Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Mwini Chuma ndi Lazaro Akumana ndi Kusintha
YESU akulongosola fanizo lonena za mwini chuma ndi wopemphapempha wosauka wotchedwa Lazaro. Mwini chumayo akuimira atsogoleri a chipembedzo omwe ayanjidwa ndi mathayo ndi mwaŵi zauzimu, ndipo Lazaro akuchitira chithunzi anthu wamba omwe ali ndi njala kaamba ka kudyetsedwa kwauzimu. Yesu akupitiriza nkhani yake, akumalongosola kusintha kozizwitsa m’mikhalidwe ya anthuwo.
“Ndipo kunali kuti,” Yesu akutero, “wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku chifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m’manda. Ndipo m’Hade anakweza maso ake, pokhala nawo mazunzo, nawona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifuwa mwake.”
Popeza kuti mwini chumayo ndi Lazaro sali anthu enieni koma akuimira magulu a anthu, mwanzeru imfa zawo zirinso zophiphiritsira. Nchiyani chimene imfa zawo zikuphiphiritsira, kapena kuimira?
Yesu wangomaliza kumene kuloza ku kusintha m’mikhalidweyo mwakunena kuti ‘Chilamulo ndi Aneneri analiko kufikira kwa Yohane Mbatizi, kuyambira pamenepo ulalikidwa Ufumu wa Mulungu.’ Chotero, chiri ndi kulalikira kwa Yohane ndi Yesu Kristu kuti onse aŵiri mwini chumayo ndi Lazaro afa ku mikhalidwe yawo yakale, kapena mkhalidwe.
Awo a gulu lodzichepetsa la Lazaro, wolapa akufa ku mkhalidwe wawo wakale womanidwa mwauzimu ndi kukhala m’malo a chiyanjo chaumulungu. Pamene kuli kwakuti kale iwo anayang’ana kwa atsogoleri achipembedzo kaamba ka zochepera zomwe zinagwa kuchokera pa gome lauzimu, tsopano chowonadi cha m’Malemba choperekedwa ndi Yesu chikudzaza zosowa zawo. Iwo mwakutero akubweretsedwa m’chifuwa, kapena m’malo oyanjidwa, a Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu.
Ku mbali ina, awo omwe akupanga gulu la mwini chumalo akubwera pansi pa kupanda chiyanjo chaumulungu chifukwa cha kukana mowumirira kulandira uthenga wa Ufumu wophunzitsidwa ndi Yesu. Iwo mwakutero akufa ku mkhalidwe wawo wakale wowoneka wachiyanjo. M’chenicheni, iwo akulankhulidwa kukhala m’chizunzo chophiphiritsira. Mvetserani pamene mwini chumayo akulankhula:
“Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m’lawi iri la moto.” Mauthenga a chiweruzo cha moto a Mulungu olalikidwa ndi ophunzira a Yesu ali amene akuzunza anthu a m’gulu la mwini chumalo. Iwo akufuna ophunzira a Yesu kuleka kulalikira mauthenga amenewa, mwakutero kuwapatsa iwo ukulu wina wa mpumulo kuchokera ku zizunzo zawo.
“Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuwoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.”
Ndi kolungama ndi koyenerera chotani nanga kutembenuka kozizwitsa kumeneko komwe kukuchitika pakati pa gulu la Lazaro ndi gulu la mwini chuma! Kusintha m’mikhalidweko kukukwaniritsidwa miyezi ingapo pambuyo pake pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene pangano lakale la Chilamulo likulowedwa m’malo ndi pangano latsopano. Icho kenaka chikukhala chowonekera mosakaikira kuti ophunzira ali oyanjidwa ndi Mulungu, osati Afarisi ndi atsogoleri ena a chipembedzo. “Phompho lalikulu” lomwe likulekanitsa mwini chuma wophiphiritsirayo kuchokera kwa ophunzira a Yesu mwakutero likuimira chiweruzo chosasinthika, cholungama cha Mulungu.
Mwini chumayo kenaka akupempha “atate Abrahamu” kutumiza Lazaro “kunyumba ya atate wanga, pakuti ndiri nawo abale asanu.” Mwini chumayo mwakutero akuwulula kuti ali ndi unansi wathithithi kwa tate wina, yemwe m’chenicheni ali Satana Mdyerekezi. Mwini chumayo akupempha kuti Lazaro apeputseko mauthenga a chiweruzo cha Mulungu kotero kuti asaike “abale ake asanu,” ogwirizana nawo ake a chipembedzo, mu “mao ano a mazunzo.”
“Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.” Inde, ngati “abale asanuwo” ati akapulumuke chizunzo, zonse zomwe afunikira kuchita ndi kulabadira zolemba za Mose ndi Aneneri zomwe zimazindikiritsa yesu monga Mesiya ndipo kenaka kukhala ophunzira ake. Koma mwini chumayo akutsutsa kuti: “Ayi, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa akufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.” Mulungu sadzapereka zizindikiro zapadera zoterozo kapena zozizwitsa kuti atsimikizire oterowo. Anthu ayenera kuŵerenga ndi kugwiritsira ntchito Malemba ngati iwo ati akapeze chiyanjo chake. Luka 16:16, 22-31; Yohane 8:44.
◆ Nchifukwa ninji imfa za mwini chuma ndi Lazaro ziyenera kukhala zophiphiritsira, ndipo nchiyani chomwe chikuchitiridwa chithunzi ndi imfa zawo?
◆ Ndi ziti zomwe ziri zizunzo zovutikidwa ndi mwini chuma, ndipo ndi kupyolera mwa njira yotani imene iye akupempha kuti zichotsedwe?
◆ Nchiyani chimene “phompho lalikulu” likuimira?
◆ Ndani amene ali tate weniweni wa mwini chuma, ndipo ndani amene ali abale ake asanu?