Kugwirizana ndi Osunga Umphumphu a Yehova
“Ponena za ine, ndidzayenda mu umphumphu wanga. . . . ndidzadalitsa Yehova pakati pa khamu losokhana.”—SALMO 26:11, 12, NW.
1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene zipembedzo zina m’Dziko Lachikristu zapezera otsatira? (b) Kodi Yesu anagwiritsira ntchito dongosolo lotani lakuphunzitsa? (Mateyu 11:28-30)
MU 1985, anthu 189, 800 anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova monga mboni zake Zachikristu. Imeneyo iri avereji ya 520 pa tsiku. Kodi anthu onse amenewa anapanga motani chosankha chawo kuti abatizidwe? Kodi iwo anafika pa misonkhano ya nakatindi, kumvetsera kwa mlaliki wosonkhezera maganizo, ndiyeno ku panga chosankha chathuku kaamba ka Kristu? Ndimo mraene zipembedzo zina Zachi protestanti ndi Zachievanjeliko zimachitira. Koma kodi imeneyo ndiyo njira imene Kristu amapezera otsatira?
2 Pamene tipenda mosamalitsa kulalikira kwapoyera kwa Yesu, sitimampeza akugwiritsira ntchito kusonkhezera maganizo. Mwa chitsanzo, kodi iye anasonkhezera omvetsera ake mwa makwaya ambiri ndi kuimba? Kapena kodi iye anagwiritsira ntchito ukatswiri wamaganizo wochenjerawo kuchititsa omvetsera ake kukhala ndi ganizo laliwongo ndiyeno kuwachititsa kupisa dzanja m’thumba kutulutsa zopereka? Kutalitali, dongosolo lake lakuphunzitsa linachititsa anthu kuganiza ndi kusinkhasinkha. Popeza kuti ambiri a omvetsera ake anali Ayuda, iwo anali kale ndi chidziwitso cha Malemba Achihebri. Iye akanawachititsa kusinkhasinkha pa maziko achidziwitso chawo chapapitapo kotero kuti akanamzindikira monga Mesiya.—Mateyu, chaputala 5-7; Luka 13:10-21.
3. Timadziwa bwanji kuti Paulo sanagwiritsire ntchito zisonkhezero m’kuphunzitsa kwake?
3 Mofananamo, Paulo, ngakhale kuti anawonedwa ndi ena kukhala wopanda luso laku lankhula, anasonkhezera mkhalidwe wakuganiza. (Machitidwe 20:7-9; 2 Akorinto 10:10;11:6) Iye analemba kuti: “Ndikupemphani mwazifundo za Mulungu, abale, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yokondweretsa Mulungu, utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu yakulingalira. . . . Sandulikani mwakusintha maganizo anu [“kotero kuti mkhalidwe wanu wonse wamaganizo usinthidwe” Phillips], kuti mukadzitsimikizire chifuniro cha Mulungu chabwino ndi chokondweretsa ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2, NW.
4. Munthu asanabatizidwe kukhala mmodzi wa Mboi za Yehova, kodi ndimasitepe otani amene iye ayenera kutenga?
4 Mofananamo lerolino, anthu amene amabatizidwa ali anthu amene aphunzira Malemba ndi kulingalira mosamalitsa asanatenge sitepe yofunika yaubatizo, kapena kumizidwa kotheratu m’madzi. (Machitidwe 17:11, 12)Chawocho sichinakhale chosankha chofulumira, ndi chathuku. Mmalo mwake, asanavomerezedwe kaamba ka ubatizo, afika mokhazikika pamisonkhano Yachikristu ncholinga chakupeza chidziwitso cholongosoka cha YehovaMulungu ndi zifuno zake kupyolera mwa Kristu Yesu. (Ahebri 10:25) Iwo akhalanso ndi phande mokhazikika muuminisitala Wachi kristu, akumagawana mbiri yabwino ya Ufumu ndi ena. (Machitidwe 5:42; 1 Akorinto 9:16) Ndiyeno, milungu yomalizira ubatizo wawo usanachitike, apenda mosamalitsa ndi akulu osiyanasiyana ampingo mafunso oposa 120 onena za chiphunzitso Chachikristu ndi kudzisungira, apendanso Malemba Abaibulo mazana ambiri ochilikiza—zonsezi zinachitidwira kuti akhale osunga umphumphu ovomerezedwa ubatizo wawo usanachitike.—Machitidwe 8:34-36.a
