Kuŵala kwa kuunika—Kwakukulu ndi Kwakung’ono (Mbali 2)
“M’kuunika kwanu tidzaona kuunika.”—SALMO 36:9.
1. Kodi ndi kuyesayesa kotani kumene kunachitidwa poyamba pofuna kumvetsetsa zizindikiro za m’buku la Chivumbulutso?
BUKU la Baibulo la Chivumbulutso lachititsa chidwi Akristu kuyambira kale. Limapereka chitsanzo chabwino cha mmene kuunika kwa choonadi kumamkabe kukuŵaliraŵalira. Mu 1917, anthu a Yehova anafalitsa mafotokozedwe a Chivumbulutso m’buku lakuti The Finished Mystery. Linavumbula mopanda mantha atsogoleri achipembedzo ndi andale a Dziko Lachikristu, koma mafotokozedwe ake ambiri anali obwereka kwina kosiyanasiyana. Chikhalirechobe, The Finished Mystery inayesabe kukhulupirika kwa Ophunzira Baibulo ku njira yooneka imene Yehova anali kugwiritsira ntchito.
2. Kodi nkhani yakuti “Kubadwa kwa Mtundu” inaŵalitsa kuunika kotani pa buku la Chivumbulutso?
2 Kuŵala kwapadera kwa kuunika kunaŵalira pa buku la Chivumbulutso pamene nkhani yakuti “Kubadwa kwa Mtundu” inafalitsidwa mu The Watch Tower ya March 1, 1925. Kunkalingaliridwa kuti Chivumbulutso chaputala 12 chinafotokoza za nkhondo pakati pa Roma wachikunja ndi Roma wa apapa, mwana wamwamuna akumaimira apapa. Koma nkhaniyo inasonyeza kuti Chivumbulutso 11:15-18 chinathandizira kumveketsa tanthauzo la chaputala 12, ikumasonyeza kuti chimanena za kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu.
3. Kodi ndi zofalitsa ziti zimene zinaŵalitsira kuunika kowonjezereka pa Chivumbulutso?
3 Zonsezi zinadzetsa chidziŵitso chomveka bwino kwambiri cha Chivumbulutso chimene chinafalitsidwa m’buku la Light, mavoliyumu aŵiri, mu 1930. Kuwongolera kwinanso kunaonekera mu “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules! (1963) ndi “Then Is Finished the Mystery of God” (1969). Komabe, panalinso zina zambiri zophunzira ponena za buku laulosi la Chivumbulutso. Inde, kuunika kokulirapo kunaŵala pa ilo mu 1988 pamene Revelation—Its Grand Climax At Hand! inafalitsidwa. Kunganenedwe kuti mfungulo ya kutseguka maso kwapang’onopang’ono kumeneku njakuti ulosi wa Chivumbulutso umanena za mu “tsiku la Ambuye,” limene linayamba mu 1914. (Chivumbulutso 1:10) Chotero buku la Chivumbulutso linali kudzamvedwa bwino kwambiri m’kupita kwa tsikulo.
“Maulamuliro Apamwamba” Amveketsedwa
4, 5. (a) Kodi Ophunzira Baibulo anaona motani Aroma 13:1? (b) Kodi kaimidwe kamene pambuyo pake kanaonedwa kukhala ka Malemba kulinga ku “maulamuliro apamwamba” kanali kotani?
