‘Pangani Mabwenzi ndi Chuma Chosalungama’
“Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama . . . Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.” —LUKA 16:9, 10.
1. Kodi Mose ndi ana a Israyeli anamtamanda motani Yehova atatuluka m’Igupto?
ANAPULUMUTSIDWA mozizwitsa—chinali chokumana nacho cholimbitsa chikhulupiriro chotani nanga! Palibe aliyense amene anachititsa Israyeli kutuluka m’Igupto kusiyapo Yehova, Wamphamvuyonse. Nkosadabwitsa kuti Mose ndi Aisrayeli anaimba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa: ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa.”—Eksodo 15:1, 2; Deuteronomo 29:2.
2. Kodi nchiyani chimene anthu a Yehova anatenga potuluka m’Igupto?
2 Ha, ufulu umene Israyeli anali atapeza kumene unali wosiyana chotani nanga ndi mkhalidwe wake m’Igupto! Tsopano akakhoza kulambira Yehova popanda chopinga. Ndipo sanatuluke m’Igupto ali chimanjamanja. Mose akusimba kuti: “Ana a Israyeli . . . [a]napempha Aaigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zovala. Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aaigupto, ndipo sanawakaniza. Ndipo anawafunkhira Aaigupto.” (Eksodo 12:35, 36) Koma kodi ndimotani mmene iwo anagwiritsirira ntchito chuma cha Igupto chimenechi? Kodi chinachititsa Yehova ‘kumveketsedwa’? Kodi chitsanzo chawo chimatiphunzitsanji?—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:11.
“Chopereka cha Yehova”
3. Kodi kugwiritsira ntchito golidi kwa Israyeli m’kulambira konama kunasonkhezera Yehova kuchita motani?
3 Pamene Mose anali pa phiri la Sinai kwa masiku 40 kukalandira malangizo a Mulungu kwa Israyeli, anthu amene anali kuyembekezera mmunsi mwake sanathe kupirira. Akumathyola mphete zagolidi m’makutu mwawo, iwo analangiza Aroni kuwapangira fano loti alilambire. Aroni anawamangiranso guwa la nsembe, ndipo tsiku lotsatira mmamaŵa, anaperekerapo nsembe. Kodi kugwiritsira ntchito golidi mwanjira imeneyi kunachititsa Mpulumutsi wawo kuwakonda? Kutalitali! “Tsopano ndileke,” Yehova anatero kwa Mose, “kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha.” Yehova analekerera mtunduwo kokha pamene Mose anamchonderera, ngakhale kuti atsogoleri opandukawo anaphedwa ndi mliri wa kwa Mulungu.—Eksodo 32:1-6, 10-14, 30-35.
4. Kodi “chopereka cha Yehova” chinali chiyani, ndipo ndani anachipereka?
4 Pambuyo pake, Aisrayeli anakhala ndi mwaŵi wa kugwiritsira ntchito chuma chawo m’njira imene inakondweretsadi Yehova. Anasonkhanitsa “chopereka cha Yehova.”a Zopereka zina zomangira ndi kukometsera chihema zinali golidi, siliva, mkuwa, lamadzi, nsalu zamaŵangamaŵanga, zikopa za nkhosa zamphongo, zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu. Cholembedwacho chimasumika maganizo athu pa mkhalidwe wa maganizo wa operekawo. “Aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova.” (Eksodo 35:5-9) Israyeli analabadira ndi mtima wonse. Chifukwa chake, chihema chinali chimango “chokongola ndi chaulemerero waukulu,” malinga ndi kunena kwa katswiri wina.
Zopereka za Kachisi
5, 6. Kodi Davide anagwiritsira ntchito motani chuma chake mogwirizana ndi kachisi, ndipo kodi ena anachita motani?
