“Yehova, Mulungu Wachifundo ndi Wachisomo”
“Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi waukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.”—EKSODO 34:6.
1. (a) Kodi Baibulo limawatonthoza motani aja amene aona okondedwa awo akusiya kulambira koyera? (b) Kodi Yehova amawaona motani anthu olakwa?
“MWANA wanga wamkazi anandiuza kuti sakufunanso kukhala mumpingo wachikristu,” anatero atate wina wachikristu. “Pambuyo pake, zimenezo zinandipweteka mtima koopsa kwa masiku ambiri, milungu, ndi miyezi yomwe. Ngakhale imfa sipweteka chonchi ayi.” Zimakhaladi zosautsa kuona wokondedwa wako akusiya njira ya kulambira koyera. Kodi zinthu ngati zimenezi zinakuchitikiranipo? Ngati zinatero, tontholani podziŵa kuti Yehova amakumverani chifundo. (Eksodo 3:7; Yesaya 63:9) Nangano kodi iye amawaona motani anthu olakwawo? Baibulo limasonyeza kuti Yehova mwachifundo amawapempha kubwerera kwa iye ndi kulandiranso chiyanjo chake. Anachonderera Ayuda opanduka a m’tsiku la Malaki kuti: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu.”—Malaki 3:7.
2. Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti chifundo ndicho umunthu wa Yehova?
2 Mulungu anagogomezera chifundo chake kwa Mose pa Phiri la Sinai. Pamenepo, Yehova anavumbula kuti ali “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi waukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Chilengezo chimenechi chimagogomezera mfundo yakuti chifundo ndicho umunthu wa Yehova. ‘Amafuna kuti onse afike kukulapa,’ analemba motero mtumwi wachikristu Petro. (2 Petro 3:9) Koma sikuti chifundo cha Mulungu chilibe malire ayi. Mose anauzidwa kuti iye ‘samasula wopalamula.’ (Eksodo 34:7; 2 Petro 2:9) Komanso, “Mulungu ndiye chikondi,” ndipo mbali yaikulu ya mkhalidwe umenewu ndiyo chifundo. (1 Yohane 4:8; Yakobo 3:17) Yehova “sasunga mkwiyo wake kunthaŵi yonse,” ndipo “akondwera nacho chifundo.”—Mika 7:18, 19.
3. Kodi kusiyana kwake kunali kotani mmene Yesu ankaonera chifundo ndi mmene alembi ndi Afarisi ankachionera?
3 Yesu anali chitsanzo changwiro cha Atate wake wakumwamba. (Yohane 5:19) Pamene iye anachitira chifundo olakwa sanali kulekerera machimo awo ayi koma anaonetsa chisoni chomwe chija ankasonyeza kwa odwala. (Yerekezerani ndi Marko 1:40, 41.) Inde, Yesu ananena kuti chifundo chili chimodzi cha “zolemera” za Chilamulo cha Mulungu. (Mateyu 23:23) Kusiyana ndi zimenezo, talingalirani alembi ndi Afarisi, amene kupambanitsa kwawo potsata chilungamo sikunalole chifundo. Ataona Yesu akucheza ndi ochimwa, anadandaula kuti: “Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nawo.” (Luka 15:1, 2) Poyankha omneneza mlanduwo, Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo atatu. Fanizo lililonse limagogomezera chifundo cha Mulungu.
4. Kodi Yesu anasimba mafanizo otani aŵiri, ndipo fanizo lililonse linali ndi mfundo yotani?
4 Poyamba, Yesu anasimba za munthu yemwe anasiya nkhosa 99 napita kukafunafuna imodzi yotayika. Mfundo yake? “Kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusoŵa kutembenuka mtima.” Kenako, Yesu anasimba za mkazi amene anafunafuna ndalama yasiliva yomwe anataya komano ataipeza anakondwera. Tanthauzo lake? ‘Kumakhala chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.’ Yesu anasimba fanizo lake lachitatu monga nthano.a Ambiri amaona nkhani imeneyi kukhala nthano yabwino yoposa ina iliyonse. Kupenda fanizo limeneli kudzatithandiza kuyamikira chifundo cha Mulungu ndi kuchitsanzira.—Luka 15:3-10.
Mwana Wopanduka Achoka Panyumba
5, 6. Kodi mwana wamng’ono m’fanizo lachitatu la Yesu anaonetsa motani kuti analibiretu kuyamikira?