4 Kuŵala kwakukulu kwa kuunika kunaoneka mu 1962 mogwirizana ndi Aroma 13:1, amene amati: “Moyo uliwonse ugonjere maulamuliro apamwamba [“maulamuliro aakulu,” Revised Nyanja Version].” (King James Version) Ophunzira Baibulo oyambirira anadziŵa kuti “maulamuliro apamwamba” otchulidwa pamenepo ananena za maulamuliro adziko. Iwo anakhulupirira kuti lemba limeneli linatanthauza kuti ngati Mkristu alembedwa usilikali panthaŵi ya nkhondo, iye anayenera kuvala yunifomu, kunyamula mfuti, ndi kupita kunkhondo, m’maenje. Anaganiza kuti popeza Mkristu sangaphe munthu mnzake, iye akanakakamizika kuwombera mfuti m’mwamba ngati zinthu zafika povuta.a
5 Nsanja ya Olonda ya July 1, 1963 ndi ya July 15, 1963, inaŵalitsa kuunika kooneka bwino pa nkhaniyo pofotokoza mawu a Yesu pa Mateyu 22:21: “Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” Mawu a atumwi pa Machitidwe 5:29 anali ofunika: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” Akristu amagonjera Kaisara—“maulamuliro apamwamba”—malinga ngati kuchita zimenezo sikumafuna kuti Mkristu asemphane ndi lamulo la Mulungu. Kugonjera Kaisara kunaonedwa kukhala ndi malire, osati kopanda malire. Akristu amapatsa Kaisara zinthu zokha zimene sizimasemphana ndi zofuna za Mulungu. Kunali kokhutiritsa chotani nanga kukhala ndi kuunika kooneka bwino pankhaniyo!
Kuŵala kwa Kuunika pa Nkhani za Gulu
6. (a) Kuti apeŵe dongosolo la malo aulemu ofala m’Dziko Lachikristu, kodi ndi njira yotani imene inatengedwa? (b) Kodi nchiyani potsiriza chimene chinaonedwa kukhala njira yolondola yosankhira amene ali ndi uyang’aniro pa mpingo?
6 Panali nkhani ya amene ayenera kutumikira monga akulu ndi atumiki m’mipingo. Kuti apeŵe dongosolo la malo aulemu ofala m’Dziko Lachikristu, anagamula kuti ameneŵa ayenera kusankhidwa mwa demokrase mwa kuponya voti kwa chiŵalo chilichonse cha mpingo. Koma kuunika kowonjezereka kwa mu The Watchtower ya September 1 ndi ya October 15, 1932, kunasonyeza kuti Malemba samapereka maziko okhalira ndi akulu osankhidwa mwa chisankho. Chotero ameneŵa analoŵedwa m’malo ndi komiti yautumiki, ndipo wotsogolera wa utumiki anasankhidwa ndi Sosaite.
7. Kodi kuŵala kwa kuunika kunadzetsa kuwongolera kotani panjira imene atumiki m’mipingo anali kuikidwira?
7 The Watchtower ya June 1 ndi ya June 15, 1938, inali ndi kuŵala kwa kuunika kosonyeza kuti atumiki mumpingo sanayenera kusankhidwa mwa chisankho, koma kuikidwa, ndiko kuti, kuikidwa mwateokrase. Mu 1971 kuŵala kwina kwa kuunika kunasonyeza kuti mpingo uliwonse sunayenera kutsogozedwa ndi mtumiki wa mpingo mmodzi yekha. M’malo mwake, uliwonse uyenera kukhala bungwe la akulu, kapena oyang’anira, oikidwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Chotero mwa kuunika komawonjezereka m’zaka pafupifupi 40, kunaonekeratu kuti akulu ndiponso atumiki, tsopano otchedwa atumiki otumikira, ayenera kuikidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kupyolera mwa Bungwe lake Lolamulira. (Mateyu 24:45-47) Zimenezi zinali zogwirizana ndi zimene zinachitika m’nthaŵi za atumwi. Amuna onga Timoteo ndi Tito anaikidwa ndi bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba kukhala oyang’anira. (1 Timoteo 3:1-7; 5:22; Tito 1:5-9) Zonsezi zikukwaniritsa Yesaya 60:17 mwanjira yapadera: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.”
8. (a) Kodi choonadi chomawonjezereka chinadzetsa kuwongolera kotani panjira imene Sosaite inagwirira ntchito? (b) Kodi makomiti a Bungwe Lolamulira ndi ati, ndipo kodi ntchito yawo kapena uyang’aniro wa iliyonse payokha ngwotani?