5 Ngakhale kuti Mfumu Solomo wa Israyeli anayang’anira ntchito yomanga nyumba yachikhalire yolambirira Yehova, Davide atate wake, anali ataikonzekera kwambiri. Davide anasonkhanitsa golidi, siliva, mkuwa, chitsulo, mitengo, ndi miyala ya mtengo wapatali zochuluka kwambiri. “Popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga,” Davide anauza anthu ake motero, “chuma changachanga cha golidi ndi siliva ndili nacho ndichipereka ku nyumba ya Mulungu wanga, moenjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo; ndicho matalente zikwi zitatu za golidi, . . . ndi matalente zikwi zisanu ndi ziŵiri za siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi.” Davide analimbikitsa ena kukhala ooloŵanso manja. Iwo anapereka zochuluka: golidi, siliva, mkuwa, chitsulo, ndi miyala yamtengo wapatali yambiri. “Ndi mtima wangwiro,” anthu “anapereka mwaufulu kwa Yehova.”—1 Mbiri 22:5; 29:1-9.
6 Mwa zopereka zaufulu zimenezi, Aisrayeli anasonyeza chiyamikiro chachikulu kaamba ka kulambira Yehova. Davide anapemphera modzichepetsa kuti: “Ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere?” Chifukwa? “Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu. . . . Koma ine, ndi mtima wanga wowongoka ndapereka zonsezi mwaufulu.”—1 Mbiri 29:14, 17.
7. Kodi tsiku la Amosi limatiphunzitsa phunziro lotani la chenjezo?
7 Komabe, mafuko a Israyeli analephera kusungabe kulambira Yehova pamalo oyamba m’maganizo ndi m’mitima yawo. Pofika m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E, Israyeli wogaŵanika anali atakhala ndi mlandu wa kunyalanyaza zauzimu. Ponena za ufumu wakumpoto wa Israyeli wa mafuko khumi, Yehova anati kupyolera mwa Amosi: “Tsoka osalabadirawo m’Ziyoni, ndi iwo okhazikika m’phiri la Samariya!” Iye anawafotokoza kukhala anthu “ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa awo ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoŵeta, ndi ana a ng’ombe ochoka pakati pa khola; . . . akumwera vinyo m’zipanda.” Koma chuma chawo sichinali chitetezo chawo. Mulungu anachenjeza kuti: “Adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.” Mu 740 B.C.E., Israyeli anakumana ndi mavuto padzanja la Asuri. (Amosi 6:1, 4, 6, 7) Ndipo m’kupita kwa nthaŵi, ufumu wakummwera wa Yuda nawonso unakhala wokondetsa zinthu zakuthupi.—Yeremiya 5:26-29.
Kugwiritsira Ntchito Bwino Chuma m’Nthaŵi Zachikristu
8. Kodi Yosefe ndi Mariya akutiikira chitsanzo chabwino chotani ponena za kugwiritsira ntchito chuma?
8 Mosiyana ndi zimenezo, kusaukirapo kwa atumiki a Mulungu m’nthaŵi za pambuyo pake sikunawaletse kusonyeza changu chawo cha kulambira koona. Talingalirani za Mariya ndi Yosefe. Pomvera lamulo la Kaisara Augusto, iwo anapita kumudzi kwawo ku Betelehemu. (Luka 2:4, 5) Yesu anabadwira kumeneko. Atapita masiku 40, Yosefe ndi Mariya anapita kukachisi ku Yerusalemu wapafupi kukapereka nsembe yoyeretsa yofunikira. Zimene zinasonyeza kusauka kwawo zinali mbalame ziŵiri zazing’ono zimene Mariya anapereka. Iye kapena Yosefe sananene kuti kusauka kwawoko kunawaletsa kupereka nsembeyo. M’malo mwake, iwo momvera anagwiritsira ntchito chuma chawo chochepacho.—Levitiko 12:8; Luka 2:22-24.
9-11. (a) Kodi mawu a Yesu pa Mateyu 22:21 amatipatsa chitsogozo chotani ponena za mmene timagwiritsirira ntchito ndalama? (b) Kodi nchifukwa ninji chopereka chochepa cha mkazi wamasiye sichinali chopanda pake?