Kusiyana Kumene Ubatizo Umapanga
5. Kodi ndinjira yotani ya khalidwe imene munthuyo amadziwikitsidwa nayo mwaubatizo?
5 Kodi munthu amapindulanji mwakubatizidwa? Choyamba, amazigwirizanitsa ndi wosunga uphumphu wamkulu koposa onse amene anayenda pano padziko lapansi—Yesu Kristu. Iyemwiniyo anapereka chitsanzo mwakubatizidwa pamene anali wamsinkhu pafupifupi zaka 30. (Luka 3:21-23) Pambuyo pake analamulira otsatira ake kuphunzitsa ndi kubatiza padziko lonse. (Mateyu 28:19, 20) Koma kodi iye anatanthauza kuti ophunzira ake ayenera kubatiza anthu mosasankha, popanda kudziwa mkhalidwe wawo watsopano?
6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwa wotsatira wowona wa Kristu? (b) Kodi chiyero chimatanthauza chiyani?
6 Mtumwi Petro akutchula lingaliro lolungama pamene akulemba kuti: “Khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima; pakuti ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:15, 16) Tsopano, kwa Mkristu wodzipatu lira, kodi kukhala “woyera” kumatanthauza chiyani?
7 Mogwirizana ndi kunena kwa Expository Dictionary of New Testament Words ya W. E. Vine liwu Lachigiriki la ha’gi-os (lotembenuzidwa “oyera”) “kwakukulukulu limatanthauza olekanitsidwa . . . ndipo chifukwa chake, tanthauzo lake la m’Lemba m’makhalidwe ake abwino ndi auzimu, olekanitsidwa ku uchimo ndipo chifukwa chake odzipereka kwa Mulungu.” Katswiri wina Wachigiriki amanena kuti “kuli kwakukulukulu kufanana ndi Mulungu.” Chidziwitso chimenechi chimaika muyeso wapamwamba pa awo amene amabatizidwa monga Akristu owona. Uli muyeso waumphumphu, ndipo umphumphu ndi wo ‘kumamatira kwamphamvu ku lamulo la makhalidwe abwino’—ponena za Akristu, malamulo a Kristu.—Yohane 17:17-19; 18: 36, 37.
8. (a) Kodi ndimiyeso yotani imene inali yofunika mu mpingo woyambirira Wachikristu ponena za khalidwe? (b) Kodi Dziko Lachikristu lalondola miyezo imeneyo? Perekani zitsanzo zochokera m’zochitika za kwanuko.
8 Nthawi zonse mpingo wowona Wachikristu walimbikitsa umphumphu, kusunga gulu liri loyera. Motero Paulo anauza Akristu oyambirira kuti “musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi. . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:9-13; 2 Yohane 10, 11) Kodi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu agwiritsira ntchito muyeso wapamwamba umenewu wa umphumphu kumagulu awo? Dziko Lachikristu limavomereza anthu kukhala mamembala kaya akhale m’dzina lokha kapena okangalika amene nthawi zonse amachita tchimo lalikulu ndi upandu. Malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo samaloleza konse kulolera kotero.—Yerekezerani ndi Yeremiya 8:5, 6, 10.
9. Kodi nchiyani chimene chimakokera anthu ambiri kukudzipatulira ndi ubatizo?
9 Kwakukulukulu chifukwa cha muyeso wapamwamba weniweni umenewu pakati pa Mboni za Yehova, awo amene amakonda chowonadi ndi umphumphu amakokedwera ku kudzipatulira kwa Ambuye Mfumu wachilengedwe chonse, Yehova Mulungu. (Habakuku 3:18, 19) Iwo amawona bwino lomwe kusiyana pakati pa khalidwe la zipembedzo za udziko ndi la Mboni za Yehova. Ndithudi, anthu ambiri amanyozera kulambira koyera. (1 Petro 4:3, 4) Komabe, zikwi zambiri za okonda umphumphu zimatembenuzidwira ku chowonadi. Zimasonyeza kukonda kwawo Mulungu ndi miyezo yake pamene zilowa muubatizo wam’madzi.—Yerekezerani ndi Marko 1:10; Yohane 3:23; Machitidwe 8:36.
