MUTU 93
Mwana wa Munthu Adzaonekera
UFUMU UNALI PAKATI PAWO
N’CHIYANI CHIDZACHITIKE YESU AKADZAONEKERA?
N’kutheka kuti Yesu anali akadali ku Samariya kapena ku Galileya pamene Afarisi ankamufunsa kuti Ufumu udzabwera liti. Iwo ankayembekezera kuti padzachitika zinthu zapamwamba komanso chikondwerero chachikulu Ufumuwu ukadzabwera. Koma Yesu anawayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi. Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani kuno!’ kapena, ‘Uko!’ Pakuti ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”—Luka 17:20, 21.
Chifukwa cha zimene Yesu ananenazi, anthu ena amaganiza kuti Yesu ankatanthauza kuti Ufumu umakhala mumtima mwa munthu ndipo umalamulira moyo komanso zochita za atumiki a Mulungu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Ufumu sunali mumtima mwa Afarisi amene Yesu ankalankhula nawo. Ufumu wa Mulunguwo unali pakati pawo chifukwa Yesu, yemwe anasankhidwa kuti adzalamulire mu Ufumuwo, anali pakati pawo.—Mateyu 21:5.
Yesu anauza ophunzira ake zinthu zina zimene zidzachitike Ufumuwo ukamadzabwera ndipo ayenera kuti ananena zimenezi Afarisi aja atachoka. Pofotokoza zimene zidzachitike akadzayamba kulamulira monga Mfumu, Yesu anayamba ndi kuwachenjeza kuti: “Adzafika masiku pamene mudzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu koma simudzaliona.” (Luka 17:22) Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti Mwana wa munthu adzayamba kulamulira mu Ufumu m’tsogolo. Nthawi imeneyo isanafike, ophunzira ena adzafunafuna Ufumuwo mwakhama koma adzafunika kudikirabe mpaka nthawi imene Mulungu anakonza kuti Mwana wa munthu adzabwere itakwana.
Yesu ananenanso kuti: “Anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani uko!’ kapena ‘Onani kuno!’ Musadzapiteko kapena kuwatsatira. Pakuti monga mphezi, mwa kung’anima kwake, imawala kuchokera mbali ina pansi pa thambo kukafika mbali ina pansi pa thambo, zidzakhalanso choncho ndi Mwana wa munthu.” (Luka 17:23, 24) Kodi ophunzira a Yesu akanatani kuti asadzatsatire anthu amene adzanamizire kuti ndi mesiya? Yesu ananena kuti Mesiya weniweni adzaonekera ngati kuwala kwa mphezi kumene kumaonekera malo aakulu. Zizindikiro zosonyeza kuti Yesu wayamba kulamulira zidzaonekera bwino kwambiri kwa anthu onse amene akuyembekezera Ufumuwo mwachidwi.
Kenako Yesu anayerekezera zinthu zina zomwe zinachitikapo m’mbuyomo pofuna kusonyeza mmene khalidwe la anthu lidzakhalire nthawiyo ikadzafika. Iye anati: “Monga zinachitikira m’masiku a Nowa, zidzachitikanso chimodzimodzi m’masiku a Mwana wa munthu. . . . Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika m’masiku a Loti. M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala ndi kumanga. Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula n’kuwononga anthu onse. Zidzakhalanso choncho pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekera.”—Luka 17:26-30.
Yesu sankatanthauza kuti anthu a m’nthawi ya Nowa komanso ya Loti anawonongedwa chifukwa chakuti ankachita zinthu zimene anthu amachita nthawi zonse ngati kudya, kumwa, kugula ndi kugulitsa malonda, kulima komanso kumanga nyumba. Ndipotu Nowa ndi Loti komanso mabanja awo ankachitanso zinthu zimenezi. Koma anthu amene anawonongedwawo sankaganizira zimene Mulungu ankafuna ndipo ankanyalanyaza zizindikiro za nthawi imene ankakhala. N’chifukwa chake Yesu analangiza ophunzira ake kuti azichita zimene Mulungu amafuna komanso kuti azigwira ntchito yomwe ikanawathandiza kukhala tcheru. Choncho tinganene kuti Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa zimene angadzachite kuti adzapulumuke pa nthawi imene Mulungu adzawononge anthu oipa.
Ophunzirawo sanafunike kusokonezedwa ndi zinthu za m’dzikoli zomwe zili ngati zinthu za “m’mbuyo.” Yesu ananena kuti: “Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali m’nyumbamo, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya m’mbuyo. Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:31, 32) Paja mkazi wa Loti anasanduka chulu cha mchere.
Popitiriza kufotokoza zimene zidzachitike Mwana wa munthu akadzayamba kulamulira monga Mfumu, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Usiku umenewo amuna awiri adzagonera limodzi pamphasa. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.” (Luka 17:34) Zimenezi zikutanthauza kuti anthu ena adzapulumuka pomwe anthu ena adzasiyidwa kapena kuti kuwonongedwa.
Ndiyeno ophunzirawo anafunsa Yesu kuti: “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti Ambuye?” Yesu anawayankha kuti: “Kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zidzasonkhana komweko.” (Luka 17:37) Ophunzira ena adzakhala ndi diso loona patali ngati ziwombankhanga ndipo adzasonkhana kwa Khristu weniweni amene ndi Mwana wa munthu. Pa nthawi imeneyo, Yesu adzaphunzitsa ophunzira ake choonadi chomwe chidzawathandize kuti adzapeze moyo chifukwa chakuti amamukhulupirira.