Malo Oyenera a Kulambira Yehova M’miyoyo Yathu
“Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi.”—SALMO 145:2.
1. Ponena za kulambira, kodi Yehova amafunanji?
“INE Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.” (Eksodo 20:5) Mose anamva chilengezo cha Yehova chimenecho, ndipo anachibwereza pambuyo pake polankhula ndi mtundu wa Israyeli. (Deuteronomo 5:9) Mose sanakayikire konse kuti Yehova Mulungu anafuna kuti atumiki Ake amlambire Iye yekha.
2, 3. (a) Kodi nchiyani chimene chinakhutiritsa Aisrayeli kuti zimene zinachitika pafupi ndi phiri la Sinai zinali zachilendo? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tidzapenda onena za kulambira kwa Aisrayeli ndi kwa atumiki a Mulungu lerolino?
2 Akugonera pafupi ndi phiri la Sinai, Aisrayeli ndi “anthu ambiri [osakanikirana]” amene anachoka m’Igupto limodzi nawo anaona kanthu kachilendo. (Eksodo 12:38) Kameneko sikanali kofanana ndi kulambira milungu ya Igupto, imene tsopano inanyazitsidwa ndi masoka kapena miliri khumi. Pamene Yehova anasonyeza Mose kukhalapo kwake, zinthu zowopsa zinachitika: mabingu, mphezi, ndi kulira kwa lipenga kogonthetsa m’kutu kumene kunachititsa msasa wonse kunjenjemera. Ndiyeno panatsatira moto ndi utsi pamene phiri lonse linagwedezeka. (Eksodo 19:16-20; Ahebri 12:18-21) Ngati Mwiisrayeli aliyense anafuna umboni wowonjezereka wakuti zimene zinalikuchitika zinali zachilendo, uwo unali kudzakhalapo posapita nthaŵi. Mwamsanga, Mose anatsika paphiripo atalandira mpambo wachiŵiri wa malamulo a Mulungu. Malinga ndi cholembedwa chouziridwa, “khungu la nkhope [ya Mose] linanyezimira; ndipo [anthu] anawopa kumyandikiza.” Ndithudi, chinali chochitika chachilendo chosaiŵalika!—Eksodo 34:30.
3 Mtundu umenewo wa Mulungu unalibenso chikayikiro cha malo amene kulambira Yehova kunali nawo. Iye anali Mpulumutsi wawo. Ndiye anawapatsa moyo wawo weniweniwo. Analinso Mpatsi wawo wa Malamulo. Koma kodi iwo anasungabe kulambira Yehova pamalo oyamba? Ndipo bwanji nanga za atumiki amakono a Mulungu? Kodi kulambira Yehova kuli ndi malo otani m’miyoyo yawo?—Aroma 15:4.
Kulambira Yehova kwa Aisrayeli
4. Kodi makhazikitsidwe a chigono cha Israyeli paulendo wawo wogonera m’chipululu anali otani, ndipo nchiyani chinali pakati pa chigono?
4 Mukanakhala m’mwamba ndi kuyang’ana Aisrayeli ogonera m’chipululu, kodi mukanaonanji? Malo aakulu, koma adongosolo a mahema okhalamo pafupifupi anthu mamiliyoni atatu kapena kuposapo, osonkhanitsidwa m’magulu a mafuko atatuatatu kumpoto, kummwera, kummaŵa, ndi kumadzulo. Posuzumira pafupi, mukanaonanso gulu lina pafupi ndi pakati pa chigonocho. M’timagulu ta mahema tinayi timeneti munali kukhala mabanja a fuko la Levi. Pakati penipeni pa chigono, pamalo otchingidwa ndi khoma la nsalu, panali chimango chapadera. Chimenechi chinali “chihema chokomanako,” kapena chihema, chimene Aisrayeli a “mtima waluso” anamanga malinga ndi pulani ya Yehova.—Numeri 1:52, 53; 2:3, 10, 17, 18, 25; Eksodo 35:10.