8 Panalinso nkhani ya kagwiridwe ka ntchito ka Watch Tower Society. Kwa zaka zambiri Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linalinso bungwe la otsogolera la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, ndipo zinthu zochuluka zinali m’manja mwa pulezidenti wake. Monga momwe 1977 Yearbook of Jehovah’s Witnesses (masamba 258-9) ikusonyezera, Bungwe Lolamulira linayamba kugwira ntchito ndi makomiti asanu ndi imodzi mu 1976, iliyonse yokhala ndi ntchito yosamalira mbali zina za ntchito ya padziko lonse. Komiti ya Ogwira Ntchito imasamalira nkhani zokhudza antchito, kuphatikizapo zinthu za onse otumikira m’banja la Beteli padziko lonse. Komiti Yofalitsa imasamalira nkhani zonse zokhudza boma ndi zamalamulo, monga za malo ndi kusindikiza. Komiti Yautumiki imasamalira ntchito yaumboni ndi kuyang’anira oyang’anira oyendayenda, apainiya, ndi zochita za ofalitsa a mpingo. Komiti Yophunzitsa imakonza misonkhano yampingo, masiku a msonkhano wapadera, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo ndi yamitundu yonse limodzinso ndi sukulu zosiyanasiyana za maphunziro auzimu a anthu a Mulungu. Komiti Yolemba imayang’anira kukonzedwa ndi kutembenuzidwa kwa zofalitsa zonse, ikumatsimikizira kuti zonse zikugwirizana ndi Malemba. Komiti ya Tcheyamani imasamalira zamwadzidzidzi ndi nkhani zina zofulumira. Ndiponso m’ma 1970, maofesi a nthambi za Watch Tower Society anayamba kuyang’aniridwa ndi komiti m’malo mwa woyang’anira mmodzi.b
Kuunika pa Khalidwe Lachikristu
9. Kodi kuunika kwa choonadi kunakhudza motani unansi wa Akristu ndi maboma a dziko?
9 Kuŵala kochuluka kwa kuunika kwakhudza khalidwe Lachikristu. Mwachitsanzo, talingalirani nkhani ya kusatenga mbali m’zadziko. Kuŵala kwakukulu kwambiri kwa kuunika kunaunikira nkhani imeneyi m’mutu wakuti “Kusatenga m’Mbali m’Zadziko” yotulutsidwa mu The Watchtower ya November 1, 1939. Imeneyo inali nkhani yapanthaŵi yake chotani nanga, ikumatuluka Nkhondo Yadziko II itangoyamba! Nkhaniyo inamasulira kusatenga mbali m’zadziko ndi kusonyeza kuti Akristu sayenera kuloŵa m’zandale kapena m’nkhondo za mitundu. (Mika 4:3, 5; Yohane 17:14, 16) Zimenezi zimachititsa mitundu yonse kuwada. (Mateyu 24:9) Nkhondo za Israyeli wakale sizimapereka chitsanzo kwa Akristu, monga momwe Yesu akufotokozera bwino pa Mateyu 26:52. Ndiponso, palibe mtundu uliwonse wa ndale lerolino umene uli wateokrase, wolamuliridwa ndi Mulungu, monga momwe analili Israyeli wakale.
10. Kodi kuŵala kwa kuunika kunavumbulanji ponena za mmene Akristu ayenera kuonera mwazi?
10 Kuunika kunaŵalanso pa kupatulika kwa mwazi. Ophunzira Baibulo ena anaganiza kuti chiletso cha kudya mwazi, cha pa Machitidwe 15:28, 29, chinali cha Akristu Achiyuda okha. Komabe, Machitidwe 21:25 amasonyeza kuti m’nthaŵi ya atumwi lamulo limeneli limanenanso za aja amitundu ina amene anakhulupirira. Chotero kupatulika kwa mwazi kumakhudza Akristu onse, monga momwe The Watchtower ya July 1, 1945 inasonyezera. Zimenezo zimatanthauza osati chabe kukana kudya mwazi wa nyama, monga m’masoseji amwazi, komanso kusala mwazi wa anthu, monga m’kuthira mwazi.