Umphumphu Wochokera pa Chikondi ndi Chipiriro
10. Kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwa Mkristu kuti asunge umphumphu wake?
10 Uphumphu uli ndi mphotho. Yesu anamveketsa zimenezo pamene anaitana anthu kukhala otsatira ake. “Ngati aliyense afuna kunditsata ine, adzikane yekha [“kudzisiya kumbuyo,” The New English Bible] ndi kunyamula mtengo wake wozunzirapo ndi kunditsata ine mosalekeza.” (Marko 8:34, NW) Njira ya umphumphu Wa chikristu imalowetsamo mayeso ndi kudzimana ndipo kaamba ka chifukwa chofanana chimene inachitira Kristu—tiri ndi mdani wofananayo, Satana. (Aefeso 6:11, 12) Motero chipiriro chiri chofunika kuti titsatire Yesu “mosalekeza.” Kaamba ka chifukwa chimenecho, kudzipatulira sikuli chosankha chopepuka;sikuyenera kukhala chochitika chotayirako nthawi. Komabe owerengeka anasiya chowonadi mkati mwamiyezi yowerengeka kapena zaka pambuyo pa ubatizo wawo. Kodi nchiyani chimene tinganene kuti chinachititsa zimenezo?
11. Kodi nchifukwa ninji, mwinamwake, anthu ena sanapitirizebe m’njira yaumphumphu?
11 Mwinamwake ena analowa mu ubatizo mu mkhalidwe wathuku mmalo mwa kukhala mkhalidwe wamaganizo anzeru. Ena angakhale atafunafuna zotulukapo zofulumira napanga kudzipatulira kodziwonetsera ndi kwa kanthawi. Mulimonse mmene zingakhalire, iwo anataya unansi wawo wamphamvu ndi Yehova. ‘Sanayang’ane dwii’ pa Wopereka Chitsanzo wawo, Yesu Kristu. (Ahebri 12:1, 2) Monga chotulukapo, kukonda kwawo Mulungu kunafwifwa ndipo umphumphu wawo unali wakanthawi. Ndipo kodi nchifukwa ninji chikondi chotero chiri chinthu chofunika? Chifukwa chakuti ndicho maziko okha akudzipatulira kosatha kwa Yehova.—Marko 12:30, 31; 1 Yohane 4:7, 8, 16; 5:3.
Kuwerengera Mtengo wa Umphumphu
12. Kodi ndinjira yanzeru yotani yakuitenga ubatizo usanachitike?
12 Yesu sanalimbikitse otsatira ake kumlondola mwaumbulimbuli popanda kuwerengera mtengo. Iye anapereka uphungu wakuti: “Ndani wa inu akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo, awone ngati ali nazo za kuimaliza?” Inde, munthu wanzeru amapima mosamalitsa njira yake yamtsogolo yamachitidwe. Afunikira kutsimikizira chisonkhezero chake asanavomereze thayo lokwanira la kudzipatulira Kwachikristu ndi ubatizo. Ndipo Yesu anasonyeza chimene zimenezi zikanatanthauza pamene anatsiriza mwakumati: “Chifukwa chake tsono, yense wa inu sakana zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.”—Luka 14:28-33 .
13. Ngati mbali yaikulu ya chiphunzitso cha Yesu iri chikondi, kodi iye anatanthauzanji pamene analankhula za ‘kuda’ mamembala abanja a munthuwe? (Mateyu 22:37-40)
13 Kudzipatulira kwa Yehova kumafunikiritsa umphumphu wa moyo wonse m’kuchita chifuniro cha Mulungu. Palibe anthu kapena chuma zimene zingaloledwe kukhala pamwamba pa kukonda Mulungu kwa munthuyo. Ndicho chifukwa chake Yesu anafotokoza kuti: “Munthu akadza kwa ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iyemwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:26) Tsopano kodi Yesu anatanthauzanji pamene analankhula za kuda mamembala abanja la munthuwe ndipo ngakhale iwemwini? Popeza kuti anaphunzitsa otsatira ake kukonda ngakhale adani awo, kodi ndim’li ngaliro lotani m’limene panopa anagwiritsira ntchito liwu la kuda? (Luka 6:27, 35) Panopa liwu la kuda liri ndi lingaliro lakukonda mocheperapo.—Yerekezerani ndi Mateyu 12:46-50.