5 “Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri; ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigaŵirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagaŵira za moyo wake. Ndipo pakupita masiku oŵerengeka mwana wamng’onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe achitayiko.”—Luka 15:11-13.b
6 Mwana wamng’onoyo apapa anaonetsa kuti analibiretu kuyamikira. Choyamba, anaumirira kuti ampatse choloŵa chake, ndiyeno anachimwaza “ndi makhalidwe achitayiko.” Mawuwo “makhalidwe achitayiko” atembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki lotanthauza “khalidwe losadziletsa.” Katswiri wina wamaphunziro anati liwulo “limanena za kupandiratu khalidwe.” Ndiye pali chifukwa chabwino chimene nthaŵi zambiri mnyamatayo wa m’fanizo la Yesu amatchedwera woloŵerera (wosakaza), liwu lofotokoza munthu womwazamwaza ndi wowawanya.
7. Ndani lero amene ali ngati mwana wosakaza, ndipo nchifukwa chiyani anthu ambiri ngati amenewo amakafuna ufulu “kudziko lakutali”?
7 Kodi alipo anthu lero amene ali ngati mwana wosakazayo? Inde. Nzachisoni kuti anthu oŵerengeka asiya “nyumba” yachisungiko ya Atate wathu wakumwamba, Yehova. (1 Timoteo 3:15) Ena mwa ameneŵa amaganiza kuti m’nyumba ya Mulungu munthu amakhala womangika kwambiri, kuti diso la Yehova loyang’anitsitsa limapingapinga munthu m’malo momteteza. (Yerekezerani ndi Salmo 32:8.) Taganizani za mkazi wina wachikristu amene analeredwa malinga ndi mapulinsipulo a Baibulo kuyambira ukhanda wake ndiye pambuyo pake anayamba kumwetsa moŵa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Pokumbukira nthaŵi yoipa imeneyo pamoyo wake, iye anati: “Ndinafuna kuonetsa kuti pandekha ndingaukonze moyo wanga kukhala wabwino. Ndinafuna kuchita zimene ndinkaganiza, ndipo sindinafune wina aliyense kundiuza zina.” Monga mwana wosakaza uja, mtsikana ameneyu anafuna ufulu. Kuipa kwake nkwakuti anafika pomchotsa mumpingo wachikristu chifukwa cha machitachita ake otsutsana ndi Malemba.—1 Akorinto 5:11-13.
8. (a) Kodi aja amene akufuna kutsata njira yotsutsana ndi malamulo a Mulungu angathandizidwe motani? (b) Kodi nchifukwa chiyani munthu ayenera kuganizapo kwambiri pa zimene asankha pankhani ya kulambira?
8 Mtima umaswekadi pamene wokhulupirira mnzathu aonetsa kuti akufuna kutsata njira yotsutsana ndi malamulo a Mulungu. (Afilipi 3:18) Zimenezi zikachitika, akulu ndi ena okhala nazo ziyeneretso zauzimu amayesetsa kumbweza wolakwayo. (Agalatiya 6:1) Komabe, munthu aliyense sachita kumkakamiza kulandira goli la kukhala wophunzira wachikristu. (Mateyu 11:28-30; 16:24) Atafika pamsinkhu, ngakhale achinyamata ayenera kudzisankhira okha pankhani ya kulambira. Koma mfundo njakuti, aliyense wa ife ali ndi ufulu wodzisankhira ndipo adzaziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu. (Aroma 14:12) Ndipotu ‘tidzatutanso chimene tifesa’—zimene posapita nthaŵi anali kudzaphunzira mwana wosakaza uja wa m’fanizo la Yesu.—Agalatiya 6:7, 8.
Athedwa Nzeru Kudziko Lakutali
9, 10. (a) Kodi mwana wosakaza zake uja zinthu zinamsinthira motani, ndipo anatani? (b) Fotokozani mwa chitsanzo mmene ena lero amene amasiya kulambira koona amazunzikira monga mwana wosakaza zakeyo.
9 “Pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusoŵa. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaŵeta nkhumba. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.”—Luka 15:14-16.
