Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Akhate Khumi Achiritsidwa Mkati Mwa Ulendo Womaliza wa Yesu Wopita ku Yerusalemu
YESU akusokoneza zoyesayesa za Bwalo Lalikulu la Milandu la Ayuda za kumupha iye mwa kuchoka ku Yerusalemu ndi kupita ku mzinda wa Efraimu, mwinamwake kokha makilomita 24 kapena ochulukirako kumpoto cha kum’mawa kwa Yerusalemu. Kumeneko akukhala ndi ophunzira ake, kutali ndi adani ake.
Ngakhale kuli tero, nthaŵi ya Paskha ya 33 C.E. ikuyandikira, ndipo mofulumira Yesu alinso pa ulendo. Iye akuyenda kudzera ku Samariya ndi kufika kuloŵa mu Galileya. Uwu ndi ulendo wake womalizira ku gawo limeneli imfa yake isanafike. Pamene ali mu Galileya, mwachidziŵikire iye ndi ophunzira ake agwirizana ndi ena omwe ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu kaamba ka phwando la Paskha. Iwo atenga njira yodzera m’boma la Pereya, kum’mawa kwa Mtsinje wa Yordano.
Kuchiyambiyambi kwa ulendowo, pamene Yesu akuloŵa m’mudzi kaya mu Samariya kapena mu Galileya, iye akumana ndi amuna khumi omwe ali ndi khate. Nthenda yowopsya imeneyi mwapang’onopang’ono imadya ziŵalo zathupi la munthu—zala zake zakumanja, zala zake zakumapazi, makutu ake, mphuno yake, ndi milomo yake. Kuti achinjirize ena kusayambukiridwa, Chilamulo cha Mulungu chikunena ponena za wakhate kuti: “Aphimbe iye mlomo wake wam’mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa! Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa. . . . Akhale kunja kwa chigono.”
Akhate khumiwo akusunga ziletso za Chilamulo kaamba ka akhate ndipo akukhala pa mtunda wautali kuchoka kwa Yesu. Komabe, iwo akufuula ndi mawu okweza akumati: “Yesu, [Mlangizi, NW] mutichitire chifundo.”
Akumawawona iwo patali, Yesu akulamula kuti: “Pitani, kadziwonetseni nokha kwa ansembe.” Yesu akunena ichi chifukwa chakuti Chilamulo cha Mulungu chimavomereza ansembe kulengeza kukhala ochiritsidwa akhate omwe achira kuchokera ku kudwala kwawo. Mwanjira imeneyi oterowo amalandira chivomerezo cha kukhalanso ndi anthu aumoyo.
Akhate khumiwo ali ndi chidaliro mu mphamvu zozizwitsa za Yesu. Chotero akuthamanga kukawona ansembe, ngakhale kuti sanachiritsidwebe. Pamene ali pa ulendo, chikhulupiriro chawo mwa Yesu chifupidwa. Iwo ayamba kuwona ndi kumva umoyo wawo wobwezeretsedwa!
Asanu ndi anayi a akhate oyeretsedwawo apitirizabe pa ulendo wawo, koma wakhate winayo, m’Samariya, abwerera kukafunafuna Yesu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ali woyamikira kwenikweni kaamba ka chimene chachitika kwa iye. Iye atamanda Mulungu ndi mawu okweza, ndipo pamene ampeza Yesu, akugwa pa mapazi ake, kumuyamika iye.
M’kuyankha Yesu akuti: “Kodi sanakonzedwa khumi? Koma ali kuti asanu ndi anayi aja? Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?”
Kenaka iye akuwuza m’Samariyayo kuti: “Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.”
Pamene tiŵerenga ponena za kuchiritsa akhate khumi kwa Yesu, tiyenera kutenga ku mtima phunziro lotanthauzidwa ndi funso lake lakuti: “Koma ali kuti asanu ndi anayi aja?” Kusayamikira komwe kunasonyezedwa ndi asanu ndi anayiwo kuli kuphophonya kwakukulu. Kodi ife, mofanana ndi m’Samariyayo, tidzadzisonyeza ife eni kukhala oyamikira kaamba ka zinthu zimene timalandira kuchokera kwa Mulungu, kuphatikizapo lonjezo lotsimikizirika la moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama la Mulungu? Yohane 11:54, 55; Luka 17:11-19; Levitiko 13:16, 17, 45, 46; Chibvumbulutso 21:3, 4.
◆ Ndimotani mmene Yesu akusokonezera zoyesayesa za kumupha iye?
◆ Ndi kuti kumene Yesu kenaka akupita, ndipo ndi ati omwe ali malo amene akafika?
◆ Nchifukwa ninji akhate akuima patali, ndipo nchifukwa ninji Yesu akuwawuza iwo kupita kwa ansembe?
◆ Kodi ndi phunziro lotani limene tiyenera kuphunzira kuchokera ku chokumana nacho chimenechi?
[Chithunzi chachikulu patsamba 9]