9 Pambuyo pake, Afarisi ndi otsatira chipani cha Herode anayesa kukola Yesu, akumati: “Chifukwa chake, mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iyayi?” Yankho la Yesu linasonyeza kuzindikira kwake. Akumasonyeza ndalama imene anampatsa, Yesu anafunsa kuti: “Nchayani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?” Iwo anayankha kuti: “Cha Kaisara.” Mwanzeru iye anati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:17-21) Yesu anadziŵa kuti boma lopanga ndalamayo linafuna kuti misonkho idzilipiridwa. Koma pamenepo anathandizanso otsatira ake ndi adani ake omwe kuzindikira kuti Mkristu woona amafunanso kupatsa kwa “Mulungu zake za Mulungu.” Zimenezi zimaphatikizapo kugwiritsira ntchito bwino chuma chake chakuthupi.
10 Chochitika chimene Yesu anaona m’kachisi chimasonyeza zimenezi. Anali atangotsutsa kumene alembi aumbombo amene ‘anawononga nyumba za akazi amasiye.’ Pamene “anakweza maso, naona anthu enichuma alikuika zopereka zawo mosungiramo ndalama,” akusimba motero Luka. “Ndipo [Yesu] anaona mkazi wina wamasiye waumphaŵi alikuika momwemo timakobiri tiŵiri. Ndipo iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.” (Luka 20:46, 47; 21:1-4) Anthu ena ananena kuti kachisiyo anali wokonzeka ndi miyala yamtengo wapatali. Yesu anayankha kuti: “Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa.” (Luka 21:5, 6) Kodi chopereka chochepa cha mkazi wamasiyeyo chinali chopanda pake? Kutalitali. Iye anachirikiza makonzedwe amene Yehova anali atakhazikitsa panthaŵiyo.
11 Yesu anauza otsatira ake oona kuti: “Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye aŵiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Luka 16:13) Chotero, kodi tingasonyeze motani uchikatikati pogwiritsira ntchito ndalama zathu?
Adindo Okhulupirika
12-14. (a) Kodi Akristu ali adindo a chuma chiti? (b) Kodi ndi m’njira zapadera zotani zimene anthu a Yehova lerolino amachitira udindo wawo mokhulupirika? (c) Kodi ndalama zochirikizira ntchito ya Mulungu lerolino zimachokera kuti?
12 Pamene tipatulira miyoyo yathu kwa Yehova, kwenikweni timanena kuti zonse zimene tili nazo, chuma chathu chonse, nzake. Pamenepa, kodi ndimotani mmene tiyenera kugwiritsirira ntchito zimene tili nazo? Pofotokoza utumiki Wachikristu mumpingo, Mbale C. T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, analemba kuti: “Aliyense ayenera kudziona monga woikidwa ndi Ambuye kukhala mdindo wa nthaŵi yake, mphamvu, ndalama, ndi zina zotero, ndipo aliyense ayenera kuyesetsa kugwiritsira ntchito maluso ameneŵa malinga ndi kukhoza kwake, ku ulemerero wa Ambuye.”—The New Creation, tsamba 345.
13 “Pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika,” amatero 1 Akorinto 4:2. Monga gulu la m’mitundu yonse, Mboni za Yehova zimayesayesa kuchita mogwirizana ndi malongosoledwe amenewo, zikumagwiritsira ntchito nthaŵi yawo yochuluka monga momwe zingathere mu utumiki Wachikristu, zikumakulitsa bwino lomwe maluso awo a kuphunzitsa. Ndiponso, magulu a antchito odzifunira otsogozedwa ndi ma Regional Building Committee mofunitsitsa amapereka nthaŵi yawo, nyonga, ndi maluso awo kupangira maholo abwino osonkhanamo kaamba ka kulambira. Zonsezi Yehova amakondwera nazo kwambiri.
14 Kodi ndalama zochirikizira mkupiti wa kuphunzitsa waukulu umenewu ndi ntchito yomanga zimachokera kuti? Kwa a mtima wofunitsitsa, monga momwedi zinalili m’masiku akumanga chihema. Kodi ife patokha tikuchita nawo zimenezo? Kodi njira imene timagwiritsirira ntchito chuma chathu imasonyeza kuti utumiki wa Yehova uli wofunika koposa kwa ife? Pankhani za ndalama, tiyeni tikhale adindo okhulupirika.
Chitsanzo cha Kuoloŵa Manja
15, 16. (a) Kodi Akristu a m’tsiku la Paulo anasonyeza motani kuoloŵa manja? (b) Kodi nkhani imene tikukambitsiranayi tiyenera kuiona motani?