11. Kodi nchiyani chinaonedwa ponena za lingaliro la Mkristu la kusuta fodya?
11 Chifukwa cha kuunika kowonjezereka, zizoloŵezi zimene poyamba zinangokanidwa pambuyo pake zinaonedwa kukhala machimo aakulu. Chitsanzo cha zimenezi ndicho cha kusuta fodya. Mu Zion’s Watch Tower ya August 1, 1895, Mbale Russell anasonyeza 1 Akorinto 10:31 ndi 2 Akorinto 7:1 nalemba kuti: “Sinditha kuona mmene kusuta fodya kwa mtundu uliwonse kungadzetsere ulemerero kwa Mulungu, kapena phindu kwa Mkristu aliyense.” Chiyambire 1973 kwamveka bwino lomwe kuti munthu aliyense wosuta fodya sangakhale Mboni ya Yehova. Mu 1976 kunafotokozedwa bwino lomwe kuti palibe Mboni iliyonse imene ingalembedwe ntchito pakampani ya juga imene ingakhalebe mumpingo.
Kuwongolera Kwina
12. (a) Kodi kuŵala kwa kuunika kunavumbulanji ponena za chiŵerengero cha mfungulo za Ufumu zopatsidwa kwa Petro? (b) Kodi ndi m’mikhalidwe iti imene Petro anagwiritsira ntchito mfungulo iliyonse?
12 Pakhalanso kuunika kowonjezereka pa chiŵerengero cha mfungulo zophiphiritsira zimene Yesu anapatsa Petro. Ophunzira Baibulo anakhulupirira kuti Petro analandira mfungulo ziŵiri zimene zinatsegulira anthu njira yokhalira oloŵa Ufumu—ina kwa Ayuda, yogwiritsiridwa ntchito pa Pentekoste wa 33 C.E., ndipo ina kwa Akunja, yogwiritsiridwa ntchito choyamba mu 36 C.E., pamene Petro analalikira kwa Korneliyo. (Machitidwe 2:14-41; 10:34-48) M’kupita kwa nthaŵi, kunaonedwa kuti panalinso gulu lachitatu—Asamariya. Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yachiŵiri powatsegulira mwaŵi wa Ufumu. (Machitidwe 8:14-17) Chotero, mfungulo yachitatu inagwiritsiridwa ntchito pamene Petro analalikira kwa Korneliyo.—Nsanja ya Olonda, April 1, 1980, masamba 14-20, 24.
13. Kodi kuŵala kwa kuunika kunavumbulanji ponena za makola a nkhosa otchulidwa mu Yohane chaputala 10?
13 Mwa kuŵala kwina kwa kuunika, kunaonedwa kuti Yesu sanangotchula za makola aŵiri okha koma atatu. (Yohane, chaputala 10) Ameneŵa anali (1) khola la Ayuda limene Yohane Mbatizi anali wapakhomo wake, (2) khola la oloŵa Ufumu odzozedwa, ndi (3) khola la “nkhosa zina,” amene ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi.—Yohane 10:2, 3, 15, 16; Nsanja ya Olonda, August 1, 1984, masamba 10-21.
14. Kodi ndimotani mmene kuunika kowonjezereka kunamveketsera zinthu ponena za chiyambi cha Chaka Choliza Lipenga chophiphiritsira?
14 Kumvetsetsa Chaka Choliza Lipenga chophiphiritsira kunawongoleredwanso. Pansi pa Chilamulo, chaka chilichonse cha 50 chinali Choliza Lipenga chofunika kwambiri, pamene zinthu zinabwezedwa kwa eni ake. (Levitiko 25:10) Kwa nthaŵi yaitali zimenezi zinamvedwa kukhala zikuimira Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Komabe, posachedwapa, kunaonedwa kuti Chaka Choliza Lipenga chophiphiritsiracho chinayamba kwenikweni pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene olandira mzimu woyera wotsanuliridwawo anamasulidwa ku ukapolo wa pangano la Chilamulo cha Mose.—Nsanja ya Olonda, January 1, 1987, masamba 22-32.