5. Kodi chihema chinali ndi chifuno chotani m’Israyeli?
5 Pachigono chilichonse mwa zigono pafupifupi 40 mu ulendo wawo wa m’chipululu, Israyeli anaimikapo chihema, ndipo chinakhala phata la chigono chawo. (Numeri, chaputala 33) Moyenerera, Baibulo limanena kuti Yehova akukhala mwa anthu ake pakati penipeni pa chigono chawo. Ulemerero wake unadzala m’chihemacho. (Eksodo 29:43-46; 40:34; Numeri 5:3; 11:20; 16:3) Buku lakuti Our Living Bible limati: “Kachisi wonyamulika ameneyu anali wofunika kwambiri, popeza anapereka malo a misonkhano yachipembedzo kwa mafukowo. Motero anawagwirizanitsa m’zaka zambiri za kupupulika m’chipululu ndipo anatheketsa kuchitira zinthu pamodzi.” Ndiponso, chihemacho chinakhala chikumbutso chosalekeza chakuti kulambira kwa Aisrayeli Mlengi wawo kunali mbali yofunika kwambiri pa miyoyo yawo.
6, 7. Kodi ndi chimango chiti cholambirirako chimene chinaloŵa m’malo mwa chihema, ndipo chinautumikira motani mtundu wa Israyeli?
6 Aisrayeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa, chihema chinapitiriza kukhala phata la kulambira kwa Israyeli. (Yoswa 18:1; 1 Samueli 1:3) M’kupita kwa nthaŵi, Mfumu Davide analinganiza za kumanga chimango chachikhalire. Chimenechi chinakhala kachisi, amene Solomo mwana wake anamanga pambuyo pake. (2 Samueli 7:1-10) Pa kupatuliridwa kwake mtambo unatsika kusonyeza kuti Yehova anavomereza nyumbayo. “Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo inu,” anapemphera motero Solomo, “ndiyo malo okhalamo inu nthaŵi zosatha.” (1 Mafumu 8:12, 13; 2 Mbiri 6:2) Kachisi womangidwa chatsopano ameneyo panthaŵiyo anakhala phata la kulambira kwa mtunduwo.
7 Katatu pachaka, amuna onse Achiisrayeli ankapita ku Yerusalemu kukapezeka pamapwando osangalatsa pakachisi chifukwa chozindikira dalitso la Mulungu. Moyenerera, mayanjano ameneŵa anatchedwa “nyengo zoikika za Yehova,” akumagogomezera kulambira Mulungu. (Levitiko 23:2, 4) Akazi odzipereka anapezekapo limodzi ndi ziŵalo zina za banja.—1 Samueli 1:3-7; Luka 2:41-44.
8. Kodi Salmo 84:1-12 limasonyeza motani kufunika kwa kulambira Yehova?
8 Amasalmo ouziridwa anavomereza bwino lomwe mmene kulambira kunalili kofunika kwambiri m’miyoyo yawo. “Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu!” anaimba motero ana a Kora. Ndithudi iwo sanali kuthokoza nyumba wamba. M’malo mwake, anafuula kutamanda Yehova Mulungu, akumalengeza kuti: “Mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.” Alevi anapeza chimwemwe chachikulu mu utumiki wawo. “Odala iwo akugonera m’nyumba mwanu;” iwo anatero. “Akulemekezani chilemekezere.” Ndithudi, Aisrayeli onse anakhoza kuimba kuti: “Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu; mumtima mwake muli makwalala. . . . Apita mwamphamvu nawonjezapo mphamvu, aoneka pamaso pa Mulungu m’Ziyoni.” Ngakhale kuti ulendo wa Mwiisrayeli kumka ku Yerusalemu unali wautali ndi wotopetsa, nyonga yake inatsitsimulidwa pamene anafika pamalikulupo. Mtima wake unadzala ndi chimwemwe pamene anatama mwaŵi wake wa kulambira Yehova kuti: “Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa. . . . Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.” Mawu amenewo amasonyeza mmene Aisrayeliwo anapatsira kulambira Yehova malo oyamba.—Salmo 84:1-12.
