Miyambo
8 Nzerutu ikuitana,
Ndipo kuzindikira kukufuula.+
3 Pambali pa mageti, olowera mumzinda,
Pakhomo lolowera mumzindawo,
Ikungokhalira kufuula mokweza kuti:+
6 Mvetserani, chifukwa zimene ndikulankhula ndi zofunika.
Pakamwa panga pamalankhula zinthu zabwino.
7 Chifukwa pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,
Ndipo milomo yanga imanyansidwa ndi zoipa.
8 Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.
Pa mawu onsewo palibe abodza kapena achinyengo.
9 Ndi osavuta kumva kwa munthu wozindikira
Komanso ndi olondola kwa anthu odziwa zinthu.
10 Landirani malangizo* anga osati siliva,
Komanso kudziwa zinthu mʼmalo mwa golide woyenga bwino kwambiri,+
11 Chifukwa nzeru ndi zabwino kwambiri kuposa miyala ya korali.*
Zinthu zina zonse zamtengo wapatali sizingafanane nazo.
12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.
Ndimadziwa zinthu ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+
13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+
Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso mawu achinyengo.+
16 Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,
Ndipo anthu olemekezeka amaweruza mwachilungamo.
19 Zimene munthu amapeza kwa ine nʼzabwino kuposa golide, ngakhale golide woyengedwa bwino kwambiri,
Ndipo mphatso zimene ndimapereka nʼzabwino kuposa siliva wabwino kwambiri.+
20 Ndimayenda mʼnjira yachilungamo,
Komanso pakati pa misewu yachilungamo.
21 Anthu amene amandikonda, ndimawapatsa cholowa chamtengo wapatali,
Ndipo ndimadzazitsa nyumba zawo zosungiramo zinthu.
22 Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova,+
Ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.+
25 Mapiri asanaikidwe mʼmalo ake,
Komanso mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinabadwa,
26 Iye asanapange dziko lapansi ndi nthaka yake,
Kapena zibuma zoyamba za dothi lapadziko lapansi.
27 Pamene ankakonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+
Pamene ankaika malire pakati pa mlengalenga ndi nyanja,+
28 Pamene ankakhazikitsa* mitambo kumwamba,
Pamene ankakhazikitsa akasupe a madzi akuya,
29 Pamene ankaikira nyanja lamulo
Kuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+
Pamene ankakhazikitsa maziko a dziko lapansi,
30 Pa nthawi imeneyo, ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+
Iye ankasangalala kwambiri ndi ine+ tsiku ndi tsiku.
Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+
31 Ndinkasangalala ndi dziko lapansi limene anakonza kuti anthu azikhalamo,
Ndipo ana a anthu ndi amene ankandisangalatsa kwambiri.*
32 Tsopano ana anga, ndimvereni.
Ndithu, osangalala ndi amene amayenda mʼnjira zanga.