10 Ngakhale kuti anali wosoŵa, mwana wosakazayo sanaganize kaye zobwerera kunyumba. Koma anakumana ndi munthu wina mfulu yemwe anamloŵetsa ntchito yoŵeta nkhumba. Popeza kuti Chilamulo cha Mose chinkanena kuti nkhumba zinali nyama zodetsedwa, ntchito imeneyo sakanailandira nkomwe Myuda aliyense. (Levitiko 11:7, 8) Koma ngati mwana wosakazayo chikumbumtima chake chinamsautsa, anangochipondereza. Ndipotu sakanayembekezera kuti womlemba ntchito, munthu wakomweko, akanavutika mtima poona mmene chikumbumtima chinali kumvutira iyeyo, mmphaŵi komanso mlendo. Kuzunzika kwa mwana wosakazayo nkofanana ndi zimene zimachitikira ambiri lero amene amasiya njira yoongoka ya kulambira koyera. Kaŵirikaŵiri, oterewa amayamba kuchita zinthu zimene kale akanaziona kukhala zoipa. Mwachitsanzo, ali ndi zaka 17, mnyamata wina anapandukira moyo wachikristu umene anakula nawo. “Chisembwere ndi mankhwala osokoneza bongo zinachotseratu ziphunzitso za Baibulo zimene ndinaphunzira kwa zaka zambiri,” anatero. Posakhalitsa, mnyamata ameneyu anapezeka ali m’ndende chifukwa cha kuba ndi mfuti ndi kupha munthu. Ngakhale kuti pambuyo pake anachira mwauzimu, zimene zinamchitikirazo zinali zoopsa chotani nanga pofuna chabe kuti ‘akondwere nawo uchimo kanthaŵi pang’ono’!—Yerekezerani ndi Ahebri 11:24-26, NW.
11. Kodi vuto la mwana wosakaza linakula chifukwa chiyani, ndipo ena lero apeza motani kuti zokopa za dzikoli zili “chinyengo chopanda pake”?
11 Vuto la mwana wosakazayo linakula chifukwa chakuti “palibe munthu anamninkha kanthu.” Kodi mabwenzi ake atsopano anali kuti? Tsopano pokhala analibe ndi khobiri lomwe, anakhala ngati ‘wodedwa’ kwa iwo. (Miyambo 14:20) Momwemonso, ambiri lero amene amataya chikhulupiriro amapeza kuti zokopa za dzikoli ndi malingaliro ake zili “chinyengo chopanda pake.” (Akolose 2:8) “Ndinazunzika ndipo mtima wanga unandipweteka chifukwa chosoŵa chitsogozo cha Yehova,” anatero mtsikana wina amene anasiya gulu la Mulungu kwakanthaŵi. “Ndinayesa kufanana ndi dziko, koma chifukwa chosafananadi ndi ena, anandinyanyala. Ndinakhala ngati mwana wotayika wofunikira atate woti anditsogoze. Panthaŵiyo mpamene ndinazindikira kuti ndifunikira Yehova. Sindinafunenso kukhala pandekha popanda kudalira iye.” Nayenso mwana wosakaza wa m’fanizo la Yesu anafika pozindikira mfundo ngati imeneyo.
Mwana Wosakaza Akumbukira Mumtima
12, 13. Kodi ndi zinthu zotani lerolino zimene zathandiza ena kukumbukira mumtima? (Onani m’bokosi.)
12 “Koma mmene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndiwonongeke kuno ndi njala? Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu; sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu [olipidwa]. Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake.”—Luka 15:17-20.
13 Mwana wosakazayo “anakumbukira mumtima.” Kwanthaŵi yaitali, anali kusangalala ndi zokondweretsa, monga ngati anali m’dziko lamaloto. Koma tsopano anazindikira za mkhalidwe wake weniweni wauzimu. Inde, ngakhale kuti analoŵerera, panali chiyembekezo chakuti zinthu zimkhalira bwino mnyamatayu. Mwa iye munali kanthu kena kabwino. (Miyambo 24:16; yerekezerani ndi 2 Mbiri 19:2, 3.) Bwanji nanga za aja amene amasiya gulu la Mulungu lerolino? Kodi kungakhale bwino kuganiza kuti palibe chiyembekezo choti zinthu ziwakhalira bwino, kuti kupanduka kwawo konse kuli umboni wakuti achimwira mzimu woyera wa Mulungu? (Mateyu 12:31, 32) Osati kwenikweni. Ena a iwo amazunzika chifukwa cha kupulupudza kwawo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi ambiri mwa ameneŵa amakumbukira mumtima. “Sindinamuiŵale Yehova ngakhale tsiku limodzi,” anatero mlongo wina, polingalira za nthaŵi imene anali kunja kwa gulu la Mulungu. “Nthaŵi zonse ndinkapemphera kuti tsiku lina iye akandilandirenso m’choonadi.”—Salmo 119:176.