15 Mtumwi Paulo analemba za mzimu wa kuoloŵa manja wa Akristu ku Makedoniya ndi ku Akaya. (Aroma 15:26) Ngakhale kuti anali kuvutika, iwo anapereka zopereka mwamsanga kuthandiza abale awo. Mofananamo, Paulo analimbikitsa Akristu a ku Korinto kupereka mooloŵa manja, kupereka zochuluka zawo kukwaniritsa kusoŵa kwa ena. Palibe aliyense amene moyenerera akanaimba Paulo mlandu wa kulanda. Iye analemba kuti: “Iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”—2 Akorinto 8:1-3, 14; 9:5-7, 13.
16 Zopereka zooloŵa manja zimene abale athu ndi anthu okondwerera amapereka kaamba ka ntchito ya Ufumu ya padziko lonse lerolino zimapereka umboni wa mmene iwo amalemekezera kwambiri mwaŵi umenewu. Koma, monga momwe Paulo anakumbutsira Akorinto, tingachite bwino ngati tingaone nkhani imeneyi kukhala chikumbutso.
17. Kodi Paulo analimbikitsa dongosolo lotani popereka zopereka, ndipo kodi limeneli lingagwire ntchito lerolino?
17 Paulo analimbikitsa Akristu kutsatira dongosolo popereka zopereka zawo. “Tsiku loyamba la sabata,” iye anatero, “yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.” (1 Akorinto 16:1, 2) Zimenezo zingakhale chitsanzo kwa ife ndi ana athu ponena za zopereka zathu, kaya tikutero kupyolera mumpingo kapena kutumiza mwachindunji ku ofesi ya nthambi yapafupi ya Watch Tower Society. Banja lina la amishonale logaŵiridwa kulalikira m’tauni ina ku East Africa linapempha okondwerera kupita nawo kukaphunzira Baibulo. Pamapeto a msonkhano woyamba umenewu, amishonalewo mwaluso anaika ndalama m’kabokosi kolembedwapo kuti “Zopereka za ntchito ya Ufumu.” Opezekapo ena anachitanso chimodzimodzi. Pambuyo pake, atsopano ameneŵa atalinganizidwa kukhala mpingo Wachikristu, woyang’anira dera anawachezera nawathokoza kaamba ka kupereka kwawo zopereka nthaŵi zonse.—Salmo 50:10, 14, 23.
18. Kodi ndimotani mmene tingathandizire abale athu amene ali m’nsautso?
18 Tilinso ndi mwaŵi wa kugwiritsira ntchito chuma chathu kuthandiza okanthidwa ndi masoka achilengedwe ndi amene akukhala m’madera ankhondo. Tinakondwera chotani nanga pamene tinaŵerenga za mitokoma yachithandizo yotumizidwa ku Eastern Europe pamene kugwa kwa chuma ndi chipolowe cha ndale zinakantha mbali imeneyo ya dziko! Zopereka za katundu ndi ndalama zomwe zinasonyeza kuoloŵa manja kwa abale athu ndi umodzi wawo ndi Akristu osoŵawo.b—2 Akorinto 8:13, 14.
19. Kodi ndi zinthu ziti zogwira ntchito zimene tingachite kuthandiza amene ali mu utumiki wanthaŵi yonse?
19 Timalemekeza kwambiri ntchito ya abale athu amene ali mu utumiki wanthaŵi yonse monga apainiya, oyang’anira oyendayenda, amishonale, ndi antchito a pa Beteli, sichoncho kodi? Pamene mikhalidwe yathu ilola, mwina tingawapatse thandizo lakuthupi mwachindunji. Mwachitsanzo, pamene woyang’anira dera achezera mpingo wanu, mungampatse malo ogona, chakudya, kapena kumthandiza ndi ndalama zoyendera. Kuoloŵa manja kotero kumaonedwa ndi Atate wathu wakumwamba, amene amafuna kuti atumiki ake asamaliridwe. (Salmo 37:25) Zaka zingapo zapitazo, mbale wina amene anali wokhoza kupereka chakudya chopepuka chokha anaitanira woyang’anira woyendayenda ndi mkazi wake kunyumba kwawo. Pamene banjalo linali kupita mu utumiki wakumunda wa madzulo, mbaleyo anapatsa alendo akewo envulopu. Mkati mwake munali ndalama (yokwanira dola imodzi ya United States) ndi kakalata kolembedwapo kuti: “Ya kapu ya tiyi kapena galoni ya petulo.” Ha, ndi chiyamikiro chachikulu chotani nanga chimene chinasonyezedwa modzichepetsa chotere!
