Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kusankha Atumwi Ake
PAPITA pafupifupi chaka chimodzi ndi theka kuyambira pamene Yohane Mbatizi anadziwikitsa Yesu kukhala “Mwanawankhosa wa Mulungu,” ndi pamene Yesu anayamba uminisitala wake wapoyera. Panthawiyo, Andreya, Simoni Petro, Yohane, ndipo mwinamwake Yakobo (mbale wake wa Yohane), kuphatikizapo Filipo ndi Nataniyeli (wotchedwanso Batolomeyo), anali atakhala ophunzira ake oyamba. M’nthawi yokwanira, ena ambiri anagwirizana nawo m’kutsatira Kristu.
Tsopano Yesu wakonzekera kusankha atumwi ake. Amenewa adzakhala atsamwali ake apafupi amene adzaphunzitsidwa mwapadera. Koma asanawasankhe, Yesu akumka m’phiri ndi kuthera usiku wathunthu kupemphera, mwachiwonekere kupempha dalitso la Mulungu kukhala pa aliyense wa iwo. Pamene kucha akuitana ophunzira ake ndipo pakati pawo akusankhapo 12. Komabe, popeza kuti iwo akupitirizabe kukhala ophunzitsidwa ndi Yesu, iwo akali kutchedwabe ophunzira.
Asanu ndi mmodzi amene Yesu akusankha, otchulidwa pamwambapa, ali awo amene anakhala ophunzira ake oyamba. Mateyu, amene anamuitana pa ofesi wake wamsonkho, nayenso wasankhidwa. Asanu ena osankhidwawo ndiwo Yudase (Wotchedwanso Tadeyo), Yudase Iskariote, Simoni Mkanani, Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo. Yakobo ameneyu akutchedwanso Yakobo Wamng’ono, mwina mwake kumlekanitsa ndi mtumwi Yakobo winayo.
Podzafika tsopano 12 amenewa anali atakhala ndi Yesu kwanthawi zingapo ndipo, iye akuwadziwa bwino lomwe. Kwenikweni, angapo a iwo ngachibale a iyemwini. Mwachiwonekera Yakobo ndi mbale wake Yohane ndi asuwani ake a Yesu. Ndipo kukuwonekera ngati kuti Alifeyo anali mbale wa Yosefe, atate wolera wa Yesu. Chotero mtumwi Yakobo, mwana wa Alifeyo, akanakhalanso msuwani wa Yesu.
Ndithudi, Yesu, analibe vuto la kukumbukira maina a atumwi ake. Koma kodi inu mungawakumbukire? Eya, ingokumbukirani kuti pali awiri otchedwa Simoni, awiri otchedwa Yakobo, ndi awiri otchedwa Yudase ndi kuti Simoni ali ndi mbale wake Andreya, ndi kuti Yakobo ali ndi mbale wake Yohane. Ndiyo mfungulo yokumbukirira atumwi asanu ndi atatu. Anai enawo amaphatikizapo wokhometsa msonkho (Mateyu), ndi uja amene pambuyo pake anakaikira (Tomasi), ndi uja amene anaitanidwa atakhala pansi pa mtengo (Natanieli), ndi bwenzi lake Filipo.
Khumi ndi mmodzi a atumwiwo ngochokera ku Galileya, gawo la kwawo kwa Yesu. Nataniyeli ngwa ku Kana. Poyambirira Filipo, Petro, ndi Andreya anachokera ku Betsaida. Komabe, pambuyo pake Petro ndi Andreya anasamukira ku Kapernao, kumene Mateyo akuwonekera kukhala anakhalako. Yakobo ndi Yohane anali m’bizinesi lausodzi ndipo mwachiwonekere anali kukhala ku Kapernao ka pena pafupi. Kukuwonekera ngati kuti Yudase Isikariote, amene pambuyo pake anapereka Yesu, ndiye mtumwi yekha wochokeraku Yudeya. Marko3:13-19; Luka 6:12-16.
◆ Kodi ndiatumwi ati amene angakhale anali achibale a Yesu?
◆ Kodi ndiati amene ali atumwi a Yesu, ndipo mungakumbukire motani maina awo?
◆ Kodi ena a atumwiwo anachokera kuti?
[Chithunzi pa tsamba 25]
Asanasankhe atumwi ake 12, Yesu anachezera usiku wonse mpwmphero kwa Yehova