aakulu. Timakhala ndi mwayi wokhala “m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba.” (Werengani Salmo 91:1.) Malowa ndi ophiphiritsa ndipo ndi otetezeka mwauzimu. Tikakhala m’malo amenewa palibe chimene chingatiwononge mwauzimu. Malowa ndi “ngaka” chifukwa ndi obisika kwa anthu amene saona zinthu mwauzimu ndipo sakhulupirira Mulungu. Tikamachita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwathu ndiponso tikamakhulupirira Yehova ndi mtima wonse, zimakhala ngati tikumuuza kuti: ‘Ndinu pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndim’khulupirira.’ (Sal. 91:2) Yehova Mulungu amakhala malo otetezeka amene tifunika kukhalamo. (Sal. 91:9) Ndithudi, palibe malo amene tingakhale omwe ndi otetezeka kwambiri kuposa amenewa.
11 Munthu akakhala “m’ngaka” ya Yehova zimasonyezanso kuti ali naye paubwenzi wolimba. Zimenezi zimayamba pamene tadzipereka ndi kubatizidwa. Kenako, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu mwa kuyandikira kwa iye. Kuphunzira Baibulo, kupemphera mochokera pansi pamtima ndiponso kumumvera ndi mtima wonse n’kumene kumatithandiza kuchita zimenezi. (Yak. 4:8) Yesu sanasiyepo kukhulupirira Mlengi ndipo palibe munthu amene anakhalapo paubwenzi wolimba ndi Yehova kuposa iye. (Yoh. 8:29) Choncho, tisakayikire kuti Yehova ali ndi mphamvu zakuti angatithandize kukwaniritsa lumbiro lathu lodzipereka kwa iye ndiponso kuti amafunitsitsa kutithandiza. (Mlal. 5:4) Zinthu zauzimu zimene Mulungu wapereka kwa anthu ake ndi umboni wamphamvu wakuti amatikonda ndipo amatifunira zabwino pom’tumikira.
Muziona Kuti Paradaiso Wathu Wauzimu Ndi Wofunika Kwambiri
12, 13. (a) Kodi paradaiso wauzimu n’chiyani? (b) Kodi anthu atsopano tingawathandize bwanji?
12 Kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa kumatibweretseranso mwayi wokhala m’paradaiso wauzimu. Paradaiso ameneyu ndi malo auzimu apadera amene Akhristu omwe ali pamtendere ndi Yehova Mulungu ndiponso Akhristu anzawo amakhalamo. (Sal. 29:11; Yes. 54:13) M’dzikoli mulibe malo amene tingawayerekezere ndi paradaiso wauzimu ameneyu. Zimenezi zimaonekera kwambiri pamisonkhano ya mayiko, pamene abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana ndiponso ochokera m’mitundu yosiyanasiyana amasonkhana pamodzi mogwirizana ndiponso mwachikondi kwambiri.
13 Paradaiso wauzimu amene tikukhalamo amasiyana kwambiri ndi makhalidwe oipa amene ali m’dzikoli masiku ano. (Werengani Yesaya 65:13, 14.) Tikamalengeza uthenga wa Ufumu, timakhala ndi mwayi woitanira anthu ena kuti alowe nawo m’paradaiso wauzimu ameneyu. Ndiponso ndi mwayi kuthandiza anthu amene angoyamba kumene kusonkhana nafe. Anthu amenewa angapindulenso ndi zimene angaphunzire tikamalalikira nawo. Akulu akatipempha kuti tiwaphunzitse atsopano ena, timakhala ndi mwayi ngati mmene zinalili kwa Akula ndi Purisikila amene ‘anafotokoza njira ya Mulungu molondola’ kwa Apolo.—Mac. 18:24-26.
Pitirizanibe Kuphunzira kwa Yesu
14, 15. Kodi tili ndi zifukwa zomveka ziti zotilimbikitsa kuti tipitirizebe kuphunzira kwa Yesu?
14 Tili ndi zifukwa zomveka zotilimbikitsa kuti tipitirizebe kuphunzira kwa Yesu. Iye asanakhale munthu padzikoli, anakhala zaka zosawerengeka akugwira ntchito ndi Atate ake. (Miy. 8:22, 30) Iye ankadziwa kuti moyo wabwino koposa wagona pa kutumikira Mulungu ndi kuchitira umboni choonadi. (Yoh. 18:37) Zinali zodziwikiratu kwa Yesu kuti kukhala moyo wosiyana ndi umenewu, kunali kudzikonda ndiponso kusaganiza bwino. Iye ankadziwa kuti adzayesedwa kwambiri kenako n’kuphedwa. (Mat. 20:18, 19; Aheb. 4:15) Popeza Yesu ndi chitsanzo chathu, iye anatiphunzitsa mmene tingakhalire ndi mtima wosagawanika.