14. Kodi mwana wosakaza uja anasankha kuchitanji, ndipo mwa kuchita zimenezo anaonetsa motani kuti anadzichepetsa?
14 Koma kodi aja amene atayika angachitenji ponena za vuto lawo? M’fanizo la Yesu mwana wosakazayo anasankha zopanga ulendo kubwerera kunyumba ndi kupempha atate wake kuti amkhululukire. “Mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu olipidwa,” anati akawauza zimenezo. Wantchito wolipidwa anali munthu amene ankamlemba ntchito yatsiku limodzi ndipo zinkatheka kumchotsa ntchito popanda kumuuziratu pasadakhale. Ameneyu sanali kuŵerengeredwa kwambiri pomuyerekezera ndi kapolo amene, m’lingaliro lina, anali ngati wapabanja. Chotero mwana wosakaza uja sanaganize zopempha kuti akhalenso mwana monga analili kale. Anafunitsitsa kulandira malo apansi kwambiri kuti aonetse kukhulupirika kwake kwatsopano kulinga kwa atate wake tsiku ndi tsiku. Komabe, zimene zinachitika nzoti mwana wosakazayo sanaziyembekezere.
Amlandira Bwino
15-17. (a) Kodi atateyo anatani ataona mwana wake? (b) Kodi mwinjiro, mphete, ndi nsapato zomwe atateyo anapatsa mwana wake zikusonyeza chiyani? (c) Kodi kukonza madyerero kumene atateyo anachita kukuonetsa chiyani?
15 “Koma pakudza iye kutali, atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. [Mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu olipidwa.] Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwana wa ng’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.”—Luka 15:20-24.
16 Kholo lililonse lachikondi limalakalaka kuti bwenzi mwana wake atachira mwauzimu. Ndiye titha kuganiza kuti tsiku lililonse atate wa mwana wosakazayo ankaima kutsogolo kwa nyumba yake kuyang’ana kunjira polakalaka kumuona mwana wake akubwera. Panopo wamuona mwana wake akubwera cha apo kunjira! Mosakayikira mnyamatayo anali atasintha maonekedwe ake. Ngakhale zili tero, atateyo akumzindikira “pakudza iye ali kutali.” Sakuona zovala zake zausiwa ndi mzimu wake wosweka; akuona mwana wake, ndipo athamanga kukamchingamira!
17 Atateyo atafika pamene panali mwana wake, anamkupatira m’khosi mwake nampsompsonetsa. Kenako analamula akapolo ake kumpatsa mwinjiro mwana wake, mphete, ndi nsapato. Mwinjirowo sunali chovala wamba ayi, koma “wokometsetsa”—mwina chovala chamtengo wapatali chokometseredwa bwino chonga chimene amapatsidwa mlendo wolemekezeka. Popeza sizinkachitikachitika kuti akapolo nkuvala mphete ndi nsapato, atateyo panopo anali kuonetseratu kuti anali kumlandira mwana wakeyo monga mwana wa m’nyumba ndithu. Koma atateyo anachitabe zina zambiri. Analamula kuti pakhale madyerero okondwerera kubwera kwa mwana wake. Inde, munthu ameneyu sanali kukhululukira mwana wake moumira kapena chabe chifukwa chokakamizika kutero poti mwana wakeyo anali atabwera kale ayi; anafuna kumkhululukira. Zinamsangalatsa.
18, 19. (a) Kodi fanizo la mwana wosakaza limakuphunzitsani chiyani za Yehova? (b) Malinga ndi mmene Yehova anachitira ndi Yuda ndi Yerusalemu, kodi iye ‘amadikira’ motani kubwerera kwa wochimwa?
18 Mpaka pano, kodi fanizo la mwana wosakaza likutiphunzitsa chiyani ponena za Mulungu amene tili ndi mwayi wa kumlambira? Choyamba, kuti Yehova ali “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Inde, chifundo ndicho mkhalidwe waukulu wa Mulungu. Ndi mmene amachitira ndi amene akuvutika. Komanso, fanizo la Yesu limatiphunzitsa kuti Yehova ali “wokhululukira [“wokonzeka kukhululukira,” NW].” (Salmo 86:5) Amayang’anira, titero kunena kwake, kuti aone ngati pali kusintha kulikonse mumtima wa anthu olakwa ndiyeno akhale ndi maziko oonetsera chifundo.—2 Mbiri 12:12; 16:9.
19 Mwachitsanzo, taganizani mmene Mulungu anachitira ndi Israyeli. Yehova anauzira mneneri Yesaya kuti afotokoze kuti Yuda ndi Yerusalemu anali ‘odwala kuchokera kumutu kufikira kuphazi.’ Komanso anati: ‘Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo.’ (Yesaya 1:5, 6; 30:18; 55:7; Ezekieli 33:11) Mofanana ndi atate wa m’fanizo la Yesu, Yehova ‘amayang’ana kunjira,’ titero kunena kwake. Amalakalaka kuti aliyense amene wachoka m’nyumba yake abwerere. Kodi si zimene timayembekezera kwa atate wachikondi?—Salmo 103:13.
20, 21. (a) Kodi ndi motani mmene ambiri lero chimawakokera chifundo cha Mulungu? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambitsirana zotani?