20. Kodi ndi mwaŵi ndi thayo lotani zimene sitiyenera kunyalanyaza?
20 Mwauzimu, anthu a Yehova ali odala! Timakhala ndi mapwando auzimu pamisonkhano yathu yadera ndi yachigawo, pamene timalandira zofalitsidwa zatsopano, chiphunzitso chabwino, ndi uphungu wothandiza. Ndi mitima yodzala chiyamikiro kaamba ka madalitso athu auzimu, sitimaiŵala mwaŵi ndi thayo lathu la kupereka ndalama zogwiritsira ntchito kupititsira patsogolo zinthu za Ufumu wa Mulungu padziko lonse.
‘Pangani Mabwenzi ndi Chuma Chosalungama’
21, 22. Kodi nchiyani chimene posachedwapa chidzachitikira “chuma chosalungama,” zikumafuna kuti ife tichitenji tsopano lino?
21 Ndithudi, pali njira zambiri zimene tingasonyezere kuti timaika kulambira Yehova pamalo oyamba m’miyoyo yathu, ndipo njira yofunika kwambiri imaphatikizapo kulabadira kwathu uphungu wa Yesu wakuti: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusoŵani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.”—Luka 16:9.
22 Onani kuti Yesu analankhula za kusoŵa kwa chuma chosalungama. Inde, lidzafika tsiku pamene ndalama za dongosolo lino zidzakhala zopanda pake. “Adzataya siliva wawo kumakwalala, nadzayesa golidi wawo chinthu chodetsedwa;” Ezekieli analosera motero. “Siliva wawo ndi golidi wawo sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Ezekieli 7:19) Kufikira zimenezo zitachitika, tiyenera kugwiritsira ntchito nzeru ndi luntha ponena za mmene tigwiritsirira ntchito chuma chathu chakuthupi. Motero sitidzachita chisoni chifukwa cholephera kulabadira chenjezo la Yesu lakuti: “Ngati simukhala okhulupirika m’chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? . . . Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.”—Luka 16:11-13.
23. Kodi nchiyani chimene tiyenera kugwiritsira ntchito mwanzeru, ndipo mphotho yathu idzakhala yotani?
23 Chifukwa chake, tiyeni tonsefe tilabadire mokhulupirika zikumbutso zimenezi za kuika kulambira Yehova pamalo oyamba m’miyoyo yathu ndi kugwiritsira ntchito mwanzeru chuma chathu chonse. Motero tidzasunga ubwenzi wathu ndi Yehova ndi Yesu, amene akulonjeza kuti pamene ndalama zisoŵa adzatilandira “m’mahema osatha,” ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya mu Ufumu wakumwamba kapena padziko lapansi laparadaiso.—Luka 16:9.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu Lachihebri lomasuliridwa “chopereka” limachokera ku mneni amene amatanthauza “khala pamwamba; khala wokuzika; kwezeka.”
b Onani Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 307-15, lofalitsidwa mu 1993 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Israyeli analabadira motani pempho la Yehova la kupereka zopereka zomangira chihema?
◻ Kodi nchifukwa ninji chopereka cha mkazi wamasiye sichinali chopanda pake?
◻ Kodi Akristu ali ndi thayo lotani ponena za njira imene amagwiritsira ntchito chuma chawo?
◻ Kodi tingapeŵe motani kuchita chisoni ndi njira imene timagwiritsirira ntchito ndalama zathu?
[Chithunzi patsamba 15]
Ngakhale kuti chopereka cha mkazi wamasiye chinali chochepa, sichinali chopanda pake
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Zopereka zathu zimachirikiza ntchito ya Ufumu ya padziko lonse