Kuunika Kowonjezereka pa Mawu
15. Kodi ndi kuunika kotani kumene kunaŵala pa liwu lakuti “kuŵerengera mtengo”?
15 “Mlalikiyo anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu oona.” (Mlaliki 12:10) Mawu ameneŵa angagwire ntchito pa nkhani yathu imene tikukambitsiranayi, pakuti kuunika kwaŵala osati chabe pa nkhani zofunika zonga chiphunzitso ndi khalidwe komanso pa mawu Achikristu ndi matanthauzo ake olondola. Mwachitsanzo, pakati pa Ophunzira Baibulo, chimodzi cha zofalitsa zimene anakonda kwambiri chinali voliyumu yoyamba ya Studies in the Scriptures, yamutu wakuti The Divine Plan of the Ages. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, anazindikira kuti Mawu a Mulungu amanena kuti anthu okha ndiwo amaŵerengera mtengo. (Miyambo 19:21) Malemba samanena konse kuti Yehova akuŵerengera mtengo. Iye safunikira kuŵerengera mtengo. Zilizonse zimene wafuna kuchita zidzachitikadi chifukwa cha nzeru zake zosatha ndi mphamvu, monga momwedi timaŵerengera pa Aefeso 1:9, 10: “Monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo.” Chotero kunaonedwa pang’onopang’ono kuti liwulo “chifuno” linali loyenera kwambiri ponena za Yehova.
16. Kodi nchiyani chimene chinaonedwa pang’onopang’ono kukhala tanthauzo lolondola la Luka 2:14?
16 Ndiyeno panali nkhani ya kufuna kumvetsetsa bwino kwambiri Luka 2:14. Malinga ndi King James Version, imati: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pa dziko lapansi mtendere, chiyanjo kulinga kwa anthu.” Kunaonedwa kuti mawu ameneŵa sanapereke lingaliro lolondola, popeza kuti chiyanjo cha Mulungu sichimasonyezedwa kwa oipa. Chotero Mboni zinaona zimenezi kukhala nkhani ya mtendere kwa anthu amene anali achiyanjo kulinga kwa Mulungu. Chotero ankatcha ofuna kuphunzira Baibulo anthu achiyanjo. Komano anazindikira kuti nkhaniyi imanena za chiyanjo, osati cha anthu, koma cha Mulungu. Chifukwa chake, mawu amtsinde a New World Translation pa Luka 2:14 amanena za “anthu amene iye [Mulungu] amavomereza.” Akristu onse amene amachita mogwirizana ndi choŵinda chawo cha kudzipatulira ali nacho chiyanjo cha Mulungu.
17, 18. Kodi Yehova adzatsimikiza chiyani, ndipo adzayeretsa chiyani?
17 Momwemonso, kwa nthaŵi yaitali, Mboni zinkalankhula za kutsimikiza dzina la Yehova. Koma kodi Satana anakayikira dzina la Yehova? Ponena za nkhaniyo, kodi atumiki a Satana anachita zimenezo, monga ngati kuti Yehova sanali woyenera kukhala ndi dzinalo? Iyayi, kutalitali. Si dzina la Yehova limene linakayikiridwa kuti lifunikire kutsimikizidwa. Nchifukwa chake zofalitsa zaposachedwapa za Watch Tower Society sizimalankhula za dzina la Yehova kukhala likutsimikizidwa. Zimalankhula za ulamuliro wa Yehova kukhala ukutsimikizidwa ndi dzina lake kukhala likuyeretsedwa. Zimenezi zimagwirizana ndi zimene Yesu anatiuza kupempherera: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Mobwerezabwereza, Yehova anati anali kudzayeretsa dzina lake, limene Aisrayeli sanalikayikire koma limene anaipitsa.—Ezekieli 20:9, 14, 22; 36:23.