9. Kodi chinachitikira mtundu wa Israyeli nchiyani pamene unalephera kuika kulambira Yehova pamalo oyamba?
9 Nzachisoni kuti Aisrayeli analephera kuika kulambira koona pamalo oyamba. Iwo analola kulambira milungu yonama kululuza changu chawo kwa Yehova. Chifukwa chake, Yehova anawapereka kwa adani awo, akumalola kuti iwo atengeredwe ku ukapolo ku Babulo. Atabwezeretsedwa kwawo pambuyo pa zaka 70, Yehova anapereka kwa Israyeli machenjezo osonkhezera a aneneri okhulupirikawo Hagai, Zekariya, ndi Malaki. Ezara wansembe ndi Bwanamkubwa Nehemiya anasonkhezera anthu a Mulungu kumanganso kachisi ndi kukhazikitsanso kulambira koona kumeneko. Koma patapita zaka mazana ambiri, kulambira koona kunakhalanso kosafunika kwambiri kwa mtunduwo.
Changu cha m’Zaka za Zana Loyamba cha Kulambira Koona
10, 11. Kodi kulambira Yehova kunali ndi malo otani m’miyoyo ya anthu okhulupirika pamene Yesu anali padziko lapansi?
10 Panthaŵi yoikika ya Yehova, Mesiya anaonekera. Anthu okhulupirika anali kuyembekezera chipulumutso kwa Yehova. (Luka 2:25; 3:15) Cholembedwa cha Uthenga Wabwino wa Luka chimafotokoza molunjika kuti Anna wazaka 84 anali mkazi wamasiye “amene sanachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.”—Luka 2:37.
11 “Chakudya changa,” Yesu anatero, “ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kumbukirani zimene Yesu anachita pamene anayang’anizana ndi osintha ndalama m’kachisi. Anagubuduza magome ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Marko akusimba kuti: “[Yesu] sanalola munthu aliyense kunyamula chotengera kupyola pakati pa Kachisi. Ndipo anaphunzitsa, nanena nawo, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.” (Marko 11:15-17) Inde, Yesu sanalole ngakhale mmodzi yense kudutsa m’bwalo la kachisi pokapereka zinthu kumbali ina ya mzinda. Zimene Yesu anachita zinalimbitsa uphungu wake umene anali atapereka wakuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo [cha Mulungu].” (Mateyu 6:33) Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri pa kupatsa Yehova kudzipereka kwake kotheratu. Iye anachitadi zimene analalikira.—1 Petro 2:21.
12. Kodi ophunzira a Yesu anasonyeza motani kuti anaika kulambira Yehova pamalo oyamba?
12 Ndiponso Yesu anaikira ophunzira ake chitsanzo choti atsatire mwa njira imene anakwaniritsira ntchito yake ya kumasula Ayuda ophwanyika koma okhulupirika ku mtolo wa machitachita a chipembedzo chonyenga. (Luka 4:18) Pomvera lamulo la Yesu la kupanga ophunzira ndi kuwabatiza, Akristu oyambirira analengeza molimba mtima chifuniro cha Yehova mogwirizana ndi Ambuye wawo woukitsidwa. Yehova anakondwera kwambiri ndi kupatsa kwawo malo oyamba kulambira Kwake. Motero, mngelo wa Mulungu anamasula mozizwitsa atumwiwo, Petro ndi Yohane m’ndende nawauza kuti: “Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m’Kachisi kwa anthu onse mawu a Moyo umene.” Atalimbitsidwanso, analabadira. Masiku onse, m’kachisi wa Yerusalemu ndi kunyumba ndi nyumba “sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”—Machitidwe 1:8; 4:29, 30; 5:20, 42; Mateyu 28:19, 20.
13, 14. (a) Chiyambire nthaŵi zoyambirira Zachikristu, kodi Satana wakhala akuyesa kuchitanji kwa atumiki a Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene atumiki a Mulungu okhulupirika apitirizabe kuchita?