14. Kodi ndimotani mmene mabwenzi ena ndi achibale amachitira pamene munthu afikira kukhala Mboni ya Yehova? (Yohane 15:18, 19)
14 Ndithudi, pamene munthu akhala Mboni Yachikristu ya Yehova, mwadzidzidzi amapeza amene ali mabwenzi ake owona. Mwinamwake ena adzamnyanyala kapena kumkana chifukwa chakuti wasiya chipembedzo chake choyamba, ngakhale ngati kwenikweni iwo eni saali m’chipembedzo chirichonse. Koma Yesu analonjeza kuti pakakhala kukwichizidwa kwa kutaikiridwa kulikonse kotero, akumati: “Palibemunthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi ino, . . . ndipo nthawi irinkudza, moyo wosatha.”—Marko 10:29, 30.
15. Kodi nchifukwa ninji anthu ena anganyozere Mboni za Yehova?
15 M’zochitika zina njira yakudzipatulira ndi umphumphu ingatanthauze kutaikiridwa ndi ulemu m’maso mwa anthu ena. (1 Akorinto 4: 12, 13) Kodi nchifukwa ninji ziyenera kukhala choncho? Chifukwa chakuti tsopano mukugwi ritsira ntchito chipembedzo chimene sichimawonedwa kukhala “cholemekezeka.” (Yerekezerani ndi Marko 2:15, 16) Ndiiko komwe, sikuli kulemekezeka ‘kumka nimuvutitsa anthu ena ndi chipembedzo chanu kunyumba ndi nyumba.’ Sikuli kulemekezeka kumka kundende mmalo mwakuswa umphumphu wa munthuwe pankhani za utundu ndi kukonda dziko la munthuwe. (Yohane 18:36) Sikuli kulemekezeka kukana kuthiridwa mwazi chifukwa chachikumbumtima chophunzitsidwa ndiBaibulo . . . ngakhale kuti mliri wamakono wa AIDS ukuchititsa anthu ena kuyamba aganiza kaye asanalandire magazi.—Yerekezerani ndi Machitidwe 15:28, 29; 17:6, 7; 24:5.
16. Kodi timathandizidwa motani kuti tisunge umphumphu wathu?
16 Ngakhale kuli kwakuti njira ya umphumphu Wachikristu njopapatiza ndi yopereka chiyeso, tiri nacho chithandizo chopezeka nthawi zonse. (Mateyu 7:13, 14) Chifukwa chake Paulo akanatha kunena kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Ndipo tingathe kupeza mphamvu imeneyo kupyolera mwapemphero laphamphu, mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, ndi kupyolera mwa kugwirizana ndi mpingo Wachikristu. Monga osunga umphumphu obatizidwa tingakhalebe okhulupirika, tithokoza mphamvu imene Mulungu amagawira.—Aefeso 4:11-13; 6:18; Salmo 119:105
Mapindu a Njira Yosunga Umphumphu
17. Kodi ubatizo umatsogolera kumapindu otani?
17 Njira ya kudzipatulira ndi ubatizo imatsogolera kumadalitso ambiri. Choyamba, ingatanthauze utumiki wowonjezereka kwambiri ndi wokhutiritsa maganizo. Pali chiyembekezo cha utumiki wamtsogolo monga mpainiya wotha ndiza, umene m’zochitika zina ungatsogolere ku ntchito yaupainiya wokhazikika ndi wapadera, utumiki waumishonale, ntchito yadera ndi yachigawo, ndi utumiki wa pa Betele. (Wonani bokosi patsamba 26. ) Kwa abale obatizidwa njirayo imawatsegukira kuti atumikire ena mu mpingo monga atumiki otumikira ndipo, m’kupita kwanthawi, monga akulu. Koma pali chofunika chachikulu chimodzimodzicho kuti mupeze madalitso onse amenewa—umphumphu.—1 Timoteo 3:1-10.
18. Kodi moyo wathu wakudzipatulira uyenera kuyambukira motani anthu ena amene timawonana nawo?
18 Mapindu a moyo wakudzipatulira ndi umphumphu amafalikira kuyambukira ena. Monga chotulukapo cha kulondola chitsanzo cha Kristu mosamalitsa, munthuyo amakhala mwamuna kapena mkazi wabwinopo, atate kapena amayi wabwinopo. (1 Petro 2:21; Aefeso 5:21-33; 6:4) Achichepere amakulitsa unansi wolimba ndi makolo awo, aphunzitsi, ndi akulu mu mpingo. (Tito 2:6, 7) Mkristu wobatizidwa aliyense amakhala mnansi, wolemba ntchito, kapena wolembedwa ntchito wabwino kwambiri. (Mateyu 22:39; Aefeso 6:5-9; Tito 2:9, 10) Ndipo mofanana ndi Kristu, Mkristu aliyense ayenera kukhala bwenzi lotsitsimula kwa ena, monga momwe Yesu ananenera kuti: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”—Mateyu 11:29.