18 Nkokondweretsa kuti mu 1971, buku lakuti “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”—How? linasiyanitsa zimenezi: “Yesu Kristu akumenyera nkhondo . . . kutsimikiza Ulamuliro wachilengedwe chonse ndi kulemekeza dzina la Yehova.” (Masamba 364-5) Mu 1973, God’s Kingdom of a Thousand Years Has Approached inati: “‘Chisautso chachikulu’ chikudzacho ndicho nthaŵi ya Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ya kutsimikiza ulamuliro wake wachilengedwe chonse ndi ya kuyeretsa dzina lake lolemekezekalo.” (Tsamba 409) Ndiyeno, mu 1975, Man’s Salvation Out Of World Distress at Hand! inati: “Chochitika chachikulu koposa m’mbiri yonse chidzakhala chitachitika, kutsimikizidwa kwa ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake lopatulikalo.”—Tsamba 281.
19, 20. Kodi tingasonyeze motani chiyamikiro chathu kaamba ka kuŵala kwa kuunika kwauzimu?
19 Anthu a Yehova ali odala chotani nanga kukhala m’kuunika kwauzimu kumeneku! Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, mawu otsatirawa a mtsogoleri wachipembedzo amasonyeza mdima wauzimu umene atsogoleri a Dziko Lachikristu alimo: “Nchifukwa ninji pali uchimo? Nchifukwa ninji pali kuvutika? Nchifukwa ninji pali mdyerekezi? Awa ndi mafunso amene ndifuna kukafunsa Ambuye ndikapita kumwamba.” Koma Mboni za Yehova zikhoza kumuuza chifukwa chake: Chifukwa cha nkhani ya kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova ndi nkhani yakuti kaya zolengedwa zaumunthu zingasunge umphumphu kwa Mulungu ngakhale pali chitsutso cha Mdyerekezi.
20 M’zaka zonsezi, kuŵala kwa kuunika kwakukulu ndi kwakung’ono komwe kwaunikira mayendedwe a atumiki odzipatulira a Yehova. Zimenezi zakwaniritsa malemba onga Salmo 97:11 ndi Miyambo 4:18. Koma tisaiŵaletu kuti kuyenda m’kuunika kumatanthauza kuyamikira kuunika kowonjezerekako ndi kuchita mogwirizana nako. Monga momwe taonera, kuunika kowonjezereka kumeneku kumaphatikizapo ponse paŵiri khalidwe lathu ndi ntchito yathu yolalikira.
[Mawu a M’munsi]
a Chifukwa cha lingaliro limeneli, The Watch Tower ya June 1 ndi ya June 15, 1929, inafotokoza “maulamuliro apamwamba” kukhala Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Linali makamaka lingaliro limenelo limene linawongoleredwa mu 1962.
b Nsanja ya Olonda ya April 15, 1992, inalengeza kuti abale osankhidwa makamaka a “nkhosa zina” anali kuikidwa kuthandiza makomiti a Bungwe Lolamulira, mofanana ndi Anetini a m’nthaŵi ya Ezara.—Yohane 10:16; Ezara 2:58.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi kuunika kotani kumene kwaŵala pa kugonjera “maulamuliro apamwamba”?
◻ Kodi kuŵala kwa kuunika kwachititsa zinthu zotani m’gulu?
◻ Kodi kuunika kowonjezereka kwakhudza motani khalidwe Lachikristu?
◻ Kodi kuunika kwauzimu kwadzetsa kuwongolera kotani pa kumvetsetsa kwathu mfundo zina za Malemba?
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Mfungulo patsamba 24: Zojambulidwa pa chithunzi chotengedwa mu Cooper-Hewitt, National Design Museum, Smithsonian Institution