13 Pamene chitsutso pa kulalikira kwawo chinakula, Mulungu anatsogolera atumiki ake okhulupirika kulemba uphungu wa panthaŵi yake. ‘Tayani pa [Yehova] nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu,’ analemba motero Petro mwamsanga pambuyo pa 60 C.E. “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu [M]dyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” Ndithudi Akristu oyambirira anapeza chilimbikitso m’mawu amenewo. Iwo anadziŵa kuti atavutika kwa kanthaŵi, Mulungu akamaliza kuphunzira kwawo. (1 Petro 5:7-10) M’masiku otsiriza amenewo a dongosolo la zinthu Lachiyuda, Akristu oona anakweza kulambira Yehova kokondeka kwambiri kumeneko kuposa ndi kale lonse.—Akolose 1:23.
14 Monga momwe mtumwi Paulo anali ataloserera, mpatuko, kutanthauza kuchoka pa kulambira koona, unachitika. (Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3) Umboni wa m’zaka makumi ambiri zomalizira za m’zaka za zana loyamba unasonyeza zimenezi. (1 Yohane 2:18, 19) Satana anafesadi mbewu za Akristu onamizira pakati pa Akristu oona, akumakuchititsa kukhala kovuta kusiyanitsa “namsongole” ameneyu ndi Akristu onga tirigu. Komabe, m’zaka mazana ambiri zapitazo, anthu ena anaika kulambira Mulungu pamalo oyamba, ngakhale kuika miyoyo yawo pachiswe. Koma Mulungu anasonkhanitsanso atumiki ake kuti akweze kulambira koona m’zaka makumi ambiri zomalizira za “nthaŵi zawo za anthu akunja.”—Mateyu 13:24-30, 36-43; Luka 21:24.
Kulambira Yehova Kuli Kokwezeka Lerolino
15. Chiyambire 1919, kodi maulosi a Yesaya 2:2-4 ndi Mika 4:1-4 akwaniritsidwa motani?
15 Mu 1919, Yehova anapatsa mphamvu otsalira odzozedwa kuti ayambe mkupiti wa kuchitira umboni molimba mtima padziko lonse umene wakweza kulambira Mulungu woona. Ndi kubwera kwa makamu a “nkhosa zina” zophiphiritsira kuyambira mu 1935 kufikira lerolino, gulu la anthu amene mwauzimu akukwera “phiri la nyumba ya Yehova” lakhala likukulirakulira. M’chaka chautumiki cha 1993, Mboni za Yehova 4,709,889 zinamtamanda mwa kuitanira ena kugwirizana nazo pa kulambira kwake kokwezeka. Zimenezi zili zosiyana chotani nanga ndi mkhalidwe woipa mwauzimu wa “zitunda” zampatuko za ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, makamaka m’Dziko Lachikristu!—Yohane 10:16; Yesaya 2:2-4; Mika 4:1-4.
16. Kodi atumiki onse a Mulungu afunikira kuchitanji polingalira za zimene zaloseredwa pa Yesaya 2:10-22?
16 Azipembedzo zonyenga amaona matchalitchi awo aang’ono ndi aakulu ndipo ngakhale atsogoleri awo achipembedzo monga “apamwamba,” (NW) akumawapatsa maina ndi ulemu wopambanitsa. Koma tamverani zimene Yesaya analosera: “Maso a munthu akuyang’anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaŵeramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.” Kodi zimenezi zidzachitika liti? Mu chisautso chachikulu chimene chikuyandikira mofulumiracho pamene “mafano adzapita psiti.” Polingalira za kukhala pafupi kwa nthaŵi yowopsa imeneyo, atumiki onse a Mulungu afunikira kupenda mosamalitsa malo amene kulambira Yehova kuli nawo m’miyoyo yawo.—Yesaya 2:10-22.
17. Kodi atumiki a Yehova lerolino amasonyeza motani kuti aika kulambira Yehova pamalo oyamba?
17 Monga gulu la abale la padziko lonse, Mboni za Yehova zili zodziŵika chifukwa cha changu chawo polengeza Ufumu. Kulambira kwawo sikuli kupembedza kwachiphamaso, kochitidwa pafupifupi kwa ola limodzi pamlungu. Ayi, kuli njira ya moyo wawo wonse. (Salmo 145:2) Indedi, chaka chatha Mboni zoposa 620,000 zinalinganiza zochita zawo kuti zikhale ndi phande mu utumiki Wachikristu wanthaŵi yonse. Ndithudi zotsalazo sizimanyalanyaza kulambira Yehova. Kuli mbali yaikulu pa makambitsirano awo atsiku ndi tsiku ndi mu ulaliki wawo wapoyera, ngakhale ngati mathayo awo a banja amafuna kuti zigwire zolimba ntchito yolembedwa.