19. Kodi ndiphindu lalikulu lotani la kutenga sitepe la kudzipatulira?
19 Phindu lalikulu koposa la sitepe la kudzipatulira ndi ubatizo pamene tigwirizana ndi ziwerengero za osunga umphumphu a Yehova ndilo kupeza unansi wamtendere ndi Mlengi. Umenewu umatsogolera ku mtendere wamaganizo. Monga momwe Paulo anaperekera uphungu wakuti: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
20. (a) Kodi “mtendere wa Mulungu” umachokera pa chiyani? (b) Kodi ndi mwawi wotani umene umatsegukira munthu wobatizidwa?
20 “Mtendere wa Mulungu” umenewo uli wozikidwa pa chidziwitso chozama cha chitsanzo cha Yesu chimenechi ndi kudzipereka. Chidziwitso cha Kristu chikutsogolera ambiri ku kulapa kowona mtima ndi kusintha mkhalidwe wowona kapena ‘kupotoloka’ pa uchimo. (Machitidwe 3:19, 20) Monga chotulukapo, anthu odzipatulira akulankhula, monga momwe ana chitira wamasalmo, kuti “ponena za ine ndi dzayenda mu umphumphu wanga . . . ndidzadalitsa Yehova pakati pa makamu osonkhana.” (Salmo 26:11, 12, NW) Munthu amene amabatizidwa m’madzi kusonyeza kudzipatulira kwake kwa Mulungu akudzigwirizanitsa ndi osunga umphumphu a Yehova kuzungulira dziko. (1 Petro 2:17) Ndiponso iye ‘akugwiritsitsa moyo weniweni,’ moyo wosatha, umene Yehova analonjeza kupyolera mwa Kristu Yesu.—1 Timoteo 6:19; Tito 1:2.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda ya November 15, 1985 tsamba 19-31 imalongosola mchitidwe wolungama wonena za ubatizo, ndipo yalongosola mafunso awiri amene amaperekedwa kwa oyembekezera ubatizo chakumapeto kwa nkhani yaubatizo.
Kodi Mukanayankha Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene Akristu oyambirira anakopedwera ku chowonadi chophunzitsidwa ndi Kristu ndi atumwi?
◻ Kodi chiyero chiri chogwirizana motani ndi Mkristu aliyense payekha ndi mpingo?
◻ Kodi umphumphu uyenera kuchokera pachiyani?
◻ Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa pa mtengo waumphumphu?
◻ Kodi ndiati amene ali mapindu akusunga umphumphu?
[Bokosi patsamba 20]
Mwawi mu Uminisitala wa nthawi Yonse
Upainiya Wothandiza: Minisitala wobatizidwa amene amathera maora osachepera 60 m’ntchito yolalikira mkati mwa mwezi.
Mpainiya Wokhazikika: Minisitala wobatizidwa amene amathera avereji ya maora 90 pamwezi m’ntchito yolalikira.
Mpainiya Wapadera: Minisitala wobatizidwa amene amathera maora okwanira 140 pa mwezi muuminisitala nalandira alawansi yaing’ono mwezi uliwonse kaamba ka zofunika zazikulu. Kawirikawiri apainiya amenewa amagawiridwa ku timagulu takutali ndi mipingo yaing’ono.
Mmishonale Wagileadi: Minisitala wobatizidwa amene waphunzitsidwa ku Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower kaamba ka utumiki ku dziko lachilendo ndi amenenso amathera maora osachepera 140 pamwezi muutumiki.
Woyang’anira dera ndi chigawo: Akulu oyendayenda amene amachezetsa mipingo ndi madera ncholinga cha kulimbikitsa abale muutumiki wawo ndi m’misonkhano. Amathera maora ambiri muutumiki wakumunda.
Utumiki wa Betele: Wochitidwa ndi aminisitala anthawi yonse mu iriyonse ya maofesi anthambi a Watch Tower Society ndi makina osindikizira kuzungulira dziko.
[Chithunzi patsamba 18]
Ubatizo umatsegula njira . . .
[Chithunzi patsamba 19]
. . . ya kukhala minisitala wosunga umphumphu