20 Chaka chilichonse, chifundo cha Yehova chimasonkhezera ambiri kukumbukira mumtima ndi kuyambiranso kulambira koona. Zimenezi zimawasangalatsa kwambiri okondedwa awo! Mwachitsanzo, titenge atate wachikristu wotchulidwa poyamba nkhani ino. Zosangalatsa nzakuti mwana wake wamkazi uja anachira mwauzimu ndipo tsopano iye akutumikira monga mtumiki wanthaŵi zonse. “Chimwemwe changa ndi chimene munthu angakhale nacho m’dongosolo ili lakale la zinthu,” akutero atateyo. “Chisoni changa chakhala chimwemwe.” Inde, Yehova amasangalalanso!—Miyambo 27:11.
21 Komano fanizo la mwana wosakaza lili ndi zambiri. Yesu anapitiriza nthano yake kuti asiyanitse chifundo cha Yehova ndi khalidwe laliuma ndi lokonda kuweruza limene alembi ndi Afarisi ambiri anali nalo. M’nkhani yotsatira, tidzakambitsirana mmene anachitira zimenezo ndi tanthauzo lake.
[Mawu a M’munsi]
a Sikuti nthano ndi mafanizo ena omwe Baibulo limasimba ndi zinthu zomwe zinachitikadi. Ndiponso, popeza cholinga cha nkhani zimenezi ndi kuphunzitsa za khalidwe, sitifunikira kuyesa kupeza tanthauzo la mawu ake alionse.
b Tanthauzo laulosi la fanizo limeneli lafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1989, masamba 16, 17.
Kubwereza
◻ Kodi kusiyana kwake kunali kotani mmene Yesu ankaonera chifundo ndi mmene Afarisi ankachionera?
◻ Ndani lero amene ali ngati mwana wosakaza, ndipo motani?
◻ Kodi ndi zinthu zotani zomwe zinachititsa mwana wosakaza uja kukumbukira mumtima?
◻ Kodi atateyo anaonetsa motani chifundo kwa mwana wake wolapa?
[Bokosi patsamba 11]
ANAKUMBUKIRA MUMTIMA
Kodi nchiyani chimene chawathandiza ena amene kale anachotsedwa mumpingo wachikristu kukumbukira mumtima mwawo? Ndemanga zotsatira zikuunika pankhani imeneyi.
“Mumtima mwanga ndinkadziŵabe kumene choonadi chinali. Kuphunzira Baibulo ndi kupita kumisonkhano yachikristu kwa zaka zambiri kunandikhudza kwambiri. Kodi ndikanamfulatira motani Yehova? Sanandisiye; ndinamsiya. Pomaliza, ndinavomereza kuti ndinali wolakwa ndi wouma khosi ndi kuti Mawu a Yehova ali oona nthaŵi zonse—‘umatuta chimene ufesa.’”—C.W.
“Mwana wanga wamkazi anayamba kulankhula, ndipo zimenezo zinandikhudza mtima popeza ndinafuna kumphunzitsa zinthu zonga amene Yehova ali ndi mmene angapempherera kwa iye. Sindinali kugona tulo, ndipo tsiku lina usiku kwambiri ndinapita kupaki pagalimoto ndipo ndinalira. Ndinalira ndi kupemphera kwa Yehova nthaŵi yoyamba, zimene sindinachitepo kwanthaŵi yaitali. Zokha zomwe ndinaganiza nzakuti ndifunikiranso Yehova pamoyo wanga, ndipo ndinafuna kuti andikhululukire.”—G.H.
“Tikamakambitsirana za chipembedzo, ndinkawauza anthu kuti ngati ndifuna kusankha chipembedzo chimene chimaphunzitsa choonadi, ndidzakhala wa Mboni za Yehova. Ndiyeno ndinkawauzanso kuti ndinali momwemo, koma kuti ndinasiya chifukwa cholephera kuchita zofunika. Pozindikira zimenezi, ndinkadzimva wamlandu ndi wosakondwa nthaŵi zambiri. Pomaliza, ndinavomereza kuti, ‘Koma ndazunzika. Ndifunikira kusintha kwambiri.’”—C.N.
“Zaka makumi atatu ndi zisanu zapita, ineyo ndi amuna anga tinachotsedwa. Ndiyeno, mu 1991, tinadabwa potichezera akulu aŵiri amene anatiuza kuti zitheka kubwerera kwa Yehova. Patapita miyezi isanu ndi umodzi, tinabwezeretsedwa ndipo tinali okondwa kwambiri. Ineyo ndili ndi zaka 63, amuna anga 79.”—C.A.