18, 19. Tchulani zitsanzo za chilimbikitso chimene mungakhale mutalandira mwa kuŵerenga nkhani za moyo wa Mboni.
18 Nkhani za moyo wa Mboni zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda zimapereka chidziŵitso chonena za njira zimene abale ndi alongo osiyanasiyana aikira kulambira Yehova pamalo oyamba m’miyoyo yawo. Mlongo wina wachichepere amene anapatulira moyo wake kwa Yehova pausinkhu wa zaka zisanu ndi chimodzi anaika utumiki waumishonale kukhala chonulirapo chake. Abale ndi alongo achicheperenu, kodi ndi chonulirapo chotani chimene mungasankhe chimene chidzakuthandizani kuika kulambira Yehova pamalo oyamba m’miyoyo yanu?—Onani nkhani yakuti “Kulondola Chonulirapo Choikiridwa Pausinkhu Wazaka Zisanu ndi Chimodzi,” mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1992, masamba 26-30.
19 Mlongo wina wachikulire wamasiye ali chitsanzo china chabwino cha kuika kulambira Yehova pamalo ake oyenera. Anapeza chilimbikitso chachikulu cha kupirira kwa amene anawathandiza kuphunzira choonadi. Iwo anali “banja” lake. (Marko 3:31-35) Ngati mukhala mumkhalidwe wofananawo, kodi mudzavomera kulandira chichirikizo ndi chithandizo cha achichepere mumpingo? (Chonde taonani zimene Mlongo Winifred Remmie anafotokoza m’nkhani yakuti “Ndinalabadira m’Nthaŵi Yakututa,” yofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1992, masamba 21-3.) Inu atumiki anthaŵi yonse, sonyezani kuti kulambira Yehova kulidi koyamba m’miyoyo yanu mwa kutumikira modzichepetsa kumene mwagaŵiridwa, mukumagonjera mwaufulu zitsogozo za teokrase. (Chonde onani chitsanzo cha Mbale Roy Ryan, chosimbidwa m’nkhani yakuti “Kumamatira Zolimba ku Gulu la Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1991, masamba 24-7.) Kumbukirani kuti pamene tiika kulambira Yehova pamalo oyamba, timakhala ndi chitsimikizo chakuti adzatisamalira. Sitifunikira kudera nkhaŵa za kumene tidzapeza zofunika za moyo. Zokumana nazo za Alongowo Olive ndi Sonia Springate zimasonyeza zimenezi.—Onani nkhani yakuti “Tafunafuna Ufumu Choyamba,” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1994, masamba 20-5.
20. Kodi ndi mafunso ati oyenera amene tiyenera kudzifunsa tsopano?
20 Pamenepa, kodi ifeyo aliyense payekha sitifunikira kudzifunsa mafunso ena ofufuza? Kodi kulambira Yehova kuli ndi malo otani m’moyo wanga? Kodi ndikukwaniritsa kudzipatulira kwanga kwa kuchita chifuniro cha Mulungu malinga ndi kukhoza kwanga? Kodi ndi mbali ziti za moyo wanga zimene ndingawongolere? Kulingalira mosamalitsa nkhani yotsatira kudzapereka mpata wa kupenda mmene timagwiritsirira ntchito chuma chathu mogwirizana ndi chinthu choyamba m’moyo chimene tasankha—kulambira Ambuye Mfumu Yehova, Atate wathu wachikondiyo.—Mlaliki 12:13; 2 Akorinto 13:5.
Kupenda
◻ Ponena za kulambira, kodi Yehova amafunanji?
◻ Kodi chihema chinali chikumbutso cha chiyani?
◻ M’zaka za zana loyamba C.E., kodi ndani amene anali zitsanzo zapadera za changu cha kulambira koona, ndipo motani?
◻ Chiyambire 1919, kodi kulambira Yehova kwakhala kokwezeka motani?