15 Yesu atangobatizidwa, Satana anam’yesa kuti amusiyitse kukhala moyo wabwino koposa koma sizinatheke. (Mat. 4:1-11) Zimenezi zikutiphunzitsa kuti ngakhale Satana atatiyesa chotani, tikhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Iye makamaka amalimbana ndi anthu amene akuganiza zobatizidwa kapena amene angobatizidwa kumene. (1 Pet. 5:8) Nthawi zina, amene angatitsutse ndi achibale athu otiganizira koma amene anauzidwa zabodza zokhudza Mboni za Yehova. Koma mayesero oterewo angatipatse mwayi wosonyeza makhalidwe abwino monga ulemu ndiponso luso. Mwayi umenewu ungapezeke tikamayankha mafunso awo komanso tikamawalalikira. (1 Pet. 3:15) Choncho, zimenezi zingachititse kuti anthu amene timalankhula nawo asinthe maganizo awo.—1 Tim. 4:16.
Pitirizanibe Kukhala Moyo Wabwino Koposa
16, 17. (a) Kodi ndi mfundo zitatu ziti zofunika kuti tikhale ndi moyo wabwino zomwe zikupezeka pa Deuteronomo 30:19, 20? (b) Kodi Yesu, Yohane ndi Paulo anasonyeza bwanji kufunika kwa zimene Mose analemba?
16 Zaka 1,500 Yesu asanabwere padzikoli, Mose analangiza Aisiraeli kuti asankhe moyo wabwino koposa. Iye anati: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira Iye.” (Deut. 30:19, 20) Aisiraeli anakhala osakhulupirika kwa Mulungu, koma mfundo zitatu zimene Mose anatchula zomwe n’zofunika kuti munthu akhale ndi moyo wabwino, sizinasinthe. Yesu ndi anthu ena anadzatchulanso mfundo zomwezi.
17 Choyamba, ‘tiyenera kukonda Yehova Mulungu wathu.’ Timasonyeza kuti timakonda Mulungu mwa kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. (Mat. 22:37) Chachiwiri, ‘tiyenera kumvera mawu a Yehova’ mwa kuphunzira Mawu ake ndiponso kumvera malamulo ake. (1 Yoh. 5:3) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kupezeka pamisonkhano yampingo nthawi zonse chifukwa n’kumene timaphunzira Baibulo. (Aheb. 10:23-25) Chachitatu, ‘tiyenera kum’mamatira Yehova.’ Kaya tikumane ndi zotani, tiyeni nthawi zonse tizikhulupirira Mulungu ndiponso tizitsatira Mwana wake.—2 Akor. 4:16-18.
18. (a) Mu chaka cha 1914, kodi Nsanja ya Olonda inafotokoza zotani zokhudza choonadi? (b) Kodi masiku ano tiyenera kumva bwanji pa nkhani ya kuwala kwa choonadi?
18 Kutsatira choonadi cha m’Baibulo ndi dalitso lalikulu kwambiri. Mu chaka cha 1914, mu Nsanja ya Olonda munali mfundo zofunika izi: “Kodi sitinganene kuti tili ndi mwayi ndiponso ndife achimwemwe? Nanga Mulungu wathu, kodi si wokhulupirika? Kodi alipo amene angatsutse zimenezi? Tikukhulupirira kuti palibe, chifukwa akanakhalapo akananena. Palibe n’komwe zinthu zabwino zimene tingazipeze kwina kulikonse kuposa zimene tapeza m’Mawu a Mulungu. . . . N’zovuta kufotokoza mtendere, chimwemwe ndiponso madalitso amene tapeza chifukwa cha kudziwa bwino choonadi chonena za Mulungu. Nkhani yonena za Nzeru, Chilungamo, Mphamvu ndiponso Chikondi cha Mulungu imatifika pa mtima kwabasi. Sitingachitirenso mwina, koma kupitiriza kuphunzira za Mulungu wathu.” (Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 15, 1914, masamba 377 ndi 378) Mpaka pano timayamikirabe choonadi ndiponso kuwala kwauzimu. Ndipotu, panopo m’pamene tifunika kusangalala kwambiri kuti ‘tikuyenda m’kuwala kwa Yehova.’—Yes. 2:5; Sal. 43:3; Miy. 4:18.
19. N’chifukwa chiyani anthu amene akuchita bwino ndipo angayenerere kubatizidwa afunika kuchita zimenezi mwamsanga?
19 Ngati mukufuna ‘kuyenda m’kuwala kwa Yehova’ koma simunadziperekebe kwa Mulungu ndi kubatizidwa, musazengereze. Chitani zilizonse zimene mungathe kuti mukwaniritse zimene Baibulo limafuna kuti munthu abatizidwe. Ndipo kuchita zimenezi ndiye njira yaikulu imene tingasonyezere kuyamikira zimene Mulungu ndi Khristu atichitira. Perekani kwa Yehova moyo wanu, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa chilichonse chimene tingapereke. Chitani zinthu zosonyeza kuti mukufuna kuchita zimene Mulungu amafuna mwa kutsatira Mwana wake. (2 Akor. 5:14, 15) Umenewu ndiwo moyo wabwino koposa.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ubatizo wathu umaimira chiyani?
• Kodi kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa kumabweretsa madalitso otani?
• N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzira kwa Yesu?
• N’chiyani chingatithandize kupitirizabe kukhala moyo wabwino koposa?
[Chithunzi patsamba 25]
Ubatizo wanu umasonyeza kuti mwasankha moyo wabwino koposa
[Zithunzi patsamba 26]
Kodi ndinu otetezeka “m’ngaka yake”?